Kunyalanyaza Machenjezo ndi Kuyesa Mulungu
“Ngakhale pamene madzi anafika mu kakolo kawo iwo sanafune kuthaŵa.”—El País, Colombia.
MUTU waukulu umenewo wochokera ku nyuzipepala ya tsiku ndi tsiku ya Colombia unawunikira chimodzi cha zifukwa za kutaya kowopsya kwa moyo mu tsoka la chigumula cha Armero cha mu November 1985. Dora Elisa Rada Esguerra, wogwira ntchito ku ofesi ya lamya ku Armero, atagalamutsidwa ndi kugwa kwa phulusa ndi kusefukira kwa mitsinje, analingalira zothaŵa. Kenaka iye anachenjeza anzake ogwira nawo ntchito pa malo osinthira lamya za tsoka lomadzalo. Iye pambuyo pake analongosola kuti: “Iwo anawona madziwo, omwe anali . . . kuyenda mwamphamvu, mwamphamvu kwambiri, koma ngakhale pamenepo iwo sanasunthe. Dora anathaŵa kuchokera ku mzinda wosakazidwawo.
Ogwira ntchito pa ofesi ya lamya enawo anafa limodzi ndi minkhole ina 21,000 ya mtsinje wa matope a kuphulika kwa thanthwe lotentha la pansi pa nthaka, madzi owundana, ndi miyala yaikulu yomwe inayenda kutsika kuchokera ku kuphulika kwa thanthwe lotentha la pansi pa nthaka la Nevado del Ruiz. Pakati pa awo omwe anasesedwa anali nduna yaikulu ya mzindawo ndi ambiri a gulu la apolisi a kumaloko, chomwe chikusonyeza kuti palibe ndi m’modzi yemwe anatenga chiwopsyezocho mosamalitsa kufikira—chinali kuchedwa kwenikweni.
Nchifukwa Ninji Sanathaŵe?
Panali zizindikiro ndi machenjezo a kudza kwa tsoka. Nchifukwa ninji anthu ambiri chotero mu Armero ananyalanyaza iwo? Choyambirira, machenjezo alamulo anabwera mochedwa, pamene tsokalo linali kale kukantha mzindawo. Kumayambiriro kwa ichi, anthu anali atauzidwa kukhala bata, kuti pangakhale kusefukira kwa madzi koma sichidzakhala chinachake chowopsya kwambiri. M’malomwake, mzindawo unasesedwa pa mapu ndi khoma lalikulu la imfa lomwe linagwera pa mtsinje wa Lagunilla.
Mwachidziŵikire, ena sanafune kusiya nyumba zawo ndi chuma chawo, akumadziŵa kuti posakhalitsa ofunkha adzaloŵa ndi kuba. Ichi chinatembenuka kukhala chiwopsyezo chenicheni. Ofunkha ochepa anaphedwa ndi gulu la nkhondo. Ena omwe anapulumuka tsokalo anabwerera kunyumba zawo zodzazidwa ndi madzi popeza kuti maloko anachotsedwa pa zitseko ndipo zinthu zamtengo wapatali zinabedwa. Koma ambiri a anthu a mu mzindawo sanakhale ndi moyo kwa utali wokwanira kubwereranso ku nyumba zawo. Ndipo mu nkhani zambiri, panalibe nyumba zoti abwerereko.
Mwinamwake ena anachimva kuti Mulungu kapena Namwali Mariya adzaloŵereramo m’malo mwawo. Komabe, kodi chiri chanzeru kuyembekezera Mulungu kuloŵerera lerolino m’malo mwa anthu ena pamene tsoka la chilengedwe lichitika? Nchifukwa ninji ena ayenera kupulumutsidwa mwa kuloŵerera kwa umulungu ndipo ena, mkhalidwe umodzimodziwo, kuloledwa kuwonongedwa?
