Perekani Chisamaliro Chokhazikika ku Chiphunzitso Chanu
“[Pereka chisamaliro chokhazikika kwa iwemwini ndi chiphunzitso chako, NW]. Uzikhala mu izi pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.”—1 TIMOTEO 4:16.
1. Nchifukwa ninji ino siiri nthaŵi kaamba ka ife kufooka mu ntchito yathu yolalikira Ufumu?
YEHOVA tsopano akufulumiza kusonkhanitsidwa kwa onga nkhosa. Ndithudi, chotero, iyi si nthaŵi kaamba ka anthu ake ya kulefuka mu ntchito yawo yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Yesaya 60:8, 22; Mateyu 24:14; 28:19, 20) Tifunikira kuchita m’chigwirizano ndi mzimu wa chimene Mulungu akuchita mu nthaŵi yathu. Pamene mapeto akuyandikira, tidzibwerera kwa anansi athu mobwerezabwereza. Ndithudi, ntchito yowonjezereka yochitira umboni ndi ofalitsa ndi apainiya ambiri owonjezereka tsopano ikusonkhezera munda wa dziko. Ndipo mlingo wokulira wa kusonkhanitsa kosangalatsa kumeneku udzakulabe.—Yesaya 60:11; yerekezani ndi Masalmo 126:5, 6.
2. (a) Mogwirizana ndi Yesaya 40:28-31, ndi magwero ati a mphamvu amene tingakoke kaamba ka mphamvu yofunikira kumaliza ntchito yolalikira Ufumu? (b) Nchiti chomwe chiri chifukwa chabwino kaamba ka kuperekera chisamaliro chopambanitsa ku mtundu wa utumiki wathu pa nthaŵi ino?
2 M’malo mwa kugonjera ku lingaliro lirilonse la kudzimva ‘wotopa’ chifukwa gawo lina likukwaniritsidwa mobwerezabwereza, tiyenera kuzindikira kuti iyi iri nthaŵi kaamba ka ife kupemphera kwa Yehova kaamba ka “mphamvu” yofunikirayo kuti timalize ntchitoyo. (Yesaya 40:28-31; 1 Yohane 5:14) Zowona, mamiliyoni a “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” asonkhanitsidwa kale. Koma chimene kalelo chinali chachipambano m’kuthandiza anthu ena sichingakhale chokhutiritsa m’kuthandiza ena m’magawo athu. (Chivumbulutso 7:9, 10; Yohane 10:16) Chotero, mtundu wa utumiki wathu ufunikira chisamaliro chowonjezereka.
3. Ndimotani mmene kutenthedwa maganizo kwatsopano kungapangitsidwire mu utumiki wathu wa m’munda?
3 Ndi kugamulapo kokhalitsidwanso chatsopano, tingasumike maganizo pa kuwongolera kukhutiritsa kwathu mu utumiki. Ichi chingayambitse kutenthedwa mtima kwatsopano mu utumiki wathu wa m’munda. Koma ndimotani mmene chimenechi chingachitidwire? Mwa ‘kupereka chisamaliro chokhazikika kwa ife eni ndi chiphunzitso chathu,’ osati kokha kupanga utumiki wathu mwa nthaŵi zonse. (1 Timoteo 4:16) Milomo yathu iyenera kupereka zoposa kukwaniritsa “nsembe ya chiyamiko.” (Ahebri 13:15) Tiyenera kukhala aluso pa ntchito yathu. (Miyambo 22:29) Chotero, chimene chikufunikira, chiri kugwira ntchito mwaluso m’gawo lathu. Pano pali mbali zina za utumiki wathu ku zimene tifunikira “kupereka chisamaliro chokhazikika.”
