Kupita Patsogolo Kukagonjetsa Komaliza!
“Taonani, kavalo woyera, ndipo wom’kwerayo anali nawo uta; ndipo anam’patsa korona; ndipo anatulukira wolakika kuti alakike.”—CHIVUMBULUTSO 6:2.
1. Kodi n’zochitika zam’tsogolo ziti zomwe Yohane anaona m’masomphenya?
MOUZIRIDWA ndi Mulungu, mtumwi Yohane anatha kuona za m’tsogolo zaka 1,800 ndi kufotokoza za kukhala pampando kwa Kristu monga Mfumu. Yohane anafunika chikhulupiriro kuti atsimikize kuti masomphenya omwe anaonawo adzakwaniritsidwa. Ife lerolino tili ndi umboni wogwira mtima wosonyeza kuti kukhala pampando wachifumu koloseredwako kunachitika m’chaka cha 1914. Ndi maso achikhulupiriro, tikuona Yesu Kristu ‘akutulukira wolakika kuti alakike.’
2. Kodi Mdyerekezi anachitanji Ufumu utakhazikitsidwa, nanga zimenezi ndi umboni wa chiyani?
2 Ufumuwo utakhazikitsidwa, Satana anachotsedwa kumwamba. Izi zinam’chititsa kumenya nkhondo molimbika ndi mochititsa mantha kwambiri koma popanda chilichonse chosonyeza kuti adzapambana. (Chivumbulutso 12:7-12) Mkwiyo wakewo wachititsa zinthu kuipiraipira padziko lapansi. Mgwirizano wa anthu ukuoneka kuti wasokonezekeratu. Kwa Mboni za Yehova, umenewu ndi umboni woonekeratu wakuti Mfumu yawo ikupita patsogolo kukatsiriza kugonjetsa.
Kupanga Gulu Lokhala M’dziko Latsopano Kuli M’kati
3, 4. (a) Ndi kusintha kotani kwa gulu komwe kwachitika mumpingo wachikristu kuchokera pamene Ufumu unakhazikitsidwa, nanga n’chifukwa chiyani kunali kuyenera? (b) Kodi kusintha kumeneku kwadzetsa phindu lotani, monga momwe Yesaya analoserera?
3 Atatsiriza kukhazikitsa Ufumuwo, nthaŵi inakwana yoti mpingo wachikristu wobwezeretsedwa, umene tsopano unali ndi maudindo owonjezeka autumiki mu Ufumuwo—augwirizanitse kwambiri m’zochitika zake ndi mpingo wachikristu wa m’zaka za zana loyamba. Pa chifukwa chimenechi, makope achingelezi a Nsanja ya Olonda a June 1 ndi 15, 1938, anafotokoza mwatsatanetsatane mmene gulu lachikristu liyenera kuyendera. Kenako, kope lachicheŵa la May 15, 1972, linapitiriza kufotokoza momveka bwino za Bungwe Lolamulira lamakono m’nkhani yakuti “Bungwe Lolamulira Monga Losiyana ndi Gulu Lalamulo.” M’chaka cha 1972, mabungwe a akulu anaikidwa kuti azithandiza ndi kutsogolera mipingo yawo.
4 Kukhazikitsidwa kwa dongosolo loyenera la uyang’aniro kunalimbitsa kwambiri mpingo wachikristu. Chinanso chomwe chinathandiza kwambiri pambali imeneyi ndi dongosolo lomwe Bungwe Lolamulira linapanga lophunzitsa akulu mmene azigwirira ntchito yawo, kuphatikizapo kuwaphunzitsa mmene angachitire ndi nkhani zachiŵeruzo. Kupita patsogolo kwa pang’onopang’ono m’zochita za gulu la Mulungu lapadziko lapansi ndi zotsatira zake zosangalatsa zinaloseredwa kale pa Yesaya 60:17 kuti: “M’malo mwa mkuwa ndidzatenga golidi, ndi m’malo mwa chitsulo ndidzatenga siliva, ndi m’malo mwa mtengo ndidzatenga mkuwa, ndi m’malo mwa miyala ndidzatenga chitsulo; ndidzakuikira akapitawo a mtendere, ndi oyang’anira ntchito a chilungamo.” Kusintha kosangalatsa kumeneku kunasonyeza kuti Mulungu anali kudalitsa oikira kumbuyo Ufumu wake mwakhama, ndiponso zinachitira umboni kuti Mulungu anali kugwirizana nawo.
