Onyamula Kuunika—Kaamba ka Chifuno Chotani?
“Ndakuika iwe kuunika kwa amitundu.”—MACHITIDWE 13:47.
1. Kodi mtumwi Paulo anasonkhezeredwa motani ndi lamulo lonenedwa pa Machitidwe 13:47?
“ANATILAMULIRA [Yehova, NW] ndi kuti, Ndakuika iwe kuunika kwa amitundu, kuti udzakhala iwe chipulumutso kufikira malekezero a dziko,” anatero mtumwi Paulo. (Machitidwe 13:47) Sikokha kuti iye ananena zimenezo komanso anazindikira ukulu wa thayolo. Atakhala Mkristu, Paulo anapereka moyo wake m’kuchita lamulo limenelo. (Machitidwe 26:14-20) Kodi lamulolo laikidwanso pa ife lerolino? Ngati nditero, kodi nchifukwa ninji liri lofunika m’tsiku lathu?
Pamene ‘Nyali Zinazima’ pa Mtundu wa Anthu
2. (a) Pamene dziko linaloŵa m’nthaŵi yake yamapeto, kodi chinachitika nchiyani chimene chinayambukira kwambiri mkhalidwe wake wauzimu ndi wamakhalidwe? (b) Kodi nduna yaboma la Briteni inanenanji powona zimene zinali kuchitika mu August 1914?
2 Asanabadwe anthu ochuluka okhala ndi moyo lerolino, dziko lino linaloŵa m’nthaŵi yake ya mapeto. Panachitika zinthu zazikulu m’kutsatizana kofulumira. Satana Mdyerekezi, wochirikiza wamkulu wa mdima wauzimu ndi wamakhalidwe, anaponyedwa padziko lapansi. (Aefeso 6:12; Chivumbulutso 12:7-12) Mtundu wa anthu unali utagwera kale m’nkhondo yake yoyamba ya dziko lonse. Kuchiyambiyambi kwa August 1914, pamene nkhondoyo inawonekera kukhala yosapeweka, Bwana Edward Grey, nduna ya boma la Briteni yoyang’anira nkhani zakunja, anaima pazenera la ofesi yake m’London ndi kunena kuti: “Nyali zikuzima pa Ulaya yense; sitidzaziwona zikuyakanso m’nthaŵi ya moyo wathu.”
3. Kodi ndichipambano chotani chimene atsogoleri adziko akhala nacho m’kuyesa kuwongolera mkhalidwe wa mtundu wa anthu?
3 Mwakuyesayesa kuyatsanso nyalizo, Chigwirizano cha Mitundu chinayambitsidwa mu 1920. Koma nyalizo zinangoyaka mophetiraphetira. Kumapeto kwa nkhondo yadziko yachiŵiri, olamulira adziko anayesanso, koma tsopano ndi bungwe la Mitundu Yogwirizana. Kachiŵirinso, nyalizo sizinayake moŵala. Komabe, malinga ndi zochitika zaposachedwapa, olamulira adziko akhala akulankhula za “dongosolo la dziko latsopano.” Koma sitinganene konse kuti pali “dziko latsopano” lirilonse limene lapereka mtendere weniweni ndi chisungiko. Mosiyana ndi zimenezo, kumenyana ndi zida, kulimbana kwaufuko, upandu, ulova, umphaŵi, kuipitsidwa kwa malo okhala, ndi matenda, zonsezo zikupitiriza kudodometsa chisangalalo cha anthu cha moyo.
4, 5. (a) Kodi nliti ndipo ndimotani mmene mdima unaphimbira banja la anthu? (b) Kodi chofunikira nchiyani kuti pakhale chimasuko?
4 Kunena zowona, nyali zinazimira mtundu wa anthu kalekale 1914 isanafike nkomwe. Zimenezo zinachitika zoposa zaka 6,000 zapitazo mu Edene, pamene makolo athu aumunthu oyamba anasankha kudzipangira zosankha zawo monyalanyaza chifuniro cha Mulungu chosonyezedwacho. Zokumana nazo zomvetsa chisoni za fuko la anthu chiyambire pamenepo zangokhala zina za zochitika pansi pa wotchedwa m’Baibulo “ulamuliro wa mdima.” (Akolose 1:13) Chinali chisonkhezero cha Satana Mdyerekezi kuti mwamuna woyamba, Adamu, analoŵetsa dzikoli muuchimo; ndipo kuchokera kwa Adamu uchimo ndi imfa zinafalikira pa mtundu wonse wa anthu. (Genesis 3:1-6; Aroma 5:12) Motero mtundu wa anthu unataya chivomerezo cha Yehova, Magwero a kuunika ndi moyo.—Salmo 36:9.
