“Wosamalira Chidzudzulo Amachenjera”
LEMBA la Miyambo 23:12 limati: “Lozetsa mtima wako kumwambo, ndi makutu ako ku mawu a nzeru.” Mu lembali, “mwambo,” kapena kuti kuphunzira khalidwe labwino, kumaphatikizapo kudziletsa ndiponso chidzudzulo chimene ena amatipatsa. Zimenezi zimafuna kudziwa chilangizo choyenera kuperekedwa komanso mmene tingachiperekere. Choncho, popereka mwambo, n’kofunika kugwiritsa ntchito “mawu a nzeru” ochokera ku gwero lodalirika.
Buku la Baibulo la Miyambo ndi gwero labwino kwambiri la mawu a nzeru. Miyambi imene inalembedwa m’bukuli imathandiza munthu “kudziwa nzeru ndi mwambo, . . . kulandira mwambo wakusamalira machitidwe, chilungamo, chiweruzo ndi zolunjika.” (Miyambo 1:1-3) Tingakhale anzeru ngati ‘timvera’ miyambi imeneyi. Chaputala 15 cha Miyambo chimapereka chitsogozo chodalirika cha mmene tingalamulirire mkwiyo, mmene tingagwiritsire ntchito lilime, ndiponso mmene tingaphunzitsire. Tiyeni tione mavesi ena a m’chaputala chimenechi.
N’chiyani Chomwe ‘Chimabweza Mkwiyo’?
Polongosola za mmene mawu angayambitsire msunamo kapena mkwiyo, Solomo, mfumu ya Israyeli wakale anati: “Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mawu owawitsa aputa msunamo.” (Miyambo 15:1) Kodi ndi motani mmene mwambi umenewu ungatithandizire kudziwa mmene tingachitire ndi mkwiyo wa munthu wina kapena mkwiyo wathu womwe?
Mawu okhadzula amene amachititsa munthu kumva ululu, angapangitse munthu yemwe wakwiya kale kukwiya mopitirira. Mosiyana ndi zimenezo, mayankhidwe ofatsa ali ndi mphamvu yoziziritsa. Koma kumuyankha mofatsa munthu amene wakwiya, si kophweka. Komabe, kungakhale kosavuta kuyankha mofatsa ngati tikuyesa kumvetsetsa chimene chapangitsa munthuyo kukwiya. Baibulo limati: “Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.” (Miyambo 19:11) Kodi zingatheke kuti munthuyo wakwiya chifukwa chakuti ali ndi nkhawa kapena kuti akufuna chisamaliro? Mwina chifukwa chenicheni chimene wakwiya nacho sichingakhale chimene ife talankhula kapena kuchita. Munthu akatikwiyira tili mu utumiki wachikristu, kodi kawirikawiri sichikhala chifukwa chakuti mwininyumbayo ananamizidwa za zimene ife timakhulupirira kapena kuti mwina anangochititsidwa khungu ndi mabodza ena? Kodi ifenso tingabwezere kuyankha mwamwano ngati kuti anthuwo akuyambana nafe? Ngakhale ngati sitikudziwa zimene zachititsa munthu wina kukwiya, kuyankha ndi mawu omwe angam’chititse wina kumva kuwawa kungasonyeze kuti ndife osadziletsa. Tiyenera kupewa mayankhidwe oterowo.
Uphungu woyankha mofatsa n’ngofunikanso kwambiri pankhani yolamulira mkwiyo wathu. Tingagwiritse ntchito uphungu umenewo mwa kuphunzira kulankhula maganizo athu m’njira yosakhumudwitsa anthu amene akutimvetsera. Tikamalankhula ndi anthu a m’banja mwathu, m’malo molankhula mwamwano kapena kutchulana maina achipongwe, tingayese kulankhula maganizo athu mofatsa. Kulankhula mokwiya kawirikawiri kumachititsa kuti munthu winayo abwezere. Kuuza munthu mofatsa za mmene tikumvera, kumachititsa munthu wina uja kumva kuti sitikumuimba mlandu ndipo tingathe kum’pangitsa kuti asinthe khalidwe lakelo kapena kuti apepese.
