NKHANI YOPHUNZIRA 1
“Usayang’ane Uku ndi Uku Mwamantha, Pakuti Ine Ndine Mulungu Wako”
“Usachite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.”—YES. 41:10.
NYIMBO NA. 7 Yehova Ndiye Mphamvu Zathu
ZIMENE TIPHUNZIREa
1-2. (a) Kodi mawu a pa Yesaya 41:10 analimbikitsa bwanji Yoshiko? (b) Kodi Yehova analola kuti mawuwa asungidwebe kuti azilimbikitsa ndani?
MLONGO wina wokhulupirika dzina lake Yoshiko anauzidwa ndi dokotala kuti wangotsala ndi miyezi yochepa kuti amwalire. Kodi mlongoyu anatani? Iye anakumbukira lemba limene ankalikonda kwambiri la Yesaya 41:10. (Werengani.) Kenako anauza dokotalayo mtima uli m’malo kuti sakuopa chilichonse chifukwa Yehova anali atagwira dzanja lake.b Mawu olimbikitsa amulembali anathandiza mlongoyu kuti azidalira kwambiri Yehova. Vesi limeneli lingatithandizenso ifeyo kuti tisamade nkhawa tikakumana ndi mavuto aakulu. Kuti timvetse mfundoyi, tiyeni tikambirane chifukwa chimene Mulungu anaperekera uthenga umenewu kwa Yesaya.
2 Poyamba, Yehova anauza Yesaya kuti alembe mawu amenewa n’cholinga choti alimbikitse Ayuda amene anadzatengedwa kupita ku ukapolo wa ku Babulo. Koma Yehova analola kuti mawuwa asungidwebe kuti azilimbikitsanso anthu ake ena mpaka masiku ano. (Yes. 40:8; Aroma 15:4) Panopa tikukhala ‘m’nthawi yovuta’ ndipo kuposa kale lonse, tikufunika kulimbikitsidwa ndi mawu a m’buku la Yesaya.—2 Tim. 3:1.
3. (a) Palemba la Yesaya 41:10, lomwe ndi lemba la chaka cha 2019, kodi Mulungu analonjeza zinthu ziti? (b) N’chifukwa chiyani nafenso tikufunika kulimbikitsidwa?
3 Munkhaniyi tikambirana zinthu zitatu zolimbikitsa zimene Yehova analonjeza pa Yesaya 41:10. Zinthu zake ndi izi: (1) Yehova ali nafe, (2) iye ndi Mulungu wathu komanso (3) azitithandiza. Malonjezo a Yehovac amenewa ndi ofunika kwambiri masiku ano chifukwa, mofanana ndi Yoshiko, nafenso timakumana ndi mavuto. Zochitika za m’dzikoli zimachititsanso kuti tizipanikizika. Ndipo enafe tikuzunzidwa ndi maboma amene amatitsutsa. Tiyeni tikambirane zimene Mulungu analonjezazi chimodzi ndi chimodzi.
“NDILI NAWE”
4. (a) Kodi tiyamba ndi kukambirana lonjezo liti? (Onani mawu a m’munsi.) (b) Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amatikonda? (c) Kodi mumamva bwanji mukaganizira mawu olimbikitsa amene Mulungu ananena?
4 Tiyeni tiyambe ndi kukambirana lonjezo loyamba la Yehova lakuti: “Usachite mantha, pakuti ndili nawe.”d Yehova amasonyeza kuti ali nafe chifukwa amatiganizira komanso amatikonda kwambiri. Paja anati: “Ndiwe wamtengo wapatali kwa ine, ndimakulemekeza ndipo ndimakukonda.” (Yes. 43:4) Palibe chilichonse m’chilengedwe chimene chingachititse kuti Yehova asiye kukonda anthu amene amamutumikira. Iye ndi wokhulupirika kwambiri kwa ife. (Yes. 54:10) Chikondi cha Mulungu komanso kukhala naye pa ubwenzi wabwino zimatithandiza kuti tikhale olimba mtima kwambiri. Iye adzatiteteza ngati mmene anachitira ndi Abulamu (Abulahamu), yemwe anali bwenzi lake. Yehova anamuuza kuti: “Usaope Abulamu. Ine ndine chishango chako.”—Gen. 15:1.
5-6. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova amafuna kutithandiza pa mavuto athu? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yoshiko?
5 Timadziwa kuti Yehova amafuna kuti azitithandiza pa mavuto athu chifukwa analonjeza kuti: “Ukamadzadutsa pamadzi, ine ndidzakhala nawe. Ukamadzawoloka mitsinje, madzi sadzakumiza. Ukamadzayenda pamoto sudzapsa ndipo ngakhale lawi la moto silidzakuwaula.” (Yes. 43:2) Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani?