5. (a) Kodi Satana anachitanji Yehova atadalitsa anthu Ake? (b) Mogwirizana ndi Afilipi 1:7, kodi anthu a Yehova athana nawo motani mkwiyo wa Satana?
5 Satana anaona chisamaliro ndi malangizo achikondi omwe Mulungu anapatsa anthu ake pambuyo pokhazikitsa Ufumuwo. Talingalirani zitsanzo zotsatirazi. Mu 1931 gulu laling’ono limeneli la Akristu linalengeza poyera kuti sanali Ophunzira Baibulo wamba. Mogwirizana ndi Yesaya 43:10, iwo anali Mboni za Yehova! Kaya panali kugwirizana kulikonse ndi zimenezi kapena ayi, Mdyerekezi anayambitsa chizunzo chosasimbika padziko lonse lapansi. Ngakhale mayiko otchuka ndi ufulu wachipembedzo, monga United States, Canada, ndi Germany, Mboni zinali kuumirizidwa mobwerezabwereza kumenyera ufulu kuti makhoti abwezeretse ufulu wawo wolambira. Pofika m’chaka cha 1988, Khoti Lalikulu ku United States linali litazenga milandu 71 yokhudza Mboni za Yehova, ndipo iŵiri mwa milandu itatu iliyonse inakomera Mbonizo. Lerolino, kumenyera ufulu m’makhoti kukupitirizabe padziko lonse lapansi pofuna “kuteteza ndi kukhazikitsa mwalamulo uthenga wabwino,” monga momwe zinalili m’zaka za zana loyamba.—Afilipi 1:7, NW.
6. Kodi kutsekeratu choonadi ndi kukaniza anthu a Yehova kuchita zinthu zina zinalepheretsa kupita kwawo patsogolo? Perekani chitsanzo.
6 M’zaka za m’ma 1930, nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itatsala pang’ono kuyamba, maboma olamulidwa ndi anthu opondereza anatseka choonadi kapena kukaniza Mboni za Yehova kuchita zinthu zina ku Germany, Spain, ndi Japan, kungotchula mayiko atatu okha. Koma m’chaka cha 2000, mayiko atatu omwewa anali ndi olengeza Ufumu wa Mulungu achangu pafupifupi 500,000. Chiŵerengerochi n’chofanana ndi kuŵirikiza chiŵerengero cha Mboni padziko lonse cha m’chaka cha 1936 pafupifupi nthaŵi khumi! Mwachionekere, kutsekeratu choonadi ndi kukaniza anthu a Yehova kuchita zinthu zina sizingawalepheretse kupita patsogolo pansi pa Mtsogoleri wawo wopambana, Yesu Kristu.
7. Kodi n’chochitika chosaiŵalika chiti chomwe chinachitika mu 1958, nanga n’kusintha kochititsa chidwi kotani komwe kwachitika kuchokera m’nthaŵiyo?
7 Kupita patsogolo kumeneku kunaonekera m’chaka cha 1958 pa msonkhano waukulu kuposa yonse imene Mboni za Yehova zinali zitachita. Pa Msonkhano wa Mayiko umenewo wakuti Chifuno cha Mulungu umene unachitikira ku New York City, panali chiŵerengero chapamwamba cha osonkhana 253,922. Pofika chaka cha 1970 Mboni zinali zitayamba kugwira ntchito yawo momasuka m’mayiko atatu omwe tatchula aja, kupatulapo m’dziko lomwe m’nthaŵiyo linkadziŵika kuti East Germany. Komabe Mboni zinali zoletsedwabe m’dziko lalikulu la Soviet Union ndi m’mayiko ena ang’onoang’ono omwe anali ogwirizana ndi Soviet Union m’pangano la zankhondo lotchedwa Warsaw Pact. Lerolino, m’mayiko ameneŵa, omwe kale anali achikomyunizimu, muli Mboni zachangu zoposa 500,000.
8. Kodi madalitso a Yehova pa anthu ake akhala ndi zotsatira zotani, nanga kodi Nsanja ya Olonda mu 1950 inanenanji pankhani imeneyi?