5 Njira yokha imene nyalizo zikayakiranso aliyense wa mtundu wa anthu ikakhala mwakupeza chivomerezo cha Yehova Mulungu, Mlengi wa mtundu wa anthu. Pamenepo, ‘chophimba nkhope chovundikira mitundu yonse ya anthu,’ kutsutsidwa chifukwa cha uchimo, chikakhoza kuchotsedwa. Kodi zimenezi zikatheka motani?—Yesaya 25:7.
Wopatsidwayo “Monga Kuunika kwa Amitundu”
6. Kodi nziyembezo zazikulu zotani zimene Yehova watipatsa kupyolera mwa Yesu Kristu?
6 Ngakhale pamene Adamu ndi Hava anali asanapitikitsidwe m’Paradaiso, Yehova adaneneratu za ‘mbewu’ imene ikakhala mpulumutsi wa okonda chilungamo. (Genesis 3:15) Pambuyo pakubadwa kwaumunthu kwa Mbewu yolonjezedwayo, Yehova anachititsa Simeoni wokalambayo, pakachisi m’Yerusalemu, kudziŵikitsa ameneyo kukhala ‘kuunika kochotsera mitundu chophimba.’ (Luka 2:29-32) Mwakukhulupirira nsembe ya moyo wa Yesu wangwiro waumunthu, anthu akakhoza kuchotseredwa chiweruzo cha imfa chochokera muuchimo wobadwa nawo. (Yohane 3:36) Mogwirizana ndi chifuniro cha Yehova, iwo tsopano akayang’ana kutsogolo ku moyo wamuyaya wangwiro monga mbali ya Ufumu wakumwamba kapena monga nzika zake zapadziko lapansi laparadaiso. Ndimakonzedwe abwino chotani nanga!
7. Kodi nchifukwa ninji zonse ziŵiri, malonjezo apa Yesaya 42:1-4 ndi kukwaniritsidwa kwawo kwa m’zaka za zana loyamba zimatidzaza ndi chiyembekezo?
7 Yesu Kristu mwiniyo ndiye chitsimikiziro cha kukwaniritsidwa kwa ziyembekezo zazikulu zimenezi. Ponena za kuchiritsa odwala kwa Yesu, mtumwi Mateyu anagwiritsira ntchito pa iye zolembedwa pa Yesaya 42:1-4. Mbali yake ya lembalo imati: “Tawona mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.” Ndipo kodi zimenezi sindizo zimene anthu a mitundu yonse amafunikira? Ulosiwo ukupitiriza kuti: “Iye sadzafuula, ngakhale kukuwa, pena kumvetsa mawu ake m’khwalala. Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi laŵi lozilala sadzalizima.” Mogwirizana nzimenezi, Yesu sanachitire anthu odwala kale mwaukali. Anawachitira chifundo, nawaphunzitsa zifuno za Yehova, ndi kuwachiritsa.—Mateyu 12:15-21.
8. Kodi ndi m’lingaliro lotani limene Yesu wapatsidwira ndi Yehova “monga pangano la anthu” ndi monga “kuunika kwa amitundu”?
8 Wopereka ulosi umenewu akulankhula za iyemwini kwa Mtumiki wake, kwa Yesu, nati: “Ine Yehova ndakuitana iwe m’chilungamo, ndipo ndidzagwira dzanja lako ndi kusunga iwe, ndi kupatsa iwe ukhale pangano la anthu, ndi kuunika kwa amitundu; kuti utsegule maso akhungu, utulutse am’nsinga m’ndende, ndi iwo amene akhala mumdima, atuluke m’nyumba ya akaidi.” (Yesaya 42:6, 7) Inde, Yehova wapereka Yesu Kristu monga pangano, monga chitsimikizo chalamulo cha lonjezo. Nzolimbikitsa chotani nanga zimenezo! Yesu anasonyeza kudera nkhaŵa kowona kulinga kwa mtundu wa anthu pamene anali padziko lapansi; anaperekeradi moyo wake anthu. Iye ndiye amene Yehova wamuikizira ulamuliro pamitundu yonse. Mposadabwitsa kuti Yehova anamutcha kuunika kwa mitundu. Yesu iyemwini anati: “Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi.”—Yohane 8:12.