6 Yehova salonjeza kuti adzathetsa mavuto athu onse panopa. Koma sadzalola kuti mavuto okhala ngati “mitsinje” atimize kapena mayesero okhala ngati “moto” atiwonongeretu. Iye amatitsimikizira kuti adzakhala nafe ndipo adzatithandiza “kudutsa” bwinobwino pa mavuto athu. Kodi adzatithandiza bwanji? Adzatithandiza kuti tisamachite mantha n’cholinga choti tikhalebe okhulupirika kwa iye ngakhale titatsala pang’ono kufa. (Yes. 41:13) Yoshiko, amene tamutchula kale uja, anaona kuti zimenezi ndi zoona. Mwana wake ananena kuti: “Tinadabwa kuona kuti mayi sankaopa ngakhale pang’ono. Tinaonatu kuti Yehova ankawapatsa mtendere wamumtima. Mayi ankauza manesi ndiponso odwala ena za malonjezo a Yehova mpaka tsiku limene anamwalira.” Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yoshiko? Tikamakhulupirira lonjezo la Mulungu loti adzakhala nafe, tidzakhalanso olimba mtima pokumana ndi mavuto.
“INE NDINE MULUNGU WAKO”
7-8. (a) Kodi tikambirana lonjezo liti limene Yesaya analemba, nanga limatanthauza chiyani? (b) N’chifukwa chiyani Yehova anauza Ayuda amene anadzapita ku ukapolo kuti ‘asayang’ane uku ndi uku mwamantha?’ (c) Kodi ndi mawu ati pa Yesaya 46:3, 4 omwe ayenera kuti analimbikitsa anthu a Mulungu?
7 Chachiwiri, tiyeni tikambirane lonjezo limene Yesaya analemba lakuti: “Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako.” Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani? Mawuwa angatanthauze “kuyang’ana kumbuyo poopa kuti kukhoza kubwera chinachake choopsa” kapena “kucheukacheuka chifukwa cha mantha.”
8 N’chifukwa chiyani Yehova anauza Ayuda amene anadzapita ku ukapolo ku Babulo kuti “asayang’ane uku ndi uku mwamantha?” Iye ankadziwa kuti anthu a ku Babulowo adzachita mantha. Koma kodi n’chiyani chikanawachititsa mantha? Chakumapeto kwa zaka 70 za ukapolo uja, asilikali a Mediya ndi Perisiya anaukira Babulo. Yehova anagwiritsa ntchito asilikali amenewa kuti amasule anthu ake ku ukapolo. (Yes. 41:2-4) Ababulo ndi anthu ena ataona kuti adani akuyandikira, anayamba kulimbikitsana pouzana kuti: “Limba mtima.” Iwo anapanganso mafano ena ambiri poganiza kuti awateteza. (Yes. 41:5-7) Koma Yehova analimbikitsa Ayuda powauza kuti: “Iwe Isiraeli, ndiwe mtumiki wanga [mosiyana ndi mitundu inayo] . . . Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako.” (Yes. 41:8-10) Onani kuti Yehova ananena kuti “Ine ndine Mulungu wako.” Apa Yehova ankatsimikizira atumiki ake okhulupirika kuti sanawaiwale, anali adakali Mulungu wawo ndipo iwo anali adakali anthu ake. Anawauzanso kuti ‘awanyamula ndiponso kuwapulumutsa.’ Ayudawo ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri ndi mawu amenewa.—Werengani Yesaya 46:3, 4.
9-10. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuchita mantha? Perekani chitsanzo.
9 Masiku anonso, anthu ambiri akuchita mantha chifukwa choti zinthu m’dzikoli zikuipiraipira. N’zoona kuti nafenso timakhudzidwa ndi mavuto a m’dzikoli. Koma palibe chifukwa chochitira mantha. Paja Yehova akutiuza kuti: “Ine ndine Mulungu wako.” Kodi mfundo imeneyi ingatithandize bwanji kuti tisamade nkhawa?
