Mutu 2
Malangizo a Mmene Mungakhalire ndi Moyo Wokhutiritsa
1. Kodi vuto mungathane nalo motani pamoyo wanu?
PAMENE mukumana ndi vuto linalake, kodi uphungu mumakaufuna kuti? Mwina mungapite kwa mnzanu amene mumam’dalira kapena kwa mlangizi waluso. Kufufuzanso m’mabuku, monga mu laibulale kungathandizenso. Kapenanso mungafunsire kwa agogo kuti mutape pa nzeru za mvula zakale. Njira iliyonse imene mungaitsatire, mungachite bwino kuganizira mawu achidule komanso anzeru ali m’munsiŵa omwe amatilangiza njira zothetsera mavuto. Ameneŵa ndi ena a malangizo anzeru omwe mungawaone kukhala othandiza.
2-4. Kodi ndi mawu anzeru ati amene angateteze banja kuti lisasokonekere?
2 Moyo wa Banja: Makolo ambiri ali ndi nkhaŵa ya mmene angalerere ana awo m’dziko lino lodzaza mikhalidwe yoipa. Kuganizira uphungu wotsatirawu kungakhale kothandiza: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.”1 Pamene ana akula, amafunikira “njira,” kapena kuti malangizo amene ayenera kuwatsatira. Akatswiri ambiri azindikira kuti n’kofunika kupereka malamulo opindulitsa kwa ana. Malangizo anzeru a makolo amachititsa ana kuona kukhala otetezeka. Kuwonjezera apo: “Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru; koma mwana wom’lekerera achititsa amake manyazi.”2 “Nthyole” imatanthauza ulamuliro wa makolo umene ayenera kugwiritsa ntchito mwachikondi pofuna kuteteza ana kuti asasochere. Kugwiritsa ntchito ulamuliro umenewo sikuphatikizapo kuchitira mwana nkhanza m’njira iliyonse. Uphungu kwa makolo ndi wakuti: “Musaputa ana anu, kuti angataye mtima.”3
3 Kumvana kwabwino pakati pa mwamuna ndi mkazi wake ndiko maziko a banja lachimwemwe. Kodi chofunikira n’chiyani kuti kumvana koteroko kukhalepo? “Yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna.”4 Chikondi ndi ulemu zimakhala ngati mafuta oletsa kukwechesana m’banja. Kuti uphungu umenewu ugwire ntchito, kulankhulana n’kofunika chifukwa “zolingalira zizimidwa popanda upo.”5 Kuti tilimbikitse kulankhulana zakukhosi, tiyenera kuyesetsa kuzindikira maganizo a mnzathu, kumvetsa mmene iye akumvera. N’kwanzeru kukumbukira kuti “mtima [wa] munthu ndiwo madzi akuya; koma munthu wozindikira adzatungapo.”6
4 Okalamba ambiri amasungulumwa kwambiri m’zaka zawo zaukalamba, pamene ana awo awasiya okha, ngakhalenso m’mayiko kumene ulemu kwa makolo unaliko kale. Komabe, ndi bwino kuti ana awowo aganizire mawu anzeru aŵa: “Lemekeza atate wako ndi amako.”7 “Usapeputse amako atakalamba.”8 “Wolanda [“wovutitsa,” NW] atate, ndi wopitikitsa amayi, ndiye mwana wochititsa manyazi.”9 Komanso makolo okalamba ayenera kukhala othandiza ndi kumayesetsa kulimbikitsa ubale wachikondi. “Wopanduka afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.”10
5. Kodi ndi chenjezo lotani lonena za kumwa zaukali limene mungachite mwanzeru kulimvera?
5 Kumwa Zakumwa Zaukali: N’zoona kuti ‘vinyo akondweretsa moyo,’11 ndipo kumwa zakumwa zaukali ‘kungaiŵalitse [munthu] umphaŵi wake.”12 Koma kumbukirani kuti: “Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa; wosochera nazo alibe nzeru.”13 Taganizirani zotsatira zake za kumwa mwauchidakwa: “Pachitsiriziro chake [vinyo] aluma ngati njoka, najompha ngati mamba. Maso ako adzaona zachilendo, mtima wako udzalankhula zokhota. . . . Ndidzauka nthaŵi yanji? Ndidzafunafunanso vinyoyo.”14 Kumwa zaukali pamlingo woyenera kungakhale kopindulitsa, koma nthaŵi zonse tiyenera kupeŵa kumwa mwauchidakwa.
