Muzitsatira Lamulo la Kukoma Mtima Polankhula
“Atsegula pakamwa pake ndi nzeru, ndipo chilangizo cha chifundo [lamulo la kukoma mtima] chili pa lilime lake.”—MIY. 31:26.
1, 2. (a) Kodi anthu amene amalambira Yehova akulimbikitsidwa kukhala ndi khalidwe liti? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino?
MAWU amphamvu amene Mfumu Lemueli inauzidwa ndi mayi ake anali ndi mfundo zimene ndi ziyeneretso za mkazi wabwino. Iye anauzidwa kuti mkazi wabwino ‘amatsegula pakamwa pake ndi nzeru, ndipo chilangizo cha chifundo [lamulo la kukoma mtima] chili pa lilime lake.’ (Miy. 31:1, 10, 26) Kukoma mtima ndi khalidwe lofunika kwambiri kwa mkazi wanzeru ndiponso anthu onse amene amafuna kukondweretsa Yehova Mulungu. (Werengani Miyambo 19:22.) Anthu onse amene amalambira Mulungu ayenera kukhala okoma mtima.
2 Kodi kukoma mtima kumatanthauza chiyani? Kodi tiyenera kukomera mtima ndani? Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizilankhula mokoma mtima? Kodi kukoma mtima kungathandize bwanji polankhulana ndi anthu m’banja lathu ndiponso Akhristu anzathu?
Munthu Amakhala Wokoma Mtima Chifukwa cha Chikondi
3, 4. (a) Kodi kukoma mtima kumatanthauza chiyani? (b) Kodi kukoma mtima kumene tikukambirana m’nkhani ino kumasiyana bwanji ndi kukoma mtima kumene anthu amasonyeza kawirikawiri?
3 M’chinenero choyambirira mawu amene anamasuliridwa kuti kukoma mtima amaphatikizapo zinthu zambiri. Sikuti amangonena za kungokomera mtima ena chifukwa chowakonda kenako n’kuwachitira zinthu kapena kuwalankhula mawu osonyeza kuti timawaganizira. Munthu wokoma mtima amafunitsitsa ndi mtima wonse kuthandiza ena ndipo sasiya kukhala wokhulupirika mpaka cholinga chake chowathandizacho chitakwaniritsidwa.
4 Kawirikawiri munthu amatha kukomera mtima ngakhale munthu wachilendo. Mwachitsanzo, chombo chimene mtumwi Paulo limodzi ndi anthu ena 275 anakwera chitawonongeka, anthu a ku Melita anawakomera mtima ngakhale kuti anali asanakumanepo. (Mac. 27:37–28:2) Koma kukoma mtima kumene tikukambirana m’nkhani ino ndi kumene munthu amasonyeza kwa mnzake.a Kukoma mtima kumeneku n’kumene Akeni anasonyeza ‘ana a Isiraeli onse, pakufuma iwo ku Aigupto.’—1 Sam. 15:6.
Kusinkhasinkha ndi Kupemphera N’kofunika
5. Kodi n’chiyani chingatithandize kulamulira lilime lathu?
5 Kulankhula mokoma mtima si nkhani yapafupi. Ponena za lilime, Yakobe yemwe anali wophunzira wa Yesu analemba kuti: “Palibe munthu ndi mmodzi yemwe angathe kuliweta. Ndiko kanthu kamodzi kosalamulirika ndi kovulaza, kodzala ululu wakupha.” (Yak. 3:8) Kodi n’chiyani chingatithandize kulamulira lilime lomwe ndi losalamulirika? Mawu amene Yesu anauza atsogoleri a chipembedzo akhoza kutithandiza kudziwa zimene tingachite. Iye anawauza kuti: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mu mtima.” (Mat. 12:34) Ngati tikufuna kuti kukoma mtima kuziteteza lilime lathu, tiyenera kuyesetsa kuti khalidweli likhazikike mumtima mwathu womwe umaimira munthu wam’kati. Tiyeni tikambirane mmene kusinkhasinkha ndi kupemphera kungatithandizire kuchita zimenezi.
6. N’chifukwa chiyani tiyenera kusinkhasinkha moyamikira mmene Yehova anasonyezera kukoma mtima?
6 Baibulo limati Yehova Mulungu ndi “wa ukoma mtima wochuluka.” (Eks. 34:6) Wamasalmo anaimba kuti: “Dziko lapansi lidzala nacho chifundo chanu, [kukoma mtima kwanu] Yehova.” (Sal. 119:64) M’Malemba muli nkhani zambiri zofotokoza mmene Yehova anasonyezera kukoma mtima kwa anthu amene amamulambira. Kupatula nthawi yosinkhasinkha moyamikira zimene Yehova anachitira anthu kungatithandize kukhala ndi mtima wofunitsitsa kutengera khalidwe limeneli.—Werengani Salmo 77:12.
