-
Yehova Amakometsera Anthu Ake ndi KuunikaNsanja ya Olonda—2002 | July 1
-
-
4, 5. (a) Kodi Yehova akulamula mkazi kuchita chiyani, ndipo akum’lonjeza chiyani? (b) Kodi ndi uthenga wosangalatsa uti umene uli mu Yesaya chaputala 60?
4 Mawu oyamba a Yesaya chaputala 60 akumuuza mkazi amene akumvetsa chisoni kwambiri. Iye wagona pansi mumdima. Mwadzidzidzi, pamdimapo pakuwala, ndipo Yehova akuitana kuti: “Nyamuka, [mkazi iwe, NW] wala, pakuti kuunika kwako kwafika, ndi ulemerero wa Yehova wakutulukira.” (Yesaya 60:1) Nthaŵi yakwana yoti mkaziyu aimirire ndi kusonyeza kuunika kwa Mulungu, ulemerero Wake. Chifukwa chiyani? Yankho tikulipeza m’vesi lotsatira limene likuti: “Taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu; koma Yehova adzakutulukira, ndi ulemerero wake udzaoneka pa iwe.” (Yesaya 60:2) Mkaziyu akumutsimikizira kuti akamvera lamulo la Yehova, zotsatira zake zidzakhala zabwino. Yehova akuti: “Amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kutuluka kwako.”—Yesaya 60:3.
5 Mawu osangalatsa a m’mavesi atatu ameneŵa ndiwo mawu otsegulira Yesaya chaputala 60 komanso akutipatsa chithunzithunzi cha zimene zili m’chaputala chonsecho. Akulosera zimene zidzachitikire mkazi waulosi ndiponso akufotokoza mmene tingakhalire mu kuunika kwa Yehova ngakhale kuti anthu ali mumdima. Koma kodi mawu ophiphiritsa amene ali m’mavesi atatu ameneŵa akutanthauzanji?
6. Kodi mkazi amene amutchula pa Yesaya chaputala 60 ndani, ndipo ndani akuimira mkazi ameneyo padziko lapansi?
6 Mkazi amene amutchula pa Yesaya 60:1-3 ndi Ziyoni, gulu la kumwamba la Yehova la zolengedwa zauzimu. Lerolino Ziyoni akuimiridwa pa dziko lapansi ndi otsalira a “Israyeli wa Mulungu,” gulu lapadziko lonse la Akristu odzozedwa ndi mzimu, omwe ali ndi chiyembekezo chokalamulira ndi Kristu kumwamba. (Agalatiya 6:16) Mtundu wauzimu umenewu uli ndi anthu 144,000, ndipo kukwaniritsidwa kwamakono kwa Yesaya chaputala 60 kwagona pa amene ali ndi moyo padziko lapansi mu “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1; Chivumbulutso 14:1) Ulosiwu ukunenanso zambiri za anzawo a Akristu odzozedwawa, “khamu lalikulu” la “nkhosa zina.”—Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16.
-
-
Yehova Amakometsera Anthu Ake ndi KuunikaNsanja ya Olonda—2002 | July 1
-
-
8. Kodi zinthu zinasintha kwambiri motani mu 1919, ndipo n’chiyani chinachitika chifukwa cha kusinthaku?
8 Komabe, zinthu zinasintha kwambiri m’chaka cha 1919. Yehova anawalitsa kuunika pa Ziyoni. Opulumuka a Israyeli wa Mulungu anadzuka kuti awalitse kuunika kwa Mulungu, kuyambanso kulengeza uthenga wabwino mopanda mantha. (Mateyu 5:14-16) Chifukwa chakuti Akristu ameneŵa anakhalanso achangu, anakokera ena ku kuunika kwa Yehova. Oyamba mwa anthu atsopanoŵa anali odzozedwa, omwe analoŵa m’gulu la Israyeli wa Mulungu. Pa Yesaya 60:3 akuwatcha mafumu chifukwa chakuti adzalamulira limodzi ndi Kristu mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu. (Chivumbulutso 20:6) Kenako, khamu lalikulu la nkhosa zina anayamba kulibweretsa m’kuunika kwa Yehova. Ameneŵa ndiwo “amitundu” amene awatchula mu ulosiwu.
-