9. Kodi nchifukwa ninji Yesu sanadzipereke m’kuwongolera dongosolo lazinthu lokhalako panthaŵiyo?
9 Kodi ncholinga chotani chimene Yesu anatumikirira monga kuunika kwa dziko? Ndithudi sikunali ndi cholinga chaudziko chirichonse kapena chakukondetsa zinthu zakuthupi. Iye anakana kuyesa kuwongolera dongosolo landale zadziko lapanthaŵiyo ndipo anakana kulandira ufumu kaya wochokera kwa Satana, wolamulira wa dziko, kapena wochokera kwa anthu. (Luka 4:5-8; Yohane 6:15; 14:30) Yesu anasonyeza chifundo chachikulu kwa odwalawo nawapatsa mpumulo mwanjira zimene ena sanakhoze kutero. Koma iye anadziŵa kuti mpumulo wachikhalire sukapezeka m’makonzedwe a chitaganya cha anthu chimene chinatsutsidwa ndi Mulungu chifukwa cha uchimo wobadwa nawo ndi cholamuliridwa ndi mphamvu zosawoneka za mizimu yoipa. Ndi chidziŵitso chaumulungu, Yesu anasumika moyo wake wonse pakuchita chifuniro cha Mulungu.—Ahebri 10:7.
10. Kodi Yesu anatumikira monga kuunika kwa dziko mwanjira zotani ndipo ndi chifuno chotani?
10 Pamenepo, kodi ndimwanjira zotani ndipo ndicholinga chotani chimene Yesu anatumikirira monga kuunika kwa dziko? Anadzipereka pakulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. (Luka 4:43; Yohane 18:37) Mwakuchitira umboni chowonadi chonena za chifuno cha Yehova, Yesu analemekezanso dzina la Atate wake wakumwamba. (Yohane 17:4, 6) Ndiponso, monga kuunika kwa dziko, Yesu anavumbula poyera zinyengo zachipembedzo ndipo motero anapereka ufulu wauzimu kwa am’nsinga zachipembedzo. Anavumbula Satana kukhala wosonkhezera wosawoneka wa awo amene adzilola kugwiritsiridwa ntchito ndi iye. Yesu anasonyezanso momvekera bwino ntchito za mdima. (Mateyu 15:3-9; Yohane 3:19-21; 8:44) Mwanjira yapadera, iye anatsimikizira kukhala kuunika kwa dziko mwakutaya moyo wake wangwiro waumunthu monga dipo, mwakutero akumatsegulira njira awo amene amasonyeza chikhulupiriro m’makonzedwe ameneŵa akukhululukiridwa machimo, unansi wovomerezedwa ndi Mulungu, ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya monga mbali ya banja lachilengedwe chonse la Yehova. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16) Ndiyeno, mwakusunga kudzipereka kwake kwaumulungu kwangwiro m’moyo wake wonse, Yesu anachirikiza uchifumu wa Yehova natsimikizira Mdyerekezi kukhala wabodza, mwakutero akumatheketsa madalitso osatha kwa okonda chilungamo. Koma kodi Yesu ndiye yekha anali kudzakhala wonyamula kuunika?
“Inu Ndinu Kuunika kwa Dziko Lapansi”
11. Kuti akhale onyamula kuunika, kodi otsatira a Yesu anafunikira kuchitanji?
11 Pa Mateyu 5:14, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi.” Iwo anafunikira kulondola mapazi ake. Ponse paŵiri mwanjira yawo ya moyo ndi mwakulalikira, anafunikira kutsogolera ena kwa Yehova monga Magwero a kuunikira kowona. Mwakutsanzira Yesu, iwo anafunikira kudziŵitsa dzina la Yehova ndi kuchirikiza uchifumu Wake. Monga momwe Yesu anachitira, nawonso anafunikira kubukitsa Ufumu wa Mulungu monga chiyembekezo chokha cha mtundu wa anthu. Anafunikiranso kuvumbula zinyengo zazipembedzo, ntchito za mdima, ndi woipayo amene akusonkhezera zinthu zimenezi. Otsatira a Kristu anayenera kuuza anthu kulikonse ponena za makonzedwe achikondi a Yehova a chipulumutso kupyolera mwa Yesu Kristu. Akristu oyambirira anachita ntchitoyo ndi changu chotani nanga, akumayambira m’Yerusalemu ndi m’Yudeya ndiyeno kuloŵa m’Samariya, monga momwe Yesu anawalamula!—Machitidwe 1:8.