6-9. Perekani zitsanzo za mmene mungawongolere kasamalidwe kanu ka ndalama.
6 Kasamalidwe ka Ndalama: Nthaŵi zina, mavuto a zandalama angapeŵedwe mwa kusamala ndalama mwanzeru. Tamverani uphungu uwu: “Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka. Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka; ndipo kusinza kudzaveka munthu nsanza.”15 Mwa kupeŵa kumwa moŵa mwauchidakwa ndi mankhwala osokoneza bongo komanso zizolowezi zina ngati njuga, tikhoza kugwiritsa ntchito ndalama zathu kusamalira banja lathu m’njira yabwino. Komabe, ambiri amatenga ngongole zoposa ndalama zimene amapeza kwakuti amakakamizika kugwira ntchito zolimba kungoti abweze ngongolezo. Ena amachita kutenganso ngongole ina kuti akalipire chiwongola dzanja cha ngongole ina. Kukumbukira mawu anzeru otsatiraŵa kungakhale kothandiza: ‘Wotsata zinthu zopanda pake umphaŵi udzam’kwanira.’16 Tingadzifunse kuti: ‘Kodi zinthu zimene ndikufuna kugula n’zofunikiradi? Kodi ndi zinthu zingati zimene ndimangozitsekera m’sutukesi n’tangozivala kangapo kokha?’ Winawake wolemba nkhani m’magazini anati: “Zimene munthu amafunikira kwenikweni ndi zochepa—zimene safunikira kwenikweni ndiye zankhaninkhani.” Tamverani mawu anzeru aŵa: “Sitinatenga kanthu poloŵa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire. . . . Muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, . . . adzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.”17
7 Kukhala wakhama kumathandiza kwambiri kuthetsa mavuto a zandalama. “Pita kunyerere, wolesi iwe, penya njira zawo nuchenjere. . . . Tulo tapang’ono, kuodzera pang’ono, kungomanga manja pang’ono, ndi kugona; ndipo umphaŵi wako udzafika ngati mbala.”18 Kukonzekera mosamala ndi kukonza bajeti yabwino kungathandizenso: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza?”19
8 Koma bwanji ngati tili osauka, osati kuja kodzipangitsa tokha? Mwachitsanzo, chifukwa cha mavuto a zachuma cha dziko, tingachotsedwe ntchito ngakhale kuti timagwira ntchito mwamphamvu. Kapena tingakhale m’dziko kumene anthu ambiri ali osauka kwambiri. Pamenepo tingatani? “Nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza; koma kudziŵa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.”20 Taganiziraninso uphungu uwu: “Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake? Adzaima pamaso pa mafumu.”21 Kodi palibe maluso amene tingaphunzire kuti tipeze ntchito?
9 Uphungu wotsatirawu ungamveke wosayenera, koma ulidi wothandiza: “Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu. . . . Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nawo inu.”22 Apa sakutanthauza kupatsa moyembekezera kubwezeredwa zabwino. Kusiyana ndi zimenezo, uphungu ndi wakuti tiyenera kukulitsa mzimu wopatsa: “Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.”23 Mwa kugaŵana zinthu panthaŵi yakusoŵa, timalimbikitsa mzimu wopatsa umene nthaŵi ina ungadzatipindulitse.
10, 11. Kodi mungachite chiyani kuti muthane ndi kaduka ndi mkwiyo?
