Kodi Yesu Ankatanthauza Chiyani Pomwe Ananena Kuti ‘Kondani Adani Anu’?
Yankho la m’Baibulo
Pa ulaliki wake wotchuka wapaphiri, Yesu anati: ‘Kondani adani anu.’ (Mateyu 5:44; Luka 6:27, 35) Mawu a Yesu amenewa amatanthauza kuti tiyenera kuchitira zabwino anthu amene amatida kapenanso kutichitira zinthu zopanda chilungamo.
Yesu anasonyeza kuti ankakonda adani ake pomwe anawakhululukira ngakhale kuti anamuchitira zankhanza. (Luka 23:33, 34) Zimene anaphunzitsa pankhani yokhudza kukonda adani athu, zimagwirizana ndi zimene zili m’Malemba a Chiheberi, amene amadziwikanso kuti Chipangano Chakale.—Ekisodo 23:4, 5; Miyambo 24:17; 25:21.
“Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.”—Mateyu 5:43, 44.
Zimene zili munkhaniyi
N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda adani athu?
Mulungu amatipatsa chitsanzo pankhaniyi. Mulungu “ndi wachifundo kwa osayamika ndi kwa oipa.” (Luka 6:35) Iye “amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa.”—Mateyu 5:45.
Chikondi chingapangitse mdani wathu kuti asinthe. Baibulo limatilimbikitsa kuti tizikomera mtima mdani wathu chifukwa tikatero timakhala ngati ‘tikumuunjikira makala amoto pamutu pake.’ (Miy. 25:22) Fanizo limeneli limanena zomwe zimachitika posungunula mwala womwe umakhala ndi zitsulo zamtengo wapatali mkati mwake. Choncho tikamakomera mtima anthu amene amatida, tikhoza kusungunula mkwiyo wawo ndi kuwathandiza kukhala ndi makhalidwe abwino.
Mungasonyeze m’njira ziti kuti mumakonda adani anu?
‘Muzichitira zabwino amene amadana nanu.’ (Luka 6:27) Baibulo limati: “Ngati mdani wako ali ndi njala, um’patse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, um’patse chakumwa.” (Aroma 12:20) Mungapeze njira zina zosonyezera kukonda mdani wanu potsatira mawu a Yesu odziwika kwambiri akuti: “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo.”—Luka 6:31.
‘Muzidalitsa omwe amakutembererani.’ (Luka 6:28) Timadalitsa adani athu polankhula nawo mokoma mtima ndiponso mowaganizira, ngakhale pomwe iwowo akutilankhula mwachipongwe. Baibulo limati: “Osabwezera . . . chipongwe pa chipongwe, koma m’malomwake muzidalitsa.” (1 Petulo 3:9) Malangizo amenewa angatithandize kuthetsa chidani.
‘Muzipempherera amene amakunyozani.’ (Luka 6:28) Ngati munthu akukunyozani, musabwezere “choipa pa choipa.” (Aroma 12:17) Koma m’malomwake, muzipempha Mulungu kuti amukhululukire. (Luka 23:34; Machitidwe 7:59, 60) Komanso m’malo mobwezera, muzisiya zonse m’manja mwa Mulungu kuti iye aweruze munthuyo mogwirizana ndi mfundo zake zolungama.—Levitiko 19:18; Aroma 12:19.
“Pitirizani kukonda adani anu ndi kuchita zabwino kwa amene akudana nanu. Pitirizani kudalitsa okutembererani ndi kupempherera amene akukunyozani.”—Luka 6:27, 28.
Muzikhala ‘oleza mtima ndiponso okoma mtima.’ (1 Akorinto 13:4) M’mawu ake odziwika bwino ofotokozera tanthauzo la mawu akuti chikondi, Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito mawu ena ochokera ku mawu a Chigiriki akuti a·gaʹpe omwe amapezeka pa Mateyu 5:44 ndi Luka 6:27, 35. Timasonyeza chikondi chachikhristu chimenechi ngakhale kwa adani athu pokhala oleza mtima komanso okoma mtima. Tingachitenso zimenezi tikamapewa mtima wansanje, wodzitukumula komanso tikamapewa kukhala amwano.
“Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima.” Chikondi sichichita nsanje, sichidzitama, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichisamala zofuna zake zokha, sichikwiya. Sichisunga zifukwa. Sichikondwera ndi zosalungama, koma chimakondwera ndi choonadi. Chimakwirira zinthu zonse, chimakhulupirira zinthu zonse, chimayembekezera zinthu zonse, chimapirira zinthu zonse. Chikondi sichitha.”—1 Akorinto 13:4-8.
Kodi muyenera kupita kunkhondo kukamenyana ndi adani anu?
Ayi, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti sayenera kumenyana ndi adani awo. Mwachitsanzo, atawachenjeza za kuukiridwa kwa Yerusalemu, sanawauze kuti akhalebe mumzindawo ndi kumenya nkhondo, koma anawauza kuti athawe. (Luka 21:20, 21) Yesu anauzanso mtumwi Petulo kuti: “Bwezera lupanga lako m’chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mateyu 26:52) Baibulo komanso mabuku ofotokoza mbiri, amasonyeza kuti otsatira a Yesu oyambirira sankamenya nkhondo yolimbana ndi adani awo.a—2 Timoteyo 2:24.
Maganizo olakwika pankhani yokonda adani athu
Maganizo olakwika: Chilamulo cha Mulungu chinkalola Aisiraeli kuti azidana ndi adani awo.
Zoona zake: M’chilamulo munalibe lamulo limeneli. Koma chinkalimbikitsa Aisiraeli kuti azikonda anzawo. (Levitiko 19:18) Ngakhale kuti mawu akuti “mnzako” anganene za munthu wina aliyense, Ayuda ena ankaona kuti mawuwa ankanena za Ayuda anzawo basi, ndipo ankakhulupirira kuti anthu amene sanali Ayuda anali adani awo ndipo ankayenera kudana nawo. (Mateyu 5:43, 44) Yesu anawongolera maganizo olakwikawo powauza fanizo la Msamariya wachifundo.—Luka 10:29-37.
Maganizo olakwika: Ukamakonda mdani wako umasonyeza kuti ukugwirizana ndi khalidwe lake loipa.
Zoona zake: Baibulo limasonyeza kuti ndi zotheka kukonda munthu popanda kusekerera khalidwe lake loipa. Mwachitsanzo, Yesu ankadana ndi zachiwawa komabe anapempherera anthu amene anamupha. (Luka 23:34) Yesu ankadananso ndi kusamvera malamulo kapena kuti kuchita machimo. Komabe ngakhale zinali choncho, iye anapereka moyo wake chifukwa cha anthu ochimwa.—Yohane 3:16; Aroma 6:23.
a Buku lina lomwe analemba E. W. Barnes limati: “Tikaona bwinobwino maumboni amene alipo, amasonyeza kuti pofika m’nthawi ya Marcus Aurelius [yemwe anali Mfumu yachiroma kuyambira mu 161 kudzafika mu 180 C.E.] palibe Mkhristu amene analowa usilikali; komanso palibe amene anapitiriza kugwira ntchito yausilikali atakhala Mkhristu.”—The Rise of Christianity.