-
Tiziona Ndalama MoyeneraGalamukani!—2007 | June
-
-
Zimene Baibulo Limanena
Tiziona Ndalama Moyenera
BAIBULO limati: “Ndalama zitchinjiriza.” (Mlaliki 7:12) Ndalama zingatitchinjirizedi kuti tisakhale pa umphawi chifukwa chakuti zingatithandize kupeza chakudya, zovala ndi pogona. Ndithudi, ndalama zingakuthandizeni kugula pafupifupi chinthu chilichonse. Lemba la Mlaliki 10:19 limati: “Ndalama zivomera zonse.”
-
-
Tiziona Ndalama MoyeneraGalamukani!—2007 | June
-
-
Chuma Choposa Ndalama
Mfumu Solomo itanena kuti ndalama zimatchinjiriza, inanenanso kuti “nzeru itchinjiriza” chifukwa “isunga moyo wa eni ake.” (Mlaliki 7:12) Kodi Solomo anatanthauza chiyani? Anali kunena za nzeru yobwera chifukwa chodziwa Malemba molondola ndi kuopa Mulungu. Mosiyana ndi ndalama, nzeru yochokera kwa Mulungu ingateteze munthu ku mavuto ambiri ndipo angakhale ndi moyo wautali. Komanso, anthu amene ali ndi nzeru imeneyi amakhala ngati avala korona, ndipo amapatsidwa ulemu. (Miyambo 2:10-22; 4:5-9) Nzeruyi imatchedwa “mtengo wa moyo” chifukwa chakuti imathandiza munthu kuti ayanjidwe ndi Mulungu.”—Miyambo 3:18.
Anthu amene amakonda nzeru imeneyi ndiponso amayesetsadi kuifunafuna, amaipeza. Baibulo limati: “Mwananga, . . . ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kum’dziwadi Mulungu. Pakuti Yehova apatsa nzeru; kudziwa ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake.”—Miyambo 2:1-6.
-