Kudziŵa Mtundu Wabwino wa Mthenga
“Ndine amene ndilimbitsa mawu a mtumiki wanga, kuchita uphungu wa amithenga anga.”—YESAYA 44:25.
1. Kodi Yehova amadziŵikitsa motani mtundu wabwino wa amithenga, ndipo amavumbula motani wonyenga?
YEHOVA MULUNGU ndiye Wodziŵikitsa Wamkulu wa amithenga ake oona. Amawadziŵikitsa mwa kuchititsa mauthenga amene amapereka kudzera mwa iwo kukhaladi oona. Yehova ndiyenso Wovumbula Wamkulu wa amithenga onyenga. Kodi amawavumbula motani? Amalepheretsa zizindikiro zawo ndi maulosi awo. Mwa njirayi amasonyeza kuti ali aneneri odziikapo okha, amene mauthenga awo kwenikweni amachokera m’maganizo awo onyenga—inde, maganizo awo opusa, aumunthu!
2. Kodi ndi mkangano wotani umene unali pakati pa amithenga m’nthaŵi ya Aisrayeli?
2 Onse aŵiri Yesaya ndi Ezekieli ankanena kuti ali aneneri a Yehova Mulungu. Kodi iwo analidi aneneriwo? Tiyeni tione. Yesaya analosera m’Yerusalemu kuyambira cha m’ma 778 B.C.E. mpaka cha pambuyo pa 732 B.C.E. Ezekieli anatengeredwa ku Babulo monga wandende mu 617 B.C.E. Kumeneko ankalosera kwa abale ake achiyuda. Aneneri onse aŵiri analengeza molimba mtima kuti Yerusalemu adzawonongedwa. Aneneri ena ankanena kuti Mulungu sangalole zimenezi kuchitika. Kodi ndani anakhala amithenga oona?
Yehova Avumbula Aneneri Onyenga
3, 4. (a) Kodi ndi mauthenga aŵiri ati otsutsana amene anaperekedwa kwa Aisrayeli ku Babulo, ndipo Yehova anamvumbula motani mthenga wonyenga? (b) Kodi nchiyani chimene Yehova anati chidzachitikira aneneri onyenga?
3 Ezekieli, akali ku Babulo, anapatsidwa masomphenya a zimene zinali kuchitika m’kachisi wa ku Yerusalemu. Poloŵera kuchipata chakummaŵa panali amuna 25. Pakati pawo panali akalonga aŵiri, Yazaniya ndi Pelatiya. Kodi Yehova anawaona motani? Ezekieli 11:2, 3 akuyankha kuti: “Wobadwa ndi munthu iwe, awa ndi anthu olingirira za mphulupulu, ndi kupangira uphungu woipa m’mudzi muno; ndiwo akuti, siinafike nyengo yakumanga nyumba[?]” Amithenga a mtendere odzitukumula ameneŵa anali kunena kuti, ‘Yerusalemu saali pangozi. Eya, posachedwapa tidzamangamo nyumba zowonjezereka!’ Choncho Mulungu anauza Ezekieli kuti apereke ulosi wotsutsa aneneri amabodza ameneŵa. M’vesi 13 la chaputala 11, Ezekieli akutiuza chimene chinachitikira mmodzi wa iwo kuti: “Kunali, pakunenera ine, anamwalira Pelatiya mwana wa Benaya.” Zimenezi zinachitika motere mwina chifukwa chakuti Pelatiya ndiye anali kalonga wamkulu ndi wosonkhezera kwambiri ndipo wolambira mafano koposa. Kufa kwake mwadzidzidzi kunasonyeza kuti anali mneneri wonyenga!
4 Kupha Pelatiya kwa Yehova sikunachititse aneneri onyenga enawo kuleka kunama m’dzina la Mulungu. Anthu onyenga ameneŵa anapitiriza ndi njira yawo yauchitsiru yolosera zinthu motsutsana ndi chifuniro cha Mulungu. Choncho Yehova Mulungu anauza Ezekieli kuti: “Tsoka aneneri opusawo akutsata mzimu wawowawo, chinkana sanaona kanthu.” Mofanana ndi Pelatiya, iwo anali kudzakhala “palibe” chifukwa cha kuonera Yerusalemu monyenga “masomphenya a mtendere, pamene palibe mtendere.”—Ezekieli 13:3, 15, 16.
5, 6. Mosasamala kanthu za mauthenga onse onyenga, kodi Yesaya anakwezedwa motani kukhala mneneri woona?
