Mzimu
Tanthauzo: Liwu Lachihebri ruʹach ndi Lachigiriki pneuʹma, amene kaŵirikaŵiri amatembenuzidwa “mzimu,” ali ndi matanthauzo angapo. Iwo onse amasonya kuchinthu chosawoneka ndi maso aumunthu ndi chimene chimapereka umboni wa mphamvu mwa kuyenda. Mawu Achihebri ndi Achigiriki amagwiritsidwa ntchito kutanthauza (1) mphepo, (2) mphamvu yogwira ntchito ya moyo m’zolengedwa za padziko lapansi, (3) mphamvu yosonkhezera imene imatuluka mu mtima wophiphiritsira wa munthu ndi imene imamchititsa kunena ndi kuchita zinthu mwanjira ina yake, (4) mawu ouziridwa ochokera m’magwero osawoneka, (5) anthu auzimu, ndi (6) mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, kapena mzimu woyera wa Mulungu. Kugwiritsiridwa ntchito kungapo kwa zimenezi kwakambitsiridwa panopa mogwirizana ndi mitu yankhani imene ingabuke muuminisitala wakumunda.
Kodi mzimu woyera nchiyani?
Kuyerekezera malemba a Baibulo amene amatchula mzimu woyera kumasonyeza kuti umanenedwa kunakhala ‘ukudzaza’ anthu; iwo angakhoze ‘kubatizidwa’ nawo; ndipo angakhoze “kudzozedwa” nawo. (Luka 1:41; Mat. 3:11; Mac. 10:38) Palibe alionse a mawu ameneŵa akakhala oyenerera ngati mzimu woyera unali munthu.
Yesu anatchulanso mzimu woyera kukhala “nkhoswe” (Chigiriki, pa·raʹkle·tos), ndipo ananena kuti nkhoswe imeneyi ikakhoza ‘kuphunzitsa,’ “kuchitira umboni,” “kulankhula,” ndi ‘kumva.’ (Yoh. 14:16, 17, 26; 15:26; 16:13) Sikuli kwachilendo m’Malemba kuti kanthu kena kanenedwe monga munthu. Mwachitsanzo, nzeru ikunenedwa kukhala iri ndi “ana.” (Luka 7:35) Uchimo ndi imfa zimanenedwa kukhala monga mafumu. (Aroma 5:14, 21) Pamene kuli kwakuti malemba ena amanena kuti mzimu “unalankhula,” malemba ena amanena momvekera bwino kuti zimenezi zinachitidwa kudzera mwa angelo kapena anthu. (Mac. 4:24, 25; 28:25; Mat. 10:19, 20; yerekezerani ndi Machitidwe 20:23 ndi 21:10, 11.) Pa 1 Yohane 5:6-8, simzimu wokha umene wanenedwa kukhala “ukuchitira umboni” komanso “madzi ndi mwazi.” Chotero, palibe alionse a mawu opezedwa m’malemba ameneŵa amene mwa iwo okha amatsimikizira kuti mzimu woyera ndimunthu.
Tanthauzo lolungama la mzimu woyera liyenera kuyenerana ndi malemba onse amene amatchula mzimuwo. Tiri ndi lingaliro limeneli, kuli koyenera kunena kuti mzimu woyera ndiwo mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu. Suli munthu, koma ndiyo nyonga yamphamvu imene Mulungu amachititsa kutuluka mwa iye kukwaniritsa chifuniro chake.—Sal. 104:30; 2 Pet. 1:21; Mac. 4:31.
Wonaninso tsamba 393, 394, pamutu wakuti “Utatu.”
Kodi nchiyani chimene chimapereka umboni wakuti munthu alidi ndi mzimu woyera, kapena “Mzukwa Woyera” (KJ)?
