Nzeru Yaumulungu—Kodi Imaonetsedwa Motani?
“ANYOZA nzeru ya wosauka, osamvera mawu ake.” Ndi mawu ameneŵa, Mfumu yanzeru Solomo inamaliza nkhani ya wosauka koma wanzeru amene anapulumutsa mudzi wonse kuchiwonongeko. Komabe, n’zokhumudwitsa kuti, “panalibe anthu anakumbukira wosauka ameneyo.”—Mlaliki 9:14-16.
Anthu amaoneka kuti amadelera anthu osauka, ngakhale ngati osaukawo anachitapo zinthu zotchuka. Zimenezi zinali zoona pankhani ya Yesu. Yesaya analosera za iye kuti: “Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziŵa zowawa.” (Yesaya 53:3) Yesu ananyozedwa ndi ena chabe chifukwa chakuti analibe udindo kapena sanali wotchuka monga atsogoleri a m’tsiku lake. Komabe, anali ndi nzeru kwambiri kuposa munthu aliyense wochimwa. Anthu a kumudzi kwawo kwa Yesu anakana kuti “mwana wa mmisiri wa mitengo” ameneyu angaonetse nzeru yoteroyo ndi kuchita ntchito zamphamvu zoterozo. Komabe, kumeneko kunali kulakwa kwabasi, popeza nkhaniyo imapitiriza kunena kuti “chifukwa cha kusakhulupirira kwawo, [Yesu] sanachita kumeneko zamphamvu zambiri.” Kwa anthu amenewo kunali kutayikiridwa bwanji!—Mateyu 13:54-58.
Tisalakwitsetu chimodzimodzi. “Nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake,” anatero Yesu. Amene akuchita ntchito ya Mulungu ndi kugaŵira nzeru ya kumwamba amadziŵika, osati ndi udindo wawo kapena makhalidwe awo, koma ndi “zipatso zokoma” zimene amaonetsa—chikhulupiriro chawo chochokera m’Baibulo ndi zochita zawo.—Mateyu 7:18-20; 11:19.