-
Chilichonse Chili ndi NthawiNsanja ya Olonda—2009 | March 1
-
-
Ponena kuti kalikonse kali ndi nthawi yake, sikuti wolemba Baibuloyu ankatanthauza kuti Mulungu anakonzeratu zochitika za pa moyo wa munthu aliyense, koma anali kunena za cholinga cha Mulungu ndi mmene chidzakhudzire anthu. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Tikudziwa zimenezi chifukwa cha zimene nkhaniyo ikunena. Atatchula zinthu zambiri zokhala ndi “nthawi yake,” Solomo anati: “Ndaona vuto [zochita, NW] limene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti avutidwe nalo. Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake.”—Mlaliki 3:10, 11.
Inde, Mulungu anapatsa anthu zochita zambirimbiri ndipo Solomo anatchulapo zingapo. Mulungu anatipatsanso ufulu wosankha tokha zochita. Komano chilichonse chili ndi nthawi yake yabwino kwambiri yochichitira. Mwachitsanzo, taganizirani mawu a Solomo akuti “mphindi yakubzala ndi mphindi yakuzula zobzalazo” omwe ali pa Mlaliki 3:2. Alimi amadziwa kuti mbewu iliyonse ili ndi nthawi yabwino yobzalira. Ndiye kodi chingachitike n’chiyani ngati mlimi atanyalanyaza mfundo imeneyi n’kubzala mbewu panyengo yolakwika? Kodi zingakhale zomveka ngati mlimiyo atanena kuti walephera kukolola bwino chifukwa choti zinalembedweratu? Ayi n’zosamveka. Vuto n’lakuti iyeyo sanabzale mbewuzo panthawi yoyenera. Mlimiyo akanachita bwino akanatsatira dongosolo lobzalira mbewu limene Mlengi anakhazikitsa m’chilengedwe.
Motero, tingathe kuona kuti Mulungu sanakonzeretu zochitika pa moyo wa munthu kapena zotsatirapo za zinthu zonse zimene zimachitika, koma anakonzeratu mfundo zinazake zothandiza kuti zochita za anthu zigwirizane ndi cholinga chake. Motero, kuti zochita za anthu ziwayendere bwino, iwo ayenera kudziwa cholinga cha Mulungu ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi cholingacho. Choncho cholinga cha Mulungu n’chimene chinakonzedweratu ndipo sichingasinthidwe koma osati zochitika za pa moyo wa munthu. Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova anati: “Momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka mkamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”—Yesaya 55:11.
-
-
Chilichonse Chili ndi NthawiNsanja ya Olonda—2009 | March 1
-
-
M’pofunika Kumvetsa Nthawi ya Mulungu
Mawu a Solomo angatithandize kumvetsa nkhaniyi. Iye atanena kuti “chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake” anatinso “ndipo waika zamuyaya m’mitima yawo ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.”—Mlaliki 3:11.
Pali zambiri zimene zalembedwa pofotokozera lemba limeneli. Koma mfundo ndi yakuti, tonsefe panthawi inayake tinadzifunsapo kuti, ‘Kodi cholinga cha moyo n’chiyani nanga tsogolo lathu n’lotani?’ Kuyambira kalekale, anthu akhala akuvutika kumvetsa kuti n’chifukwa chiyani timavutika kugwira ntchito mwakhama pamoyo wathu koma kenako n’kumwalira. Ndi anthu okha amene amaganiza za moyo wawo panopo komanso za tsogolo lawo. Anthufe timalakalakanso kukhala ndi moyo wamuyaya. Timatero chifukwa Malemba amafotokoza kuti, Mulungu “waika zamuyaya m’mitima” ya anthu.
Chifukwa cha mtima wofuna moyo wamuyayawu, anthu akhala akudzifunsa kuti, ‘Kodi palinso moyo wina umene munthu amakhala nawo pambuyo pa imfa?’ Ena amanena kuti pali chinachake chimene chimakhalabe ndi moyo munthu akamwalira. Ena amakhulupirira kuti munthu akafa amakabadwanso kwina monga munthu kapena chamoyo chinachake, ndipo zimenezi zimapitirira kuchitika kwamuyaya. Palinso anthu ena amene amakhulupirira kuti chilichonse chimene chimachitika pa moyo chinakonzedweratu ndi Mulungu ndipo kuti palibe zimene munthu angachite kuti asinthe zimenezi. N’zomvetsa chisoni kuti mfundo zonsezi n’zosakhutiritsa. Zili choncho chifukwa choti Baibulo limanena kuti, anthu paokha sangathe ‘kulondoloza ntchito zimene Mulungu wazipanga kuyambira pachiyambi mpaka chitsiriziro.’
Kuyambira kale, akatswiri oganiza mozama komanso akatswiri a maphunziro ofufuza nzeru zapamwamba alephera kupeza mfundo zokhutiritsa pankhani imeneyi. Komano, pakuti Mulungu ndiye anaika chikhumbo chimenechi mumtima mwathu, kodi sipomveka kunena kuti iyeyu ndi amene angatipatse mfundo zokhutiritsa pankhaniyi? Ndipotu Baibulo limanena za Yehova kuti: “Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.” (Salmo 145:16) Mwa kuphunzira Mawu a Mulungu, Baibulo, tingapeze mfundo zokhutiritsa zokhudza moyo ndiponso imfa. Tingaphunzirenso za cholinga cha Mulungu polenga dziko lapansi komanso anthu.—Aefeso 3:11.
-
-
Nthawi YosankhaNsanja ya Olonda—2009 | March 1
-
-
“Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adam’lenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.”—Genesis 1:27.
MAWU otchuka amenewa ali m’mavesi oyambirira a m’Baibulo ndipo amanena za chimodzi mwa zinthu zosangalatsa kwambiri zimene Mulungu ‘anazikongoletsa pa mphindi yake.’ Chinthu chimenechi ndicho kulenga mwamuna ndi mkazi wangwiro, Adamu ndi Hava. (Mlaliki 3:11) Monga Mlengi wawo, Yehova Mulungu anawauza kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.”—Genesis 1:28.
-