Kodi pali maziko olimba kaamba ka munthu kukhulupirira kuti iye angatsogoze moyo wachisomo ndi chinjirizo lapadera kuchokera kwa Mulungu? Mwachitsanzo, kodi woyendetsa galimoto angakhulupirire mwa “mngelo wake wotetezera” kapena “woyera” kapena wa pamtima? Akatolika owona mtima ambiri okhala ndi mamedulo a Christopher “Woyera” anafa mu ngozi za galimoto chifukwa cha kukhulupirira chimenecho. Kapena kodi Mkristu ayenera kukhulupirira kuti iye ali ndi chinjirizo lapadera la Mulungu pamene akuyenda pa ulendo wa pa ndege? Bwanji ponena za chinjirizo lapadera pamene tikutengamo mbali m’maseŵera ena owopsya? Kodi chiri chanzeru kuyesa Mulungu m’mikhalidwe yotero?
Dzanja la Yehova Silalifupi
Malemba amatithandiza ife kuwona kuti kuli mikhalidwe mu imene Yehova Mulungu angalowereremo m’malo mwa anthu ake pamene kulalikira kwa mbiri yabwino ya Ufumu kwayandikira kapena pamene mpingo wake wawopsyezedwa. Mneneri Yesaya anatitsimikizira ife kuti: “Tawonani! mkono wa Yehova sufupika, kuti sangathe kupulumutsa; khutu lake siliri logontha, kuti silingamve.”—Yesaya 59:1.
Baibulo limapereka zitsanzo zomvekera bwino za dzanja lochinjiriza la Yehova m’chigwirizano ndi atumwi. Mfumu Herode, akufuna kupeza chiyanjo ndi Ayuda, anapangitsa Petro kuikidwa m’ndende pansi pa olindilira amphamvu. Mpingo mu Yerusalemu unapemphera mofunitsitsa m’malomwake. Nchiyani chimene chinachitika? Mngelo wa Yehova anabwera ndi kumasula Petro kuchokera ku ukaidi. Ngakhale Petro anazizwitsidwa ndi zomwe zinali kuchitika. Kenaka iye anazindikira zimene zinali kuchitika ndipo ananena kuti: “Tsopano ndidziŵa zowona, kuti [Yehova NW] anatuma mngelo wake nandilanditsa ine m’dzanja la Herode.”—Machitidwe 12:1-11.
Mbiri imodzimodziyo ikutiwuza ife kuti Herode anali atapha kale mtumwi Yakobo, mbale wa Yohane. Yehova anavomereza kufa kumeneko kuchitika. Chotero, chiri chodziŵikiratu kuti pamene kuli kwakuti Yehova angapereke chinjirizo ndi chipulumutso, iye angavomereze zinthu kuchitika m’njira zake, ndipo chotero kulola ena a atumiki ake odzipereka kutsimikizira umphumphu wawo ngakhale kufikira imfa. Mawu a Yakobo, mbale wopeza wa Yesu, ali oyenera: “Simudziŵa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuwonekera kanthaŵi, ndi pamenepo ukanganuka. Mukadanena inu: ‘Akalola [Yehova NW], ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakuti kakuti.’”—Yakobo 4:14, 15; yerekezani ndi Yobu 2:3-5.
Chinthu chimodzi chiri chotsimikizirika, mu nthaŵi za tsoka ndi ngozi za chilengedwe, prinsipulo la Baibulo limagwira ntchito mofanana kwa anthu onse: “Nthaŵi ndi zochitika zosawonekeratu zimagwera iwo onse.” (Mlaliki 9:11, NW) Ndipo pamene kuli kwakuti chiri choyenerera kupemphera kaamba ka thandizo ndi chinjirizo mu nthaŵi za chizunzo, tiyenera kuzindikira kuti “chizunzo chiri chosapeweka kwa awo amene azitsimikizira kukhala ndi miyoyo ya Chikristu.”—2 Timoteo 3:12, Phillips.
