Kodi Nyumba Yanu Iri Malo a Mpumulo ndi Mtendere?
“Yehova [apange mphatso kwa inu, NW], akuloleni mupeze mpumulo yense m’nyumba ya mwamuna wake.”—RUTE 1:9.
1. Zaka zina 3,000 zapitazo, ndi akazi atatu ati omwe anayamba ulendo wopita ku Yuda?
ZAKA zina 3,000 zapitazo, akazi atatu anayamba ulendo wotopetsa. Ukawatengera iwo m’zigawo zomwe mwachisawawa ziri zodzazidwa ndi mbala ndi amuna osowa chochita. Akaziwo akuyenda kupyola dziko lopanda kanthu la Moabu. Wamkulu kwambiri anali mkazi wamasiye Naomi, akukhumba kufika ku Betelehemu m’dziko la kwawo lokondedwa, Yuda. Kumbali kwake kuli akazi amasiye aŵiri achichepere, Olipa ndi Rute, akazi a ku Moabu owme anakhala akazi a ana amuna omwalira a Naomi Kilioni ndi Maloni. Tamvetserani!
2. Naomi anali ndi chikhumbo chotani kaamba ka Olipa ndi Rute?
2 “Mukani,” anatero Naomi, “bwererani, yense wa inu kunyumba ya amayi ake. Yehova akuchitireni zokoma, monga umo munachitira akufa aja ndi ine.” Ndipo Naomi analongosola chikhumbo chowonjezereka kaamba ka chiyani? “Yehova [apange mphatso kwa inu, NW],” iye anatero, “akuloleni mupeze mpumulo yense m’nyumba ya mwamuna wake.” (Rute 1:8, 9) Inde, Naomi anasonkhezera apongozi ake a akazi kubwerera kwa anthu awo, akumayembekezera kuti pakati pawo Mulungu akapatsa mkazi wachichepere aliyense mpumulo ndi chitonthozo chomwe chimatuluka m’kukhala ndi mwamuna wabwino ndi nyumba.
3. Ndi kaimidwe kotani kamene Rute anatenga, ndipo ndi chotulukapo chokulira chotani?
3 Olipa anabwerera, koma osati Rute wokhulupirika. Akumakana kusiya mpongozi wake, Rute anagamulapo: “Anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga.” Chotulukapo chake chotheratu? Nkulekelanji, popeza Rute anapeza nyumba ya mpumulo ndi mtendere ndi Boazi ndipo anapatsidwa “malipiro angwiro”! Iye anakhala kholo lachikazi la Mfumu Davide ndi Mbuye wake wosayerekezeka, Yesu Kristu.—Rute 1:16; 2:12; 4:13-22; Salmo 110:1; Mateyu 1:1-6.
4. Ndi funso lodzutsa maganizo lotani lomwe ladzutsidwa?
4 Naomi anakhumba kuti Yehova apereke kwa aliyense wa apongozi ake a akazi mphatso ya ukwati wa chisungiko ndi nyumba ya mpumulo ndi mtendere. Ndithudi, Mulungu amafuna moyo wa panyumba wa atumiki ake kukhala wa bata. Ngati muli mboni ya Yehova, chotero, kodi nyumba yanu iri malo a mpumulo ndi mtendere?
Kusankha Mnzanu wa mu Ukwati Woyenera
5. Ngati muli Mkristu wosakwatira woyembekezera kukwatira, nchiyani chomwe chiri sitepi yoyambirira kulinga ku moyo wa banja wa bata?
5 Ngati muli Mkristu wosakwatira wolingalira ukwati, inu mosakaikira mumayembekezera kaamba ka moyo wa panyumba wa bata. Sitepi loyambirira m’chitsogozo chimenecho lamveketsedwa bwino ndi mtumwi Paulo, yemwe analemba kuti: “Mkazi amangika pokhala mwamuna wake ali ndi moyo. Koma atamwalira mwamunayo, ali womasuka kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye.”—1 Akorinto 7:39.