5 Ponena za Yesaya, mauthenga ake onse a Mulungu onena za Yerusalemu anakhala oona. M’chilimwe cha mu 607 B.C.E., Ababulo anawononga mzindawo ndi kutenga Ayuda otsalira napita nawo ku Babulo monga andende. (2 Mbiri 36:15-21; Ezekieli 22:28; Danieli 9:2) Kodi masoka ameneŵa anachititsa aneneri onyengawo kuleka kuvutitsa anthu a Mulungu ndi mawu auchitsiru opanda pake? Ayi, aneneri amabodza amenewo analimbikira bodza lawo!
6 Kuwonjeza pa zimenezi, Aisrayeli okhala mu ukapolo anakumananso ndi oombeza ula ndi openda nyenyezi odzitama a Babulo. Komabe, Yehova anasonyeza kuti amithenga onyenga onsewa anali zitsiru zogwiritsidwa mwala, zolosera zinthu zosemphana ndi zimene zidzachitika. M’kupita kwa nthaŵi anasonyeza kuti Ezekieli anali mthenga wake woona, monga momwe Yesaya analili. Yehova anakwaniritsa mawu onse amene ananena kudzera mwa iwo, monga momwe analonjezera kuti: “Ndine amene nditsutsa zizindikiro za matukutuku, ndi kuchititsa misala oombeza ula; ndi kubwezera m’mbuyo anthu anzeru, ndi kupusitsa nzeru zawo: Ndine amene ndilimbitsa mawu a mtumiki wanga, kuchita uphungu wa amithenga anga.”—Yesaya 44:25, 26.
Mauthenga Odabwitsa Onena za Babulo ndi Yerusalemu
7, 8. Kodi ndi uthenga wouziridwa wotani wa Babulo umene Yesaya anali nawo, ndipo mawu ake anatanthauzanji?
7 Yuda ndi Yerusalemu anali kudzakhala bwinja zaka 70, popanda munthu wokhalamo. Komabe, Yehova analengeza kudzera mwa Yesaya ndi Ezekieli kuti mzindawo udzamangidwanso ndipo m’dzikolo mudzakhalanso anthu panthaŵi yeniyeniyo imene ananeneratu! Umenewu unali ulosi wodabwitsa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Babulo ankadziŵika kuti samamasula andende ake. (Yesaya 14:4, 15-17) Chotero kodi ndani akanatha kumasula andende ameneŵa? Ndani akanagwetsa Babulo wamphamvuyo, wokhala ndi malinga aakuluwo ndi mitsinje yomtetezera? Yehova wamphamvuyonseyo akanatha kuchita zimenezo! Ndipo ananena kuti adzachitadi zimenezo: “Ndine amene nditi kwa nyanja yakuya [ndiko kuti, madzi otetezera mzindawo], Iphwa, ndipo ndidzaumitsa nyanja zako; ndi kunena za Koresi, Iye ndiye mbusa wanga, ndipo adzachita zofuna zanga zonse; ndi kunena za Yerusalemu, Adzamangidwa; ndi kwa Kachisi, Maziko ako adzaikidwa.”—Yesaya 44:27, 28.
8 Talingalirani zimenezo! Mtsinje wa Firate, chopinga chachikuludi kwa anthu, unali ngati dontho lamadzi pachiwaya choofiira ndi kutentha kwa Yehova. Shoo, chopingacho chidzauma! Babulo adzagwa. Ngakhale panali zaka ngati 150 Koresi Mperisi asanabadwe, Yehova anachititsa Yesaya kuneneratu kuti mfumuyi idzalanda Babulo ndi kumasula andende achiyuda mwa kuwalola kubwerera kwawo kukamanganso Yerusalemu ndi kachisi wake.
9. Kodi Yehova anati mtumiki wake wolangira Babulo ndani?
9 Ulosiwu tikuupeza pa Yesaya 45:1-3: “Atero Yehova kwa wodzozedwa wake kwa Koresi, amene dzanja lake lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake, . . . atsegule zitseko pamaso pake, ndi zipata sizidzatsekedwa; Ndidzakutsogolera ndi kusalaza pokakala; ndidzatyolatyola zitseko zamkuwa, ndi kudula pakati akapichi achitsulo; ndipo ndidzakupatsa iwe chuma cha mumdima, ndi zolemera zobisika za m’malo amtseri, kuti iwe udziŵe kuti Ine ndine Yehova, amene ndikuitana iwe dzina lako.”
