Khulupirirani Yehova—Osati mu “Chiwembu!”
1. Kodi ndi uti womwe unali mkhalidwe wa gulu lowoneka ndi maso la Yehova mkati mwa Nkhondo ya Dziko I?
MKATI mwa Nkhondo ya Dziko I, mathayo a anthu a Yehova anachepetsedwa kotheratu ndi ampatuko. Chizunzo chofulumizidwa ndi adani achipembedzo chinaulika motsutsana ndi iwo. Malikulu awo, mu Brooklyn, New York, anatsekedwa. M’kuwonjezerapo, iwo analibe thandizo la prezidenti wa Sosaite, mlembi wosunga chuma, manijala wa ofesi, ndi mlembi wa bungwe la mkonzi, ndi oimira anayi a Sosaite—onse a iwo anaikidwa m’ndende mu ndende ya chibalo ya Atlanta, Georgia. Chinawonekera ngati kuti mapeto anali atafika kaamba ka Ophunzira Baibulo odzozedwa ndi mzimu ndikuti ulemerero wawo wakumwamba unali pafupi. Koma sitero!
2. Kodi ndi ulosi uti wa Yesaya womwe unali ndi kugwiritsiridwa ntchito kwa makono mu 1919?
2 M’chenicheni, mu ngululu ya 1919 mafunso ofunsidwa ndi mneneri Yesaya anafuulidwa kachiŵirinso m’kugwiritsira ntchito kwamakono kwa Yesaya 66:6-8: “Mawu a phokoso achokera m’mudzi, mawu ochokera m’kachisi! Iwo ali mawu a Yehova amene abwezera adani ake chilango. Mkazi asanamve zowawa, anabala mwana, kupweteka kwake kusanadze, anabala mwana wamwamuna. Ndani anamva kanthu kotereko? Ndani anawona zinthu zoterezo? Kodi dziko lidzabadwa tsiku limodzi? Kodi mtundu udzabadwa modzidzimutsa? Pakuti pamene Ziyoni anamva zowawa, pomwepo anabala ana ake.”
3. Kodi ndi chitsimikizo chotani chimene chinalipo mu 1919 kuti Ziyoni anali atabala ana ndikuti “mtundu” watsopano unali utabadwa “panthaŵi imodzi”?
3 Monga ngati kuukitsidwa kuchoka kwa akufa, Ophunzira Baibulo a Dziko Lonse anapanga msonkhano wawo woyamba pambuyo pa nkhondo pa Cedar Point, Ohio, pa September 1-8, 1919. Prezidenti wa Sosaite, mlembi wosunga chuma, manijala wa ofesi, ndi andende ena akale, omasulidwa kotheratu ku milandu yonse, analiko kaamba ka chochitika chosangalatsa chimenechi. Ku chimwemwe cha osonkhanawo, Prezidenti Rutherford analengeza kufalitsidwa kwa magazini yatsopano, The Golden Age—yodziŵika tsopano monga Galamukani! Ndiponso, ubatizo wa anthu odzipereka atsopano oposa 200 unachitidwa. Gulu la teokratiki la Yehova linabweretsa ana ake ku moyo wokangalika mu nyengo ya pambuyo pa nkhondo. Icho chinaitanira kaamba ka njira za upainiya zatsopano, inde, zofunika kulimbika mtima, kumbali ya “mtundu” wobadwawo, pakuyesera kumodzi ndi kukhazikika “padziko” lobadwa modzidzimutsa.
4. (a) Kodi ndi chiyambukiro chotani chimene zonsezi zinayenera kukhala nacho pa “Babulo Wamkulu”? (b) Kuvumbulutsidwa kwa kaimidwe kenikeni ka Babulo Wamkulu ndi mphamvu yoposa ya munthu ya mphamvu zakumwamba kuli kotsogolera ku chiyani?
