Akristu Amapeza Chimwemwe Potumikira
“Kupatsa kumadzetsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” —MACHITIDWE 20:35, NW.
1. Ndi malingaliro olakwika otani amene afala lerolino, ndipo n’chifukwa chiyani ali oopsa?
M’ZAKA zakumapeto kwa ma 1900, anthu ochuluka anasonyeza kuti amafuna kukhala patsogolo pa wina aliyense. Kwenikweni, zimenezi zimasonyeza malingaliro a dyera ndi umbombo ophatikana ndi kusaganizira ena. Sitingakayike m’pang’ono pomwe kuti m’chaka cha 2000, malingaliro amenewo akupitirirabe. Ndi kangati pamene mumamva anthu akufunsa kuti, “Ndipezapo chiyani?” kapena, “Ndipindulapo chiyani?” Mtima wongosamala za iwe mwini umenewu subala chimwemwe. Ndi wosiyana kwambiri ndi mfundo yamakhalidwe imene Yesu anainena kuti: “Kupatsa kumadzetsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”—Machitidwe 20:35, NW.
2. Titha kuonera chiyani kuti kupatsa kumadzetsa chimwemwe?
2 Kodi n’zoona kuti kupatsa kumadzetsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira? Inde. Lingalirani za Yehova Mulungu. Iye ndiye mwini “chitsime cha moyo.” (Salmo 36:9) Amatipatsa zonse zomwe tifunikira kuti tikhale ndi moyo wosangalatsa ndi watanthauzo. Ndithudi, iye ndiye Gwero la “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro.” (Yakobo 1:17) Yehova, “Mulungu wachimwemwe,” amakhala akupatsa nthaŵi zonse. (1 Timoteo 1:11, NW) Amakonda anthu ake amene anawalenga, amene amawapatsa zochuluka. (Yohane 3:16) Lingaliraninso za banja la anthu. Ngati ndinu kholo, mukudziŵa kudzimana komanso kupatsa kumene kumafunikira polera mwana. Ndipo kwa zaka zambiri mwanayo sadziŵa n’komwe kuti m’madzimana. Saonapo vuto lililonse. Komabe, zimakupatsani chimwemwe kuona mwana wanu akukula bwino chifukwa cha kupatsa kwanu kosaumira. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mumam’konda.
3. N’chifukwa chiyani kutumikira Yehova ndi okhulupirira anzathu kuli kosangalatsa kwambiri?
3 Mofananamo, kulambira koona kumaonekera mwa kupatsa kozikidwa pa chikondi. Popeza kuti timakonda Yehova ndipo timakondanso okhulupirira anzathu, timasangalala kuwatumikira, kudzipereka ife eni kwa iwo. (Mateyu 22:37-39) Anthu amene amalambira ndi zolinga zadyera sapeza chimwemwe chilichonse. Koma amene amatumikira mosadzikonda, amene nkhaŵa yawo yaikulu ndiyo kupereka ndipo osati zimene akuyembekeza kulandira, amapezadi chimwemwe. Choonadi chimenechi tikuchiona mwa kupenda mmene mawu ena a m’Baibulo okhudzana ndi kulambira kwathu amagwiritsidwira ntchito m’Malemba. M’nkhani ino ndi yotsatira yake tidzakambirana atatu mwa mawu ameneŵa.
Utumiki wa Yesu Wothandiza Anthu
4. Kodi “utumiki wapoyera” ndi wotani m’Matchalitchi Achikristu?
4 M’Chigiriki choyambirira, liwu limodzi lalikulu lokhudzana ndi kulambira ndilo lei·tour·giʹa, lomwe latembenuzidwa kuti “utumiki wothandiza anthu” m’Baibulo la New World Translation. M’Matchalitchi Achikristu liwulo lei·tour·giʹa latembenuzidwa kukhala “mapemphero.”a Komabe, mwambo wa mapemphero a m’Matchalitchi Achikristu si utumiki wothandiza anthu moonadi.
