Pamene Kufa Kumakhaladi Kufa
“Galu wamoyo aposa mkango wakufa. Pakuti amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.”—Mlaliki 9:4, 5.
ANTHU ambiri ali ndi chikhulupiriro chosamveka bwino chakuti munthu ali ndi mzimu umene umapitiriza kukhalapo pambuyo pakuti munthuyo wafa kapena amangopitiriza kumakabadwanso kwina. Ena amakhulupiriranso kuti munthu akhoza kuuka atafa. Thomas Lynch, wogwira ntchito m’motchale, posachedwapa anafunsidwa malingaliro ake ponena za moyo wa pambuyo pa imfa. Iye anati: “Anthu aja amene amati aona kuwala ndi zina zotero sakhala atabwera kuchokera kwa akufa—amakhala kuti anafika chabe pakuti sitimatha kupima ndi kupeza zizindikiro zakuti ali moyo. Chifukwa ‘kufa’ mpamene wafika poti sungabwerekonso.”—The New York Times Magazine.
Baibulo linanena kale molondola zaka zikwi zambiri zapita. “Galu wamoyo aposa mkango wakufa. Pakuti amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi, sadzalandira mphotho; pakuti angoiŵalika.” (Mlaliki 9:4, 5) Mutangoyendera pang’ono manda akale mudzatsimikiza choonadi chimenechi.
Kodi zikutanthauza kuti palibe chiyembekezo kwa akufa? Baibulo silinenapo konse za chikhulupiriro cha moyo womwe umapitiriza kukhalapobe pambuyo pa imfa. (Genesis 2:7; Ezekieli 18:4, 20) Koma Yesu Kristu ankalalikira za kuukira ku moyo m’paradaiso padziko lapansi. Womtsatira wachiyuda wotchedwa Marita, amene mlongo wake, Lazaro, anali atangofa kumene, ankakhulupirira chiukiriro, popeza anati ponena za Lazaro: “Ndidziŵa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomaliza.” (Yohane 11:24) Pa zimenezi, Yesu anayankha kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthaŵi yonse. Kodi ukhulupirira ichi?” (Yohane 11:25, 26) Nkuti kumbuyoko anali atanena kuti: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.” Koma onani, Yesu sananenepo za mzimu womwe sukufa!—Yohane 5:28, 29; Luka 23:43.
[Mawu Otsindika patsamba 31]
“‘kufa’ mpamene wafika poti sungabwerekonso.”—Thomas Lynch, mortician