4 Mkhalidwewu unali wotokosa. Unagwira “Babulo Wamkulu,” ufumu wa dziko la chipembedzo chonyenga, modzidzimutsa. Kukhala chiwalo kwake, makamaka Dziko la Chipembedzo, kunakhala kovutitsidwa mokulira. Iye anadzimva kuti mtendere wake unali kulowereredwa. Chisungiko chake monga chinthu chosatheka kupikisana nacho m’munda wa ntchito ya chipembedzo unali m’tsoka. Iye anayenera kuvumbulutsidwa ponena za unansi wake weniweni ndi mphamvu yoposa anthu ya kumwamba, osati ndi Mulungu wa Baibulo Loyera, koma ndi “mulungu wa dongosolo iri la zinthu”—Satana, wopititsa patsogolo wa Kukana Kristu wonenedweratu mu ulosi wa Baibulo. (2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 2:18) Kuvumbulutsidwa kumeneku kunali chabe chiyambi cha zowawa za imfa yake. Kenaka Woweruza Wamkulu wa chilengedwe chonse adzamtenga iye mwachindunji m’dzanja ndi kumupha, osamupatsa iye chipulumuko chirichonse kuchokera kwa omkonda ake amene tsopano ali otenthedwa kotheratu, omkonda ake andale zadziko.
5. (a) Kodi nchifukwa ninji Dziko la Chipembedzo lidzagwidwa losagalamuka, ndipo ndimotani mmene ilo limawonedwera ndi Mulungu wa Baibulo? (b) Kodi nchiyani chimene “Babulo Wamkulu” sakuwona?
5 Ngakhale Dziko la Chipembedzo, lomwe liri ndi Baibulo lomwe limaneneratu zonsezi, lidzagwidwa losagalamuka. Ilo lidzakhulupirira mu mfuu ikudzayo ya “mtendere ndi chisungiko” monga kwaganiziridwa ndi mitundu mu chimene ilo lakhala likumamatira mosamalitsa ku ziphunzitso zake za chipembedzo. Panthaŵi imodzimodziyo, matchalitchi ake amapititsa mbale ya chopereka, kudzilemeretsa iwo eni ndi zoperekedwa zoikidwa mmenemo. Kwa Mulungu wa Malemba Oyera, ngakhale kuli tero, ilo liri “losauka ndi lakhungu ndi lamaliseche.” Ilo silikhulupirira mwa Yehova, ndiponso silimadzipereka ilo lokha ku mapindu enieni auzimu amene iye amapereka. (Chivumbulutso 3:17, 18) Ilo silikuwona mawu olembedwa pakhoma. Kodi nchiyani chimene tikutanthauza ndi ichi?
Dzanja Lolemba Pakhoma Liwoneka
6. Kodi ndi mphamvu ya dziko yakale iti imene tsopano imafika m’maganizo, ndipo ndimotani mmene anthu odziŵika a Yehova anali kuchitira?
6 Kuti timvetsetse, tiyenera kuyang’ana m’mbuyo pa ora lomalizira la mphamvu ya dziko yachitatu ya mbiri ya Baibulo, Babulo, pagombe la Mtsinje wa Firate. Belisazara anali wolamulira womalizira wa Babulo, yemwe anaphatikizapo mbali ya nsanja ya Babele, kumene Mulungu wamphamvuyonse anasokoneza chilankhulidwe chimodzi cha omanga, kuwamwaza iwo. (Genesis 11:1-9) Pa nthaŵi ya maora omalizira a Babulo, anthu odziŵika a Yehova, Ayuda, anali othaŵa kwawo andende m’dziko lachikunja limenelo. Koma zaka zawo 70 zaukapolo zinali pafupi kutha.
7. (a) Nchifukwa ninji Mfumu Belisazara anakonza madyerero kaamba ka akulu ake ndi chidaliro chotheratu? (b) Kodi nchiyani chimene chidachitika mkati mwa madyererowo, ndipo ndi chotulukapo chotani pa mfumuyo?
7 Amedi ndi Aperisi ogwirizana, omwe anayenera kupanga mphamvu ya dziko yachinayi ya mbiri ya Baibulo, anabwera moyang’anizana ndi linga lolimbikitsidwa kwambiri, lowoneka kukhala losalowereredwa, la mzinda wa Babulo. Mtsinje wa Firate unali kuyenda kupyola mkati mwa mzinda, wokhala ndi madoko m’mphepete mwagombe lake mu limene zitseko ziŵiri za mkuŵa za mzindawo zinali kutsegulidwa. Ndi chidaliro chotheratu m’chisungiko cha mzindawo. Mfumu Belisazara anakonzera “anthu ake a akulu chikwi chimodzi madyerero a akulu”—madyerero a akulu omwe anatsimikizira kukhala madyerero ake otsirizira. Mwadzidzidzi, mkati mwa mzera wakutha kuwona wa Belisazara, panawoneka pakhoma dzanja loyenda. Ndipo linalemba pakhomalo mawu ochititsa ngozi awa “MENE, MENE, TEKEL UFARSIN.” (Danieli 5:1, 5, 25) Umenewo unali usiku wa October 5, 539 B.C.E. Mawuwo anali ndi chisonkhezero chochititsa mantha. Mfumu Belisazara ananjenjemera ndi mantha. Dikirani tsopano! Tengani amuna anzeru—amatsenga ndi openda nyenyezi omwe ali ndi chivomerezo chokhoza kulongosola zizindikiro ndi matsenga. Koma kalembedwe ka mawu achilendowo, omwe sanakhoze ngakhale kuwaŵerenga, anali owaposa iwo. Kodi nchiyani tsopano chimene chinakachitidwa?
