-
“Ine, Yehova Mulungu Wako, Ndagwira Dzanja Lako Lamanja”Nsanja ya Olonda—2012 | January 1
-
-
“Ine, Yehova Mulungu Wako, Ndagwira Dzanja Lako Lamanja”
TAYEREKEZANI kuti mwana wina ndi bambo ake akufuna kuwoloka msewu wodutsa magalimoto ambiri. Mwanayo akuchita mantha kuwoloka msewuwo koma bambo ake akumuuza kuti: “Bwera ndikugwire dzanja.” Kodi mukuganiza kuti mwanayo angamve bwanji? N’zosakayikitsa kuti mantha ake onse angathe ndipo angamve kuti ndi wotetezeka. Kodi nthawi zina mumalakalaka munthu wina atakugwirani dzanja n’kumakutsogolerani pa nthawi imene mukukumana ndi mavuto? Ngati ndi choncho, mawu amene Yesaya analemba angakulimbikitseni kwambiri.—Werengani Yesaya 41:10, 13.
Yesaya ndi amene analemba mawu a Mulungu amenewa ndipo ankauza Aisiraeli. Ngakhale kuti Mulungu ankaona mtundu wa Isiraeli ngati ‘chuma chake chapadera,’ mtunduwu unali utazunguliridwa ndi adani ambiri. (Ekisodo 19:5) Kodi Aisiraeli ankayenera kuchita mantha? Yehova anagwiritsa ntchito Yesaya kuuza Aisiraeli mawu olimbikitsa. Pamene tikukambirana mawu amenewa, tisaiwale kuti mawuwa akugwiranso ntchito kwa atumiki a Mulungu masiku ano.—Aroma 15:4.
-
-
“Ine, Yehova Mulungu Wako, Ndagwira Dzanja Lako Lamanja”Nsanja ya Olonda—2012 | January 1
-
-
Ndiye kodi atumiki a Yehova akanayembekezera kuti iye awachitira chiyani? Iye anawalonjeza kuti: “Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.” (Vesi 10) Iye ananenanso kuti: “Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja.” (Vesi 13) Kodi n’chiyani chimabwera m’maganizo mwanu mukamva mawu amenewa? Buku lina linanena kuti: “Mavesi awiri amenewa akutipangitsa kuganizira za bambo ndi mwana wake. Sikuti [bambo] amangodikirira kuti athandize mwana wake zinthu zikavuta. Nthawi zonse iye amaonetsetsa kuti ali ndi mwanayo.” Ndi mmenenso Yehova amachitira. Iye nthawi zonse amaonetsetsa kuti ali ndi anthu ake ngakhale pa nthawi imene iwo angaone kuti ndi yovuta kwambiri pa moyo wawo.—Aheberi 13:5, 6.
-