‘Zochita Zandichulukira’
AKATSWIRI onyamula zitsulo mu mpikisano wa Olympic sanyamula zitsulo zolemera kwambiri kamodzi n’kamodzi. Iwo nthawi zambiri amayamba kunyamula zitsulo zopepuka ndipo pang’ono ndi pang’ono amayamba kunyamula zitsulo zolemera kwambiri. Ngati atadzikakamiza kunyamula zitsulo zopitirira muyezo, angadzivulaze ndipo ukatswiri wawo ungathere pomwepo.
N’chimodzimodzinso ndi inuyo. Tikukhulupirira kuti mumalimbikira kwambiri sukulu. Ndipo mukapatsidwa ntchito yovuta kapena mukamakonzekera mayeso, mumachita khama kwambiri.a Koma bwanji ngati nthawi yanu yonse imatha mukuchita za kusukulu? Zimenezi zingakuchititseni kuti musamadye kapena kugona mokwanira. Ngati nthawi zonse mumapanikizika kwambiri mungayambe kudwala. N’kutheka kuti mmenemu ndi mmene mukumvera panopa.b
Homuweki Yosatha
Mtsikana wazaka 15 wa ku Japan, dzina lake Hiroko,c anati: “Ndikamayamba kalasi ina, ndi pamenenso homuweki imakhala yambiri ndiponso yovuta. Ndimakhala ndi zinthu zina zambiri zoti ndichite, koma homuweki imakhalanso ikufunika mwamsanga. Nthawi zambiri ndimapanikizika.” Mtsikana wa ku Russia wazaka 14, dzina lake Svetlana, analemba kuti: “Zikumandivuta kwambiri kumaliza homuweki masiku ano. Chaka chilichonse ndimakhala ndi zowerenga zambiri ndipo aphunzitsi amangotipatsabe zochita. Mphunzitsi aliyense amaona kuti phunziro lake ndi lofunika kwambiri. Zimandivuta kuchita zonsezi.”
N’chifukwa chiyani aphunzitsi amalimbikira kupereka homuweki? Mnyamata wina wazaka 18 ku Brazil, dzina lake Gilberto, anati: “Aphunzitsi amanena kuti akufuna kutithandiza kuti tisadzavutike kupeza ntchito. Komabe, homuweki imene amatipatsa imakhala yambiri ndipo imatipanikiza kwambiri.” Choncho kuti musamapanikizike, muzikonda ntchito imene mwapatsidwa komanso muzigawa bwino nthawi yanu.
Ngakhale ngati homuweki imakuvutani, muziionabe kuti ndi yofunika chifukwa zimene mumaphunzira pochita homuweki zidzakuthandizani m’tsogolo. N’zoona kuti nthawi zina mungamaone kuti homuweki siikukutherani, koma dziwani kuti sukulu sichedwa kutha. Mukadzayamba ntchito, muzidzanyadira kuti munakwanitsa kuchita mahomuweki ovuta kwambiri. Ndipo mudzasangalala mukamaganizira kuti munali munthu wolimbikira sukulu.—Mlaliki 2:24.
Kuti musamapanikizike kwambiri, muzidziletsa kuchita zinthu zina komanso muzigawa bwino nthawi yanu. (Onani bokosi kudzanja lamanja) Mukazolowera kuchita homuweki yanu mokhulupirika ndiponso mwadongosolo, aphunzitsi adzayamba kukudalirani ndipo adzakhala ofunitsitsa kukuthandizani. Ngati mphunzitsi wanu amakudalirani, ndipo mwalephera kulemba homuweki pazifukwa zomveka bwino, iye angathe kukumvetsani. Chitsanzo chabwino pankhaniyi ndi Danieli. Iye anali mtumiki wa Mulungu “wokhulupirika; ndipo sanaona chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye.” Mfumu inkamulemekeza ndi kum’khulupirira Danieli chifukwa ankagwira bwino ntchito. (Danieli 6:4) Mukatengera chitsanzo cha Danieli pochita homuweki, aphunzitsi anu angamakumvetseni kwambiri.
Kodi kumvetsera m’kalasi ndiponso kuchita homuweki panthawi yake kungathetseretu kupanikizika? Ayi. Nthawi zina mungamapanikizike chifukwa chofuna kukhoza bwino. M’malo monyalanyaza zinthu za kusukulu, mungafune kuphunzira zambiri kuti zidzakuthandizeni m’tsogolo.
Ngati mumapanikizika mwanjira imeneyi musade nkhawa. Komabe kupanikizika kwina n’koipa ndiponso n’kosafunika.
Musadzichulukitsire Zochita
Taganizirani munthu amene amayendetsa galimoto mosasamala. Akamayandikira malo ofunika kuima, amakhala akuthamanga kwambiri ndipo amaima modzidzimutsa. Akatero amanyamukanso mochititsa mantha. Kodi n’chiyani chingachitike ndi galimoto ya dalaivala wosasamalayu? Injini komanso zipangizo zina za galimotoyo zingawonongeke. Mwinanso zimenezi zisanachitike, angachite ngozi yoopsa n’kuwononga galimotoyo.
