“Zolingalira Zako Zidzakhazikika”
WAMASALMO Davide ananena izi m’nyimbo imene analemba: “Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m’kati mwanga. Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu; ndipo mzimu wakulola undigwirizize.” (Salmo 51:10, 12) Pambuyo pochita tchimo ndi Bateseba, Davide anasonyeza mtima wolapa. Ndipotu palembali Davideyu anachonderera Yehova Mulungu kuti ayeretse mtima wake ndi kukonza mzimu wake, n’cholinga choti azitha kuchita zinthu zabwino.
Kodi Yehova amatilengeradi mtima watsopano, ngakhalenso kutiikira mzimu watsopano wakulola kapena kuti wofunitsitsa m’kati mwathu? Kapena kodi ifeyo ndi amene tiyenera kuyesetsa kuti tikhale ndi mtima woyera ndiponso kuyesetsa kuuteteza? N’zoona kuti “Yehova [amayesa] mitima.” Koma kodi iye amayesa kapena kuunika zimene zili m’mitima yathu mpaka kufika pati? (Miyambo 17:3; Yeremiya 17:10) Ndipo Yehovayu amafika mpaka pati akamatsogolera moyo wathu, zolinga zathu, ndiponso zochita zathu?
Chaputala 16 cha buku la Miyambo chikusonyeza mmene tingachitire kuti Mulungu azititsogolera n’cholinga choti mapulani athu, kapena kuti ‘zolingalira zathu zikhazikike.’ (Miyambo 16:3) M’chaputala chimenechi, dzina la Mulungu likupezekamo ka eyiti, ndipo mavesi 10 mpaka 15 akutchula za udindo wa mfumu kapena wolamulira.
Ndani Ayenera ‘Kulongosola Mtima’?
“Malongosoledwe a mtima nga munthu,” limatero lemba la Miyambo 16:1a. N’zoonekeratu kuti ndi udindo wathu ‘kulongosola mtima’ wathu. Sikuti Yehova amakonza mtima wathu kapena kutipatsa mzimu wofunitsitsa m’njira yodabwitsa. Tiyenera kuchita khama kuti tidziwe molondola Mawu ake Baibulo, kusinkhasinkha zimene tikuphunzirazo, ndiponso kugwirizanitsa maganizo athu ndi ake.—Miyambo 2:10, 11.
Zikuoneka kuti Davide anazindikira chizolowezi chake chochita tchimo, choncho anapempha kwa Mulungu “mtima woyera” ndi “mzimu [watsopano],” n’cholinga choti ayeretse mtima wake. Chifukwa choti ndife opanda ungwiro, nthawi zina tingakopeke kuti tichite “ntchito za thupi.” (Agalatiya 5:19-21) Tikufunikira thandizo la Yehova kuti tichititse “ziwalo za thupi [lathu] pa dziko lapansi kukhala zakufa ku dama, chonyansa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje.” (Akolose 3:5) Tikufunikiradi kumapemphera kwambiri kuti Yehova atithandize kupewa ziyeso ndiponso kuti tichotse zizolowezi zauchimo m’mitima yathu.
Kodi tingathandize ena ‘kulongosola’ mitima yawo? Baibulo limati, “alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga, koma lilime la anzeru lilamitsa.” (Miyambo 12:18) Kodi lilime lathu lingalamitse kapena kuti kuchiritsa ena motani? Lingatero pamene “mayankhidwe a lilime achokera kwa Yehova.” Zimenezi zikutanthauza kulankhula mawu ogwirizana ndi choonadi cha m’Baibulo.—Miyambo 16:1b.
“Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika,” limatero Baibulo. (Yeremiya 17:9) Mtima wathu wophiphiritsa umatichititsa kuti tizidzilungamitsa ndiponso kudzinyenga tokha. Pochenjeza za ngozi imeneyi, Mfumu Solomo ya Isiraeli wakale inati: “Njira zonse za munthu ziyera pamaso pake; koma Yehova ayesa mizimu.”—Miyambo 16:2.
Kudzikonda kungatichititse kusavomereza zolakwa zathu, kubisa makhalidwe athu oipa, ndiponso kusaona zolakwa zathu. Komatu Yehova sangapusitsidwe. Iye amayesa mizimu, kapena kuti mitima. Mzimu umene ukutchulidwa pano ndi zimene munthu amaganiza nthawi zonse ndipo n’ngogwirizana ndi mtima wake. Ndipotu mzimu umenewu umagwirizana kwambiri ndi mtima wathu wophiphiritsa womwe ndi maganizo athu, zolinga zathu, ndiponso mmene tikumvera. Mzimu ndi umene umayesedwa ndi Yehova yemwe ndi ‘woyesa mitima,’ ndipo iye amaweruza mosakondera ndiponso mopanda tsankho. Choncho ndibwino kutetezera mzimu wathu.