8 Mboni za Yehova zawonjezeka chifukwa chakuti zapitiriza ‘kufunafuna Ufumu choyamba ndi chilungamo [cha Mulungu].’ (Mateyu 6:33) M’lingaliro lenileni, ulosi wa Yesaya wakwaniritsidwa kale. Ulosiwo umati: “Wang’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.” (Yesaya 60:22) Ndipotu kuwonjezekaku kukupitirizabe. M’zaka khumi zapitazi, chiŵerengero cha ogwirizana ndi ulamuliro wa Ufumu achangu chinawonjezeka ndi anthu oposa 1,750,000. Modzifunira, ameneŵa agwirizana ndi gulu lofotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya 1950 kuti: “Tsopano Mulungu akupanga gulu la m’dziko latsopano. . . . Gulu limeneli lidzadutsa pa Armagedo, . . . lidzakhala loyamba kuonekera ‘m’dziko lapansi latsopano’ . . . , lolinganizidwa mogwirizana ndi mmene Mulungu akulamulira, lodziŵa bwino lomwe mmene zinthu ziyenera kuyendera m’gulu.” Nkhani imeneyo inamaliza ndi mawu akuti: “Chotero, tonsefe tipite limodzi patsogolo, mogwirizana, monga gulu la m’dziko latsopano!”
9. Kodi zinthu zomwe Mboni za Yehova zaphunzira m’zaka zambiri zasonyeza motani kuti n’zopindulitsa?
9 Pakali pano, gulu la m’dziko latsopano lomakula mowonjezekali laphunzira mmene lingachitire zinthu moyenera. Zimenezi zathandiza kwambiri lerolino ndipo mwina zidzathandizanso pa ntchito yobwezeretsa pambuyo pa Armagedo. Mwachitsanzo, Mboni zaphunzira kulinganiza misonkhano ikuluikulu, kupereka mofulumira thandizo lofunika mwadzidzidzi, ndi kumanga nyumba mofulumira. Zimenezi zachititsa ambiri kusirira Mboni za Yehova ndi kuzilemekeza.
Kuwongolera Malingaliro Olakwika
10, 11. Fotokozani mmene malingaliro olakwika okhudza Mboni za Yehova awawongolera.
10 Ngakhale zili choncho, pali anthu ena omwe amanyoza Mboni za Yehova kuti zochita zawo n’zosemphana ndi za anthu ena. Izi zili choncho makamaka chifukwa cha chikhulupiriro cha Mboni chozikika pa Baibulo pankhani za kuika magazi, kusaloŵerera m’ndale, kusuta fodya, ndi makhalidwe abwino. Koma anthu ochuluka ayamba kuvomereza kuti malingaliro a Mboni ndi ofunika kuwalingalira mozama. Mwachitsanzo, dokotala wina ku Poland anaimbira telefoni ofesi yoyang’anira ntchito ya Mboni za Yehova ndi kunena kuti iyeyo ndi anzake ogwira nawo ntchito pachipatala anakambirana kwa maola angapo nkhani ya kuika magazi. Chomwe chinautsa mapiri pachigwa inali nkhani yomwe inatuluka m’nyuzipepala ya ku Poland komweko yotchedwa Dziennik Zachodni. Dokotalayo ananenetsa kuti: “Ineyo pandekha ndimadandaula kwambiri kuona magazi akugwiritsidwa ntchito mopyola muyeso m’zipatala. Zimenezi ziyenera kusintha, ndipo ndikusangalala kuti winawake wabutsa nkhani imeneyi. Ndingakonde kumva zambiri.”
11 Pa msonkhano womwe unachitika chaka chathachi, akatswiri a zamakhwala a ku Canada, Europe, Israel, ndi ku United States anakambirana nkhani yomwe cholinga chake n’kuthandiza madokotala kuchiza odwala popanda kugwiritsa ntchito magazi. Pa msonkhano umenewu, womwe unachitikira ku Switzerland, ananena mosabisa kuti, mosiyana ndi mmene anthu ambiri amaganizira, chiŵerengero cha odwala amene amamwalira atalandira magazi n’chokwera kwambiri kuposa omwe salandira magazi. Mboni zodwala kaŵirikaŵiri zimatuluka m’chipatala mofulumira kusiyana ndi amene awaika magazi, ndipo zimenezi nthaŵi zambiri zimathandiza kuti ndalama zolipirira kuchipatala zikhale zochepa.