Mofanana ndi zimenezi, ana asukulu ochuluka amadzipanikiza kwambiri asanapite kusukulu komanso akaweruka. Denise Clark Pope analemba m’buku lake za ana asukulu angapo amene akuwadziwa, kuti: “Iwo ankadzuka m’mamawa kwambiri mwina ola limodzi kapena awiri akuluakulu asanadzuke ndipo ankagonanso mochedwa kwambiri atamaliza kusewera mpira, kuvina, msonkhano wa ana a sukulu, kugwira ganyu ndiponso kuchita homuweki.”—Doing School.
Ana a sukulu akamadzipanikiza motere tsiku lililonse, zinthu siziwayendera bwino. Thupi lawo limafooka ndipo amayamba kudwala m’mimba, mutu kapena matenda ena. Kenako amalephera kuchita zinthu zimene amachita poyamba ndipo zimatenga nthawi kuti akhalenso bwino. Kodi zimenezi zikukuchitikirani?
Kugwira ntchito mwakhama kuti mukwaniritse zolinga zanu ndi kofunika, koma simungathe kuchita zonse tsiku limodzi ngakhale mutakhala ndi mphamvu zambiri bwanji. Baibulo limalangiza kuti: “Kulolera kwanu kudziwike kwa anthu onse.” (Afilipi 4:5) Mawu akuti “kulolera” amatanthauza “kusachita zinthu monyanyira” ndiponso “kuganiza bwino.” Munthu wololera amachita zinthu zimene sizingamuvulaze kapena kuvulaza ena. Amachita zinthu mwanzeru, ndipo zimenezi ndi zofunika masiku ano. Choncho kuti mukhale ndi thanzi labwino, musamachite zinthu monyanyira ndipo chepetsani kuchita zinthu zina zosafunikira kwambiri.
Kufunafuna Chuma
Komabe ana a sukulu ena amaona kuti kulolera n’kosathandiza ndiponso kungawalepheretse kukwaniritsa zolinga zawo. Ana otere amaona kuti chinthu chofunika kwambiri ndi ntchito yabwino ndiponso ndalama zimene angapeze pantchitoyo. Ana ena amene Denise Pope anakumana nawo anali ndi maganizo amenewa. Iye anati: “Anawa ankafuna atamagona mokwanira kuti akhale ndi thanzi labwino, koma zimenezi sizinkatheka chifukwa chotanganidwa kusukulu, kunyumba ndi kuntchito. Ndiponso ankafuna kucheza ndi anzawo, kugwira ntchito zina, kapena kupuma. Koma ana ambiri aona kuti sangathe kuchita zimenezi n’kumakhozabe bwino m’kalasi. Iwo aona kuti ndi bwino kudzasangalala m’tsogolo m’malo mosangalala panopo.”
Ana amene amadzipanikiza kwambiri ndi sukulu ayenera kuganizira mawu anzeru amene Yesu ananena, akuti: “Munthu angapindulenji ngati apata dziko lonse ndi kutaya moyo wake? Kapena munthu angapereke chiyani chosinthanitsa ndi moyo wake?” (Mateyo 16:26) Apa Yesu Khristu anachenjeza kuti zinthu zimene tingafune kupeza m’dzikoli n’zosapindulitsa kwenikweni ndipo zimangotiwonongera mphamvu zathu, kutitopetsa ndiponso kutisokonezera moyo wathu wauzimu.
Dokotala wina, dzina lake Madeline Levine, analemba m’buku lake kuti: “Ndalama, maphunziro, ulamuliro, kutchuka ndiponso chuma sizithandiza anthu osasangalala kuti ayambe kusangalala kapena amene ali ndi matenda a maganizo kuti achire.” (The Price of Privilege) Denise Pope, yemwe tamutchula kale uja, anati: “Ndaona ana ambiri a sukulu ndiponso makolo akuyesetsa kuti akhale ochita bwino pachilichonse chifukwa amaona kuti munthu wotere ndi amene zikumuyendera. . . Koma chofunika kwambiri ndi kuyesetsa kukhala ndi thanzi labwino ndiponso kuona zinthu moyenera.”
Pali zinthu zina zofunika kwambiri kuposa ndalama. Zinthu zimenezi ndi thanzi labwino, chikumbumtima chabwino ndiponso kukhala pa ubwenzi ndi Mlengi wathu. Zimenezi ndi mphatso za mtengo wapatali zochokera kwa Mulungu. Ngati mutataya zinthuzi chifukwa chofuna kutchuka kapena kulemera, mwina simungadzazipezenso. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, popeza ufumu wa kumwamba ndi wawo.”—Mateyo 5:3.