5, 6. (a) Ndi utumiki wothandiza anthu wotani womwe unkachitika mu Israyeli, ndipo panali mapindu otani? (b) Ndi utumiki wothandiza anthu waukulu kwambiri uti womwe unaloŵa m’malo uja wochitika mu Israyeli, ndipo chifukwa chiyani?
5 Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito mawu ofanana ndi lei·tour·giʹa ponena za ansembe a mu Israyeli. Iye anati: “Wansembe aliyense amaima tsiku ndi tsiku, natumikira [“nachita utumiki wothandiza anthu,” NW] [mawu ofanana ndi lei·tour·giʹa], napereka nsembe zomwezi kaŵirikaŵiri.” (Ahebri 10:11) Alevi ansembe ankachita utumiki wothandiza anthu wofunika kwambiri mu Israyeli. Ankaphunzitsa Chilamulo cha Mulungu ndi kupereka nsembe zomwe zinaphimba machimo a anthu. (2 Mbiri 15:3; Malaki 2:7) Pamene ansembe ndi anthu onse anatsatira Chilamulo cha Yehova, mtunduwo unalidi ndi zifukwa zokhalira wosangalala.—Deuteronomo 16:15.
6 Kuchita utumiki wothandiza anthu motsogozedwa ndi Chilamulo unali mwayi waukulu zedi kwa ansembe a mu Israyeli, koma utumiki wawo unatha ntchito pamene Israyeli anakanidwa chifukwa cha kusakhulupirika. (Mateyu 21:43) Yehova anapanga makonzedwe ena aakulu kwambiri—utumiki wothandiza anthu wochitidwa ndi Yesu, Mkulu wa Ansembe woposa onse. Ponena za ameneyo, timaŵerenga kuti: “Iye chifukwa kuti akhala Iye nthaŵi yosatha ali nawo unsembe wosasinthika, kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nawo moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.”—Ahebri 7:24, 25.
7. N’chifukwa chiyani utumiki wothandiza anthu wa Yesu umadzetsa mapindu osayerekezeka?
7 Yesu adzapitiriza unsembe wake kwamuyaya, popanda kuloŵedwa m’malo ndi wina. Motero, ndi yekhayo amene angapulumutse anthu kotheratu. Utumiki wake wopambana umenewu wothandiza anthu sakuuchitira m’kachisi womangidwa ndi anthu ayi, koma m’kachisi wophiphiritsa, makonzedwe aakulu a Yehova a kulambira omwe anayambika m’chaka cha 29 C.E. Panopo Yesu akutumikira m’Malo Opatulikitsa a kachisi ameneyo, kumwamba. Iye ndi “mtumiki [wothandiza anthu, NW] [lei·tour·gosʹ] wa malo opatulika, ndi wa chihema choona, chimene Ambuye anachimanga, si munthu ayi.” (Ahebri 8:2; 9:11, 12) Ngakhale kuti Yesu ali paudindo wapamwamba chonchi, iye ndi “mtumiki wothandiza anthu.” Ulamuliro wake waukulowo amaugwiritsa ntchito popatsa, osati kutenga. Ndipo kupatsa kotero kumam’patsa chimwemwe. Ndi mbali ya “chimwemwe choikidwacho pamaso pake” imenenso inam’limbikitsa kupirira panthaŵi yonse yomwe anali padziko lapansi.—Ahebri 12:2.
8. Kuti pangano la Chilamulo liloŵedwe m’malo ndi lina, kodi Yesu anachitapo utumiki wotani wothandiza anthu?
8 Utumiki wa Yesu wothandiza anthu ulinso ndi mbali ina. Paulo analemba kuti: “Iye [Yesu] walandira chitumikiro chomveka choposa [“utumiki wothandiza anthu wabwino koposa,” NW], umonso ali Nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano oposa.” (Ahebri 8:6) Mose anali nkhoswe ya pangano lomwe linali maziko a unansi wa Israyeli ndi Yehova. (Eksodo 19:4, 5) Yesu anali nkhoswe ya pangano latsopano, lomwe linachititsa kubadwa kwa mtundu watsopano, “Israyeli wa Mulungu,” wopangidwa ndi Akristu odzozedwa ndi mzimu ochokera m’mitundu yambiri. (Agalatiya 6:16; Ahebri 8:8, 13; Chivumbulutso 5:9, 10) Ndi utumiki wothandiza anthu wabwino koposa umenewo! Ndife osangalala kwambiri kum’dziŵa Yesu, mtumiki wothandiza anthu mwa amene tingalambirire Yehova movomerezeka!—Yohane 14:6.
