Zimene Mlengi Wathu Amatiphunzitsa Zimatipatsa Chiyembekezo
Mulungu watilonjeza zinthu zabwino kwambiri zimene zichitike posachedwapa. Iye adzathetsa mavuto onse ndipo adzachititsa kuti anthu azisangalala ndi moyo padzikoli. (Salimo 37:11) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira malonjezo amenewa? Chifukwa “Mulungu si munthu, woti anganene mabodza.” (Numeri 23:19) Tiyeni tione zinthu zina zabwino zimene Mlengi wathu adzachite.
Mulungu Adzawononga Anthu Oipa
“Anthu oipa akamaphuka ngati msipu, ndipo anthu onse ochita zopweteka anzawo akamaphuka ngati maluwa, amatero kuti awonongeke kwamuyaya.”—SALIMO 92:7.
Monga taonera munkhani yapita ija, zinthu zoipa zikungochulukirachulukirabe. Koma zimenezi siziyenera kutidabwitsa. Ndipotu Baibulo linaneneratu pa lemba la 2 Timoteyo 3:1-5 kuti ‘m’masiku otsiriza’ anthu adzakhala oipa kwambiri. Kodi tikutanthauza chiyani tikamati masiku otsiriza? Tikutanthauza masiku otsiriza a dzikoli, limene anthu ake safuna kumvera Mulungu. Posachedwapa, Mulungu awononga anthu onse amene safuna kusiya zinthu zoipa zimene amachita. Koma anthu okhawo amene ndi abwino, omwe amamvera Mulungu, ndi amene adzakhale padzikoli. “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.
Mulungu Adzawononga Satana
“Mulungu amene amapatsa mtendere aphwanya Satana.”—AROMA 16:20.
Anthu oipa onse akadzawonongedwa kuphatikizapo Satana ndi ziwanda zake, padziko lonse padzakhala mtendere. Mlengi wathu analonjeza kuti: “Sipadzakhala wowaopsa.”—Mika 4:4.
Mulungu Adzathetsa Matenda Komanso Imfa
“Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. . . . Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—CHIVUMBULUTSO 21:3, 4.
Mavuto komanso matenda onse adzatha chifukwa Mulungu adzakonza zinthu zonse zimene zinawonongedwa ndi Satana, Adamu, Hava komanso chifukwa cha kupanda ungwiro kwa anthufe. Chifukwa cha zimenezi “imfa sidzakhalaponso.” Anthu amene amakonda komanso kumvera Mlengi adzakhala ndi moyo mpaka kalekale. Koma kodi azidzakhala kuti?
Mlengi Wathu Adzakonza Dzikoli Kuti Likhale Lokongola Kwambiri
“Chipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala. Dera lachipululu lidzakondwa ndipo lidzachita maluwa n’kukhala lokongola ngati duwa la safironi.”—YESAYA 35:1.
Mulungu akadzawononga anthu oipa, dzikoli lidzakhala lopanda mavuto. Kudzakhala malo okongola komanso minda yamaluwa okongola ndiponso kudzakhala chakudya chochuluka kwambiri. (Salimo 72:16) Madzi a m’nyanja komanso m’mitsinje adzakhala abwino kwambiri ndipo mudzakhala zamoyo zochuluka. Pa nthawiyo mawu akuti “kuwonongeka kwa chilengedwe” adzaiwalika. Anthu azidzakhala m’nyumba zawo zomwe amanga okha. Ndipo sipadzapezeka munthu ndi mmodzi yemwe wosowa pokhala, wosowa chakudya kapena wosauka.—Yesaya 65:21, 22.
Mulungu Adzaukitsa Anthu Amene Anamwalira
“Kudzakhala kuuka.”—MACHITIDWE 24:15.
Kodi mungakonde kudzaonananso ndi okondedwa anu amene anamwalira? Mulungu yemwe ndi wamphamvuyonse adzawaukitsa kuti akhalenso ndi moyo m’Paradaiso pa dziko lapansili. Mudzawazindikira ndipo iwonso adzakuzindikirani. Taganizirani mmene nonse mudzasangalalire. Koma kodi tingatsimikize bwanji kuti zimenezi zidzachitikadi? M’Baibulo muli zitsanzo za ana komanso anthu akuluakulu amene anaukitsidwa ndipo anayamba kukhalanso ndi anthu a m’banja lawo. Ndipotu kawirikawiri Yesu ankaukitsa anthu, ena akuona.—Luka 8:49-56; Yohane 11:11-14, 38-44.