7, 8. (a) Fotokozani zimene Yehova anachita chifukwa chokomera mtima Loti ndi banja lake. (b) Kodi Davide anamva bwanji Yehova atamukomera mtima?
7 Mwachitsanzo, taganizirani zimene Yehova anachita populumutsa Loti, yemwe anali mwana wa m’chimwene wake wa Abulahamu, pamodzi ndi banja lake pa nthawi imene ankawononga mzinda wa Sodomu umene ankakhala. Atatsala pang’ono kuwononga mzindawu, angelo amene anabwera kwa Loti anamuuza kuti atenge banja lake n’kutuluka mumzindawo mofulumira. Baibulo limati: ‘Koma atayamba kuchedwa; [angelowo] anam’gwira dzanja lake, ndi dzanja la mkazi wake ndi dzanja la ana ake aakazi awiri; chifukwa cha kum’chitira chifundo Yehova; ndipo anam’tulutsa iye, namuika kunja kwa mudzi.’ Tikaganizira zimene anachita populumutsa anthuwa, timakhudzidwa mtima kwambiri ndipo timavomereza kuti pamenepa Mulungu anasonyeza kukoma mtima.—Gen. 19:16, 19.
8 Taganiziraninso chitsanzo cha Mfumu Davide ya Isiraeli, yomwe inaimba kuti: “[Yehova] akhululukira mphulupulu zako zonse; nachiritsa nthenda zako zonse.” Davide ayenera kuti anayamikira kwambiri pamene Yehova anamukhululukira tchimo lake ndi Bateseba. Iye anatamanda Yehova ndi mawu akuti: “Pakuti monga m’mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye.” (Sal. 103:3, 11) Tiyenera kusinkhasinkha moyamikira nkhani zimenezi, ndiponso nkhani zina za m’Malemba. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tikhale ndi mtima woyamikira kukoma mtima kwa Yehova ndiponso kuti tizimutamanda komanso kumuyamikira. Tikakhala ndi mtima woyamikira kwambiri tizifunitsitsa ndi mtima wonse kutsanzira Mulungu woona.—Aef. 5:1.
9. Tchulani chifukwa chachikulu chimene atumiki a Yehova ayenera kusonyezera kukoma mtima tsiku ndi tsiku.
9 Zitsanzo za m’Malemba zimasonyeza kuti Yehova amakomera mtima anthu onse amene ali naye pa ubwenzi wabwino. Nanga bwanji za anthu amene sali pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu? Kodi Yehova amawachitira nkhanza? Ayi. Lemba la Luka 6:35 limanena kuti: “[Mulungu] ndi wachifundo kwa osayamika ndi kwa oipa.” Iye “amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” (Mat. 5:45) Tisanaphunzire choonadi ndiponso kuchitsatira pa moyo wathu, Mulungu ankatikomera mtima ngati mmene amachitira ndi anthu ena onse. Koma pamene tinayamba kumulambira, iye amatikomera mtima m’njira yapadera kwambiri. (Werengani Yesaya 54:10.) Kodi sitiyenera kuyamikira kwambiri zimenezi? Chimenechitu ndi chifukwa chake tiyenera kusonyeza kukoma mtima kwambiri pa zolankhula zathu ndiponso pa zochita zathu za tsiku ndi tsiku.
10. N’chifukwa chiyani tinganene kuti pemphero ndi lofunika kwambiri kuti tikhale ndi khalidwe la kukoma mtima?
10 Pemphero nalonso ndi lofunika kwambiri kuti tikhale okoma mtima. Tikutero chifukwa chakuti chikondi ndiponso kukoma mtima ndi zipatso za mzimu woyera wa Yehova. (Agal. 5:22) Tikhoza kukhala okoma mtima ngati tingalole kuti mzimu woyera uzititsogolera. Njira yachidule kwambiri yolandirira mzimu woyera ndi kudzera m’pemphero. (Luka 11:13) Choncho, ndi bwino kupemphera kawirikawiri kuti tilandire mzimu wa Mulungu ndiponso kuulola kuti uzititsogolera. Motero, kusinkhasinkha ndiponso pemphero ndi zofunika kwambiri ngati tikufuna kuti tizitsatira lamulo la kukoma mtima polankhula.