12. (a) Kodi kuunika kwauzimu kunafunikira kuŵalira kufikira kuti? (b) Kodi nchiyani chimene mzimu wa Yehova unatheketsa Paulo kuzindikira ponena za Yesaya 42:6, ndipo kodi ulosiwo uyenera kuyambukira motani miyoyo yathu?
12 Komabe, kulalikira mbiri yabwino sikunayenera kulekezera kumeneko. Yesu analangiza otsatira ake “kupanga ophunzira a anthu amitundu yonse.” (Mateyu 28:19, NW) Panthaŵi yakutembenuzidwa kwa Saulo wa ku Tariso, Ambuye anasonyeza molunjika kuti Saulo (yemwe anadzakhala mtumwi Paulo) anafunikira kudzalalikira osati kwa Ayuda okha komanso kwa Akunja. (Machitidwe 9:15) Mwachithandizo cha mzimu woyera, Paulo anadzazindikira zoloŵetsedwamo. Chifukwa chake, iye anazindikira kuti ulosi wa pa Yesaya 42:6, umene unakwaniritsidwa mwachindunji pa Yesu, umaperekanso lamulo kwa onsewo osonyeza chikhulupiriro mwa Kristu. Chotero, pa Machitidwe 13:47, pamene anagwira mawu Yesaya, Paulo anati: “Anatilamulira [Yehova, NW] ndi kuti, Ndakuika iwe kuunika kwa amitundu, kuti udzakhala iwe chipulumutso kufikira malekezero a dziko.” Koma bwanji za inu? Kodi mwalandira ndi mtima wonse thayolo lakukhala wonyamula kuunika? Mofanana ndi Yesu ndi Paulo, kodi mumasumika moyo wanu pakuchita chifuniro cha Mulungu?
Titsogoleredwe ndi Kuunika ndi Chowonadi cha Mulungu
13. Mogwirizana ndi Salmo 43:3, kodi pemphero lathu laphamphu nlotani, ndipo kodi limeneli limatitetezera kuchiyani?
13 Ngati mwazipangizo zathuzathu tinati tiyese ‘kuyatsanso nyalizo,’ kuti tiŵalitse mtsogolo mwa mtundu wa anthu, tikakhala tikuphonya momvetsa chisoni chifuno cha Mawu a Mulungu ouziridwa. Komabe, mosasamala kanthu ndi zimene dziko lonse likuchita, Akristu owona amayang’ana kwa Yehova monga Magwero owona a kuunika. Pemphero lawo liri ngati lija lolembedwa pa Salmo 43:3, limene limati: “Tumizirani kuunika kwanu ndi chowonadi chanu zinditsogolere: Zindifikitse ku phiri lanu loyera, Kumene mukhala inuko.”
14, 15. (a) Kodi ndimwanjira yotani imene Yehova tsopano akutumizira kuunika kwake ndi chowonadi? (b) Kodi tingasonyeze motani kuti kuunika kwa Mulungu ndi chowonadi zimatitsogoleradi?
14 Yehova akupitirizabe kuyankha pemphero la atumiki ake okhulupirikalo. Iye amatumiza kuunika kwake mwakulengeza chifuno chake, mwakutheketsa atumiki ake kuchizindikira, ndiyeno mwakukwaniritsa zimene walengeza. Pamene tipemphera kwa Mulungu, sikuyenera kungokhala chizoloŵezi chabe, kumangotero kuti tiwonekere kukhala olambira. Chikhumbo chathu chowona mtima nchakuti kuunika kumene kumachokera kwa Yehova kutitsogolere, monga momwe salmolo likunenera. Timavomereza thayo loloŵetsedwamo m’kulandira kuunika koperekedwa ndi Mulungu. Mofanana ndi mtumwi Paulo, timazindikira kuti kukwaniritsidwa kwa Mawu a Yehova kumaphatikizapo lamulo kwa onse owakhulupirira. Timadzimva kukhala amangawa kwa anthu ena kufikira titawapatsa mbiri yabwino imene Mulungu watiikizira pachifuno chimenecho.—Aroma 1:14, 15.