6. (a) ‘Kukwatira kokha mwa Ambuye’ kumatanthauzanji? (b) Ndi mafunso otani amene amafunikira kulingaliridwa ndi wina wofuna mnzake wa mu ukwati? (c) Nchifukwa ninji wina afunikira kusankha mnzake wa mu ukwati wobatizidwa mwa pemphero?
6 ‘Kukwatira kokha mwa Ambuye’ kumatanthauza kulowa mu ukwati kokha ndi wokhulupirira mnzanu. Koma Mkristu safunikira kuthamangira mu ukwati, ngakhale kwa munthu yemwe ali wodzipereka kwa Yehova. Kodi munthuyo ndithudi ‘amafuna chilungamo ndi chifatso’? (Zefaniya 2:3) Kodi mwamunayo kapena mkaziyo amatumikira Mulungu ndi mtima wonse? Kodi munthuyo amalankhula kuchokera mu mtima wodzazidwa ndi mawu a chikondi a chitamando kwa Yehova? Kodi utumiki wa m’munda uli mbali yokhazikika ndipo yaikulu m’moyo wa munthuyo? Kodi mwamunayo kapena mkaziyo ali ndi ziyeneretso zofunikira kaamba ka utumiki ndi kaamba ka ukwati Wachikristu? Inde, ngakhale mnzanu wobatizidwa ayenera kusankhidwa mwanzeru, mwapemphero. Monga mmene kuliri kothekera, khalani wotsimikizira kuti wokhulupirirayo ali ndi mikhalidwe yabwino yauzimu. Kugwirizana koteroko kumapewa chitsenderezo chosokoneza mtendere ndi kuwawidwa mtima komwe kaŵirikaŵiri kumapezeka m’nyumba zogawanikana mwachipembedzo.
7. Kaamba ka chimwemwe chokulira koposa mu ukwati, nchiyani chomwe chimafunikira?
7 Zosowa za malingaliro zingakwaniritsidwe ndipo zinthu zauzimu zingagawanidwe mu ukwati wa Akristu aŵiri odzipereka. Ichi chimatulukamo m’chomangira chathithithi chaumunthu chothekera. Amuna ndi akazi Achikristu ndithudi amakhumba chomangira chathithithi ndi anzawo a mu ukwati. Anthu analengedwa ndi chisonkhezero cha kulambira, ndipo chimwemwe chathu chachikulu koposa chimatulukapo pamene titenga masitepi oyenera kukhutiritsa zosowa zathu zauzimu. (Mateyu 5:3) Kuzindikira ichi, ndithudi sitikafuna kusamvera Yehova mwa kukwatira wosakhulupirira ndipo mwakutero kudzilanda ife eni umodzi wauzimu umenewu womwe umalimbikitsa ukwati. (;Deuteronomo 7:3, 4) Inde, kaamba ka chimwemwe chachikulu koposa mu ukwati, tsimikizirani kuti Mulungu ali mu ukwati wanu. “Chingwe cha nkhosi zitatu [chophiphiritsira chimenecho] sichingadulidwe mwamsanga.” (Mlaliki 4:12) Ndithudi, kukhala ndi Yehova Mulungu mu ukwati wanu kudzaupanga iwo kukhala wamphamvu ndipo kudzathandiza kupanga nyumba yanu kukhala malo a mpumulo ndi mtendere.
Uphungu Womwe Umapititsa Patsogolo Mtendere wa M’banja
8. Kwa Akristu okwatira, ndi uphungu wotani umene uli wofunikira mwapadera?
8 Pakati pa Akristu omwe ali okwatirana kale, nchiyani chomwe chikufunikira kaamba ka nyumba ya mpumulo ndi mtendere? Zinthu zambiri, ndithudi, koma makamaka wofunika koposa uli uphungu wa Paulo pa Aefeso 5:21-33. Zowonadi, mwamuna kapena mkazi angayesere kugwiritsira ntchito mawu amenewo kuwunikira zophophonya za mnzake wa mu ukwati. Koma chikakhala chabwino chotani nanga kusumika maganizo pa uphungu womwe upezeka pamenepo kaamba ka inu kuwugwiritsira ntchito mwaumwini!