Akristu Nawonso Amachita Utumiki Wothandiza Anthu
9, 10. Kodi Akristu amachita mitundu inanso iti ya utumiki wothandiza anthu?
9 Palibe munthu amene amachita utumiki wothandiza anthu wokwezeka wofanana ndi wa Yesu. Komabe, Akristu odzozedwa akalandira mphoto yawo ya kumwamba amakakhala pamalo awo pambali pa Yesu ndi kuchita naye utumiki wothandiza anthu monga mafumu ndi ansembe akumwamba. (Chivumbulutso 20:6; 22:1-5) Komanso, Akristu padziko lapansi amachitabe utumiki wothandiza anthu, ndipo amapeza chimwemwe chochuluka pochita zimenezo. Mwachitsanzo, pamene kunali njala ku Palestina, mtumwi Paulo ananyamula zopereka za abale a ku Ulaya kuti akathandize Akristu achiyuda ku Yudeya pamavuto awo. Umenewo unali utumiki wothandiza anthu. (Aroma 15:27; 2 Akorinto 9:12) Lerolino, Akristu amasangalala kuchita utumiki wofananawo, kupereka thandizo msangamsanga abale awo akagwidwa ndi umphaŵi, masoka achilengedwe akawagwera, kapena akakumana ndi mavuto ena.—Miyambo 14:21.
10 Paulo anatchulanso utumiki wina wothandiza anthu pamene analemba kuti: “Ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira [anthu, NW] kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse.” (Afilipi 2:17) Kugwira ntchito kwa Paulo molimbika pofuna kuthandiza Afilipi unali utumiki wothandiza ena wochitidwa mwachikondi ndi mwakhama. Utumiki wothandiza anthu wofananawo ukuchitidwa lerolino, makamaka ndi Akristu odzozedwa, amene akutumikira monga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” popereka chakudya chauzimu panthaŵi yake. (Mateyu 24:45-47) Komanso, monga gulu, ameneŵa ndiwo “ansembe oyera mtima,” omwe apatsidwa ntchito yokhala monga “akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Kristu” ndi ‘kulalikira zoposazo za Iye amene anawaitana atuluke mumdima, aloŵe kuunika kwake kodabwitsa.’ (1 Petro 2:5, 9) Mofanana ndi Paulo, iwo amasangalala ndi mwayi umenewu pamene adzipereka ndi mtima wonse pokwaniritsa maudindo awo. Ndiponso anzawo a “nkhosa zina” akugwirizana nawo ndi kuwachirikiza pantchito youza anthu za Yehova ndi zifuno zake.b (Yohane 10:16; Mateyu 24:14) Umenewotu ndi utumiki waukulu ndi wosangalatsa zedi wothandiza anthu!—Salmo 107:21, 22.
Chitani Utumiki Wopatulika
11. Kodi mneneri wamkazi Anna anapereka motani chitsanzo chabwino kwa Akristu onse?
11 Mawu enanso achigiriki okhudza kulambira kwathu ndiwo la·treiʹa, otembenuzidwa kuti “utumiki wopatulika” m’Baibulo la New World Translation. Utumiki wopatulika n’ngwokhudzana ndi zochita za munthu zosonyeza kulambira. Mwachitsanzo, Anna, mkazi wamasiye komanso mneneri wazaka 84 zakubadwa akunenedwa kuti “sanali kusoŵa pakachisi, kuchita utumiki wopatulika [mawu achigiriki ofanana ndi la·treiʹa] usana ndi usiku ndi kusala kudya ndi mapembedzero.” (Luka 2:36, 37, NW) Anna analambira Yehova mosaleka. N’chitsanzo chabwino kwambiri kwa tonsefe—achinyamata ndi achikulire, amuna ndi akazi. Monga momwe Anna anali kupemphera kwa Yehova ndi mtima wonse ndi kum’lambira pakachisi, utumiki wathu wopatulika umaphatikizapo kupemphera ndi kusonkhana.—Aroma 12:12; Ahebri 10:24, 25.