“Pereka Zochita Zako kwa Yehova”
Kukonza zolingalira, kapena kuti mapulani kumafuna kuganiza ndithu, ndipo kuganizako kumagwirizana kwambiri ndi mtima wathu. Kenaka timachita zinthu mogwirizana ndi mapulani athuwo. Koma kodi tingatani kuti mapulani athu agwire bwino ntchito? Solomo anati: “Pereka zochita zako kwa Yehova, ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.” (Miyambo 16:3) Kupereka zochita zathu kwa Yehova kukutanthauza kum’khulupirira, kum’dalira, ndi kugonjera ulamuliro wake. Tikamachita zimenezi ndiye kuti tikum’senza nkhawa zathu. Wamasalmo anayimba kuti: “Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso iye, adzachichita.”—Salmo 37:5.
Komano kuti mapulani athu akhazikike, ayenera kukhala ogwirizana ndi Mawu a Mulungu ndiponso zolinga za mapulaniwo zikhale zabwino. Kuwonjezera apo, tiyenera kupemphera kwa Yehova kuti atithandize ndi kutichirikiza, ndipo tikatero tiziyesetsa mwakhama kutsatira malangizo a m’Baibulo. M’pofunika kwambiri ‘kum’senza Yehova nkhawa zathu’ makamaka panthawi imene tili m’mavuto kapena tikamayesedwa, ndipo ‘iye adzatigwiriziza.’ Inde, “nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.”—Salmo 55:22.
“Zonse Yehova Anazipanga Zili Ndi Zifukwa Zawo”
Kodi chinanso n’chiyani chimene chingachitike ngati titapereka zochita zathu kwa Yehova? Mfumu yanzeruyi inati: “Zonse Yehova anazipanga zili ndi zifukwa zawo.” (Miyambo 16:4a) Mlengi wa chilengedwe chonsechi ndi Mulungu amene ali ndi zolinga. Tikapereka zochita zathu kwa iye, zochita zathu zonse zimakhala zopindulitsa, osati zachabechabe kapena zogwiritsa mwala. Ndipo Yehova ali ndi cholinga choti dziko lapansili pamodzi ndi anthu adzakhale kosatha. (Aefeso 3:11) Iye analenga dziko lapansili kuti “akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18) Komanso, n’zosakayikitsa kuti cholinga chake choyambirira chimene analengera anthu padziko lapansili chidzakwaniritsidwa. (Genesis 1:28) Motero kukhala wodzipereka kwa Mulungu woona n’kofunika kuti tikhale ndi moyo wopindulitsa komanso tidzakhale ndi moyo wosatha.
Yehova wapanga “ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa.” (Miyambo 16:4b) Iye sanalenge anthu oipa, chifukwatu “ntchito yake ndi yangwiro.” (Deuteronomo 32:4) Koma walola anthu oipawa kuti apitirize kukhalapo mpaka panthawi imene iye adzaone kuti n’njoyenera kuwaononga. Mwachitsanzo, Yehova anauza Farao, mfumu ya ku Iguputo kuti: “Chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi.” (Eksodo 9:16) Milili Khumi ndiponso kuwonongedwa kwa Farao limodzi ndi magulu ake ankhondo pa Nyanja Yofiira, n’chinthu chosaiwalika chosonyeza kuti Mulungu ali ndi mphamvu zosayerekezereka.
Yehova angachititsenso zinthu m’njira yoti anthu oipa akwaniritse zolinga zake mosadziwa. Wamasalmo anati: “Indedi, kuzaza [kapena kuti kukalipa] kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.” (Salmo 76:10) Yehova angalole kuti adani ake akwiyire atumiki ake, koma osati mopitirira muyeso, n’cholinga choti atumiki akewo alangidwe ndiponso aphunzirepo kanthu. Ndipo akachita zimenezi mopitirira malire, Mulungu amachitapo kanthu.
Yehova amachilikiza atumiki ake odzichepetsa. Nanga bwanji anthu onyada ndi odzikuza? “Yense wonyada mtima anyansa Yehova,” inatero mfumu ya ku Isiraeli. “Zoonadi sadzapulumuka chilango.” (Miyambo 16:5) Anthu ‘onyada mtima’ angasonkhane pamodzi mwa kupanga mgwirizano, koma sangathe kuzemba chilango. Choncho, kaya timadziwa zinthu zochuluka bwanji, kapena tili ndi udindo wotani, ndibwino kuti tikhale odzichepetsa kwambiri.