9. Ndi uphungu wotani umene Paulo anapereka kwa amuna Achikristu?
9 Ngati muli mwamuna Wachikristu, kugwiritsira ntchito mwaumwini uphungu wa Paulo kudzathandiza kupanga nyumba yanu kukhala malo a mpumulo ndi mtendere. Mtumwiyo akusonkhezera kuti: “Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda [mpingo, NW] nadzipereka yekha m’malo mwake.” Paulo ananenanso kuti: “Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha adzikonda yekha, pakuti munthu sanadana nalo thupi lake ndi kalelonse; komatu alilera nalisunga, monganso Kristu [Mpingo, NW] . . . Komanso inu yense pa yekha akonde mkazi wa iye yekha monga adzikonda yekha.” Mwamuna ayenera ‘kukonda mkazi wake monga iyemwini’—ngati kuti iye anali iyemwiniyo. Chiri choyenera chotani nanga, popeza kuti ‘aŵiriwo akhala thupi limodzi’!—Genesis 2:24.
10. M’chiyang’aniro cha 1 Timoteo 5:8, ndi thayo lotani limene mwamuna Wachikristu ali nalo?
10 Mwamuna yemwe amakonda mkazi wake monga amadzichitira iyemwini adzatenga chitsogozo mu zinthu zauzimu. Iye amatenga thayo kaamba ka mkhalidwe wokhalapo m’banja mwake ndipo molondola sangalole zinthu kulowelera m’mbali, monga mmene kunaliri. Ayi, iye afunikira kusamalira bwino kaamba ka zikondwerero zakuthupi ndi zauzimu za banja lonse. “Ndithudi,” anatero Paulo, “ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye ndipo aipa koposa wosakhulupirira.”—1 Timoteo 5:8.
11. Ndi uphungu wotani umene Paulo akupereka kaamba ka akazi Achikristu?
11 Mkazi Wachikristu angachite zochulukira kupanga nyumba kukhala malo a mpumulo ndi mtendere. Kwa akazi, Paulo akupereka uphungu wouziridwa uwu: “Akazi inu mverani amuna anu a inu eni monga kumvera ambuye, pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi monganso Kristu ndiye mutu wa [mpingo, NW], ali yekha mpulumutsi wa thupilo. Komatu, monga [mpingo, NW] umvera Kristu, koteronso akazi amvere amuna awo mu zinthu zonse. . . . [Mkazi ayenera kukhala ndi ulemu wakuya kaamba ka mwamuna wake, NW].” (Aefeso 5:22-24, 33) “Ulemu wakuya” umenewu umagawirako kulinga ku kupanga nyumba kukhala malo a mpumulo ndi mtendere. Ndithudi, zimasiyana mokulira ndi mkhalidwe wa akazi ambiri a kudziko omwe ali ndi mzimu wodziimira pawokha, wotokosa womwe umasokoneza ndi kukhumudwitsa nyumba.
12. Ndimotani mmene amuna ndi akazi Achikristu ayenera kuchitira?
12 Amuna ndi akazi Achikristu afunikira kuchita m’njira zomwe zimapititsa patsogolo chikondi ndi ulemu. Mwamuna ayenera kukhala wolingalira, wachikondi, wachikulire mwauzimu. Ndipo mkazi ayenera kukhala wowopa Mulungu, wogwirizana, wokondeka. Sichiri chovuta kuwona mmene mikhalidwe imeneyi ingapangire nyumba kukhala malo a mpumulo ndi mtendere.