Mmene Mungapangire Gawo “Latsopano”
4. Ndi mwanjira yotani mmene tingapangire gawo “latsopano” m’gawo logawiridwa la mpingo wathu?
4 Tiyeni tiyang’ane pa mkhalidwewo m’njira yokhoza kugwira ntchito. M’malo ambiri, palibe gawo latsopano kapena losagwiridwa ntchito kaŵirikaŵiri. Chotero bwanji osapanga gawo “latsopano” mkati mwa gawo logawiridwa la mpingo? Motani? Chabwino, pamene timaitanira kaŵirikaŵiri, sitingachite ngati kuti sitinayambe tafikapo pa nyumba imeneyo mwa kunena kokha chimene takhala tikunena pa makomo. Mwachidziŵikire, eninyumba adzatizindikira ife mwa njira iriyonse ngati takwaniritsa gawolo mobwerezabwereza. Bukhu la Reasoning From the Scriptures limapereka mawu oyamba oposa 40 omwe tingagwiritsire ntchito mu utumiki wathu. Tiyenera kukonzekera iwo bwino lomwe monga chinachake chatsopano ndipo chosangalatsa mwa kuwagwirizanitsa iwo ndi nkhani za kumaloko ndi zokondweretsa za posachedwapa. M’malo mwa kudzimva kukhala opempha chikhululukiro ponena za kuitanira mobwerezabwereza, tifunikira kukhala ndi mkhalidwe wabwino ndi kupanga gawo lathu “latsopano” ndi maperekedwe a mtundu wabwino. Koma kodi ichi chidzathandiza ngati eninyumba ali opanda ubwenzi?
5. (a) Ndimotani mmene tingapangire mkhalidwe wakale wopanda ubwenzi kugwira ntchito ku ubwino wathu? (b) Nchiyani chomwe mwachipeza kukhala chogwira ntchito bwino kumaloko? (c) Nchifukwa ninji kumvetsera ndi kuyamikira kowona mtima kuli kothandiza?
5 Kudziŵa mkhalidwe wakale wa mwininyumba kungatulukemo m’malingaliro oipa ponena za kuitanira kwachiŵirinso. Koma bwanji osapanga chidziŵitso chimenecho kugwira ntchito ku ubwino wanu? Motani? Mwinamwake mwa kuchifikira icho osati mwachindunji choyamba ndipo kenaka kumangirira pa chimene chinanenedwa mkati mwa kuitanira koyamba. Inu munganene kuti: “Mwadzuka bwanji, Bambo Harris!” Ngati chikuwoneka kukhala choyenerera, mungawonjezere kuti: “Kodi munakhala bwanji?” Kenaka munganene kuti: “Pamene ndinali pano mlungu wapita, munandiwuza kuti tchalitchi chanu chinayang’anira kaamba ka zosowa zanu zonse zauzimu ndipo kuti munali wolowetsedwamo monga chiwalo. Monga mnansi amene amatenganso chipembedzo mosamalitsa, kodi ndingakufunseni chimene chipembedzo chanu chikunena ponena za chiyembekezo cha chipulumuko mu mbadwo wa nyukliya?” Kenaka, muloleni iye akuwuzeni inu. Yamikirani mwininyumba pamene inu mowona mtima mungatero. Kumvetsera kwa iye ndi kumuyamikira kungasinthe mkhalidwe wake. Kaŵirikaŵiri, anthu angavomereze ulendo wina ngati iwo eni apanga kwina kwa kulankhulako. Ndithudi, mudzafuna kugwirizanitsa uthenga wanu ku chimene mwininyumba akunena.
6. (a) Ndimotani mmene tingaphunzitsire eninyumba kutiyembekezera ife kuitanira mokhazikika? (b) Ndi malongosoledwe a mfungulo otani amene angatithandize ife kukhala ndi chipambano? (c) Nchiyani chomwe chimagwira bwino ntchito m’gawo la kumaloko?
6 Ndi zimene mumanena, mungaphunzitse eninyumba kutiyembekezera ife kuitanira mokhazikika. Yesani kunena kuti: “Moni, Akazi a Fredericks! Kodi muli bwanji pa tsiku lalero? Pa ulendo uno kwa anansi athu, tikukambitsirana . . . ” Kapena munganene kuti: “Mwadzuka bwanji! Tikupanga kuitanira kwathu kokhazikika kwa mlungu ndi mlungu. Chiri chabwino kubwereranso kuno. Anansi anu asangalala ndi nkhani yatsopano imene tikukambitsirana pa ulendo uno.” Kenaka pitirizani. Ichi chimatumikiranso kulipanga gawolo “latsopano” kaamba ka inu. Mawu enieniwo angasiyane mwa njira inayake m’dziko lanu, koma ichi chikupereka lingaliro lenileni. Bwanji osapanga mbali yokulira ya icho, ku ubwino wanu?