Mmene Anthu Okwatirana Angasonyezere Kukoma Mtima
11. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova amayembekezera kuti amuna azikomera mtima akazi awo? (b) Kodi lamulo la kukoma mtima lingathandize bwanji mwamuna kukhala wodziletsa polankhula ndi mkazi wake?
11 Mtumwi Paulo analangiza amuna kuti: “Pitirizani kukonda akazi anu, monga Khristu anakonda mpingo nadzipereka yekha chifukwa cha mpingowo.” (Aef. 5:25) Paulo anakumbutsanso amuna zimene Yehova anauza Adamu ndi Hava. Mtumwiyu analemba kuti: “Mwamuna adzasiya atate wake ndi amayi wake, ndipo adzaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.” (Aef. 5:31) Apa n’zoonekeratu kuti Yehova amayembekezera amuna kukhala okhulupirika kwa akazi awo ndiponso kuchita zinthu mowakomera mtima nthawi zonse. Mwamuna wachikondi sauza ena zinthu zimene mkazi wake amalephera kuchita ndipo salankhula zomunyoza. Iye amakonda kumuyamikira. (Miy. 31:28) Pakakhala kusemphana maganizo m’banja, mwamuna wachikondi amadziletsa kuti asalankhule mawu onyoza mkazi wake.
12. Kodi mkazi wokwatiwa angasonyeze bwanji kuti amatsatira lamulo la kukoma mtima polankhula?
12 Nayenso mkazi ayenera kutsatira lamulo la kukoma mtima polankhula. Iye sayenera kulankhula motengera mzimu wa dziko. Chifukwa chokhala “ndi ulemu waukulu kwa mwamuna wake,” iye amalankhula zabwino za mwamuna wake pa gulu ndipo kuchita zimenezi kumathandiza kuti anthu ena apitirize kulemekeza mwamunayo. (Aef. 5:33) Pofuna kuti ana azilemekeza bambo awo, mkazi wabwino amapewa kutsutsa kapena kukayikira maganizo a mwamuna wake pamaso pa ana. Ngati ali ndi maganizo ena pa nkhani zina iye amakambirana ndi mwamuna wake ali awiri. Baibulo limanena kuti: “Mkazi yense wanzeru amanga banja lake.” (Miy. 14:1) Panyumba ya mkazi wotereyu anthu onse amakhala omasuka ndiponso osangalala.
13. Kodi n’kuti makamaka kumene anthu ayenera kutsatira lamulo la kukoma mtima ndipo kodi angachite bwanji zimenezi?
13 Ngakhale pamene ali awiriwiri kunyumba kwawo, anthu okwatirana ayenera kulankhulana mwaulemu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Zonsezo muzitaye kutali ndi inu, mkwiyo, kupsa mtima, kuipa, ndi mawu achipongwe; ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana.” Iye anawonjezera kuti: “Valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima. . . . Valani chikondi, pakuti ndicho chomangira umodzi changwiro.” (Akol. 3:8, 12-14) Ana akamamva makolo akulankhulana mokoma mtima kunyumba kwawo amasangalala ndipo nawonso adzatengera chitsanzo cha makolo awo polankhula.
14. Kodi mitu ya mabanja ingatani kuti izilankhula molimbikitsa kwa anthu a m’banja lawo?
14 Ponena za Yehova wamasalmo analemba kuti: “Chifundo [kukoma mtima] chanu chikhaletu chakunditonthoza.” (Sal. 119:76) Njira yapamwamba kwambiri imene Yehova amatonthozera anthu ake ndi mwa kuwalangiza ndiponso kuwatsogolera. (Sal. 119:105) Kodi mitu ya banja ingatsanzire bwanji Atate wathu wakumwamba pa nkhani yolankhula molimbikitsa anthu a m’banja lawo? Iwo angachite zimenezi mwa kuwalangiza ndi kuwalimbikitsa. Kulambira kwa Pabanja kumapereka mpata wabwino kwambiri wophunzira mfundo za m’Baibulo.—Miy. 24:4
Sonyezani Chikondi kwa Okhulupirira Anzanu
15. Kodi akulu komanso Akhristu ena okhwima mwauzimu angatani kuti zolankhula zawo ziziteteza anthu ena mumpingo?
15 Mfumu Davide inapemphera kuti: “Chifundo [kukoma mtima] chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.” (Sal. 40:11) Kodi akulu achikhristu ndi Akhristu ena okhwima mwauzimu angatsanzire bwanji Yehova pa nkhani imeneyi? Tikamagwiritsa ntchito lilime lathu pothandiza anthu kumvetsa malangizo a m’Malemba timasonyeza kuti ndife okoma mtima.—Miy. 17:17.