10 Kukhala ndi anthu ena: Mfumu ina yanzeru inati: “Ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zom’pindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.”24 Nsanje yapangitsa anthu ambiri kuchita zinthu zopusa. Munthu akhoza kuona mnzake woyandikana naye makomo atagula wailesi yakanema ya 32 inchesi, basi iye ulendo kukagula wailesi yakanema ya 36 inchesi, ngakhale kuti imene ali nayo kale ya 27 inchesi ikugwira ntchito bwinobwino. Mzimu wakaduka woterowo ndi wopanda pake, kungosautsa mtima. Kodi simukuvomereza?
11 Mwina tingakhumudwe ndi zimene anthu ena angatinene. Koma taonani uphungu uwu: “Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m’chifuŵa cha zitsiru.”25 Zoona, nthaŵi zina kukwiya kungakhale koyenerera. Wolemba wina wakale anati: “Kwiyani, koma musachimwe; dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire.”26 Koma kodi mkwiyo wamphamvu tingaulamulire motani? “Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.”27 Chofunikira ndi kulingalira. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi chimene wachitira choncho ndi chiyani? Kodi pali zifukwa zomveka?’ Kuwonjezera pa kulingalira koteroko, ilipo mikhalidwe ina imene ingatithandize kuthana ndi mkwiyo. “Valani, . . . mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; . . . koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.”28 Inde, chikondi chimathetsa mavuto ambiri pakati pa anthu.
12. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kulesta lilime lanu?
12 Komabe, pali “chiwalo chaching’ono” chimene chimasokoneza ubale wamtendere pakati pa anthu—lilime. Akunenadi zoona mawu akuti: “Lilime palibe munthu akhoza kulizoloŵeretsa; lili choipa chotakataka, lodzala ndi ululu wakupha.”29 Uphungu winanso wofunikira ndi uwu: “Munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.”30 Komabe, pogwiritsa ntchito lilime tiyenera kusamala kuti tisamalankhule choonadi koma chokhalanso ndi bodza m’kati mwake, pofuna kusungitsa mtendere wachiphamaso. “Manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iyayi, iyayi; ndipo chowonjezedwa pa izo chichokera kwa woipayo.”31
13. Ndi motani mmene mungasungire ubale wabwino pakati pa inu ndi anthu ena?
13 Kodi tingasunge motani ubale wabwino ndi ena? Taonani mfundo ya chikhalidwe iyi: ‘Musapenyerere zanu za inu nokha, koma mupenyererenso za mnzanu.’32 Tikatero tidzakwaniritsa mawu a lamulo limene ambiri amalitcha Lamulo la Chikhalidwe lakuti: “Zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.”33
14. N’chiyani chingakuthandizeni kuthana ndi vuto la maganizo?
14 Kuvutika Maganizo: Kodi ndi motani mmene tingakhalire a maganizo okhazikika m’dziko lino lovutitsa maganizo choncho? “Mtima wokondwa usekeretsa nkhope; koma moyo umasweka ndi zoŵaŵa za m’mtima.”34 Tikhoza kukhala ndi ‘mtima wosakodwa’ pamene ena anyalanyaza zimene tikuziona kukhala zoyenera. Komabe, tiyenera kukumbukira mawu aŵa: “Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziwononga wekha?”35 Komabe, nkhaŵa za moyo zingativutitse mosalekeza. Pamenepo tingatani? Tiyeni tikumbukire kuti: “Nkhaŵa iŵeramitsa mtima wa munthu; koma mawu abwino aukondweretsa.”36 Tikhoza kusinkhasinkha “mawu abwino,” mawu okoma amene angatilimbikitse. Kukhala wokondwa mosasamala kanthu za mikhalidwe yovutitsa maganizo kungathandizenso thanzi lathu: “Mtima wosekerera uchiritsa bwino.”37 Pamene tivutika maganizo chifukwa chakuti ena akuoneka kuti sakusamala za ife, tiyeni tiyese njira iyi: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”38 Mwa kukhala wokondwa, tikhoza kuthana ndi zovutitsa maganizo zimene timakumana nazo tsiku ndi tsiku.