12. Perekani chitsanzo cha mmene anthu otchuka atamandira zochita za Mboni za Yehova pankhani ya kusaloŵerera m’ndale.
12 Patuluka ndemanga zambiri zoyamikira Mboni za Yehova chifukwa chosaloŵerera m’ndale, nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse isanayambe ndiponso ili m’kati, pamene anapirira pozunzidwa mwankhanza ndi Nazi. Vidiyo yakuti Jehovah’s Witnesses Stand Firm Against Nazi Assault, yopangidwa ndi Mboni za Yehova ndi kuonetsedwa koyamba pa msasa wa Ravensbrück ku Germany pa November 6, 1996, yachititsa anthu ambiri kuyamikira. Asanayambe kuonetsanso vidiyo imeneyi pa msasa wina wotchuka kwambiri ku Bergen-Belsen pa April 18, 1998, Dr. Wolfgang Scheel, mkulu wa Center for Political Education ku Lower Saxony anavomereza kuti: “Chochititsa chidwi kwambiri m’zochitika za m’mbiri n’chakuti Mboni za Yehova zinkakana motsimikiza mtima kwambiri kutsatira mfundo za chipani chandale cha National Socialist, kusiyana ndi matchalitchi achikristu. . . . Kaya malingaliro athu ndi otani pa ziphunzitso ndi changu cha Mboni za Yehova, mpofunika kuwalemekeza chifukwa cha kusasunthika kwawo m’chikhulupiriro m’nthaŵi ya ulamuliro wa Nazi.”
13, 14. (a) Kodi ndi malingaliro anzeru otani oikira kumbuyo Akristu oyambirira omwe anachokera kwa munthu wosayembekezeka? (b) Perekani zitsanzo za ndemanga zabwino zomwe ena anena zokhudza anthu a Mulungu lerolino.
13 Anthu otchuka akaikira kumbuyo Mboni kapena chigamulo cha khoti chikakomera Mboni za Yehova pa nkhani yomwe ambiri satha kuimvetsa, zimathandiza kuchepetsa malingaliro audani ndipo Mboni zimakondedwa. Zimenezi zimawapatsa mwayi wolankhula ndi anthu omwe kale sankafuna n’komwe kumvetsera. Mpofunikadi kuti makhoti kapena anthu otchuka azichita zimenezo, ndipo Mboni za Yehova zimayamikira moona mtima anthu oterowo. Zimenezi zikutikumbutsa zomwe zinachitika ku Yerusalemu m’zaka za zana loyamba. Bwalo lalikulu lachiyuda la Sanihedirini, litapangana zopha Akristu chifukwa cha changu chawo pa ntchito yolalikira, Gamaliyeli, “mphunzitsi wa chilamulo, wochitidwa ulemu ndi anthu onse,” anachenjeza kuti: “Amuna inu a Israyeli, kadzichenjerani nokha za anthu awa, chimene muti muwachitire. . . . Lekani anthu ameneŵa, nimuwalole akhale; pakuti ngati uphungu umene kapena ntchito iyi ichokera kwa anthu, idzapasuka; koma ngati ichokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula; kuti kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu.”—Machitidwe 5:33-39.
14 Mofanana ndi Gamaliyeli, posachedwapa anthu otchuka aikira kumbuyo Mboni za Yehova pankhani ya ufulu wachipembedzo. Mwachitsanzo, tcheyamani wakale wa International Acadamy for Freedom of Religion and Belief anati: “Ufulu wachipembedzo suyenera kuponderezedwa chabe chifukwa chakuti anthu ambiri amaona kuti zikhulupiriro zake n’zosavomerezeka kapena sagwirizana nazo ayi.” Ndipo pulofesa wa maphunziro a sayansi yachipembedzo pa yunivesite ya Leipzig anapereka funso lofunika kwambiri lokhudza bungwe lomwe boma la Germany linakhazikitsa kuti lifufuze za omwe amati ndi magulu achipembedzo ampatuko. Iye anafunsa kuti: “Kodi n’chifukwa chiyani amafufuza mosamalitsa m’zipembedzo zing’onozing’ono koma n’kusiya matchalitchi aŵiri akuluakulu [Tchalitchi cha Roma Katolika ndi Tchalitchi cha Lutheran]?” Yankho tingalipeze mosavuta m’mawu a mkulu wakale wa boma la Germany, yemwe analemba kuti: “N’zosakayikitsa n’komwe kuti anthu ojijirika pa zatchalitchi ankauza mwachinsinsi, bungwe lofufuza magulu achipembedzo lokhazikitsidwa ndi boma, kuti liphatikizemo ndale m’zochita zake.”
Kodi Timadalira Yani Kutithandiza?
15, 16. (a) N’chifukwa chiyani zomwe Gamaliyeli anachita sizinathandize mokwanira? (b) Kodi anthu ena atatu otchuka omwe anayesa kuthandiza Yesu, analephera motani?