15 Kuunika ndi chowonadi zimene Yehova watumiza m’tsiku lathu zimasonyeza kuti Yesu Kristu akulamuliradi kuchokera pampando wake wachifumu kumwamba. (Salmo 2:6-8; Chivumbulutso 11:15) Yesu ananeneratu kuti m’nthaŵi yakukhalapo kwake monga mfumu, mbiri yabwino imeneyi ya Ufumu ikalalikidwa padziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni. (Mateyu 24:3, 14) Ntchitoyo ikuchitidwa tsopano, ndipo ikutero pamlingo waukulu, kuzungulira dziko lonse. Ngati tichititsa ntchitoyo kukhala chinthu chofunika koposa m’moyo wathu, pamenepo kuunika kwa Mulungu ndi chowonadi chake zikutitsogolera, monga momwe wamasalmoyo ananenera.
Ulemerero Weniweniwo wa Yehova Ukuŵala
16, 17. Kodi ndimotani mmene Yehova anachititsira ulemerero wake kuŵala pa gulu lake longa mkazi mu 1914, ndipo anatipatsa lamulo lotani?
16 Mwamawu othutsa mtima, Malemba amalongosola njira imene kuunika kwaumulungu kumaŵalira kwa anthu kulikonse. Yesaya 60:1-3, amene amanena za “mkazi” wa Yehova, kapena gulu lake lakumwamba la atumiki okhulupirika, amati: “Nyamuka, ŵala, pakuti kuunika kwako kwafika, ndi ulemerero wa Yehova wakutulukira. Pakuti tawona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu; Koma Yehova adzakutulukira, ndi ulemerero wake udzawoneka pa iwe. Ndipo amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kutuluka kwako.”
17 Ulemerero wa Yehova unaŵalira gulu lake lakumwamba longa mkazi m’chaka cha 1914 pamene, pambuyo panyengo yaitali yakuyembekeza, linabala Ufumu Waumesiya, Yesu Kristu monga Mfumu yake. (Chivumbulutso 12:1-5) Kuunika kwa Yehova kwaulemerero kukuŵala ndi chivomerezo chake pabomalo monga loyenerera kwa onse padziko lapansi.
18. (a) Kodi nchifukwa ninji mdima ukuphimba dziko lapansi, monga momwe kunanenedweratu pa Yesaya 60:2? (b) Kodi ndimotani mmene anthu aliyense payekha angawonjoledwere ku mdima wa dziko lapansi?
18 Mosiyana nzimenezo, mdima ukuphimba dziko lapansi ndipo mdima wa ndiwe yani mitundu ya anthu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mitunduyo ikukana boma la Mwana wokondedwayo wa Mulungu nifuna ulamuliro waumunthu. Iwo aganiza kuti mwakuchotsa mtundu wina waboma ndi kuika wina, adzathetsa mavuto awo. Koma zimenezi sizimadzetsa mpumulo umene amauyembekezera. Akulephera kuzindikira uyo amene ali kumbuyo kwa zochitikazo amene akusonkhezera mitundu kuchokera ku malo auzimu. (2 Akorinto 4:4) Iyo ikukana Magwero a kuunika kowona ndipo motero ali mumdima. (Aefeso 6:12) Komabe, mosasamala kanthu ndi zimene mitundu ikuchita, munthu aliyense payekha akhoza kumasulidwa ku mdima umenewo. Mwanjira yotani? Mwakuika chikhulupiriro chonse pa Ufumu wa Mulungu ndi kuugonjera.
19, 20. (a) Kodi nchifukwa ninji ndipo ndimotani mmene ulemerero wa Yehova waŵalira otsatira a Yesu odzozedwa? (b) Kodi nchifukwa ninji Yehova wachititsa odzozedwa ake kukhala onyamula kuunika? (c) Monga momwe kunanenedweratu, kodi ndimotani mmene “mafumu” ndi “amitundu” akopedwera ndi kuunika koperekedwa ndi Mulungu?
