Kuika Ntchito ndi Kusangalala Pamlingo Wake
“KUSANGALALA ndicho chovala chokongola, koma sichingakhale chotero ngati sichisinthidwa.” Ndi mawu ameneŵa mlembi wina wosadziŵika akuchitira fanizo bwino lomwe mtengo wa kusangalala. Komabe, iye akusonyeza kuti kuyenera kulinganizidwa bwino ndi ntchito yothandiza.
Nkhani imeneyi inayankhulidwakonso ndi wolemba Baibulo wouziridwa Solomo. Mfumu yanzeru imeneyi inasonyeza zinthu zomkitsa ziŵiri zofunika kuzipeŵa. Poyamba, iye anati: “Chitsiru chimanga manja ake, nichidya nyama yake.” (Mlaliki 4:5) Inde, ulesi ungapangitse munthu kukhala waumphaŵi. Chotsatirapo chake n’chakuti ukhoza kuika pangozi thanzi la munthu waulesiyo, ngakhalenso moyo wake. Komanso, pali ena amene amagwira ntchito momkitsa. Solomo akufotokoza kugwira ntchito kwawo kosatha kukhala “chabe ndi kungosautsa mtima.”—Mlaliki 4:4.
Pachifukwa chimenechi, Solomo anati kuli bwino kuika zinthuzo m’malo mwake: “Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja aŵiri oti tho pali vuto ndi kungosautsa mtima.” (Mlaliki 4:6) Munthu ayenera ‘kuona zabwino chifukwa cha ntchito yake yaikulu’—ndiko kuti, nthaŵi zonse ayenera kumakhala ndi nthaŵi yosangalala ndi zimene wapeza. (Mlaliki 2:24) Komanso payenera kukhala zinthu zina m’moyo kuwonjezera pa ntchito yakuthupi. Banja lathu limafuna ina mwa nthaŵi yathu. Solomo anagogomeza kuti udindo wathu waukulu ndiwo utumiki wa Mulungu, osati ntchito yakuthupi. (Mlaliki 12:13) Kodi ndinu mmodzi wa iwo amene muli ndi kaonedwe kachikatikati ka ntchito?