“Poopa Yehova”
Popeza tinabadwa mu uchimo, anthufe nthawi zambiri timachita zolakwa. (Aroma 3:23; 5:12) Nangano n’chiyani chimene chingatithandize kuti tizipewa kupanga zinthu zimene zingatigwetse m’mavuto? Lemba la Miyambo 16:6 limati: “Mphulupulu iwomboledwa ndi chifundo ndi ntheradi; apatuka pa zoipa poopa Yehova.” Yehova amatikhululukira machimo athu mwachisomo ndi kukoma mtima kwake. Komano kuopa Yehova n’kumene kumatiteteza kuti tisachite tchimo. Choncho, m’pofunikatu kwambiri kuti tisamangokonda chabe Mulungu ndi kuyamikira chifundo chake, komanso tiziopa kum’kwiyitsa.
Timayamba kuopa Mulungu kuchokera mu mtima mwathu tikayamba kumamulemekeza kwambiri chifukwa cha mphamvu zake zosaneneka. Tangoganizirani mphamvu zake zimene timaziona m’chilengedwechi. Kuona mphamvu za Mulungu m’zinthu zimene analenga kunathandiza Yobu kuwongolera maganizo ake olakwika. (Yobu 42:1-6) Ifenso tingachite chimodzimodzi tikamawerenga ndi kusinkhasinkha nkhani zolembedwa m’Baibulo zofotokoza mmene Yehova anachitira zinthu ndi anthu ake. Wamasalmo anaimba kuti: “Idzani, muone ntchito za Mulungu; zochitira iye ana a anthu n’zoopsa.” (Salmo 66:5) Tisayese dala kuchita tchimo chifukwa choti Yehova n’ngwachifundo. Aisiraeli ‘atapandukira Mulungu ndi kumvetsa chisoni mzimu wake woyera, Yehova anasandulika mdani wawo, nawathira nkhondo iye yekha.’ (Yesaya 63:10) Mosiyana ndi zimenezo, “njira za munthu zikakonda Yehova, ayanjanitsana naye ngakhale adani ake.” (Miyambo 16:7) Kuopa Yehova kumatitetezatu kwambiri.
“Zapang’ono, pokhala chilungamo, ziposa phindu lalikulu lopanda chiweruzo,” inatero mfumu yanzeruyi. (Miyambo 16:8) Ndipo lemba la Miyambo 15:16 limati: “Zapang’ono, ulikuopa Yehova, zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso.” Kukhala ndi mantha aumulungu n’kofunika kwambiri kuti tiziyendabe m’njira yachilungamo.
“Mtima wa Munthu Ulingalira Njira Yake”
Munthu analengedwa kuti azitha kusankha yekha zochita, kusankha pakati pa zabwino ndi zoipa. (Deuteronomo 30:19, 20) Mtima wathu wophiphiritsa umatha kusankha zinthu ndipo pazinthu zimenezo ungasankhe chinthu chimodzi kapena zingapo. Posonyeza kuti udindo wosankha zinthu n’ngwathu, Solomo anati: “Mtima wa munthu ulingalira njira yake.” Pambuyo poti munthu wachita zimenezi, “Yehova ayendetsa mapazi ake.” (Miyambo 16:9) Popeza kuti Yehova angatsogolere mapazi athu, ndibwino kuti tizipempha thandizo lake kuti ‘zolingalira zathu zikhazikike.’
Monga mmene taonera kale, mtima ndi wonyenga ndipo ungam’chititse munthu kuganiza molakwika. Mwachitsanzo, munthu angachite tchimo, ndipo mtima wake ungam’chititse kudzilungamitsa. M’malo mosiya tchimo lakelo, iye angaganize kuti Mulungu n’ngwachikondi, wokoma mtima, wachifundo, ndiponso wokhululuka. Munthu ameneyu amakhala akunena mu mtima mwake kuti: “Mulungu waiwala; wabisa nkhope yake; sapenya nthawi zonse.” (Salmo 10:11) Komatu n’zoopsa kuchita tchimo chifukwa choganiza kuti Mulungu n’ngwachifundo.