12. Kodi mbali yaikulu ya utumiki wathu wopatulika ndi iti, ndipo ikhalanso motani utumiki wothandiza anthu?
12 Mtumwi Paulo anatchulapo mbali yaikulu ya utumiki wathu wopatulika pamene analemba kuti: “Mulungu ali mboni yanga, amene ndim’tumikira [“ndim’chitira utumiki wopatulika,” NW] mu mzimu wanga, m’uthenga wabwino wa Mwana wake, kuti kosalekeza ndikumbukira inu, ndi kupempha masiku onse m’mapemphero anga.” (Aroma 1:9) Inde, kulalikira uthenga wabwino si utumiki wothandiza ena basi kwa amene aumvetsera komanso ndi chinthu chosonyeza kuti tikulambira Yehova Mulungu. Kaya tipeze khutu lomvetsera kapena ayi, ntchito yolalikira ndi utumiki wopatulika wochitidwira Yehova. Chikhumbo chathu chofunitsitsa kuuza ena za mikhalidwe yabwino ya Atate wathu wokondedwa wa kumwamba pamodzi ndi zifuno zake zabwino zimatipatsa chimwemwe chodzaza tsaya.—Salmo 71:23.
Kodi Utumiki Wopatulika Timauchitira Kuti?
13. Kodi awo amene akuchita utumiki wopatulika m’bwalo lam’kati la kachisi wauzimu wa Yehova ali ndi chiyembekezo chotani, ndipo ndani akusangalala nawo?
13 Paulo analembera Akristu odzozedwa kuti: “Polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho [“tikachitire nacho utumiki wopatulika kwa,” NW] Mulungu mom’kondweretsa, ndi kum’chitira ulemu ndi mantha.” (Ahebri 12:28) Mwachidaliro chonse chodzaloŵa Ufumu, odzozedwa sakusunthika pachikhulupiriro chawo polambira Wam’mwambamwamba. Ndi okhawo amene akum’chitira utumiki wopatulika m’chipinda Chopatulika ndi m’bwalo lam’kati la kachisi wauzimu wa Yehova, ndipo akuyembekezera mwachidwi kukatumikira pamodzi ndi Yesu m’Malo Opatulikitsa, kumwamba kwenikweniko. Anzawo, gulu la nkhosa zina, akusangalala nawo pachiyembekezo chawo chodabwitsacho.—Ahebri 6:19, 20; 10:19-22.
14. Kodi khamu lalikulu limapindula motani ndi utumiki wa Yesu wothandiza anthu?
14 Nangano bwanji za a nkhosa zina? Monga momwe mtumwi Yohane anaoneratu, khamu lawo lalikulu laonekera m’masiku ano otsiriza, ndipo “anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 7:14) Zimenezi zikutanthauza kuti, mofanana ndi olambira anzawo odzozedwa, iwonso amasonyeza chikhulupiriro mu utumiki wothandiza anthu wa Yesu, kupereka kwake moyo wake wangwiro waumunthu kaamba ka mtundu wa anthu. A nkhosa zina akupindulanso ndi utumiki wothandiza anthu wa Yesu chifukwa chakuti ‘akugwira zolimba chipangano [cha Yehova].’ (Yesaya 56:6) Iwo sali nawo m’pangano latsopano, koma akuligwira zolimba mwa kumvera malamulo okhudzana nalo ndipo amagwirizana ndi makonzedwe opangidwa kudzera m’panganolo. Amagwirizana ndi Israyeli wa Mulungu, kudyera pathebulo limodzi lauzimu ndi kugwira ntchito limodzi ndi anthu opanga Israyeli wa Mulungu, kutamanda Mulungu poyera ndi kupereka nsembe zauzimu zom’kondweretsa.—Ahebri 13:15.