8, 9. (a) Monga yankho lotsirizira, kodi ndi njira ya kachitidwe yotani imene inayamikiridwa kwa mfumu? (b) Kodi ndimotani mmene Danieli anamasulira dzanja lolemba pakhoma? (c) Nchifukwa ninji phwando lalikulu la Mfumu Belisazara linatulukapo m’ulosi woipa wotero?
8 Itanani Myuda. Nchiyani? Myuda? Inde, mmodzi wa akalonga ndi olemekezeka omwe anatengedwa kuchokera ku Yerusalemu mu dziko lake lobadwiramo ndi kubweretsedwa ndi Mfumu Nebukadinezara ku Babulo kudzaphunzitsidwa kaamba ka utumiki wa boma. Chabwino, monga choyesera chomaliza, chimenecho chinali chinthu chabwino chomwe chikanachitidwa. Danieli anavomerezedwa ndi mfumukazi kukhala munthu wanzeru—munthu yemwe anali wokhoza kuŵerenga zinthu ndi kuzimasulira izo. (Danieli 5:10-12) Tingamve bata lomwe linalowa m’chipinda chaphwandolo pamene Danieli, mkugonjera ku chifunsiro cha Mfumu Belisazara, anapitiriza kumasulira mawu a chinsinsiwo kwa wolamulira wa mphamvu ya dziko yachitatu ya mbiri ya Baibulo ndi akulu ake.
9 Danieli anapitiriza kunena kuti: “Pamenepo nsonga ya dzanja inatumidwa kuchokera pamaso pake, nililembedwa lembali. Ndipo lemba lolembedwa ndi ili: MENE, MENE, TEKEL UFARSIN. Kumasulira kwake kwa mawu awa ndi uku: MENE, Mulungu anaŵerengera ufumu wanu nautha. TEKEL, Mwayesedwa pamiyeso, nimupezeka mwaperewera. PERES,a ufumu wanu wagawanika, nuperekedwa kwa Amedi ndi Aperisi.” (Danieli 5:24-28) Mfumu Belisazara ndi akulu ake ndi akazi a oyanjana nawo anasonyeza kupikisana kwadala, kunyazitsa kaamba ka kulambiridwa kwa Mulungu wa Danieli. Motani? Mwakumwera vinyo kuchokera mu zikho za golidi zomwe zinatengedwa kuchokera mu kachisi wa Yehova mu Yerusalemu panthaŵi ya kuwonongedwa kwa mzinda woyera umenewo m’chaka cha 607 B.C.E. Kumeneko kunali monga kuwonjezera kusamvera konyada kwa chivulazo.—Danieli 5:3, 4, 23.
Koresi Wonenedweratu Atenga Ulamuliro
10, 11. (a) Ndi ndani amene Yehova ananeneratu kukhala wogonjetsa Babulo, ndipo ndimotani mmene Yesaya analongosolera kubwera kwa kugonjetsaku? (b) Kodi ndimotani mmene Yehova anakwaniritsira ulosi umenewu ndi kubweretsa chilango chotheratu pa Mfumu Belisazara ndi akulu ake?
10 Pa Yesaya 45:1-3 Mulungu Wam’mwambamwamba ananeneratu kuti: “Atero Yehova kwa wodzozedwa wake kwa Koresi, amene dzanja lake lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake, ndipo ndidzamasula m’chuuno mwa mafumu; atsegule zitseko pamaso pake, ndi zipata sizidzatsekedwa: ‘Ndidzakutsogolera ndi kusalaza pokakala. Ndidzathyolathyola zitseko zamkuwa, ndi kudula pakati akapichi achitsulo. Ndipo ndidzakupatsa iwe chuma cha mumdima, ndi zolemera zobisika za m’malo am’tseri, kuti iwe udziŵe kuti ine ndine Yehova, amene ndikuitana iwe dzina lako.’”