Musakhoze “Kumpatsa Malo Mdyerekezi”
13. Ndi uphungu wotani umene Paulo akupereka pa Aefeso 4:26, 27?
13 Popeza kuti anthu ali opanda ungwiro, sichingakhale chopepuka kusunga nyumba kukhala ya mtendere. Mwachitsanzo, zitsenderezo zakunja zingatuluke m’chipsyinjo chomwe chngachotse mtendere wa panyumba. Koma kugwiritsira ntchito uphungu wa Paulo pa Aefeso 4:26, 27 kungathandizire ku bata la nyumba zathu. Paulo analemba kuti: “Kwiyani, koma musachimwe, dzuŵa lisalowe muli chikwiyire, ndiponso musampatse malo Mdyerekezi.” Ngakhale ngati mwamuna kapena mkazi molungamitsidwa akhala wokwiya pa chochitika china, aliyense wa iwo sayenera kulola mkhalidwe wokwiya umenewo kukhala chimo mwa kukhalabe mumkhalidwe wokwiya ndi kusunga udani. Lolani kuti tisalole nkomwe wosokoneza mtendereyo, Satana Mdyerekezi, kuchotsera nyumba zathu Zachikristu mtendere!—1 Petro 5:8.
14. Ngati vuto lapangitsa kusokonezeka kwinakwake, nchiyani chomwe chalingaliridwa kubwezeretsa mtendere wa m’banja?
14 Kaamba ka mtendere wa m’banja, ndithudi, munthu aliyense wa mu ukwati ayenera kugwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo. Ngati vuto lipangitsa kusokonezeka kwina, kupempherera pamodzi kaamba ka mzimu wa Mulungu kungatulukepo m’kusonyezedwa kwa chipatso chake ndi kubwezeretsedwa kwa mtendere wa m’banja. (Luka 11:13; Agalatiya 5:22, 23) Inde, ngakhale pansi pa mikhalidwe yoyesa kwambiri, njira imeneyi idzathandiza kupanga nyumba kukhala malo a mpumulo ndi mtendere.
Mbali ya Ana mu Mtendere wa Banja
15. Ndimotani mmene achichepere angathandizire kupititsa patsogolo mtendere wa m’banja?
15 Achichepere, nawonso, angathandize kupititsa patsogolo mtendere wa banja. Motani? Mwakusonyeza mzimu womvera ndi wogwirizanitsika. Mzimu woterowo umadalira mokulira pa kuphunzitsa kwa m’Malemba kumene iwo amalandira ndi njira imene kholo Lachikristu limakwaniritsira mbali yake yaumwini monga mphunzitsi. Mbali ya kuphunzitsa kofunika koposa kumeneku iri kukhazikitsa chitsanzo chabwino monga makolo. Monga mmene Miyambo 22:6 moyenerera imaikira nkhaniyo: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” Ndi kuphunzitsa kwabwino ndi chitsanzo chabwino cha ukholo, ana kaŵirikaŵiri sadzapatuka kuchoka ku njira yoyenera. Koma, ndithudi, zochulukira zimadalira pa mtundu ndi ukulu wa kuphunzitsa, limodzinso ndi mtima wa wachichepereyo.
16. Ndi chitsanzo chotani ponena za kuphunzitsa ana chimene tiri nacho m’nkhani ya Timoteo?
16 Yambani kuphunzitsa ana anu mwauzimu pamene adakali a ang’ono kwambiri. Chimenecho chinachitidwa m’nkhani ya Timoteo, popeza kuti Paulo anamlimbikitsa iye kuti: “Koma ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira nutsimikizika mtima nazo, podziŵa amene adakuphunzitsa ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziŵa malemba opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso mwa chikhulupiriro cha mwa Kristu Yesu.” (2 Timoteo 3:14, 15) Inde, Timoteo “anakakamizidwa kukhulupirira” zowonadi za m’Malemba. Logwiritsiridwa ntchito pano liri liwu la Chigriki lotanthauza “kukakamizidwa mwamphamvu za; kutsimikiziridwa za” chinachake. (New Thayer’s Greek-English Lexicon, tsamba 514) ‘Kukakamiza kolimba’ kumeneko kunaitanira kaamba ka kuyesetsa kwamphamvu kumbali ya amayi Achikristu a Timoteo, Yunike, ndi agogo ake, Loisi. Iwo anapambana m’kupereka kwa Timoteo ‘chikhulupiriro chopanda chinyengo,’ ngakhale kuti bambo wake mwachidziŵikire anali wosakhulupirira. (2 Timoteo 1:5) Kodi mukugwirira ntchito pa kukulitsa chikhulupiriro chofananacho mwa ana anu?