10. Kodi Koresi anali “wodzozedwa” motani, ndipo Yehova analankhula naye motani zaka zoposa zana limodzi asanabadwe?
10 Mwaonatu kuti Yehova akulankhula kwa Koresi monga kuti wakhala kale ndi moyo. Zimenezi zikugwirizana ndi mawu a Paulo akuti Yehova ‘amaitana zinthu zoti palibe, monga ngati zilipo.’ (Aroma 4:17) Ndiponso, Mulungu akudziŵikitsa Koresi kuti ndiye “wodzozedwa wake.” Anachitiranji zimenezo? Ndi iko komwe, mkulu wa ansembe wa Yehova sanatsanulire mafuta oyera odzozera pamutu pa Koresi. Ndi zoona, koma kumeneku ndi kudzoza kwaulosi. Kumasonyeza kupatsidwa thayo lapadera. Chotero Mulungu anatha kunena za kuikiratu kwake Koresi kukhala kudzoza.—Yerekezerani ndi 1 Mafumu 19:15-17; 2 Mafumu 8:13.
Mulungu Akwaniritsa Mawu a Amithenga Ake
11. Kodi nchifukwa ninji anthu a m’Babulo anadzimva ngati otetezereka?
11 Pamene Koresi anapita kukamenyana ndi Babulo, okhalamo ake anadzimva ngati otetezereka kwambiri ndi osungika. Mzinda wawo unali wozunguliridwa ndi chemba lotetezera lakuya ndipo lalikulu, lopangika ndi Mtsinje wa Firate. Pomwe mtsinjewo unadutsa mkati mwa mzinda, munali doko m’mbali mwa gombe lakummaŵa la mtsinjewo. Kuti alipatule ku mzinda, Nebukadinezara anamanga chimene anati ndi “linga lalikulu, limene silingasunthidwe monga phiri . . . Pamwamba pake [anapa]kweza ngati phiri.”a Linga limeneli linali ndi zipata zokhala ndi zitseko zazikulu zamkuwa. Kuti munthu aloŵe pazipata zimenezi, anayenera kukwera chikweza kuchokera kugombe la mtsinjewo. Nzosadabwitsa kuti andende a Babulo sanali kukhala ndi chiyembekezo cha kudzamasulidwa konse!
12, 13. Kodi mawu a Yehova kudzera mwa mthenga wake Yesaya anakwaniritsidwa motani pamene Koresi analanda Babulo?
12 Koma osati ndi andende achiyuda amenewo amene anali ndi chikhulupiriro mwa Yehova! Iwo anali ndi chiyembekezo chachikulu. Kudzera mwa aneneri ake, Mulungu analonjeza kuti adzawamasula. Kodi Mulungu analikwaniritsa motani lonjezo lake? Koresi analamula asilikali ake kupambutsa Mtsinje wa Firate pamalo ena ake makilomita ambiri kumpoto kwa Babulo. Choncho, chitetezo chachikulu cha mzindawo chinasanduka khwaŵa la madzi ochepa. Pausiku wosinthira zinthu umenewo, anthu amenewo oledzera kumapwando aphokoso m’Babulo anasiya zipata za zitseko ziŵiri zoyang’anizana ndi gombe la Firate zili zotseguka mosasamala. Sikuti Yehova anatyoladi zitseko zamkuwa kukhala zidutswa; ndiponso sanadule akapichi achitsulo otsekera zitsekozo m’lingaliro lenileni, koma njira imene anayendetsera zinthu modabwitsa kuti zikhale zotseguka ndi zopanda akapichi inali ndi chotulukapo chofanana. Malinga a Babulo anali opanda pake. Asilikali a Koresi sanafunikire kuwakwera kuti aloŵe mkati. Yehova anatsogolera Koresi, kusalaza “pokakala,” inde, zopinga zonse. Yesaya anakhaladi mthenga woona wa Mulungu.
13 Koresi atalanda mzinda wonsewo, chuma chonse cha mzindawo chinakhala m’manja mwake, kuphatikizapo chija chobisika m’zipinda zamdima ndi zamtseri. Kodi nchifukwa ninji Yehova Mulungu anamchitira zimenezi Koresi? Kuti adziŵe kuti Yehova, ‘amene amuitana iye dzina lake,’ ndiye Mulungu wa ulosi woona ndi Ambuye Mfumu wa chilengedwe chonse. Anali kudzadziŵa kuti Mulungu ndiye analinganiza kuti atenge ulamuliro kuti amasule anthu Ake, Israyeli.