10 Tiyerekeze kuti anthu awiri, omwe mayina awo ndi Jim ndi Ben, akwera ndege. Ndiyeno kwayamba chimphepo champhamvu chomwe chikukankha ndegeyo. Kenako akumva mawu akuti: “Mangani malamba. Tidutsa mumphepoyi kwakanthawi ndithu.” Ndiye Jim akuyamba kuda nkhawa kwambiri. Koma woyendetsa ndegeyo akunenanso kuti: “Ndikulankhula ndine amene ndikuyendetsa ndegeyi. Musaope chilichonse.” Kenako Jim akupukusa mutu n’kunena kuti, “Kodi zimene akunenazi zingatithandize chiyani?” Koma akuona kuti Ben sakuda nkhawa ngakhale pang’ono. Kenako akumufunsa kuti: “Kodi iwe wangoti phee bwanji, sukuopa?” Ben akumwetulira n’kunena kuti: “Amene akuyendetsa ndegeyi ndikuwadziwa bwino. Ndi bambo anga.” Kenako Ben akuti: “Dikira ndikufotokozere za bambo angawa. Sindikukayikira kuti ukawadziwa komanso kudziwa luso lawo, sungaope chilichonse.”
11. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha anthu awiri okwera ndege aja?
11 Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo chimenechi? Mofanana ndi Ben, ifeyo sitida nkhawa chifukwa timadziwa bwino Atate wathu, Yehova. Timadziwa kuti atithandiza kuti tidutse bwinobwino mavuto okhala ngati chimphepo amene tikukumana nawo m’masiku otsirizawa. (Yes. 35:4) Popeza timadalira Yehova, sitida nkhawa ngakhale kuti anthu ena onse akuchita mantha. (Yes. 30:15) Tikufanananso ndi Ben chifukwa timauza anthu ena mfundo zowathandiza kuti azikhulupirira Mulungu. Akatero, nawonso sangakayikire zoti Yehova adzawathandiza zivute zitani.
‘NDIKULIMBITSA KOMANSO NDIKUTHANDIZA’
12. (a) Kodi lonjezo lachitatu limene tikambirane ndi liti? (b) Kodi mawu oti “dzanja” la Yehova akutikumbutsa chiyani?
12 Tiyeni tsopano tikambirane lonjezo lachitatu limene Yesaya analemba lakuti: “Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.” Yesaya anali atafotokoza kale mmene Yehova adzalimbitsire anthu ake ponena kuti: “Adzabwera ngati wamphamvu ndipo dzanja lake lizidzalamulira m’malo mwa iyeyo.” (Yes. 40:10) Nthawi zambiri Baibulo limagwiritsa ntchito mawu oti “dzanja” kutanthauza mphamvu. Choncho mawu oti “dzanja lake lizidzalamulira” akutikumbutsa kuti Yehova ndi Mfumu yamphamvu. Iye anagwiritsa ntchito mphamvu zake zosagonjetseka kuti athandize komanso kuteteza atumiki ake m’mbuyomu ndipo akupitiriza kuchita zomwezo kwa anthu amene amamudalira masiku ano.—Deut. 1:30, 31; Yes. 43:10.
13. (a) Kodi Yehova amakwaniritsa lonjezo lake loti atilimbitsa makamaka pa nthawi iti? (b) Kodi ndi lonjezo liti limene limatipatsa mphamvu komanso kutilimbitsa mtima?
13 Yehova amakwaniritsa mawu ake akuti: “Ndikulimbitsa.” Amachita zimenezi makamaka pa nthawi imene tikuzunzidwa. Kumayiko ena adani athu akuyesetsa kuti aletse ntchito yathu yolalikira kapena athetse gulu lathu. Ngakhale zili choncho, sitichita mantha. Yehova watipatsa lonjezo limene limatipatsa mphamvu komanso kutilimbitsa mtima. Iye watilonjeza kuti: “Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana.” (Yes. 54:17) Mawu amenewa amatikumbutsa mfundo zitatu zofunika.
14. N’chifukwa chiyani sitidabwa adani a Mulungu akamalimbana nafe?
14 Choyamba, Akhristufe timayembekezera kuti anthu azidana nafe. (Mat. 10:22) Paja Yesu ananeneratu kuti ophunzira ake adzazunzidwa kwambiri m’masiku otsiriza. (Mat. 24:9; Yoh. 15:20) Chachiwiri, ulosi wa Yesaya unasonyeza kuti adani athu sadzangodana nafe koma adzagwiritsa ntchito zida zosiyanasiyana polimbana nafe. Zina mwa zida zimene amagwiritsa ntchito ndi chinyengo, mabodza ankunkhuniza komanso kuzunza mwankhanza. (Mat. 5:11) Yehova saletsa adani athu kugwiritsa ntchito zida zimenezi polimbana nafe. (Aef. 6:12; Chiv. 12:17) Koma sitiyenera kuchita mantha. N’chifukwa chiyani tikutero?
15-16. (a) Kodi mfundo yachitatu imene tiyenera kuikumbukira ndi iti, nanga ikugwirizana bwanji ndi lemba la Yesaya 25:4, 5? (b) Kodi lemba la Yesaya 41:11, 12 limafotokoza bwanji zimene zidzachitikire anthu amene amalimbana nafe?