Mzimu wa Kudziletsa
Pamene kuli kwakuti chiri chowona kuti nthaŵi zapita Yehova anachitapo kanthu kuchinjiriza anthu ake, monga mmene iye anapulumutsira Aisrayeli kuchokera ku Igupto ndi kuchokera ku magulu a Farao, chingakhale cholakwa kulingalira kuti Mulungu ayenera kuchinjiriza Mkristu aliyense kuchokera ku zotulukapo za ‘nthaŵi ndi mikhalidwe yosawonedweratu’ kapena kuchokera ku zotulukapo za kupanda nzeru kwake. Kalata ya Paulo kwa Akristu mu Roma, ena a amene mwinamwake anafa pambuyo pake mu bwalo la chiwonetsero monga mboni, iri ndi chiyambukiro pa ichi: “Ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa mmene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagaŵira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.” (Aroma 12:3) Matembenuzidwe a J. B. Phillips amanena kuti: “Yesani kukhala ndi kuyerekezera kwabwino kwa zothekera zanu.”
Uphungu wolongosoledwa pano uli ndi kugwira ntchito kofafanako lerolino, ngakhale kuti ndi mu mkhalidwe wosiyanako. Ngati Mkristu aganiza kuti iye angayendetse galimoto mosasamala kapena pansi pa chisonkhezero cha zakumwa zoledzeretsa ndi kupulumuka chifukwa iye ali ndi chinjirizo la Mulungu, kodi chimenechi chimasonyeza “kudziletsa yekha”? Kodi Mkristuyo ali ndi ‘kuyerekezera kwabwino kwa kuthekera kwake’? Ndiponso, ngati iye aika anthu anzake m’ngozi, kodi iye ndithudi ‘amakonda m’nansi wake monga iyemwini’?—Mateyu 22:39.
Tsopano lolani kuti tigwiritsire ntchito mzimu wa kudziletsa ku mkhalidwe umene munthu wakhazikitsa midzi m’malo omwe ali oyedzamira ku kukhala ndi zivomezi kapena kumene matanthwe otentha a pansi pa nthaka okangalika amaimira chiwopsyezo chosawoneka koma chenicheni. Chitsanzo chabwino chiri dera lotchulidwa kale kuzungulira thanthwe lotentha la pansi pa nthaka la Nevado del Ruiz mu Colombia. Mogwirizana ndi nyuzipepala ya tsiku ndi tsiku ya ku Colombia El País, katswiri wa luso la zomangamanga César Zárate anakonza phunziro mu 1982 lomwe linasonyeza kuti mtsinje wa Lagunilla unasefukira Armero mu nthaŵi yapita ndipo kuti mzindawo kufikira tsopano ulibe chinjirizo lokwanira. Chinadziŵikanso kuti thanthwe lotentha la pansi pa nthaka la Nevado del Ruiz linaphulikapo nthaŵi zisanu ndi imodzi kuyambira 1570. Mogwirizana ndi magwero a mbiri yakale, thanthwe lotentha la pansi pa nthakalo liri ndi zungulirezungulire wokhazikika wa kugwira ntchito komwe kumasinthasintha pakati pa zaka 140 miyezi 9 ndi zaka 110 miyezi 2.
Chidziŵitso chimenechi chinatumizidwa ku chofalitsidwa cha pa Sande cha nyuzipepala ya ku Colombia El Tiempo milungu ingapo kumayambiriro kwa tsoka la Armero. Chinanena mwachindunji kuti: “Kusefukira kwa madzi kotsatira . . . kudzachitika chifupifupi mkati mwa November wa chaka chino. Zizindikiro zotsimikizirika zawonedwa kale: utsi kuchokera ku chiboo cha ‘Arena’. Mvula ya phulusa ndi nthunzi. Kuipitsidwa kwa madzi ndi mbewu. Fungo lochititsa nseru. . . . Kumveka kwa kulirima kuchokera mu thanthwe lotentha la pansi pa nthaka pa September 11. Kusungunuka kopita patsogolo kwa chipale chofeŵa cha pamwamba pa phiri . . . Chotero, iri nthaŵi ya kuchitapo kanthu.”
Komabe, nkhaniyo siinafalitsidwe. Mwinamwake inawonedwa monga chenjezo losayenera la tsoka. Alembi a El Tiempo pambuyo pake anachiika icho pansi ku “kusoweka kwa kuwoneratu za mtsogolo, kusoweka kwa kuzindikira, kapena lingaliro loposa lakuti palibe chimene chingachitike.”
