N’zotheka Kukhala Wosangalala Panopa Komanso Kwamuyaya
KUTSATIRA mfundo zopezeka m’Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, kungakuthandizeni kukhala ndi moyo wosangalala ndiponso waphindu ngakhale panopa. Tiyeni tikambirane zina mwa mfundo zimenezi.
MFUNDO YA M’BAIBULO: Mfumu Solomo inalemba kuti: “Palibe chabwino kuposa kuti [munthu] adye, amwe, ndi kusangalatsa mtima wake chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.”—MLALIKI 2:24.
Anthufe tinalengedwa kuti tizisangalala tikagwira ntchito yabwino. Choncho ngakhale mutakhala kuti mukukumana ndi mavuto, mukhoza kukhalabe wosangalala chifukwa chogwira ntchito mwakhama komanso moona mtima.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”—MACHITIDWE 20:35.
Anthu ambiri aona kuti kugwiritsira ntchito nthawi komanso mphamvu zawo pothandiza anthu amene akumana ndi mavuto, kwawathandiza kuti azikhala osangalala ndiponso kuti apeze madalitso ambiri. Solomo analemba kuti: “Usalephere kuchitira zabwino anthu amene akufunikira zabwinozo, pamene dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.”—Miyambo 3:27.
Taganizirani chitsanzo cha bambo wina dzina lake Ralph. Atapuma pa ntchito, iye anayamba kuchita utumiki wachikhristu wolalikira nthawi zonse umenenso mkazi wake ankachita. Tsopano iye ndi mkazi wake amalalikira kwa maola ambiri mwezi uliwonse kuti athandize anthu kudziwa choonadi cha m’Baibulo. Ralph ananena kuti: “Tikamabwera kunyumba madzulo timakhala titatopa chifukwa cha uchikulire komanso chifukwa chogwira ntchito kwambiri potumikira Atate wathu wakumwamba. Komabe sitidandaula chifukwa timadziwa kuti tatopa pa chifukwa chabwino.” Iye ndi mkazi wake ndi osangalala kwambiri chifukwa amathera nthawi yawo yambiri akuthandiza ena.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo ilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—MIYAMBO 17:17.
Munthu amene wakumana ndi mavuto akafotokozera ena, amamvako bwino mumtima mwake. Katswiri wina wolemba nkhani wa ku England, dzina lake Francis Bacon anafotokoza kuti anthu amene alibe anzawo apamtima amakhala ngati “ali okhaokha m’chipululu.” Kukhala bwenzi labwino komanso kukhala ndi mabwenzi abwino kumathandiza munthu kuti azisangalala komanso kuti zinthu zizimuyendera bwino pa moyo wake.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—MATEYU 5:3.
Pamenepatu Yesu anatchula chinthu chofunika kwambiri chimene tiyenera kuchita ngati tikufuna kudzasangalala ndi malonjezo a Mulungu. Iye anasonyeza kuti chofunika ndi kuzindikira ‘zosowa zathu zauzimu’ ndiponso kuyesetsa kuti tizipeze. Anthufe timasiyana ndi nyama chifukwa timabadwa ndi chikhumbo chofuna kudziwa cholinga cha moyo. Yehova Mulungu yekha ndi amene angatithandize kukwaniritsa chikhumbo chimenechi ndipo amachita zimenezi kudzera m’Mawu ake Baibulo. Ndipo monga mmene taonera m’nkhani yapitayi, Baibulo limatiuza cholinga cha Mulungu polenga dziko lapansili. Limatiuzanso chifukwa chake anthufe tili padzikoli, chifukwa chake padzikoli pali mavuto ambiri chonchi, komanso zimene Mulungu amafuna kuti tizichita. Kuti tikhale ndi moyo wosangalala komanso waphindu, tiyenera kudziwa komanso kumvetsetsa mfundo za m’Baibulo ngati zimenezi. Anthu amene amayesetsa kupeza nthawi yophunzira Baibulo, n’kumatsatira zimenezo pa moyo wawo, amakhala osangalala. Izi zili choncho chifukwa akamachita zimenezi amakhala akulimbitsa ubwenzi wawo ndi Mlengi wathu Yehova, yemwe ndi “Mulungu wachimwemwe.”—1 Timoteyo 1:11.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kumbukira Mlengi wako Wamkulu . . . asanafike masiku oipa komanso zisanafike zaka zimene udzati: ‘Moyo sukundisangalatsa.’”—MLALIKI 12:1.