“Lilime la Anzeru Linena Bwino”
Kudziletsa kumakhudza mmene timalankhulira ngakhalenso zimene timalankhula. Solomo anati: “Lilime la anzeru linena bwino zomwe adziwa; koma m’kamwa mwa opusa mutsanulira utsiru.” (Miyambo 15:2) Tikakulitsa mtima wofuna kuthandiza ena ndi kuwauza za chifuniro cha Mulungu ndiponso zinthu zabwino zimene iye amatipatsa, kodi sindiye kuti ‘tikunena bwino zomwe tidziwa?’ Munthu wopusa amalephera kuchita zimenezi chifukwa palibe chimene akudziwa.
Asanapitirize kupereka chitsogozo pa kagwiritsidwe ntchito ka lilime, Solomo anaperekanso mfundo yosiyana yochititsa chidwi yakuti: “Maso a Yehova ali ponseponse, nayang’anira oipa ndi abwino.” (Miyambo 15:3) Tingasangalale ndi mawuwa chifukwa akutitsimikizira kuti: “Maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.” (2 Mbiri 16:9) Mulungu amadziwa ngati tikuchita bwino. Iye amaonanso anthu amene akuchita zoipa ndipo amawaimba mlandu.
Solomo anagogomezeranso kufunika kwa lilime lofatsa, kuti: “Kuchiza lilime ndiko mtengo wa moyo; koma likakhota liswa moyo.” (Miyambo 15:4) Mawu akuti “mtengo wa moyo” akunena za mphamvu yochiritsa ndi yolimbikitsa. (Chivumbulutso 22:2) Zolankhula za munthu wanzeru zimatsitsimula moyo wa anthu amene akumvetsera. Zimalimbikitsa makhalidwe awo abwino. Koma mosiyana ndi zimenezo, lilime lonyenga kapena lokhota limapangitsa moyo wa anthu amene akumvetsera kusweka.
Kulandira Mwambo ndi “Kuwanditsa Nzeru”
Mfumu ya nzeruyi inapitiriza kuti: “Chitsiru chipeputsa mwambo wa atate wake; koma wosamalira chidzudzulo amachenjera.” (Miyambo 15:5) Munthu ‘angasamalire bwanji chidzudzulo’ asanapatsidwe? Kodi lembali silikutanthauza kuti munthu ayenera kupatsidwa chilango ngati chikufunika? Ndi udindo wa makolo m’banja, makamaka bambo, kupereka chilango ndiponso mwana ali ndi udindo wolandira chilangocho. (Aefeso 6:1-3) Komabe, atumiki onse a Yehova amalandira chilango m’njira zosiyanasiyana. Lemba la Ahebri 12:6 limati: “Pakuti iye amene Ambuye am’konda amulanga, nakwapula mwana aliyense amulandira.” Mmene timachitira tikalandira chilango zimasonyeza ngati tili anzeru kapena opusa.
Polankhulanso za kusiyana kwina, Solomo anati: “Milomo ya anzeru iwanditsa nzeru, koma mtima wa opusa suli wolungama.” (Miyambo 15:7) Kuwanditsa nzeru kuli ngati kumwaza mbewu. M’nthawi zakale, mlimi sankadzala mbewu zonse pamalo amodzi. Iye ankamwaza mbewu, mpaka munda wonse utatha. Choncho n’zofanana ndi kuwanditsa nzeru. Mwachitsanzo, ngati titakumana ndi munthu wina muutumiki, sichingakhale chinthu chanzeru kulankhula naye zonse za m’Baibulo zimene tikudziwa nthawi imodzi. M’malo mwake, munthu wanzeru amaona zimene akulankhula. Iye ‘amawanditsa’ nzeru akamalongosola pang’onopang’ono mfundo imodzi ya choonadi cha m’Baibulo n’kumaifutukula, mogwirizana ndi mmene wophunzira wakeyo akumvera. Yesu Kristu yemwe ndi chitsanzo chathu, anachita zimenezi pamene ankalankhula ndi mkazi wachisamariya.—Yohane 4:7-26.