15 Zomwe Gamaliyeli ananena zangosonyezeratu kuti n’zosatheka kuti ntchito yotsogozedwa ndi Mulungu ilephere. Mosakayika, Akristu oyambirirawo anapindula ndi zomwe anauza Sanihedirinizo, koma sanaiwale kuti mawu a Yesu akuti otsatira ake adzazunzidwa analinso oona. Zomwe Gamaliyeli ananena zinalepheretsa zolinga za atsogoleri achipembedzo zofuna kuwapha, koma zimenezo sizinachotse chizunzo, chifukwa timaŵerenga kuti: “Ndipo anavomerezana ndi iye; ndipo mmene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.”—Machitidwe 5:40.
16 Pamene Yesu anali kumuimba mlandu, Pontiyo Pilato, sanapeze cholakwa chilichonse mwa iye, ndipo anayesetsa kuti amasule Yesu. Koma zinalephereka. (Yohane 18:38, 39; 19:4, 6, 12-16) Ngakhalenso mamembala aŵiri a Sanihedirini, Nikodemo ndi Yosefe wa ku Arimateya, omwe ankagwirizana n’zochita za Yesu, sanathe kulepheretsa khotilo kulimbana ndi Yesu. (Luka 23:50-52; Yohane 7:45-52; 19:38-40) Thandizo limene anthu angapeze pofuna kuteteza anthu a Yehova—pachifukwa chilichonse—n’lochepa kwambiri. Dziko lapansi lidzapitirizabe kudana ndi otsatira Kristu enieni, monga momwe linadera Kristu. Thandizo lokwanira lingachokere kwa Yehova yekha basi.—Machitidwe 2:24.
17. Kodi Mboni za Yehova zikudziŵa kuti chiyani, koma n’chifukwa chiyani samagwa mphwayi pa cholinga chawo chofuna kupitirizabe kulalikira uthenga wabwino?
17 Malinga ndi mmene zinthu zilili, Mboni za Yehova zikudziŵa kuti chizunzo chidzapitirizabe. Chitsutso sichidzatha pokhapokha dongosolo la Satanali litagonjetsedwa. Komabe, chizunzo chimenechi, ngakhale chili chopweteka, sichimachititsa Mboni kuleka kukwaniritsa ntchito yawo yolalikira Ufumu. Chingaletse bwanji anthu othandizidwa ndi Mulungu? Amatengera chitsanzo choyenera cha Mtsogoleri wawo wolimba mtima, Yesu Kristu.—Machitidwe 5:17-21, 27-32.
18. Kodi anthu a Yehova akuyembekezera mavuto otani m’tsogolo, koma kodi ali n’chikhulupiriro kuti zotsatira zake zidzakhala zotani?
18 Kuyambira pachiyambi penipeni, chipembedzo choona chatsutsidwa mwamphamvu. Posachedwapa, chidzaukiridwa mwamphamvu ndi Gogi, Satana amene tsopano ali padziko lapansi pompano kuchokera pamene anam’chotsa kumwamba. Koma chipembedzo choona chidzapambana. (Ezekieli 38:14-16) “Mafumu a dziko lonse,” motsogozedwa ndi Satana, “adzachita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawalaka, chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu.” (Chivumbulutso 16:14; 17:14) Inde, Mfumu yathu ikupita patsogolo kukagonjetsa komaliza ndipo posachedwapa ‘ilakika.’ Ndi mwayitu waukulu kwabasi kuyendera naye limodzi, podziŵa kuti posachedwapa palibe amene adzatsutsanso olambira Yehova pamene akunena kuti: “Mulungu ali ndi ife.”—Aroma 8:31; Afilipi 1:27, 28.
Kodi Mungafotokoze?
• Kodi Yehova wachitanji polimbikitsa mpingo wachikristu kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa Ufumu?
• Kodi Satana wachitanji poyesa kuletsa Kristu kugonjetsa komaliza, nanga zotsatira zake zakhala zotani?
• Kodi tiyenera kukhala ndi malingaliro achikatikati otani pa zinthu zabwino zimene omwe si Mboni amachita?
• Kodi Satana achitanji posachedwapa, ndipo zotsatira zake zikhala zotani?
[Chithunzi patsamba 18]
Misonkhano ikuluikulu imachitira umboni kuti anthu a Yehova akupita patsogolo
[Zithunzi patsamba 20]
Kusaloŵerera m’ndale kwa Mboni m’nthaŵi yankhondo yachiŵiri ya padziko lonse kukupitirizabe kutamanditsa Yehova