Padziko Lonse Padzakhala Mgwirizano
KODI munaonapo azimayi awiri akusinja mu mtondo umodzi moponyezana, kapena azibambo awiri akupalasa bwato, kapenanso azibambo angapo akupatsirana njerwa? Mmene amagwirira ntchitoyo zimasonyeza kuti pagona mgwirizano waukulu. Zikanakhala bwino kwambiri moyo masiku ano ukanati uzikhalanso choncho, wogwirizana ndiponso wopanda kuyambana ndi kuvutitsana kulikonse. M’malo mwake, anthu ndi “osayanjanitsika,” monga momwe Baibulo linaneneratu za nthawi yathu ino.—2 Timoteo 3:1-5.
Komabe, mu nthawi zovuta chonchizi, anthu ambirimbiri oona mtima akuphunzira kukhala pa mtendere weniweni ndiponso mogwirizana. Zikutheka bwanji? Chifukwa choti akumvera pempho lokhudza mtima limene linalembedwa m’Baibulo pa Yesaya 48:17, 18. Lemba limeneli limati: ‘Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.’
Tikamvera pempho lochokera pansi pa mtima limenelo, Yehova amakhala Mthandizi wathu. Amatisonyeza momwe “tingayendere” mwa mtendere weniweni ndiponso mogwirizana. Kuchita zosemphana ndi zimenezi potsatira nzeru ndi maganizo a anthu opanda ungwiro, n’kupusa. Mobwerezabwereza, zochitika za m’mbiri ya anthu zimatsimikizira kuti mawu olembedwa pa Yeremiya 10:23 ndi oonadi. Mawu amenewo amati: “Njira ya munthu sili mwa iye mwini. Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” M’mawu osavuta kumva, tingati sitingathe kudzilamulira tokha ndi kukhazikitsa malamulo anzeru a makhalidwe abwino omwe angasangalatsenso aliyense. Mulungu ndi amene ali ndi mphamvu yotha kuchita zimenezo.—Yesaya 33:22.
Mtendere ndi Mgwirizano Weniweni
Posachedwapa Mulungu abweretsa mgwirizano padziko pano. Analonjeza za nthawi imene ‘dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.’ (Yesaya 11:9) Zoonadi, padziko lapansi padzakhala mtendere weniweni mpaka kalekale.
Ndipotu, zinthu zamoyo padziko lapansi zizidzagwirizana m’njira yatsopano, chifukwa Mulungu adzaphunzitsa anthu ake okhulupirika momwe angasamalire bwino malo awo okhala padziko lapansi pano. Ndiponsotu, adzachita “pangano,” ndi nyama zonse zolusa, chifukwa adzaziphunzitsa kukhala mwamtendere ndiponso mogonjera anthu.—Hoseya 2:18; Genesis 1:26-28; Yesaya 11:6-8.
Chiyembekezo chimenechi si nkhambakamwa chabe. Ndipotu pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu anatchula za chiyembekezo chimenechi kawiri konse. Poyamba anati: ‘Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.’ Kenaka, pophunzitsa ophunzira ake kupemphera, iye anati: ‘Atate wathu . . . Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.’ (Mateyu 5:5; 6:9, 10) Pamapeto pa moyo wake, Yesu ananena m’mawu amodzi tanthauzo la zimenezi kwa anthu. Mawu ake anali akuti ‘paradaiso.’ (Luka 23:43) Zoonadi, mwazi umene Yesu anakhetsa unachititsa kuti zikhale zotheka kuti anthu adzakhale ndi moyo wosatha m’paradaiso pa dziko lapansi.—Yohane 3:16.
[Chithunzi patsamba 12]
M’Paradaiso wa Mulungu amene akubwera, zinthu zamoyo padziko lapansi zizidzagwirizana m’njira yatsopano