Kuphunzitsa munthu kumaphatikizapo kulankhula mfundo yomangirira ndiponso yolimbikitsa. Kuti munthu athe kulangiza ndi kulimbikitsa ena amafunika kuganiza. N’chifukwa chake “mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe.” (Miyambo 15:28) Choncho, n’kofunika kwambiri kuti mawu athu azikhala ngati mvula yomagwa pang’onopang’ono imene imalowa m’nthaka ndipo imathandiza, osati ngati madzi osefukira amene amakokolola chilichonse chimene apeza.
‘Oyera M’makhalidwe’
Kuwanditsa nzeru zonena za Yehova ndi cholinga chake ndiponso kupereka kwa iye “chipatso cha milomo” monga “nsembe yakuyamika” n’chinthu chanzeru kwambiri kuchita. (Ahebri 13:15) Komabe, kuti Yehova alandire nsembe imeneyi, tiyenera kukhala ‘oyera m’makhalidwe athu onse.’ (1 Petro 1:14-16) Pogwiritsa ntchito miyambi iwiri yosiyanayi, Solomo mwamphamvu akutiuza choonadi chofunika ichi: “Nsembe ya oipa inyansa Yehova; koma pemphero la oongoka mtima lim’kondweretsa. Njira ya oipa inyansa Yehova; koma akonda wolondola chilungamo.”—Miyambo 15:8, 9.
Kodi anthu amene amasiya njira ya kumoyo amaona bwanji chidzudzulo, ndipo kodi n’zotsatira zanji zimene anthu oterowo adzakumane nazo? (Mateyu 7:13, 14) “Wosiya njira adzalangidwa mowawa; wakuda chidzudzulo adzafa.” (Miyambo 15:10) M’malo molandira uphungu wochokera kwa anthu amene ali ndi udindo mumpingo wachikristu ndi kulapa moona mtima, ena amene akuchita zinthu zolakwika amasankha kusiya njira ya chilungamo. Kuchita motero n’kupusa.
Nanga Bwanji ngati munthu wina akuoneka ngati akulandira chidzudzulo koma mumtima mwake akudana nacho? Kumenekunso n’kupanda nzeru. Mfumu ya Israyeli inati: “Kumanda ndi kuchiwonongeko kuli pamaso pa Yehova; koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu?” (Miyambo 15:11) Palibe chinthu chimene mophiphiritsa chingakhale kutali ndi Mulungu wa moyo koposa manda. Komabe malo amenewo ali pamaso pake. Iye amadziwa maonekedwe ndi mtima wa munthu aliyense amene ali kumeneko ndipo adzawaukitsa. (Salmo 139:8; Yohane 5:28, 29) N’kosavuta kwa Yehova kudziwa zimene zili m’mitima ya anthu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.” (Ahebri 4:13) Munthu angathe kupusitsa mnzake koma osati Mulungu.
Munthu amene amakana chilango samangodana ndi chidzudzulocho koma amanyozanso amene akuchipereka. Solomo anati: “Wonyoza sakonda kudzudzulidwa.” Kuti amveketse bwino maganizowo, anatchulanso maganizo ena ofanana nawo akuti: “Samapita kwa anzeru.” (Miyambo 15:12) N’zoonadi kuti pali chiyembekezo chochepa cha munthu wotero kuti asinthe njira yake.
Kusataya Mtima
Mawu akuti “mtima” akutchulidwa molumikiza miyambi itatu yotsatirayi ya Solomo. Polongosola za kugwirizana kwa mmene tikumvera mumtima mwathu ndi mmene nkhope yathu imaonekera, mfumu yanzeruyi inati: “Mtima wokondwa usekeretsa nkhope; koma moyo umasweka ndi zowawa za m’mtima.”—Miyambo 15:13.