Achinyamata ambiri azindikira kuti mfundo imeneyi ndi yoona. Ngakhale kuti amalimbikira sukulu, amadziwa kuti kuphunzira kwambiri kapena chuma sizichititsa munthu kukhala wosangalala. Iwo amadziwa kuti kufunafuna zinthu zimenezi kumangotopetsa. Achinyamata amenewa aphunzira kuti kukwaniritsa “zosowa zawo zauzimu” n’kofunika kuti adzakhale ndi moyo wosangalala m’tsogolo. Ofalitsa magazini ino kapena Mboni za Yehova za m’dera lanu zingakuthandizeni kukwaniritsa zosowa zanu zauzimu ndiponso kukhala ndi moyo wosangalala.
[Mawu a M’munsi]
a Ophunzira amene sakhoza bwino kapena salimbikira m’kalasi, aone nkhani yakuti, “Zimene Achinyamata Amadzifunsa. . . Kodi Ndingamakhoze Kusukulu?” mu Galamukani! ya March 22, 1998, tsamba 20 mpaka 22.
b Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti, “Zimene Achinyamata Amadzifunsa . . . Kodi Ndingachitenji ndi Homuweki Yochuluka Motero?” mu Galamukani! ya April 8, 1993, tsamba 13 mpaka 15.
c Maina ena tawasintha.
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Ngakhale mutakhala ndi mphamvu zotani, simungathe kuchita zonse tsiku limodzi
[Mawu Otsindika patsamba 8]
Kudziwa Mlengi wanu ndi maphunziro ofunika kwambiri kuposa ena alionse
[Bokosi/Chithunzi patsamba 5]
NJIRA ZOKUTHANDIZANI KUTI MUSAMAPANIKIZIKE KWAMBIRI
❑ Kodi mumatha nthawi yaitali mukufufuza zinthu m’mapepala ndi m’mabuku? Anthu ena amafunika kuthandizidwa kuti azichita zinthu mwadongosolo. Ngati inunso muli ndi vutoli, musachite manyazi kupempha ena kuti akuthandizeni.
❑ Kodi mumangounjika ntchito? Yesani kumaliza ntchito yanu mofulumira. Mutachita zimenezi mungapepukidwe kwambiri ndipo mungakhale osangalala komanso zingakulimbikitseni kusiya kuunjika ntchito za kusukulu.
❑ Kodi mukakhala m’kalasi mumayamba kuganiza zina? Tayesani izi kwa mwezi umodzi: Muzimvetsera kwambiri aphunzitsi akamaphunzitsa ndipo muzilemba notsi. Mudzaona kuti homuweki yanu siidzakuvutani ndipo zimenezi zingathandize kuti musamapanikizike ndi sukulu.
❑ Kodi mwasankha maphunziro amene mungamalize mwachangu koma ofuna nthawi ndi khama? Kodi m’pofunikadi kuti muchite maphunziro amenewo? Funsani makolo anu. Pemphani munthu amene amaona maphunziro moyenera kuti akuthandizeni. Mwina mungaone kuti maphunziro ena sangakuthandizeni kwenikweni.
[Bokosi patsamba 6]
MPANDA WONGOYEREKEZERA
“Chuma cha [munthu] wolemera ndicho mudzi wake wolimba; alingalira kuti ndicho khoma lalitali.” (Miyambo 18:11) Mizinda yambiri yakale inkakhala ndi khoma kapena kuti mpanda womwe unkateteza anthu a mumzindawo kwa adani. Ndiyeno taganizirani kuti mukukhala mumzinda umene ulibe mpanda koma inuyo m’maganizo mwanu mukuona kuti mzindawo uli ndi mpanda. Ngakhale mutakhulupirira kwambiri zimenezi, mpanda wotere sungakutetezeni kwa adani.
Mofanana ndi anthu amene akukhala mu mzinda wosatetezeka, achinyamata amene amafunafuna chuma, sakhala ndi tsogolo labwino. Ngati ndinu kholo, mungachite bwino kuthandiza mwana wanu kupewa kukonda chuma komwe kuli ngati kukhala mumzinda wopanda mpanda.
Mfundo za m’Baibulo zotsatirazi, zingakuthandizeni pophunzitsa mwana wanu:
◼ Chuma chambiri chimabweretsa mavuto. “Kukhuta kwa wolemera sikum’gonetsa tulo.”—Mlaliki 5:12; 1 Timoteyo 6:9, 10.
◼ Munthu safunikira kukhala ndi chuma chambiri kuti akhale wosangalala. “Zoganizira za wakhama zichurukitsadi katundu.”—Miyambo 21:5; Luka 14:28.
◼ Munthu amene amapeza ndalama zongomuthandiza kupeza zinthu zofunika, amakhala wosangalala. “Musandipatse umphawi, ngakhale chuma.”—Miyambo 30:8.d
[Mawu a M’munsi]
d Nkhani zina zokhudza vuto lokonda chuma mungazipeze mu Galamukani! ya April 8, 2003, tsamba 20 ndi 21.
[Zithunzi patsamba 7]
Kudzichulukitsira zochita n’kosathandiza
[Chithunzi patsamba 7]
Musamaone homuweki ngati mtolo wolemetsa koma ngati yoti ingadzakuthandizeni m’tsogolo