Luka 4:18, 31-35: “[Yesu anaŵerenga m’mpukutu wa mneneri Yesaya:] ‘Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka uthenga wabwino . . . Ndipo Iye anatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mudzi wa ku Galileya. Ndipo anali kuwaphunzitsa iwo pa Sabata; ndipo anadabwa ndi chiphunzitso chake; chifukwa mawu ake anali ndi ulamuliro. Ndipo munali m’sunagoge munthu, wokhala nacho chiŵanda chonyansa; nafuula ndi mawu olimba, . . . Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nutuluke mwa iye. Ndipo chiŵandacho mmene chinamgwetsa iye pakati, chinatuluka mwa iye chosampweteka konse.” (Kodi nchiyani chimene chinatsimikizira kuti Yesu anali ndi mzimu wa Mulungu? Cholembedwacho sichimanena kuti iye anathunthumira kapena anafuula kapena kuyendayenda mokangalika. Mmalo mwake, chimanena kuti analankhula mwaukumu. Komabe, kuli kokondweretsa kuwona, kuti panthaŵiyo mzimu wachiŵanda unachititsa munthuyo kufuula ndi kumgwetsera pansi.)
Mac. 1:8 amanena kuti pamene otsatira a Yesu analandira mzimu woyera akakhala mboni zake. Mogwirizana ndi kunena kwa Machitidwe 2:1-11, pamene analandira mzimu umenewo, openyerera anachita chidwi ndi chenicheni chakuti, ngakhale kuli kwakuti olankhula anali Agalileya, iwo anali kulankhula za zinthu zazikulu za Mulungu m’zinenero zimene zinali zozoloŵereka kwa alendo ambiri amene analipo. Koma cholembedwacho sichimanena kuti panali kufuula konyanyuka kulikonse pakati pa awo amene analandira mzimu.
Kuli kokondweretsa kuwona kuti pamene Elizabeti analandira mzimu woyera ndiyeno nanena “mawu ofuula” sanali mu msokhano wakupembedza koma anali kulonjera wachibale wodzacheza. (Luka 1:41, 42) Pamene, mzimu woyera unadza pa ophunzira osonkhanawo, monga momwe kwasimbidwira pa Machitidwe 4:31, malo amenewo anagwedezeka, koma chiyambukiro cha mzimu umenewo pa ophunzira sichinali chakuti, iwo ananthunthumira kapena kugubudukagubuduka, koma kuti ‘analankhula mawu a Mulungu molimbika mtima.’ Mofananamo lerolino, kulimba mtima m’kulankhula mawu a Mulungu kukhala ndi phande mwachangu m’ntchito yochitira umboni—zimenezi ndizo zimene zimapereka umboni wakuti manthuyo ali ndi mzimu woyera.
Agal. 5:22, 23: “Chipatso cha mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.” (Ndizo zipatso zimenezi, osati kufuula kogwidwa ndi mzimu kwachipembedzo, zimene munthu ayenera kuyang’anitsitsa pofunafuna kupeza anthu amene ali ndi mzimu wa Mulungu.)
Kodi luso la kulankhula ndi chisonkhezero chachikulu m’chinenero chimene munthuyo sanaphunzire ndi kale lonse limatsimikizira kuti iye ali ndi mzimu wa Mulungu?
Wonani mutu waukulu wakuti “M’Malirime, Kulankhula.”
Kodi kuchiritsa kozizwitsa kochitidwa m’tsiku lathu kukuchitidwa mwanjira ya mzimu wa Mulungu?
Wonani mutu waukulu wakuti “Kuchiritsa.”
Kodi ndani amene amabatizidwa ndi mzimu woyera?
Wonani tsamba 366 pamutu wakuti “Ubatizo,” ndiponso mutu waukulu wakuti “Kubadwanso.”
Kodi pali mbali yamzimu ya munthu imene imapulumuka imfa ya thupi?
Ezek. 18:4: “Moyo wochimwayo ndiwo udzafa.” (RS, NE, ndi Dy onsewo amamasulira liwu Lachihebri neʹphesh m’vesili kukhala “moyo,” motero amanena kuti moyo ndiwo umene umafa. Matembenuzidwe ena amene amamasulira neʹphesh kukhala “moyo” m’mavesi ena amagwiritsira ntchito mawu akuti “munthu” kapena “ameneyo” m’vesili. Chotero, neʹphesh, moyo, ndiye munthuyo, osati mbali inayake yapadera imene imapulumuka pamene thupi lake lifa.) (Wonani mutu waukulu wakuti “Moyo (Soul)” kaamba ka maumboni owonjezereka.)