15, 16. N’chifukwa chiyani kuli kofunikira kuti muzipatula nthaŵi yoŵerenga Baibulo?
15 Kodi muganiza mawu anzeru amene takambiranaŵa angagwire ntchito kwa inu, amene mukukhala m’zaka zino za m’ma 2000? Kwenikweni, mawuŵa amapezeka m’buku lakalekale—Baibulo. Koma n’kupitiranji ku Baibulo m’malo mopita ku magwero ena opezako nzeru? Mwa zina, n’chifukwa chakuti mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo zagwira ntchito kwa nthaŵi yaitali kwambiri. Mwachitsanzo, tinene za Yasuhiro ndi Kayoko, amene analimbikitsa kwambiri bungwe lomenyera ufulu wa azimayi. Iwo anakwatirana chabe chifukwa chakuti Kayako anali ndi mimba ya Yasuhiro. Koma chifukwa cha mavuto azachuma komanso poona kuti sanali oyenerana, anasudzulana posapita nthaŵi. Pambuyo pake, wina osadziŵa za mnzake, onse anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Aliyense anatha kuona kusintha kwakukulu kwa moyo wa mnzake. Mapeto ake, Yasuhiro ndi Kayoko anaganiza zokwatirananso. Ngakhale kuti pakali mavuto ena ndi ena pamoyo wawo, iwo tsopano ali ndi mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo zimene amayesetsa kutsatira, ndipo onse amalolerana pothetsa mavuto awo. Pakati pa Mboni za Yehova, mudzaona zotsatira zabwino za kugwiritsa ntchito mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo m’moyo. Bwanji osakakhala nawo pa wina wa misonkhano yawo kuti mudziŵe anthu amene amayesetsa kukhala ndi moyo wotsatira Baibulo?
16 Mauphungu amene tawagwira mawu amenewo ndi chitsanzo chabe cha nzeru zothandiza zochuluka zimene mungatape pamgodi wa nzeru umenewu, Baibulo. Pali zifukwa zimene Mboni za Yehova zimakhalira zofunitsitsa kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo pa miyoyo yawo. Bwanji osayesa kupeza zifukwazo ndi kudziŵanso mfundo zina ponena za Baibulo lenilenilo?
PEZANI MAWU OPATSA NZERU M’BAIBULO
1. Miyambo 22:6
3. Akolose 3:21
4. Aefeso 5:28, 33
6. Miyambo 20:5, “Moffatt”
7. Mateyu 19:19
10. Miyambo 18:1
11. Mlaliki 10:19
12. Miyambo 31:6, 7
13. Miyambo 20:1
14. Miyambo 23:29-35
16. Miyambo 28:19
17. 1 Timoteo 6:7-10; Luka 12:15
18. Miyambo 6:6-11
19. Luka 14:28
20. Mlaliki 7:12
21. Miyambo 22:29
22. Luka 6:38
23. Miyambo 11:25; Mlaliki 11:1
24. Mlaliki 4:4
25. Mlaliki 7:9
26. Aefeso 4:26, 27
27. Miyambo 19:11
28. Akolose 3:12-14
29. Yakobo 3:5-8
30. Yakobo 1:19
31. Mateyu 5:37
32. Afilipi 2:4
33. Mateyu 7:12
34. Miyambo 15:13
35. Mlaliki 7:16
36. Miyambo 12:25
37. Miyambo 17:22
38. Machitidwe 20:35
[Chithunzi patsamba 5]
“Phunzitsa mwana poyamba njira yake”
[Chithunzi patsamba 5]
“Yense payekha, . . . akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha”
[Chithunzi patsamba 6]
Khalani wa mtima wokondwa, ndipo yesetsani kulimbikitsa ubale wabwino ndi ena
[Chithunzi patsamba 7]
“Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake?”
[Chithunzi patsamba 8]
“Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu”
[Chithunzi patsamba 9]
Kodi mkwiyo wamphamvu tingaulamulire motani?