11 Kuti akwaniritse ulosi umenewu, Yehova anachiika icho m’maganizo a Koresi wa ku Perisiya kupatutsa madzi a Mtsinje wa Firate ndi kuwapatutsira iwo m’nyanja ya kumaloko. Kenaka, pambuyo pa kuuma kwagombe la mtsinjewo, pansi pa mumdima, magulu ankhondo a Koresi anayenda kutsikira ku gombe la mtsinje ndi kulowa mkati mwa mzinda. Popeza kuti zitseko ziŵiri m’mphepete mwa kutsogolo kwa madzi zinasiiyidwa zotsegulidwa, iwo anakwera m’mphepete mwa mtsinje ndi kulowa m’chipinda chamadyerero, kugonjetsa olindirira. Chotero madyerero a Mfumu Belisazara anafika kumapeto ochititsa mantha monga chilango chotheratu kaamba ka iye ndi akulu ake—chifukwa cha kusunga “Mbuye wakumwamba” kumanyazi, kunyazitsa, ndi kupeputsa mwa kugwiritsira ntchito molakwika zikho zakachisi zobedwa kuchokera ku malo okhalako opatulika a Yehova mu Yerusalemu.
12. (a) Popeza Yesaya anali ataneneratu kuti Koresi adzagonjetsa Babulo, kodi nchifukwa ninji Danieli anapereka ulemerero kukugwidwa kwa Babulo kwa Dariyo Mmedi? (b) Kodi ndi ndani amene Dariyo ndi mnzake, Koresi m’Perisiya, anaimira?
12 Versi lomalizira la Danieli mutu 5 limanena kuti pambuyo pa kupha Mfumu Belisazara, Dariyo Mmedi “analandira ufumu, ali chifupifupi wa zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu ziŵiri.” Popeza Dariyo anali mkulu wake wa Koresi wa ku Perisiya, Danieli anapereka kulandidwa kwa Babulo kwa mfumu ya Amedi imeneyi. Iye analamulira kuchokera ku 539 kufika ku 537 B.C.E. monga wolamulira wolemekezeka pa ufumu wa Medo-Persia. Iye anaimira bwino Yehova Mulungu. Mnzake wa Dariyo, Koresi wa ku Perisiya, anaimira Yesu Kristu, amene mokulira adzagwiritsiridwa ntchito ndi Yehova kugonjetsa ndi kuwononga “Babulo Wamkulu,” ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga.
13, 14. Kodi nchiyani chimene Danieli mosakaikira analoza kwa Koresi m’Perisiya, ndipo kodi ndimotani mmene bukhu la Ezara lolembedwa pambuyo pa kumasulidwa kwa ukapolo limatsegulira?
13 Pa kukwera kwa Koresi ku mpando wachifumu wa Medo-Persia mu 537 B.C.E., mosakaikira mneneri Danieli anachidziŵitsa icho kwa iye mu ulosi wa Yehova wonena za iye wopezeka pa Yesaya 45. Bukhu la Ezara lolembedwa pambuyo pa kumasulidwa mu ukapolo limatsegula ndi mawu awa:
14 “Chaka choyamba tsono cha Koresi mfumu ya ku Perisiya, kuti akwaniritsidwe mawu a Yehova m’kamwa mwa Yeremiya [ponena za kutalika kwa ukapolowo kukhala zaka 70 (Yeremiya 25:12; 29:10, 14)] Yehova anautsa mzimu wa Koresi mfumu ya Perisiya kuti abukitse mawu mu ufumu wake wonse, nawalembenso ndi kuti: ‘Atero Koresi mfumu ya ku Perisiya, “Yehova Mulungu Wam’mwamba wandipatsa ine maufumu onse a pa dziko lapansi, nandilangiza ndimmangire nyumba m’Yerusalemu, ndiwo m’Yuda. Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Mulungu wake akhale naye, nakwere kumka ku Yerusalemu, ndiwo m’Yuda, nakamange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israyeli—iye ndiye Mulungu wowona—wokhala m’Yerusalemu.”’”—Ezara 1:1-3.