17. Ndi umboni wotani womwe ulipo wakuti munthu angaphunzitsidwe kuchokera ku ukhanda?
17 Timoteo anaphunzitsidwa Malemba kuchokera ku ukhanda. Chotero, musaderere kuthekera kwa kuphunzira kwa mwana. The New York Times inasimba kuti mogwirizana ndi phunziro limodzi, “pali unyinji wowirikiza kaŵiri wochulukira wa kulunzanitsidwa kwa minyewa yaing’ono ya ubongo—malo kumene nthambi zonga mitengo za maselo a ubongo zimakumanira—m’magawo ena a ubongo wa ana kuposa uja wa akulu.” Ngakhale ana achichepere kwambiri angaphunzire chinachake ponena za chimene chiri chabwino ndi chimene chiri choipa, chosangalatsa ndi chowawa. Mu bukhu lake The Brain, Richard M. Restak, M.D., akunena kuti: “Mu zamoyo zonse, zikumbukiro zingasungidwe mkati mwa ubongo mogwirizana ndi kufunika kwawo kaamba ka chipulumuko. Nyama ‘imakumbukira’ mdani wake ndipo imathaŵa pa kuwoneka koyamba kwa kufika kwa mdaniyo. Zikumbukiro zimaikidwanso m’ndandanda ya kuwonjezereka kwa zokumana nazo za malingaliro. Monga ana, sitifunikira kuuzidwa mochulukira kuposa kamodzi kusaika manja athu pa chitofu chotentha.” Ndithudi, zambiri ziyenerabe kuphunziridwa ponena za kugwira ntchito kwa ubongo, koma mwana angaphunzire mwa chokumana nacho. Mwachitsanzo, ngakhale pa msinkhu wa kumayambiriro kwenikweni, wachichepere angaphunzitsidwe kukhala chete pa misonkhano Yachikristu.
18. Pa Aefeso 6:1-4, ndi uphungu wotani umene Paulo anapereka kwa ana ndi makolo?
18 Pamene ana akula, iwo mopita patsogolo angatenge malangizo auzimu. Pakati pa zinthu zina, iwo angaphunzire kuti Mulungu amayembekezera iwo kumvera makolo awo. Ichi chimafunikira kuphunzitsa kolimba koma kwa chikondi kwa ukholo, popeza Paulo analemba kuti: “Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino: ‘Lemekeza atate wako ndi amako’’ ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano: ‘Kuti kukhale bwino ndi iwe ndi kuti ukhale wa nthaŵi yaikulu padziko.’ Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu, komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova].” (Aefeso 6:1-4) Ana omvera amathandizira mokulira kulinga ku kupanga nyumba kukhala malo a mpumulo ndi mtendere.
19. Nchiyani chomwe chingalimbikitse chomangira cha kholo ndi mwana?
19 Koma nchiyani chimene chingalimbitse chomangira cha kholo ndi mwana? Kuŵerenga Baibulo ndi mabukhu Achikristu pamodzi ndithudi kungathandize kuchita ichi. Zofalitsidwa zoterezo zonga ngati Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndi Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuruyo ziri zothandiza mwapadera m’kuthandiza achichepere. Pamene mukuŵerenga Baibulo ndi pa nthaŵi zina, gogomezerani chikondi kaamba ka Mulungu. Pamene mukudya chakudya, pangani ndemanga zomwe zimalemekeza Yehova monga Wopereka Wamkulu. Pamene mukuyenda ndi ana anu, perekani ulemerero kwa Mulungu ponena za zozizwitsa za chilengedwe—zomera, maluŵa, mitengo, mapiri, mitsinje, nyanja, ndi nyama zamoyo. Pamene mukudzilowetsa mu utumiki wa m’munda, gwirani mwaŵi wa kuchitira ndemanga pa chikondi cha Mulungu. Tsiku ndi tsiku, thandizani mwana wanu kukula m’chikondi kaamba ka Yehova monga munthu. Ndithudi, kuti mufikire mtima wa mwana wanu, chikondi choterocho chiyenera kukhala mumtima wanu weniweniwo.—Deuteronomo 6:4-7.