14, 15. Kodi tikudziŵa motani kuti Yehova ndiye anatheketsa Koresi kugonjetsa Babulo?
14 Tamvani mawu a Yehova kwa Koresi: “Ndakuitana iwe dzina lako, chifukwa cha Yakobo mtumiki wanga ndi Israyeli wosankhidwa wanga; ndakuwonjezera dzina, ngakhale iwe sunandidziŵa Ine. Ine ndili Yehova, ndipo palibe winanso; popanda Ine palibe Mulungu; ndidzakumanga m’chuuno, ngakhale sunandidziŵa; kuti anthu akadziŵe kuchokera ku matulukiro a dzuŵa ndi kumadzulo, kuti palibe wina popanda Ine; Ine ndine Yehova, palibe winanso. Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere [kwa anthu ake okhala mu ukapolo] ndi choipa [kwa Babulo], Ine ndine Yehova wochita zinthu zonse zimenezi.”—Yesaya 45:4-7.
15 Yehova ndiye anatheketsa Koresi kugonjetsa Babulo, popeza Ndiye amene anamlimbitsa kuti achite chokonda Chake motsutsana ndi mzinda woipawo ndi kumasula anthu Ake okhala mu ukapolo. Mwakutero, Mulungu anauza miyamba yake kutsanulira zisonkhezero kapena mphamvu zachilungamo. Anauza dziko lake lapansi kutseguka ndi kutulutsa zochitika zachilungamo ndi chipulumutso cha anthu ake okhala mu ukapolo. Ndipo kumwamba kwake kophiphiritsira ndi dziko lake lapansi lophiphiritsira zinayankha lamulo limeneli. (Yesaya 45:8) Zaka zoposa zana limodzi Yesaya atamwalira, iye anasonyezedwa kukhala mthenga woona wa Yehova!
Uthenga Wabwino wa Mthengayo kwa Ziyoni!
16. Kodi ndi uthenga wabwino wotani umene unalengezedwa mumzinda wabwinja wa Yerusalemu pamene Babulo anagonjetsedwa?
16 Koma palinso zina. Yesaya 52:7 akunena za uthenga wabwino wa Yerusalemu: “Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.” Mmene kunalili kosangalatsa kuona mthenga akubwera ku Yerusalemu kuchokera kumapiri! Ayenera kuti ali ndi uthenga. Kodi ndi uthenga wanji? Ndi uthenga wosangalatsa wa Ziyoni. Uthenga wa mtendere, inde, uthenga wa chiyanjo cha Mulungu. Yerusalemu ndi kachisi wake ayenera kumangidwanso! Ndipo mthengayo akulengeza ndi chimwemwe cha chipambano kuti: “Mulungu wako ndi mfumu”!
17, 18. Kodi kugonjetsa Babulo kwa Koresi kunayambukira motani dzina lake la Yehova?
17 Pamene Yehova analola Ababulo kugubuduza mpando wake wachifumu wophiphiritsira paumene mafumu a mumzera wa Davide ankakhala, zinaoneka ngati kuti Iye sanalinso Mfumu. M’malo mwake, Marduk, mulungu wamkulu wa Babulo, ndiye anaoneka kukhala mfumu. Komabe, Mulungu wa Ziyoni atagwetsa Babulo, anasonyeza uchifumu wake wa chilengedwe chonse—kuti ndiye anali Mfumu yaikulu kopambana. Ndipo kuti agogomezere choonadi chimenechi, Yerusalemu, “mzinda wa Mfumu yaikulukulu,” anali kudzakhazikitsidwanso, pamodzi ndi kachisi wake. (Mateyu 5:35) Kunena za mthenga amene anabweretsa uthenga wabwino umenewu, ngakhale mapazi ake anali otuŵa, akuda, ndi okudzuka, m’maso mwa okonda Ziyoni ndi Mulungu wake, anaonekatu okongola kwabasi!
18 M’lingaliro laulosi, kugwa kwa Babulo kunatanthauza kuti ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa ndi kuti wonyamula uthenga wabwino ndiye anali wolengeza kugwa kwa Babulo. Ndiponso, mthenga wakale ameneyu, wonenedweratu kudzera mwa Yesaya, anachitira chithunzi mthenga wa uthenga wabwino kwambiri—tikuti kwambiri chifukwa cha zofunikazo zimene ukunena ndi kugogomezera kwake Ufumu, uthenga wokhala ndi matanthauzo ochititsa chidwi kwa anthu onse a chikhulupiriro.