Pa ndandanda kwenikweni, ngakhale kuli tero, Nevado del Ruiz inaphulitsa pamwamba pake pa usiku wa November 13, 1985. Anthu oposa 20,000 anataya miyoyo yawo mu Armero, ndipo kunali zikwi za minkhole kuchokera ku Chinchiná ndi mizinda ina yapafupipo. Pakati pa awo omwe anafa mu Armero panali Mboni za Yehova 41 ndi oyanjana nawo awo. Ena mosachenjezedwa anathaŵira ku Nyumba ya Ufumu, yomwe inali pa malo otsika. Iwo anasesedwa ndi kuikidwa chiriza ndi iyo. Mwachimwemwe, mboni zina zinali zokhoza kuthaŵira ku malo okwera ndipo zinapulumuka.
Mwachiwonekere, nzeru pambuyo pa chochitika iri yopepuka. Koma chifupifupi maphunziro angatengedwe kuchokera ku zochitika zowopsya zimenezo.
Machenjezo a Kale Ananyalanyazidwa
Baibulo limapereka zitsanzo za ena omwe ananyalanyaza machenjezo a panthaŵi yake kapena analingalira kuti ‘sichingachitike m’nthawi yawo’ kapena m’dera lawo la padziko lapansi. Nkhani imodzi yodziŵika koposa inali kumene Loti anachenjezedwa kuthaŵa ku Sodomu ndi Gomora. Iye anachenjeza akamwini ake, akumanena kuti: “Taukani! Tulukani m’malo muno, popeza Yehova adzawononga mudziwu!” Ndimotani mmene iwo anavomerezera? “Akamwini ake anamuyesa [Loti] wongoseka.” “Kuseka” kumeneko kunali kwa kanthaŵi kochepa. Yehova anakupangitsa kuvumba sulfure ndi moto pa mizinda yoweruzidwa, yoipayo. Akamwiniwo anafa limodzi ndi nzika za makhalidwe oipa za gawo limenelo. Mkazi wa Loti mwachiwonekere anathaŵa kuchokera ku Sodomu ndi zikaikiro ndi kusakhulupirira. Iye “anacheuka ali kumbuyo kwake [kwa Loti], nasanduka chulu cha mchere.”—Genesis 19:12-26.
Mkati mwa zaka 1,900 zapita, Yesu analosera kuti Yerusalemu wakale adzapita pansi pa chiwonongeko chowopsya. Iye anapereka tsatanetsatane wachindunji wa zochitika zomwe zidzachitika mzindawo usanakhale bwinja, akumanena kuti: “Koma pamene pali ponse mudzawona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira.” Iye anawonjezera chenjezo lakuti: “Pamenepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri, ndi iwo ali m’kati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumiraga asalowemo.”—Luka 21:20-24.
Pamene magulu a nkhondo a Roma anazinga Yerusalemu m’chaka cha 66 C.E., Akristu mu mzinda umenewo anazindikira chizindikiro chimene Yesu anali atapereka. Kenaka, kugonjetsa kotheratu kuli pafupi naye, Nduna Cestius Gallus popanda chifukwa chenicheni anachotsa magulu ake ankhondo. Umenewo unali mwaŵi umene Akristu anali kuuyembekezera, ndipo iwo anathaŵira ku mbali ina ya Yordani. Mu 70 C.E. Aroma anabwereranso pansi pa Nduna Titus ndi kuwononga Yerusalemu. Mazana a zikwi za Ayuda omwe anatsala mu mzinda woweruzidwawo anafa mkati mwa kuukiridwa ndi kumenyana.
Zowona, m’nkhani izi chenjezo laumulungu linaperekedwa. Koma nsonga iri yakuti kokha ochepa analabadira uthengawu ndipo anapulumuka. Ambiri sanadziŵa. Iwo anakana kutenga chenjezo la Mulungu mosamalitsa.
Ndi Mwanjira Yotani Mmene Moyenerera Tingayesere Mulungu?
