Monga Ngati Ziŵala
KODI munayamba mwadutsapo m’dambo m’nyengo ya chilimwe ndi kuona ziŵala zambirimbiri zikubalalika kukuthaŵani? Zimaoneka kukhala paliponse, ngakhale kuti simunayike kwambiri chisamaliro kwa izo. Ndi iko komwe, izo zimaoneka kukhala zosavulaza ndi zopanda pake.
Komabe, kuoneka kukhala zopanda pake kwa ziŵala kumazipangitsa kukhala chizindikiro choyenera cha mtundu wa anthu. Ngakhale kuti anthu ena otchuka angadzione kukhala ofunika kwambiri, Mlengi wathu amalingalira mosiyana. Mneneri wake Yesaya ananena kuti: “Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziŵala.”—Yesaya 40:22.
Ulemerero wa Yehova Mulungu, mphamvu, ndi nzeru zake zimamkweza pamwamba kwambiri pa anthu wamba, monga momwe munthu aliri pamwamba kwambiri kuposa ziŵala m’luntha ndi mphamvu. Komabe, mkhalidwe waukulu wa Mulungu ndiwo chikondi. Ndipo chikondi chake chosayerekezereka chimamsonkhezera kutizindikira, kutithandiza, ndi kutipulumutsa—ngati timkonda ndi kummvera. Yehova amachita nafe mwachikondi, ngakhale kuti tili ngati ziŵala zopanda pake. Wamasalmo ananena kuti: “Akunga Yehova Mulungu wathu ndani? Amene akhala pamwamba patali, nadzichepetsa apenye zam’mwamba ndi za pa dziko lapansi. Amene autsa wosauka kumchotsa kufumbi.”—Salmo 113:5-7.
Monga momwe salmo limeneli limanenera, Yehova amapereka chithandizo mwachikondi kwa wodzichepetsa. Inde, Iye amathandiza awo amene modzichepetsa ‘amafunafuna Mulungu kuti ampezedi.’ (Machitidwe 17:27) Awo amene amapeza Mulungu—ndi kumtumikira—amakhaladi amtengo wapatali pamaso pake. (Yerekezerani ndi Yesaya 43:4, 10.) Chotero chiŵala chodzichepetsacho chimatikumbutsa za kupanda pake kwathu ndi chikondi cha Mlengi wathu wamphamvu yonse, amene amapatsa anthu omvera ubwenzi wake ndi kukoma mtima kwake kwaulere. Kodi mukusonyeza chiyamikiro kaamba ka chikondi cha Mulungu?