19. Kodi ndi uthenga wotani wonena za dziko la Israyeli umene Yehova anapereka kudzera mwa Ezekieli?
19 Nayenso Ezekieli anapatsidwa maulosi ochititsa chidwi a kubwezeretsedwa. Analosera kuti: “Atero Ambuye Yehova, . . . ndidzakhalitsa anthu m’midzimo; ndi pamabwinja padzamangidwa. Ndipo adzati, Dziko ili lachipululu lasanduka ngati munda wa Edene.”—Ezekieli 36:33, 35.
20. Kodi ndi chilimbikitso chotani chachisangalalo chimene Yesaya anapereka mwaulosi kwa Yerusalemu?
20 Pamene anthu a Mulungu anali m’ndende ku Babulo, iwo anali kulira Ziyoni. (Salmo 137:1) Tsopano, anali pachikondwerero. Yesaya analimbikitsa kuti: “Kondwani zolimba, imbani pamodzi, inu malo abwinja a pa Yerusalemu; pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, waombola Yerusalemu. Yehova wavula mkono wake woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.”—Yesaya 52:9, 10.
21. Kodi mawu a Yesaya 52:9, 10 anakwaniritsidwa motani Babulo atagonjetsedwa?
21 Inde, anthu osankhidwa a Yehova anali ndi chifukwa chabwino kwambiri chokondwerera. Tsopano anali kupita kukakhalanso pamalowo amene anali abwinja nthaŵi ina, kuwapanga kukhala ngati munda wa Edene. Yehova ‘anawavulira mkono wake woyera.’ Anapinda malaya ake, kunena kwake titero, kuti agwire ntchito yowabwezera kumudzi wawo wokondedwa. Chimenechi sichinali chochitika chinachake chaching’ono chosadziŵika bwino. Ayi ndithu, anthu onse omwe anali ndi moyo nthaŵiyo anaona ‘mkono wovula’ wa Mulungu ukuchita mphamvu pazochitika za anthu kuti apulumutse mtundu wake modabwitsa. Iwo anapatsidwa umboni wotsimikizika wakuti Yesaya ndi Ezekieli anali amithenga oona a Yehova. Palibe amene anakayikira kuti Mulungu wa Ziyoni ndiye Mulungu yekha wamoyo ndi woona padziko lonse lapansi. Pa Yesaya 35:2 timaŵerenga kuti: “Anthuwo adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wake wa Mulungu wathu.” Awo amene analandira umboni umenewu wa Umulungu wa Yehova anayamba kumlambira.
22. (a) Kodi tiyenera kuthokoza za chiyani lerolino? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kumthokoza kwambiri Yehova kuti amavumbula amithenga onyenga?
22 Tiyenera kumthokoza chotani nanga Yehova kuti amadziŵikitsa amithenga ake oona! Ndiyedi ‘amene alimbitsa mawu a mtumiki wake, kuchita uphungu wa amithenga ake.’ (Yesaya 44:26) Maulosi a kubwezeretsa amene anapatsa Yesaya ndi Ezekieli amasonyeza bwino lomwe chikondi chake chachikulu, chisomo chake, ndi chifundo chake pa atumiki ake. Ndithudi, Yehova akuyenerera chitamando chathu chonse pa zimenezi! Ndipo ifeyo lerolino tiyenera kumthokoza kwambiri chifukwa chakuti amavumbula amithenga onyenga. Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti pali ambiri a iwo tsopano padziko lapansi. Mauthenga awo amwano anyalanyaza zifuno za Yehova zimene walengeza. Nkhani yotsatira idzatithandiza kudziŵa amithenga onyenga amenewo.
[Mawu a M’munsi]
a The Monuments and the Old Testament, yolembedwa ndi Ira Maurice Price, 1925.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi Yehova amawadziŵikitsa motani amithenga ake oona?
◻ Kudzera mwa Yesaya, kodi Yehova anati mtumiki wake wogonjetsera Babulo ndani?
◻ Kodi maulosi a Yesaya ofotokoza kugonjetsedwa kwa Babulo anakwaniritsidwa motani?
◻ Kodi kugonjetsedwa kwa Babulo kunali ndi zotulukapo zabwino zotani pa dzina la Yehova?
[Chithunzi patsamba 9]
Babulo ankaoneka ngati wosagonjetseka kwa mitundu ya m’nthaŵi ya Ezekieli