15. Kodi khamu lalikulu likuchitira kuti utumiki wopatulika, ndipo amamva bwanji ndi dalitso limenelo?
15 Chotero, a khamu lalikulu akuonedwa kuti “akuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera.” Komanso, “ali ku mpando wachifumu wa Mulungu; ndipo am’tumikira Iye [“akum’chitira utumiki wopatulika,” NW] usana ndi usiku m’Kachisi mwake; ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu adzawachitira mthunzi.” (Chivumbulutso 7:9, 15) Mu Israyeli, munthu wotembenukira ku Chiyuda anali kulambira m’bwalo lakunja la kachisi wa Solomo. Mofananamo, khamu lalikulu likulambira Yehova m’bwalo lakunja la kachisi wake wauzimu. Kutumikira m’bwalo limenelo kumawasangalatsa. (Salmo 122:1) Ngakhale pamene womaliza wa anzawo odzozedwawo adzalandira choloŵa chake chakumwamba, iwo adzapitirizabe kuchita utumiki wopatulika kwa Yehova monga anthu ake.—Chivumbulutso 21:3.
Utumiki Wopatulika Wosavomerezeka
16. Kodi pali machenjezo otani ponena za utumiki wopatulika?
16 M’masiku a Israyeli wakale, utumiki wopatulika unayenera kuchitidwa mogwirizana ndi malamulo a Yehova. (Eksodo 30:9; Levitiko 10:1, 2) Mofananamo lerolino, pali zofunikira zina zoyenera kutsatira kuti Yehova avomereze utumiki wathu wopatulika. Ndiye chifukwa chake Paulo analembera Akolose kuti: “Ifenso . . . sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso [“chidziŵitso cholondola,” NW] cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziŵitso cha mzimu, kuti mukayende koyenera Ambuye kukam’kondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m’chizindikiritso [“m’chidziŵitso cholondola,” NW] cha Mulungu.” (Akolose 1:9, 10) Si kwa ife kulamula njira yoyenera yolambirira Mulungu. Chidziŵitso cholondola cha Malemba, chidziŵitso chauzimu, ndi nzeru yaumulungu n’zofunika kwambiri. Apo ayi, zinthu zingalakwike kwabasi.
17. (a) Kodi anthu anaulakwitsa motani utumiki wopatulika m’masiku a Mose? (b) Kodi utumiki wopatulika lerolino ungalakwitsidwe motani?
17 Kumbukirani Aisrayeli m’masiku a Mose. Timaŵerenga kuti: “Mulungu anatembenuka, nawapereka iwo atumikire [“achitire utumiki wopatulika,” NW] gulu la kumwamba.” (Machitidwe 7:42) Aisrayeli amenewo anaona ntchito zamphamvu zimene Yehova anawachitira. Koma iwo anayang’ana kwa milungu ina poganiza kuti iwathandiza. Sanali okhulupirika, ndipo kukhulupirika n’kofunika kwambiri ngati tikufuna kuti utumiki wathu wopatulika um’sangalatse Mulungu. (Salmo 18:25) Zoonadi, lerolino ndi ochepa amene angasiye Yehova n’kumalambira nyenyezi kapena ana a ng’ombe a golide, koma pali njira zina zolambirira mafano. Yesu anachenjeza za kulambira “Chuma,” ndipo Paulo anati kusirira n’kulambira mafano. (Mateyu 6:24; Akolose 3:5) Satana amadzikweza kukhala mulungu. (2 Akorinto 4:4) Kulambira mafano kotereku kuli paliponse ndipo ndi msampha. Mwachitsanzo, talingalirani za munthu amene amati akutsatira Yesu koma amene cholinga chake kwenikweni m’moyo ndicho kulemera kapena amene chidaliro chake chenicheni chili mwa iye mwini ndi malingaliro ake. Kodi iye akutumikira ndani kwenikweni? Kodi wasiyana pati ndi Ayuda a m’tsiku la Yesaya amene analumbira m’dzina la Yehova koma anatamanda mafano onyansa pa zochita za Yehova zazikulu?—Yesaya 48:1, 5.