19 Chikristu Chadziko sichinaike chikhulupiriro mu Ufumu wa Mulungu ndipo sichinaugonjere. Koma otsatira a Yesu Kristu odzozedwa ndi mzimu atero. Monga chotulukapo, kuunika kwa Yehova kwa chivomerezo chaumulungu kwaŵalira pa oimira owoneka ameneŵa a mkazi wake wakumwamba, ndipo ulemerero wake wasonyezedwa pa iwo. (Yesaya 60:19-21) Iwo amasangalala ndi kuunika kwauzimu kumene palibe kusintha kulikonse kwa ndale zadziko kapena kwa zachuma kumene kungakuchotse. Iwo amasulidwa ndi Yehova kwa Babulo Wamkulu. (Chivumbulutso 18:4) Amasangalala ndi chivomerezo chake chifukwa chakuti amalandira chilango chake ndipo mokhulupirika achirikiza uchifumu wake. Iwo akuyang’ana ku zabwino za mtsogolo, ndipo akusangalala m’chiyembekezo chimene wawaikira.
20 Koma kodi nchifukwa ninji Yehova wachita nawo mwanjirayi? Monga momwe iyemwini ananenera pa Yesaya 60:21, watero kuti iye “akuzidwe,” kuti dzina lake lilemekezedwe ndi kuti ena akopeke naye monga Mulungu yekha wowona—akumapeza madalitso osatha. Mogwirizana ndi zimenezi, mu 1931 alambiri a Mulungu wowona ameneŵa analandira dzina lakuti Mboni za Yehova. Monga chotulukapo cha kuchitira umboni kwawo, kodi “mafumu” anakopeka ndi kuunika kumene anakuŵalitsira, monga momwe Yesaya ananenera? Inde! Osati olamulira andale zadziko lapansi, koma chiŵerengero chotsalira cha awo okhala pamzera wokalamulira monga mafumu pamodzi ndi Kristu mu Ufumu wake wakumwamba. (Chivumbulutso 1:5, 6; 21:24) Ndipo bwanji za “mitundu”? Kodi iyo yakopeka ndi kuunikako? Ndithudi yatero! Palibe mtundu wathunthu wandale zadziko uliwonse umene wakopeka, koma khamu lalikulu la anthu ochokera m’mitundu yonse atenga kaimidwe kawo kumbali ya Ufumu wa Mulungu, ndipo akuyembekezera mwachidwi kupulumutsidwa kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu. Lidzakhaladi dziko latsopano m’limene chilungamo chidzafunga.—2 Petro 3:13; Chivumbulutso 7:9, 10.
21. Kodi tingasonyeze motani kuti sitinaphonye chifuno cha kukoma mtima kwachisomo kwa Yehova kwakutipatsa chidziŵitso cha chifuniro chake?
21 Kodi ndinu mmodzi wa khamu lomakulakulalo la onyamula kuunika? Yehova watipatsa chidziŵitso cha chifuniro chake kotero kuti ifenso, mofanana ndi Yesu, tingathe kukhala onyamula kuunika. Mwakusonyeza changu m’ntchito imene Yehova waikizira atumiki ake m’tsiku lathu, tonsefe tisonyezetu kuti sitinaphonye chifuno cha kukoma mtima kwachifundo kumene Mulungu watisonyeza. (2 Akorinto 6:1, 2) Palibe ntchito imene iri yofunika kuposa imeneyi m’tsiku lathu. Ndipo palibe mwaŵi umene tingaupeze woposa kulemekeza Yehova mwakuŵalitsira ena kuunika kwaulemerero kumene kumachokera kwa iye.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
◻ Kodi nziti zimene ziri zochititsa zazikulu za mavuto odzetsa chisoni a anthu?
◻ Kodi ndim’njira ziti zimene ponse paŵiri, Yesu ndi otsatira ake aliri “kuunika kwa dziko”?
◻ Kodi kuunika kwa Yehova ndi chowonadi chake zimatitsogolera motani?
◻ Kodi ndimotani mmene Yehova wachititsira ulemerero wake kuŵalira gulu lake?
◻ Kodi nchifuno chotani chimene Yehova wachitira anthu ake kukhala onyamula kuunika?
[Zithunzi patsamba 9]
Chochitika cha m’Edene chimatithandiza kumvetsetsa mavuto odzetsa chisoni a anthu lerolino
[Mawu a Chithunzi]
Tom Haley/Sipa
Paringaux/Sipa