-
N’chiyani Chingatithandize Kuti Tizisankha Zinthu Mwanzeru?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
5. Muzilemekeza zikumbumtima za anthu ena
Anthu amene ndi osiyana amasankhanso zinthu mosiyana. Ndiye tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza zikumbumtima za anthu ena? Taganizirani zochitika ziwiri izi:
Chochitika choyamba: Mlongo amene anazolowera kuphoda wasamukira mumpingo wina umene alongo amumpingomo amaona kuti kuphoda si koyenera.
Werengani Aroma 15:1 ndi 1 Akorinto 10:23, 24, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
Malinga ndi mavesiwa, kodi mlongoyo angasankhe kuchita chiyani? Nanga inuyo mungatani ngati muli ndi munthu wina amene chikumbumtima chake sichikumulola kuchita zimene inuyo chikumbumtima chanu chikukulolani kuchita?
Chochitika chachiwiri: M’bale akudziwa bwino kuti Baibulo silimaletsa kumwa mowa mosapitirira malire, koma iyeyo wasankha kuti asamamwe mowa n’komwe. Kenako m’baleyo waitanidwa kuphwando ndipo akuona kuti abale ena akumwa mowa.
Werengani Mlaliki 7:16 ndi Aroma 14:1, 10, kenako mukambirane mafunso awa:
Malinga ndi mavesiwa, kodi m’baleyu angasankhe kuchita chiyani? Nanga inuyo mungatani ngati mwaona munthu wina amene chikumbumtima chake chikumulola kuchita zimene inuyo chikumbumtima chanu sichikukulolani kuchita?
Kodi ndi zinthu ziti zimene zingathandize munthu kusankha zinthu mwanzeru?
1. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kusankha zoyenera kuchita.—Yakobo 1:5.
2. Muzifufuza m’Baibulo, mabuku ndi zinthu zina zimene gulu lathu limafalitsa kuti mupeze mfundo zimene zingakuthandizeni. Mukhozanso kulankhulana ndi Akhristu okhwima mwauzimu.
3. Muziganizira mmene zosankha zanu zingakhudzire chikumbumtima chanu komanso zikumbumtima za anthu ena.
-
-
Mungatani Kuti Zimene Mumalankhula Zizisangalatsa Yehova?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
5. Muzilankhula zinthu zabwino zokhudza ena
Kodi tingapewe bwanji kulankhula mawu omwe angakhumudwitse anthu ena? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
N’chifukwa chiyani m’bale wamuvidiyoyi ankafunika kusintha mmene amalankhulira zokhudza anthu ena?
Nanga anachita chiyani kuti asinthe?
Werengani Mlaliki 7:16, kenako mukambirane funso ili:
Kodi tizikumbukira mfundo iti kuti tipewe kulankhula zinthu zoipa zokhudza munthu winawake?
Werengani Mlaliki 7:21, 22, kenako mukambirane funso ili:
Kodi mavesiwa angakuthandizeni bwanji kuti musamafulumire kupsa mtima munthu wina akalankhula zoipa zokhudza inuyo?
-