Palembali, Mfumu Solomo inalangiza achinyamata chifukwa nthawi zina amalephera kuzindikira mavuto amene munthu angakumane nawo pa moyo. Komabe malangizowa angathandizenso aliyense. Choncho muzionetsetsa kuti cholinga chanu chachikulu ndi kutumikira Mlengi wanu. Kuchita zimenezi n’kumene kungapangitse kuti moyo wanu uzikhala waphindu. Muzipewa maganizo akuti: “Tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.” (1 Akorinto 15:32) Lemba la Mlaliki 8:12 limati mukamaika Mulungu pamalo oyamba pa moyo wanu, zinthu ‘zidzakuyenderani bwino.’
Mtsikana wina dzina lake Wendi anaona kuti zimenezi ndi zoona. Ali wamng’ono, iye ndi mng’ono wake anaphunzira Chisipanishi n’cholinga chakuti asamukire ku Dominican Republic, komwe kunali anthu ochepa olalikira uthenga wabwino wa m’Baibulo. Wendi anati: “Tinadzimana zinthu zambiri n’cholinga chakuti tithe kukatumikira kuderali, komabe timaona kuti nthawi imeneyi ndi imene tinasangalala kwambiri pa moyo wathu. Komanso ndimaona kuti palibe chilichonse chaphindu chimene ndikanachita pa miyezi 6 imeneyi choposa zimene tinachitazi. Madalitso amene tapeza ndi ambiri moti sitidandaula kuti tinasiya zinthu zina.”
Kukhulupirika Kumachititsa Munthu Kukhala Wosangalala
Anthu amene amalimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova amakhala ndi moyo wosangalala komanso waphindu kwambiri. N’chifukwa chiyani zili choncho? Pamene Satana anapangitsa kuti Adamu ndi Hava apandukire ulamuliro wa Mulungu, anasonyezanso kuti palibe munthu amene angakhalebe wokhulupirika kwa Mulungu atakumana ndi mayesero. (Yobu 1:9-11; 2:4) Choncho inunso mungathandize nawo kusonyeza kuti zimene Satana ananenazi ndi zabodza. Mungachite zimenezi mwa kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu, kutsatira malangizo ake ndiponso kusonyeza kuti mumazindikira kuti Yehova ndiye woyenera kutiuza chabwino ndi choipa.—Chivumbulutso 4:11.
Komabe, pamene tikuyesetsa kuchita zabwino pa moyo wathu tingakumane ndi mavuto. Koma kodi mavuto amenewo angatilepheretse kukhala ndi moyo waphindu? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tiyerekeze kuti pali mdani woipa kwambiri amene akuipitsa mbiri ya mnzathu kapena m’bale wathu. Ndiyeno zimene tikuchita poyesetsa kuteteza mbiri ya mnzathu kapena m’bale wathuyo zikutichititsa kuti tikumane ndi mavuto. Kodi mavuto amenewo angatichititse kuona kuti moyo wathu ndi wopanda phindu? Ayi ndithu. M’malomwake tingalolere kukumana ndi mavutowo n’cholinga choti mbiri ya mnzathu kapena m’bale wathu isaipe. Zimenezi n’zofanana ndi kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu. Anthufe tikamakhulupirika kwa Mulungu ngakhale tikukumana ndi mavuto, iye amasangalala kwambiri.—Miyambo 27:11.
Mungakhale Ndi Moyo Waphindu Panopo Mpaka Muyaya
Malinga ndi mfundo zimene takambiranazi, yesetsani kuchita chilichonse chimene mungathe kuti muphunzire za Mulungu komanso cholinga chake. Yesu Khristu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Mulungu akadzakwaniritsa cholinga chake chokhudza dziko lapansili, anthu adzakhala ndi “moyo wosatha” m’paradaiso ndipo izi n’zimene Yehova ankafuna kuyambira kale. Pa nthawi imeneyi moyo udzakhaladi wosangalatsa ndiponso waphindu.—Salimo 145:16.
Choncho popeza Yesu ananena kuti tiyenera kuphunzira za Mulungu kuti tidzapeze moyo wosatha, kodi mungaziphunzire kuti zimenezo? Mungaziphunzire m’Baibulo lomwe ndi Mawu a Mulungu. Ngati mungafune munthu wina woti akuthandizeni kuphunzira Baibulo, pemphani amene amafalitsa magazini ino. Iwo adzakonza zoti muyambe kuphunzira Baibulo.