16, 17. Fotokozani njira zina zimene tingasonyezere kuti timatsatira lamulo la kukoma mtima polankhula.
16 Kodi tiyenera kuchita chiyani tikaona Mkhristu akuyamba kuchita zinthu zosemphana ndi mfundo za m’Baibulo? Kodi sitingalankhule naye mokoma mtima n’cholinga choti timuthandize? (Sal. 141:5) Ngati tadziwa kuti Mkhristu wina wachita tchimo lalikulu, kukoma mtima kudzatilimbikitsa kumuuza kuti “aitane akulu a mpingo” n’cholinga choti “am’pempherere, am’pake mafuta m’dzina la Yehova.” (Yak. 5:14) Ngati munthu wochimwayo sakuuzabe akulu, chifukwa cha chikondi ndiponso kukoma mtima, sitiyenera kungoisiya nkhaniyo osauza akulu. Anzathu ena ndi ofooka, osungulumwa, akuvutika ndi maganizo odziona kuti ndi opanda pake kapena akuvutika chifukwa chokhumudwa. ‘Kulankhula molimbikitsa kwa a mtima wachisoni’ ndi njira yabwino yosonyezera kuti timatsatira lamulo la kukoma mtima.—1 Ates. 5:14.
17 Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati adani a Mulungu akufalitsa mphekesera zokhudza Akhristu anzathu? M’malo mokayikira zoti abale athu ndi okhulupirika, tiyenera kungoisiya nkhaniyo osayankha kena kalikonse. Ngati munthu amene akufalitsa nkhaniyo tikhoza kulankhulana naye bwinobwino, tiyenera kumufunsa ngati alidi ndi umboni wa nkhaniyo. Adani a anthu a Mulungu akamafunsa kumene abale athu achikhristu akukhala, koma ali ndi zolinga zoipa, sitiyenera kuwauza chifukwa choti timakonda abale athuwo.—Miy. 18:24.
Munthu Wokoma Mtima Adzapeza Moyo
18, 19. N’chifukwa chiyani sitiyenera kusiya kutsatira lamulo la kukoma mtima pochita zinthu ndi Akhristu anzathu?
18 Nthawi zonse tiyenera kusonyeza chikondi kwa atumiki a Yehova anzathu. Sitiyenera kusiya kutsatira lamulo la kukoma mtima ngakhale pamene zinthu zavuta. Yehova sanasangalale pamene kukoma mtima kwa ana a Isiraeli kunakhala “ngati mame akuphwa mamawa.” (Hos. 6:4, 6) Koma Yehova amasangalala ngati anthu akusonyeza kukoma mtima nthawi zonse. Taonani mmene amadalitsira anthu amene amasonyeza kukoma mtima.
19 Lemba la Miyambo 21:21 limati: “Wolondola chilungamo ndi chifundo [kukoma mtima] apeza moyo, ndi chilungamo, ndi ulemu.” Ena mwa madalitso amene munthu wokoma mtima adzalandire ndi akuti adzapeza moyo, osati wa kanthawi kochepa, koma moyo wosatha. Yehova amathandiza munthu wotereyu ‘kugwira zolimba moyo weniweniwo.’ (1 Tim. 6:12, 19) Choncho tiyeni tiyesetse kusonyezana chifundo ndi kukoma mtima zivute zitani.—Zek. 7:9.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mumvetse kusiyana pakati pa kukoma mtima ndi kukhulupirika komanso chikondi, onani Nsanja ya Olonda ya May 15, 2002, masamba 12-13, 18-19.
Kodi Mungafotokoze?
• Kodi kukoma mtima kumatanthauza chiyani?
• Kodi n’chiyani chingatithandize kutsatira lamulo la kukoma mtima polankhula?
• Kodi anthu okwatirana angasonyeze bwanji chikondi ndi kukoma mtima polankhulana?
• Kodi tingadziwe bwanji kuti timatsatira lamulo la kukoma mtima tikamachita zinthu ndi Akhristu anzathu?
[Chithunzi patsamba 23]
Davide anatamanda Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake
[Chithunzi patsamba 24]
Kodi mumachita Kulambira kwa Pabanja nthawi zonse