7. (a) Pamene zikuchoka, ndimotani mmene Mboni zina zimakonzekeretsera mwininyumba kaamba ka ulendo wina? (b) M’chigwirizano ndi ichi, nchiyani chimene chimagwira bwino ntchito m’gawo la kumaloko?
7 Kuti mukonzekeretse mwininyumba kaamba ka kuitanira kotsatira, Mboni zina zakhala ndi chipambano ndi mapeto onga ngati awa: “Tikuyang’ana kutsogolo ku kukuchezeraninso posachedwapa.” Kwa awo amene poyambirira anali osinkhasinkha kulankhula ndi inu, munganene kuti: “Ndasangalala ndi kukambitsirana kwathu. Inu motsimikizirika munapanga nsonga zina zabwino. Ichi chinatenga timphindi tochepa, koma mwapang’ono sitinalankhule ponena za mbiri yoipa, imene tingaimve pa nthaŵi iriyonse. Iyo ndithudi inali yomangirira.” Mosakaikira, mudzakulitsa njira zina zoyenerera za kulankhula ndi eninyumba. Pa mlingo uliwonse, ndi malongosoledwe abwino, maperekedwe a mtundu wabwino, ndi ubwenzi, kalamirani kuthandiza unyinji kuti usakane kuitanira kwathu kokhazikika.
Perekani Umboni Wokwanira
8, 9. Ndi malingaliro otani amene aperekedwa kaamba ka kufufuza kosamalitsa kaamba ka oyenera?
8 Chinthu china chimene tingaperekeko chisamaliro chimene chidzasunga kutenthedwa maganizo kwathu kukhala pamwamba kuli kufunafuna mokwanira oyenerera. (Machitidwe 8:25; 20:24) Mwachitsanzo, mbale angafunse kaamba ka mwamuna wapanyumba ngati mkazi kapena mwana abwera pa khomo kothera kwa mlungu kapena madzulo. Mwinamwake, ali mkazi amene talankhula naye kwa nthaŵi zambiri. Chotero tingapange kuyambanso kwatsopano ndi mwininyumba mwa kulankhula ndi mutu wa banja. Ife kenaka tingagwirizanitse uthenga wathu kwa iye, tikumanena zinthu zonga ngati, “Nchiyani chimene mukulingalira kuti chidzatsimikizira mtsogolo mwachimwemwe kaamba ka banja lanu?” kapena, “Onani mmene Baibulo limachirikizira umodzi wa banja.” Yamikirani mwamunayo kaamba ka malingaliro abwino amene angalongosole.
9 Njira ina ya kupezera gawo “latsopano” iri kufunafuna ziwalo zina za banja zokhala pansi pa nyumba imodzimodziyo—agogo a akazi, mphwathu kapena nsuwani wopita ku sukulu, mlamu wa mkazi yemwe amagwira ntchito mkati mwa mlungu. Chakhalanso chogwira ntchito kudziŵa kuti ndi mamita a magetsi angati kapena mabokosi a makalata amene alipo pa malo okhala. Izi zingasonyeze pamene anthu akonza malo apansi, kudenga, kapena malo ena kuti adzipanga lenti. Yesani kufikira awo amene akuchita lenti—ophunzira, ogwira ntchito osakwatira, akazi amasiye, ndi ena. Ichinso chimathandiza kufutukula gawo lomwe liripo.
10. Ndi iti imene iri njira ina ya kufutukulira gawo lathu la ku nyumba ndi nyumba, ndipo nchiyani chimene ena achita kufikira ogwira ntchito usiku?
