Monga Maapulo Agolidi
MAAPULO—mmene amakomera m’maso ndi m’kamwa! Baibulo limagwiritsira ntchito chipatso chokoma chimenechi m’fanizo losonkhezera maganizo pamene limati: “Mawu oyenera a panthaŵi yake akunga [maapulo agolidi, NW] m’nsengwa zasiliva.” (Miyambo 25:11) Kodi mawu ameneŵa akutanthauzanji?
“Maapulo agolidi m’nsengwa zasiliva” angatanthauze chinthu chosema, monga mbale yasiliva yochembedwa yokhala ndi zipatso zagolidi. Popeza kuti mavesi oyambirira m’chaputala chimenechi akutchula mafikidwe a kwa mfumu, vesili lingakhale likutchula mphatso zoperekedwa kwa wolamulira—zokometsera zagolidi za mpangidwe wonga wa maapulo zoikidwa pambale zasiliva. (Miyambo 25:6, 7) Nzokongola chotani nanga zimenezo!
Muli kukongola kofanana ndi kumeneko m’mawu a panthaŵi yake, oyenera, ndi aulemu, kaya akhale olembedwa kapena olankhulidwa. Amakhala okoma, olimbikitsa ndi opindulitsa mwanjira zambiri. Makamaka mawu ouziridwa mwaumulungu a m’Baibulo ndiwo ali okongola monga “maapulo agolidi m’nsengwa zasiliva.”
Monga momwe kwasonyezedwera ndi mwambi wanzeru wa Mfumu Solomo pa Miyambo 25:11, iye “anasanthula akapeze mawu okondweretsa, ndi zolemba zowongoka ngakhale mawu owona.” (Mlaliki 12:10; Miyambo 25:1) Zaka mazana ambiri pambuyo pake, mtumwi Wachikristu Paulo analemba kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa.” (2 Timoteo 3:16) Inde, Baibulo lili ndi uphungu wopindulitsa, maulosi, mafanizo, ndi chowonadi zoŵala ndi zokongola kwambiri kwakuti zimaposa zopanga za amisiri. Ndiponso, aliyense wopeza nzeru m’Mawu a Mulungu, Baibulo, amapeza chuma chamtengo wake ndipo angakhale ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya.—Miyambo 4:7-9; Yohane 17:3.