Koresi Wamkulu Agonjetsa “Babulo Wamkulu”
15. (a) Kodi ndi liti pamene Koresi wophiphiritsirayu anayamba kulamulira? (b) Ndi kaimidwe kosasinthika kotani kamene Mboni za Yehova zimatenga m’chigwirizano ndi chiwembu cha Mitundu Yogwirizana, ndipo nchifukwa ninji?
15 Koresi Wamkulu wa lerolino wophiphiritsirayo anayamba kulamulira mu 1914 pamapeto pa “nthaŵi yoikika ya amitundu,” monga wanenedwera ndi Yesu iyemwini pa Luka 21:24. Mkunyalanyaza kotheratu nsonga ya dziko lonse yofunika kwambiri imeneyi, mitundu mkati mwa Mitundu Yogwirizana inakhazikika pa chaka cha 1986 monga Chaka Chawo Cha Mtendere wa Mitundu Yonse. Koma Mboni za Yehova mu njira iriyonse sizinagwidwe zosagalamuka m’chigwirizano ndi ichi. Pamene chilengezo chonenedweratu cha “mtendere ndi chisungiko” chidzachitidwa pomalizira, iwo sadzagwirizana mkumamatira ku ndale zadziko ndi mayanjano aubwenzi wa “Babulo Wamkulu” m’kuchita madyerero panthanthi yonyenga imeneyi pa tsiku ili lochedwa mu mbiri ya mitundu ya dziko. Iwo sapititsa patsogolo chiwembu chirichonse ndi Mitundu Yogwirizana kapena njira ina yake ya mtendere. (Yesaya 8:12) Monga chodzichinjirizira, iwo amanena ndi mawu a Yesaya 8:20: “Ku lamulo ndi umboni! Ngati iwo salankhula mogwirizana ndi mawu awa, iwo alibe kuwunika kwa mbandakucha.” (New International Version) Ndipo kupereka chifukwa cha kaimidwe kawo kosasinthika, iwo amanena kuti: “Pakuti Mulungu ali nafe!” (Yesaya 8:10) Mopanda kubisa, chimenechi chikutanthauza kuti Yehova Mulungu sakutenga mbali mu machitidwe a ndale zadziko otengedwa ndi mitundu m’malo mwa “mtendere ndi chisungiko” koma, m’malomwake, mosakaikira iye ali wotsutsana nawo.
16. Kodi ndimotani mmene mawu aulosi a pa Chivumbulutso 17:16, 17 adzayeretsedwera mokulira, ndipo ndi chotulukapo chotani pa anthu a Yehova?
16 Mwakuchita zinthu mwamachenjera, Yehova, kupyolera mwa Koresi wake Wamkulu, adzachiika icho m’mtima ndi m’maganizo a atsogoleri a ndale zadziko kutembenukira motsutsana ndi “Babulo Wamkulu,” ulamuliro wa dziko la chipembedzo chonyenga. Monga ngati ndi nyanga za chirombo cholusa, izo chidzabaya iye kufikira imfa. Mawu aulosi pa Chivumbulutso 17 adzalemekezedwa mokwanira, ndipo pa ichi Mboni za Yehova za pa dziko lapansi zidzasangalala.—Chivumbulutso 17:16, 17; 19:1-3.
Kusunga Mayanjano Athu Abwino ndi Yehova
17. Ngakhale kuti Mboni za Yehova siziri mbali ya “Babulo Wamkulu,” kodi nchiyani chimene olamulira a dziko adzachita?
17 Kenaka, ngakhale kuti Mboni za Yehova siziri mbali ya “Babulo Wamkulu,” koma ziri avumbulutsi ake olumbiritsidwa, ndipo ngakhale iwo sanatenge mbali mu machitachita a ndale zadziko a dziko ili, mbali za ndale zadziko zopanda chipembedzo zimenezo zidzatembenukira motsutsana ndi Mboni zomapulumuka. Ofunitsitsa kukhala olamulira ankhalwe ndi ulamuliro wa dziko lonse pambali zonse za chitaganya cha anthu padziko lapansi, iwo adzapanga kuukira komalizira kwa dziko lonse pa Mboni zosunga umphumphu za Wamkulukuluyo, yemwe ali Magwero a boma lolungama.