Ngakhale ndi matsoka a chilengedwe, kaŵirikaŵiri kumakhala machenjezo—mbiri yakale ya deralo, zizindikiro za posachedwapa, kapena zisonyezero za usayansi—zomwe zimasonyeza kuthekera kwa mphamvu ya tsoka mkati mwa nthaŵi ya nyengo ina yake. Mwinamwake deralo liri lokhoterera ku kusefukiridwa ndi madzi. Chotero munthu wolingalira ayenera kuyesa nsonga zonse kulingalira ngati kupita ku boma lina kuli koyenerera ndipo kothekera. Ndithudi, sichiri chotheka kudziŵiratu nthaŵi ndi malo a tsoka la chilengedwe lirilonse. Komabe, lamulo la ma avereji liyenera kuŵerengeredwa ndiponso malire achitetezero ngati choipitsitsa chitachitika. Koma sichiri chanzeru kuyembekezera chinjirizo lapadera kuchokera kwa Mulungu. Kuchita tero kungakhale kuika Mulungu ku chiyeso m’njira imene siiri ya lamulo kapena yolinganizika.
Ngakhale kuli tero, mlingaliro losiyana, Yehova amatiitana ife kumuyesa iye. Kubwerera m’nthawi ya mneneri Malaki, Israyeli anali kuyesa Mulungu molakwa mwakupereka nsembe zonyansa pa guwa la nsembe. Ndi mkate wawo woipa ndi nsembe za nyama zopunduka, iwo anasonyeza kuti amanyoza gome la Yehova. Kupyolera mwa Malaki, Yehova anaitana iwo kutembenuka ndi kuwongolera njira yawo ya kachitidwe ka zinthu. “‘Mubwere nalo limodzi limodzi lonse la khumi, ku nyumba yosungiramo, kuti m’nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono,’ ati Yehova wa makamu, ‘ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.’”—Malaki 3:10.
Inde, m’chigwirizano ndi madalitso auzimu, “tingayese,” kapena kutsimikizira, kukhulupirika kwa Yehova. Ngati tifuna choyamba Ufumu wake ndi chilungamo chake, chotero, monga mmene Yesu ananenera, ‘zinthu zina zonse zoyenerera zidzawonjezeredwa kwa ife.’ Yesu ananenanso kuti: “Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza. Gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu.” Ngati anthu opanda ungwiro amapereka mphatso za chifundo kwa ana awo, “Kopambana kotani nanga Atate wanu wa kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha iye [m’chigwirizano ndi chifuno chake]?”—Mateyu 6:33; 7:7-11; 1 Yohane 5:14.
Pa nthaŵi ino, chenjezo likuperekedwa kwa mitundu ku chiyambukiro chakuti mwamsanga Yehova adzayambitsa kachitidwe kake kobwezera motsutsana ndi mbali zonse za dongosolo iri la zinthu la Satana. (Chivumbulutso 16:14, 16; 18:20) Mamiliyoni a anthu a nzeru akulabadira uthenga uwu wolalikidwa ndi Mboni za Yehova ndipo akudzipatula iwo eni kupita ku mbali ya ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu. Iwo akutuluka m’chigwirizano choipa cha ndale zadziko ndi chipembedzo mwamsanga kusanakhale kuchedwa. (Chivumbulutso 18:4) Mwakuchita tero, iwo akudzikonzekeretsa kaamba ka moyo wosatha pansi pa ulamuliro wa Kristu pa dziko lathu lapansi, lomwe lidzatembenuzidwa kukhala paradaiso wa chilungamo ndi wolingana. Kodi mukulabadira chenjezo limeneli?—2 Petro 3:13; Tito 1:2.
[Chithunzi patsamba 21]
Chikalata chosonyeza kumaliza maphunziro apamwamba chopezedwa mu bwinja la Armero chiri chikumbutso choipa chakuti zikwi sizinalabadire machenjezo
[Chithunzi patsamba 22]
Kodi zizoloŵezi zanu za kuyendetsa galimoto zimaunikira kudziletsa kwa Chikristu?
[Zithunzi patsamba 23]
Malo amene tsopano ali bwinja kumene Armero anali. Anthu oposa 20,000 anatha pano
Galimoto yophwanyikayi imalongosola bwino tsoka lomwe inakantha Armero