18. Kodi utumiki wopatulika wapotozedwa motani kalelo ndi lerolino?
18 Yesu anachenjezanso kuti: “Ikudza nthaŵi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu [“wachitira Mulungu utumiki wopatulika,” NW].” (Yohane 16:2) Saulo, amene anadzakhala mtumwi Paulo, mosakayikira anayesa kuti akutumikira Mulungu pamene ‘anavomerezana nawo pa imfa ya Stefano’ ndi “kupumira pa akuphunzira a Ambuye kuopsa ndi kupha.” (Machitidwe 8:1; 9:1) Lerolino, ena amene amachirikiza nkhondo zoyeretsa fuko ndi zopululutsa anthu amanenanso kuti akulambira Mulungu. Alipo anthu ochuluka amene amati akulambira Mulungu, pamene zenizeni zake n’zakuti amalambira milungu ya ufuko, utundu, chuma, kudzikonda, kapena mulungu winawake.
19. (a) Kodi utumiki wathu wopatulika timauona motani? (b) Ndi utumiki wopatulika wotani umene udzatidzetsera chimwemwe?
19 Yesu anati: “Ambuye Mulungu wako udzam’gwadira, ndipo iye yekha yekha udzam’lambira.” (Mateyu 4:10) Iye anali kulankhula ndi Satana, koma n’kofunikatu kwambiri kuti tonsefe tilabadire mawu ake! Kuchitira Ambuye Mfumu ya chilengedwe chonse utumiki wopatulika ndi mwayi wapamwamba kwambiri komanso wopangitsa munthu kunthunthumira. Ndipo tingatchulepo chiyani ponena za kuchita kwathu utumiki wothandiza anthu wogwirizana ndi kulambira kwathu? Kuchitira munthu mnzathu zimenezi kumadzetsa chimwemwe chachikulu. (Salmo 41:1, 2; 59:16) Ngakhale zili motero, utumiki woterewu umadzetsa chimwemwe kokha ngati ukuchitidwa ndi mtima wonse ndiponso m’njira yoyenera. Kodi ndani kwenikweni akulambira Mulungu molondola? Ndi utumiki wopatulika wa yani umene Yehova amavomereza? Tingayankhe mafunso ameneŵa ngati tikambirana liwu lachitatu la m’Baibulo lokhudzana ndi kulambira kwathu. Tidzachita zimenezi m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Mwambo wochitika pamapemphero a Matchalitchi Achikristu nthaŵi zambiri umakhala kaya kulambira kapena mwambo winawake, monga kudya Kalistiya m’Tchalitchi cha Roma Katolika.
b Pa Machitidwe 13:2, pakusimba kuti aneneri ndi aphunzitsi ku Antiokeya anali “kutumikira” Yehova [“kuchita utumiki wothandiza anthu kwa Yehova,” NW] (kutembenuza mawu achigiriki ofanana ndi lei·tour·giʹa). Utumiki wothandiza anthu umenewu uyenera kuti unaphatikizapo kulalikira kwa anthu.
Kodi Mungayankhe Motani?
• Ndi utumiki wothandiza anthu waukulu uti umene Yesu anachita?
• Kodi Akristu amachita utumiki wotani wothandiza anthu?
• Kodi utumiki wopatulika wachikristu n’chiyani, ndipo amauchitira kuti?
• Kodi tiyenera kukhala ndi chiyani ngati tikufuna kuti Mulungu akondwere ndi utumiki wathu wopatulika?
[Chithunzi patsamba 10]
Makolo amapeza chimwemwe chochuluka popatsa
[Zithunzi pamasamba 12, 13]
Akristu amachita utumiki wothandiza anthu pamene athandiza ena komanso pamene afalitsa uthenga wabwino
[Chithunzi patsamba 14]
Tiyenera kukhala ndi chidziŵitso cholondola ndi kumvetsa kuti tikhale otsimikizira kuti utumiki wathu wopatulika n’ngwovomerezeka kwa Mulungu