18. Kodi ndi chochitika chochititsa mantha chotani chimene Yehova adzachita, kuphimba Chigumula cha m’tsiku la Nowa?
18 Pano tsopano ndi pamene Wolamulira Wadziko Lonse wakumwamba ndi dziko lapansi ayenera kulowereramo ndipo ayenera kupanga asakazi a “Babulo Wamkulu” kudziŵa ndi kumvetsetsa kuti Mmodzi amene kwa iye kwakhala Mboni mu zaka za zana la 20 ali Mulungu weniweni, Mulungu wamphamvuyonse—Mulungu wokhala ndi kuyenera kwa kulambiridwa, kwamtima wonse kosagawanika ndi zolengedwa zake pano pansi pa choikapo mapazi ake, padziko lapansi. Iye adzachita ichi mu njira yochititsa mantha yomwe idzapangitsa chibwano chapansi cha pakamwa pa Mboni zowonazo m’mphepetemo kugwa ndi kudodometsedwa. Iye adzachita kachitidwe kake ka ulemerero ka nkhondo yosayembekezeredwa, kuchipambano chaumulungu. (Chivumbulutso 16:14, 16; 19:19-21) Chimenecho chidzapereka mapeto a dongosolo ili la zinthu loipa, lolamuliridwa ndi Mdyerekezi ndi ulemerero womwe udzapambana kuwononga kwa dziko lonse kwa Chigumula cha m’tsiku la Nowa.
19. Kodi ndi mboni zotani zimene Yehova adzakhala nazo ponena za kuyeretsa kwa iyemwini monga Wolamulira Wachilengedwe chonse, ndipo kodi nchiyani chimene ichi chidzasonyeza?
19 Monga mmene Yehova analiri ndi mboni kuchitira umboni mapeto a dziko lakale mu Chigumula chomwe chinamiza mtundu wonse wa anthu kunja kwa chingalawa, iye adzatero, pa maziko okulirapo, kukhalanso ndi mboni pano padziko lapansi ponena za kachitidwe kosadzabwerezedwanso ka kuyeretsa iyemwini monga Wolamulira Wachilengedwe chonse. (2 Petro 3:6, 7, 13, 14) Awa adzakhala awo amene amakhulupirira mwa iye kaamba ka mtendere ndi chisungiko mkati mwa dziko lodetsedwali. Achimwemwe mudzakhala inu pamene mudzaŵerengedwa pakati pa Mboni zoyanjidwa mozizwitsa zimenezo. Mtendere wanu ndi chisungiko zidzakhala zitasonyezedwa kukhala zochokera kwa Yehova Mulungu ndipo osati ku chigwirizano chirichonse, kapena chiwembu, ndi mphamvu za ndale zadziko za dongosolo ili la kachitidwe ka zinthu lolamuliridwa ndi Mdyerekezi.
20. Ndimotani mmene Yehova adzatulukira, ndipo nchiyani chimene tifunikira kugamulapo kuchita?
20 Yehova Mulungu adzatuluka wolemekezedwa monga Mmodzi woyenera kulambiridwa ndi kutumikiridwa monga wokhalako Wamkulukulu Waumulungu—Mulungu wa milungu, wopambana Mmodzi kwa amene mawu ouziridwa a wamasalmo anatsogozedwa: “Kuyambira nthaŵi yosayamba kufikira nthaŵi yosatha inu ndinu Mulungu.” (Masalmo 90:2) Ndi chiyamikiro chomakulakulabe, lolani kuti tisunge kukhulupirira kwathu mwa Yehova Mulungu ndi maunansi athu ndi iye kupyolera mwa Koresi Wamkulu, Yesu Kristu.
[Mawu a M’munsi]
a “Ufarsin” ili pulula la liwu lakuti “peres” ndipo limatanthauza “kugawanitsa.”
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchiyani chimene “Babulo Wamkulu” sakuwona?
◻ Kodi nchiyani chimene chotulukapo chochititsa ngozi cha madyerero a Belisazara chinaimira?
◻ Kodi ndani amene adzagonjetsa “Babulo Wamkulu”?
◻ Kodi ndi kaimidwe kotani kamene Mboni za Yehova zatenga m’chigwirizano ndi chiwembu cha Mitundu Yogwirizana?
◻ Kodi nchifukwa ninji awo onse amene amaika chidaliro chawo mwa Yehova kaamba ka mtendere ndi chisungiko adzakhala achimwemwe?
[Chithunzi patsamba 25]
Danieli akutanthauzira kulembedwa kwa chinsinsi monga uthenga wa chiweruzo kaamba ka ulamuliro wa Babulo