“Mwini Muyeso ndi Mulingo Wolungama Ndiye Yehova”
Atalongosola za mtima ndi zochita za munthu, Solomo anayamba kufotokoza za mfumu kuti: “Mawu a mlauli [Mulungu, NW] ali m’milomo ya mfumu; m’kamwa mwake simudzachita chetera poweruza.” (Miyambo 16:10) N’zosakayikitsa kuti Mfumu yomwe yakhazikitsidwa pa mpando, Yesu Khristu, idzachita zimenezi. Iye adzalamulira dziko lapansi m’njira yogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.
Posonyeza kumene chilungamo chimachokera, mfumu yanzeruyi inati: “Mwini muyeso ndi mulingo wolungama ndiye Yehova; ndiyenso anapanga miyala yonse yoyesera ya m’thumba.” (Miyambo 16:11) Yehova ndi amene amapereka miyezo ndi milingo yolungama. Ndipotu mfumu siiyenera kusintha miyezo imeneyi mwakufuna kwake. Panthawi ina ali padziko lapansi pano, Yesu ananena kuti: “Ine sindingachite chilichonse chongoganiza ndekha; ndimaweruza malinga ndi mmene ndamvera; ndipo chiweruzo chimene ndimapereka n’cholungama, chifukwa sinditsatira chifuniro changa, koma chifuniro cha amene anandituma ine.” Choncho tingayembekezere chilungamo mu ufumu umenewu popeza Atate ndiwo “anapereka kuweruza konse kwa Mwana.”—Yohane 5:22, 30.
Chinanso n’chiyani chimene tingachiyembekezere kwa mfumu yoimira Yehova imeneyi? Mfumu ya Isiraeli inati: “Kuchita mphulupulu kunyansa mafumu; pakuti mpando wawo wakhazikika ndi chilungamo.” (Miyambo 16:12) Mfundo zolungama za Mulungu n’zimene zikugwiritsidwa ntchito mu Ufumu wa Mesiya. Ufumuwu sunapange mgwirizano uliwonse ndi “mpando wachifumu wa kusakaza.”—Salmo 94:20; Yohane 18:36; 1 Yohane 5:19.
Zimene Tingachite Kuti Mfumu Itiyanje
Kodi nanga anthu olamuliridwa ndi mfumu ya ulemereroyi ayenera kuchita chiyani? Solomo anati: “Milomo yolungama ikondweretsa mafumu; wonena zoongoka am’konda. Mkwiyo wa mfumu ndi mithenga ya imfa; wanzeru adzaukhulula.” (Miyambo 16:13, 14) Masiku ano, olambira Yehova akutsatira mawu amenewa, ndipo akugwira mwakhama ntchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mateyo 24:14; 28:19, 20) Iwo akudziwa kuti kugwiritsa ntchito milomo yawo m’njira imeneyi kumakondweretsa Mfumu Mesiya, Yesu Khristu. Munthu aliyense wanzeru ankayesetsa kuchita zinthu zosakhumudwitsa mfumu yake ndiponso zoti isangalale nazo. Nanga kuli bwanji Mfumu Mesiya? Kodi si chinthu chanzeru koposa kuyesetsa kuisangalatsa?
Solomo anapitiriza kuti: “M’kuunika kwa nkhope ya mfumu muli moyo; kukoma mtima kwake kunga mtambo wa mvula ya masika.” (Miyambo 16:15) “Kuunika kwa nkhope ya mfumu” kukutanthauza kuyanjidwa ndi mfumuyo, monga mmene ‘kuunika kwa nkhope ya Yehova’ kumasonyezera kuyanjidwa ndi Yehova. (Salmo 44:3; 89:15) Mofanana ndi mitambo ya mvula imene imatitsimikizira kuti madzi othandiza mbewu kuti zikhwime apezeka, kukoma mtima kwa mfumu ndi umboni wakuti adzabweretsa zinthu zabwino. Mu ulamuliro wa Mfumu Mesiya mudzakhala madalitso ambirimbiri ndiponso chimwemwe, kuposa zimene zinali mu ulamuliro wa Mfumu Solomo.—Salmo 72:1-17.
Pamene tikudikira kuti Ufumu wa Mulungu uyambe kulamulira zinthu zonse padziko lapansili, tiyenitu tipitirize kupempha thandizo lake kuti tiyeretse mitima yathu. Komanso tikhulupirire Yehova ndiponso tiyambe kuopa kwambiri Mulungu. Tikatero tingakhale ndi chikhulupiriro chonse kuti ‘zolingalira zathu zidzakhazikika.’—Miyambo 16:3.
[Chithunzi patsamba 18]
Kodi mawu akuti Yehova wapanga “amphulupulu kuti aone tsiku loipa” akutanthauza chiyani?