Anachita Chifuniro cha Yehova
Filipo Abatiza Mdindo wa ku Aitiopiya
PAMENE anali kuyenda m’galeta lake, Mwaitiopiya anali kugwiritsira ntchito nthaŵi yake mwanzeru. Anali kuŵerenga momveka—chizoloŵezi chofala pakati pa apaulendo a m’zaka za zana loyamba. Mwamuna ameneyu kwenikweni anali “mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aaitiopiya.”a Anali “wakusunga chuma chake chonse”—kwenikweni, anali nduna yoona zachuma. Mdindoyu anali kuŵerenga Mawu a Mulungu kuti apeze chidziŵitso.—Machitidwe 8:27, 28.
Pafupi ndi pamenepo panali Filipo. Mngelo anali atamtsogolera ku malowa, ndipo tsopano anauzidwa kuti: “Yandikira, nudziphatike ku gareta uyu.” (Machitidwe 8:26, 29) Tingayerekezere Filipo akudzifunsa kuti, ‘Kodi mwamunayu ndani? Kodi akuŵerenganji? Kodi nchifukwa ninji anditsogolera kwa iye?’
Pamene Filipo anali kuthamanga pafupi ndi galetalo, anamva Mwaitiopiyayo akuŵerenga momveka mawu awa: “Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa, ndi monga mwana wa nkhosa ali du pamaso pa womsenga, kotero sanatsegula pakamwa pake: m’kuchepetsedwa kwake chiweruzo chake chinachotsedwa; mbadwo wake adzaubukitsa ndani? Chifukwa wachotsedwa kudziko moyo wake.”—Machitidwe 8:32, 33.
Pomwepo Filipo anaidziŵa ndimeyo. Inatengedwa m’cholembedwa cha Yesaya. (Yesaya 53:7, 8) Mwaitiopiyayo sanadziŵe zimene anali kuŵerenga. Filipo anayambitsa makambitsirano mwa kufunsa kuti: “Kodi muzindikira chimene muŵerenga?” Mwaitiopiyayo anayankha kuti: “Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine?” Ndiyeno anapempha Filipo kukwera naye m’galeta lake.—Machitidwe 8:30, 31.
“Chindiletsa Ine Chiyani Ndisabatizidwe?”
“Ndikupempha,” Mwaitiopiya anatero kwa Filipo, “mneneri anena ichi za yani? Za yekha, kapena za wina?” (Machitidwe 8:34) Kusokonezeka kwa Mwaitiopiya sikunali kodabwitsa, popeza “nkhosa,” kapena “mtumiki” wa muulosi wa Yesaya anali chinsinsi kwa nthaŵi yaitali. (Yesaya 53:11) Zinali zomveka kwambiri motani nanga pamene Filipo analengeza kwa Mwaitiopiyayo “[uthenga wabwino wa, NW] Yesu”! Pambuyo pake Mwaitiopiya anati: “Taonapo madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?” Chotero Filipo anambatiza nthaŵi yomweyo.—Machitidwe 8:35-38.
Kodi anafulumira kuchita zimenezi? Kutalitali! Mwaitiopiyayo anali wotembenukira ku Chiyuda.b Chotero anali kale mlambiri wa Yehova wokhala ndi chidziŵitso cha Malemba, kuphatikizapo maulosi onena za Mesiya. Komabe, chidziŵitso chake sichinali chokwanira. Tsopano atalandira chidziŵitso chofunika kwambiri ponena za ntchito ya Yesu Kristu, Mwaitiopiyayo anamvetsa zimene Mulungu anafuna kwa iye ndipo anali wokonzeka kuchita mogwirizana nazo. Ubatizo unali woyenera.—Mateyu 28:18-20; 1 Petro 3:21.
Pambuyo pake, ‘[mzimu wa Yehova, NW] unakwatula Filipo.’ Iye anapita ku gawo lina. Mwaitiopiyayo “anapita njira yake wokondwera.”—Machitidwe 8:39, 40.
Phunziro kwa Ife
Monga atumiki amakono a Yehova, tili ndi thayo la kuthandiza anthu oona mtima kuphunzira choonadi cha Mawu a Mulungu. Ambiri akhala achipambano pa kupereka uthenga wabwino kwa ena pamene ali paulendo kapena m’mikhalidwe ina yamwamwaŵi. Chifukwa cha ntchito ya kulalikira Ufumu, chaka chilichonse zikwi mazana ambiri amasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova Mulungu mwa kubatizidwa.
Zoona, achatsopano sayenera kufulumira kubatizidwa. Choyamba ayenera kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Yehova Mulungu ndi cha Mwana wake, Yesu Kristu. (Yohane 17:3) Ndiyeno ayenera kulapa, kusiya khalidwe loipa ndi kutembenuka kuti agwirizane ndi miyezo ya Mulungu. (Machitidwe 3:19) Zimenezi zimatenga nthaŵi makamaka ngati malingaliro olakwika ndi khalidwe loipa zinazika mizu. Pamene kuli kwakuti achatsopano ayenera kuŵerengera mtengo wa kukhala wophunzira wachikristu, kuloŵa muunansi wodzipatulira ndi Yehova Mulungu kumakhala ndi madalitso aakulu. (Yerekezerani ndi Luka 9:23; 14:25-33.) Awo amene ali Mboni za Yehova amatsogolera mwachangu achatsopano otero ku gulu limene Mulungu akugwiritsira ntchito kukwaniritsa chifuniro chake. (Mateyu 24:25-47) Monga Mwaitiopiya, ameneŵa adzasangalala kuphunzira za zimene Mulungu amafuna kwa iwo ndi kugwirizana nazo.
[Mawu a M’munsi]
a “Kandake” si dzina la munthu koma ndi dzina laulemu (lofanana ndi “Farao” ndi “Kaisara”) limene ankaligwiritsira ntchito kwa mfumukazi za Aaitiopiya.
b Otembenukira ku Chiyuda anali anthu osakhala Aisrayeli amene anasankha kutsatira Chilamulo cha Mose.—Levitiko 24:22.