20. Kodi chilango choyenera chiri chofunika motani?
20 Musaiwale nkomwe kuti chilango chiri choyenera. Pamene chaperekedwa moyenerera ndi kulandirikwa, “chimabala chipatso cha mtendere, ndicho, chilungamo.” (Ahebri 12:11) Ndipo ana amene mwanzeru amagonjera ku chilango cha ukholo amabweretsa chimwemwe cha banja ndi ulemu ndi kusungirira dzina lake labwino. (Miyambo 10:1; 13:1; 23:24, 25) Ndithudi, mwakudzaza mbali zawo za m’Malemba, makolo ndi ana amapanga nyumba yawo kukhala malo a mpumulo ndi mtendere.
Sungirirani Nyumba ya Mpumulo ndi Mtendere
21. Mogwirizana ndi Miyambo 24:3, 4, ndimotani mmene nyumba ingasungidwire monga malo a mpumulo ndi mtendere?
21 Ndimotani mmene nyumba ingasungidwire monga malo a mpumulo ndi mtendere? Ukutero mwambi kuti: “Nzeru imangitsa nyumba, luntha liikhazikitsa. Kudziŵa kudzaza zipinda zake ndi chuma chonse chofunika cha mtengo wake.” (Miyambo 24:3, 4) Ndi chidziŵitso ndi ntchito ya banja lokangalika, nyumba ingakhale yodzazidwa ndi zinthu zabwino za zinthu zakuthupi. Koma nyumba ingamangidwe ndi kukhazikitsidwa pa maziko olimba kokha ngati ziwalo zake zisonyeza kuzindikira ndi kusonyeza nzeru yaumulungu, kugwiritsira ntchito chidziŵitso cha m’Malemba moyenera. Inde, nzeru imamangirira banja ndi kupangitsa kukhala wothekera moyo wake wachipambano monga gulu.
22. Kugwiritsira ntchito malangizo a Mulungu kungatulukepo m’chiyani?
22 Kugwiritsira ntchito malangizo a Mulungu mkati mwa banja kudzatulukapo mu mtendere, popeza Aisrayeli anauzidwa kuti: “Ine, ndine Yehova, Mulungu wako, Amene ndikuphunzitsa kupindula, Amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga! Mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.” (Yesaya 48:17, 18) Chotero, lolani kuti amuna, akazi, ndi ana onse aumulungu agwiritsire ntchito nzeru ya kumwamba. Kenaka nyumba zathu zidzakhala nthaŵi zonse malo a mpumulo ndi mtendere.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kaamba ka moyo wa panyumba wa bata, nchosankha chotani chimene chiyenera kupangidwa ndi Mkristu wosakwatira woyembekezera kukwatira?
◻ Mogwirizana ndi Aefeso 5:21-33, nchiyani chimene amuna ndi akazi ayenera kuchita kuti afikiritse mtendere wa m’banja?
◻ Ndimotani mmene kugwiritsira ntchito uphungu wa pa Aefeso 4:26, 27 kungathandizire kupanga nyumba kukhala malo a mtendere?
◻ Ndi mwanjira yotani mmene achichepere angathandizire ku mtendere wa m’banja?
◻ Ndimotani mmene tingasungirire nyumba zathu monga malo a mpumulo ndi mtendere?
[Chithunzi patsamba 17]
Amuna ndi akazi Achikristu amafunikira kuchita m’njira zimene zimapititsa patsogolo chikondi ndi ulemu
[Chithunzi patsamba 18]
Timoteo anaphunzitsiddwa zowonadi za Mulungu kuchokera ku ukhanda. Kodi mukuthandiza ana anu kukula m’chidziwitso ndi chikondi kaamba ka Yehova?