15 Tiyeni tikambirane mfundo yachitatu imene tiyenera kuikumbukira. Yehova ananena kuti “chida chilichonse” chimene anthu angagwiritse ntchito polimbana nafe “sichidzapambana.” Mofanana ndi mmene khoma limatitetezera ku mphepo yamkuntho, Yehova amatitetezanso pamene “anthu ankhanza akuwomba” ngati mphepo. (Werengani Yesaya 25:4, 5.) Adani athu sangathe kutiwonongeratu.—Yes. 65:17.
16 Yehova amatithandizanso kuti tizimudalira potifotokozera bwinobwino zimene zidzachitikire anthu amene ‘akutipsera mtima.’ (Werengani Yesaya 41:11, 12.) Kaya adani athu alimbane nafe mwamphamvu bwanji, zotsatira zake zidzakhala zakuti adani onse a anthu a Mulungu “sadzakhalanso ngati kanthu ndipo adzatha.”
ZIMENE TINGACHITE KUTI TIZIDALIRA KWAMBIRI YEHOVA
17-18. (a) Kodi kuwerenga Baibulo kungatithandize bwanji kuti tizidalira kwambiri Mulungu? Perekani chitsanzo. (b) Kodi kuganizira kwambiri lemba la chaka cha 2019 kungatithandize bwanji?
17 Tikamamudziwa bwino Yehova m’pamene timayamba kumudalira kwambiri. Njira imodzi yokha yotithandiza kumudziwa bwino ndi kuwerenga Baibulo mosamala kenako n’kuganizira kwambiri zimene tawerengazo. M’Baibulo muli nkhani zosonyeza mmene Yehova anatetezera anthu ake m’mbuyomu. Nkhani zoterezi zimatitsimikizira kuti ifenso sangatisiye.
18 Yesaya anagwiritsa ntchito mawu abwino kwambiri pofotokoza mmene Yehova amatitetezera. Iye anayerekezera Yehova ndi m’busa ndipo atumiki ake anawayerekezera ndi ana a nkhosa. Pofotokoza za Yehova, Yesaya analemba kuti: “Adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa ndi dzanja lake, ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake.” (Yes. 40:11) Tikazindikira kuti dzanja lamphamvu la Yehova likutiteteza sitichita mantha ngakhale pang’ono. Pofuna kutithandiza kuti tisamade nkhawa ndi mavuto amene tingakumane nawo, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wasankha lemba la Yesaya 41:10 kuti likhale lemba la chaka cha 2019. Lembali limati: “Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako.” Muziganizira kwambiri mawu olimbikitsawa. Adzakuthandizani kwambiri mukadzakumana ndi mavuto m’tsogolomu.
NYIMBO NA. 38 Mulungu Adzakulimbitsa
a Lemba la chaka cha 2019, likutipatsa zifukwa zitatu zotithandiza kuti tisamade nkhawa ngakhale zinthu zoipa zitachitika m’dzikoli kapena pa moyo wathu. Nkhaniyi ifotokoza zifukwa zitatuzo ndipo itithandiza kuti tisamade nkhawa kwambiri koma tizidalira Yehova. Muziliganizira kwambiri lemba la chakali ndipo muliloweze ngati mungakwanitse. Lembali likuthandizani kwambiri pa mavuto amene mungakumane nawo m’tsogolo.
c TANTHAUZO LA MAWU ENA: Malonjezo a Yehova ndi mawu amene iye amanena osonyeza kuti zinthu zinazake zidzachitikadi. Malonjezo amenewa angatithandize kuti tisamade nkhawa ndi mavuto amene tingakumane nawo pa moyo wathu.
d MAWU A M’MUNSI: Mawu oti “Usachite mantha” amapezeka katatu pa Yesaya 41:10, 13 ndi 14. Mavesi amenewa amanenanso kuti “Ine” mobwerezabwereza (kutanthauza Yehova). N’chifukwa chiyani Yehova anachititsa kuti Yesaya anene mawu akuti “Ine” mobwerezabwereza? Anachita zimenezi pofuna kutsindika kuti tiyenera kudalira Yehova kuti tisamachite mantha.
e MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Anthu a m’banja limodzi akukumana ndi mavuto kuntchito, kuchipatala, mu utumiki komanso kusukulu.
f MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Abale ndi alongo amene asonkhana kunyumba ya m’bale apezedwa ndi apolisi koma akuchitabe zinthu modekha.
g MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Kuchita kulambira kwa pabanja mlungu uliwonse kungatithandize kuti tipirire.