Kodi n’chiyani chimene chingapangitse ululu wa mumtima? Baibulo limati: “Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu [ndi chisoni].” (Miyambo 12:25) Nanga tingachite chiyani kuti mavuto amoyo asatiswe mtima? M’malo momangoganiza za zinthu zimene sitingathe kuzithetsa, tingaganize za madalitso ochuluka auzimu amene Yehova watipatsa panopa ndiponso zimene adzatichitira m’tsogolo. Kuteroko kungatipangitse kuti timuyandikire. Inde, kukhala pafupi ndi “Mulungu wa chisangalalo” sikudzalephera kutibweretsera chimwemwe m’mitima yathu yachisoni.—1 Timoteo 1:11, NW.
Chinanso n’chakuti, uthenga wa m’Baibulo ndi gwero labwino kwambiri la chitonthozo ndi chimwemwe. Wamasalmo analongosola kuti munthu wachimwemwe ndi amene “m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.” (Salmo 1:1, 2) Ngakhale ngati titakhala ndi ululu mu mtima, kuwerenga Baibulo ndi kuganizira za zimene limanena kungatilimbikitse. Komanso tili ndi utumiki umene Mulungu watipatsa. Iye amatitsimikizira kuti: “Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera.”—Salmo 126:5.
Solomo anati: “Mtima wa wozindikira ufunitsa kudziwa; koma m’kamwa mwa opusa mudya utsiru.” (Miyambo 15:14) Mwambi umenewu ukutiuza za kusiyana kwakukulu kumene kuli pakati pa uphungu wa munthu wanzeru ndi wa munthu wopusa. Asanapereke malangizo, munthu amene ali ndi mtima wozindikira amafunafuna kudziwa. Amamvetsera bwino ndi kumvetsa nkhani yonse. Amafufuza Malemba kuti aphunzire malamulo ndi mfundo zoti akagwiritse ntchito pa nkhaniyo. Uphungu wake umakhala wochokera m’Mawu a Mulungu basi. Komabe, munthu wopusa sasamala zoti amvetsetse nkhani ndipo amangolankhula zimene zabwera m’mutu mwake. Choncho tikamafunafuna uphungu, n’chinthu chanzeru kupita kwa anthu ozindikira, ndi okhwima maganizo m’malo mopita kwa anthu amene angafune kutiuza zimene ife tikufuna kumva. N’zolimbikitsa kuti tili ndi “mphatso za amuna” mu mpingo wachikristu, amene ‘amafunafuna kudziwa’ asanapereke uphungu.—Aefeso 4:8, NW.
Mwambi wotsatira ukulongosola za phindu la kusataya mtima. Mfumu ya Israyeli inati: “Masiku onse a wosauka ali oipa; koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.” (Miyambo 15:15) Moyo uli ndi nthawi yosangalatsa ndi nthawi yamavuto, chimwemwe ndi kulira. Choncho, tikamangoganiza za mavuto, chisoni chingadzaze mu mtima mwathu, ndipo masiku onse amoyo wathu angakhale osasangalatsa. Komabe, tikamaganiza za madalitso amene tili nawo ndiponso chiyembekezo chimene Mulungu watipatsa, mavuto a moyo wathu adzaiwalika ndipo tidzakhala ndi chimwemwe cha mumtima. Chifukwa cha kusataya mtima, tidzasangalala ndi “phwando losatha.”
Choncho, tiyeni tisamalire chidzudzulo. Tichilole chikhudze mtima wathu, kalankhulidwe kathu ndi mmene timaonera zinthu.
[Chithunzi patsamba 13]
“Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo”
[Chithunzi patsamba 15]
Kupereka chilango ndi udindo wa makolo
[Chithunzi patsamba 15]
“Milomo ya anzeru iwanditsa nzeru”