Sal. 146:4: “Mpweya wake uchoka, abwerera kumka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitaika.” (Liwu Lachihebri lotembenuzidwa panopa kuti “mzimu” ndilochokera ku ruʹach. Otembenuza ena amalimasulira kukhala “mpweya.” Pamene ruʹach imeneyo kapena mphamvu ya moyo, ichoka m’thupi, malingaliro amunthuyo amawonongeka; iwo samapitirizabe kumalo ena.)
Mlal. 3:19-21: “Chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera nchimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onseŵa ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi chabe. Onse apita kumalo amodzi; onse achokera m’fumbi ndi onse abwereranso kufumbi. Ndani adziŵa mzimu wa ana a anthu wokwera kumwamba, ndi mzimu wanyama wotsikira kunsi ku dziko?” (Chifukwa cha choloŵa cha uchimo ndi imfa zochokera kwa Adamu, anthu onse amafa nabwerera kufumbi, monga momwe zimachitira nyama. Koma kodi munthu aliyense ali ndi mzimu umene umapitirizabe kukhala ndi moyo monga munthu waluntha utaleka kugwira ntchito m’thupi? Ayi; vesi 19 limayankha kuti anthu ndi nyama “onsewo ali ndi mpweya umodzi.” Kuchokera pamalingaliro a anthu, palibe munthu angayankhe motsimikizirika funso lodzutsidwa m’vesi 21 lonena za mzimu, Mawu a Mulungu amayankha kuti palibe chimene anthu ali nacho mwachibadwa chimene chimawapangitsa kukhala apamwamba kuposa nyama pamene afa. Komabe, chifukwa cha kakonzedwe ka chifundo cha Mulungu kupyolera mwa Kristu, chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha chatsegulidwa kwa anthu amene amasonyeza chikhululupiro, koma osati kuzinyama. Kwa anthu ambiri, zimenezo zidzatheketsedwa ndi chiukiriro, pamene mphamvu ya moyo yogwira ntchito yochokera kwa Mulungu idzawapatsa nyonga kachiŵirinso.)
Luka 23:46: ‘Yesu anafuula ndi mawu akulu, anati, Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu [Chigiriki, pneuʹmaʹ] wanga. Ndipo pakutero anatsirizika.’ (Tawonani kuti Yesu anatsirizika. Pamene mzimu wake unatuluka sanali kuyenda ulendo wakumwamba. Panali patsiku lachitatu pambuyo pa zimenezi pamene Yesu anaukitsidwa kwa akufa. Ndiyeno, monga momwe Machitidwe 1:3, 9 amasonyezera, panali masiku ena 40 iye asanakwere kumwamba. Chotero, kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la zimene Yesu adanena panthaŵi ya imfa yake? Iye anali kunena kuti anadziŵa kuti, pamene akafa, ziyembekezo za moyo wake wamtsogolo zinadalira kotheratu kwa Mulungu. Kaamba ka ndemanga zowonjezereka ponena za ‘mzimu umene umabwerera kwa Mulungu,’ wonani tsamba 297, 298, pamutu wakuti “Moyo (Soul).”)
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Kodi muli nawo mzimu woyera (kapena Mzukwa Woyera)?’
Mungayankhe kuti: ‘Inde, ndicho chifukwa chake ndadza pakhomo panu lerolino. (Mac. 2:17, 18)’
Kapena munganene kuti: ‘Ndiwo umene umanditheketsa kukhala ndi phande muuminisitala Wachikristu. Koma ndimapeza kuti anthu saali ndi lingaliro lofanana ponena za zimene zimapereka umboni wakuti munthu alidi ndi mzimu wa Mulungu. Kodi inu mumayang’ananji?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (Kukambitsirana kwa mfundo zina patsamba 320, 321.)