10 Njira ina imodzi yowonjezereka ya kufutukulira gawo lathu la kunyumba ndi nyumba liri kulipatsa ilo mpumulo pa nthaŵi zina pamene tikutengamo mbali m’mbali zina za utumiki wathu. Kaamba ka kusintha, tingagwire ntchito m’gawo ndi kugawira kwachindunji kwa phunziro la banja la panyumba la Baibulo laulere. Anthu ena omwe sali panyumba pamene tiitanira angapezedwe pa malo awo a bizinesi kapena a ntchito. Ndipo kuchitira umboni m’malo a bizinesi kungakhale kobala zipatso. Ena a anthu amenewa angafikiridwenso ngati tichita umboni wa m’khwalala pa maora oyenerera, opatsa phindu. Mu Canada apainiya anakhala ndi zotulukapo zabwino kuchokera ku maulendo a madzulo pa ogwira ntchito usiku wonse pa malo omwetsera mafuta a galimoto, masitolo, ndi mahotelo mmene akalaliki a pa desiki samakhala otanganidwa koposa pa nthaŵiyo ndipo kaŵirikaŵiri amayamikira kukhala ndi chinachake choti aŵerenge. Ndithudi, alongo mwapadera afunikira kupewa malo ena mkati mwa maora a madzulo.
11. (a) Nchiyani chimene Mboni zina zikuchita kumene ambiri sali panyumba pa kuitanira koyamba? (b) Kodi nchotulukapo chotani chimene khama m’kuitanira pa amene sanali panyumba liri nacho pa gawo lathu, ndi zotulukapo zotani mu utumiki?
11 Bwanji ponena za awo amene sali panyumba pamene tiitanira? Pano kachiŵirinso, tiyenera kukhala okwaniritsa kotheratu. Mboni zina zimagwiritsira ntchito zolembera zawo zosungidwa bwino za ku nyumba ndi nyumba mwamsanga pambuyo pa ntchito yawo ya ku khomo ndi khomo ndi kubwerera ku malo amene anthu sanali panyumba pamene anafikapo kumayambiriro tsiku limenelo. Kaŵirikaŵiri, eninyumba amakhala atabwerera kunyumba, kapena ogwira ntchito usiku amakhala atadzuka pa nthaŵiyo. M’malo ambiri, 50 peresenti kapena owonjezerekapo sakhala panyumba mkati mwa tsiku. Chotero ife, m’chenicheni, tingawirikize kaŵiri gawo mwa kupanga kuitanira pa omwe sali panyumba maora osiyana kufikira pamene tipeza wina panyumba. Apainiya ndi ofalitsa ozoloŵera amavomereza kuti khama m’kugwira ntchito pa osakhala panyumba kaŵirikaŵiri limatulutsa zotulukapo zabwino zoposa mmene kumapangira kukwaniritsa kwathu gawo kwa poyamba. Mwa kupereka chisamaliro ku mbaliyi ya utumiki wathu, mwachidziŵikire tidzatuta madalitso ambiri.—Miyambo 10:22.
Awo Amene Amadandaula
12. Ndimotani mmene tiyenera kuvomerezera pamene anthu adandaula kuti timaitanira mobwerezabwereza? Nchifukwa ninji?
12 Nchiyani chomwe chinganenedwe kwa anthu amene amadandaula kuti tikuitanira mobwerezabwereza? Pamwamba pa zonse, tiyenera kusonyeza kumvetsetsa. (Mateyu 7:12) Kwa iwo, chimawonekera ngati kuti tabwerera mofulumira koposa. Koma chiri chabwino kukumbukira kuti ngakhale zaka zapitazo anthu anali kunena kuti, ‘Munali pano mlungu watha,’ pamene tikudziŵa bwino lomwe kuti papita miyezi isanu ndi umodzi kapena yowonjezerekapo kuyambira pamene tinaitanirapo. Pambali pa icho, kuitanira kobwerezabwereza kungadzutse chikondwerero. Mu Guadeloupe mwamuna wina anathamangira Mboni ndi kunena kuti: “Ndakuyang’anani tsopano kwa milungu yochulukira. Kaŵirikaŵiri, sindimvetsera kwa Mboni, koma ndiyenera kudziŵa chifukwa chimene mumachezera anthu kaŵirikaŵiri chotero!” Phunziro la Baibulo latsopano linatulukapo.
13, 14. Ndimotani mmene akhulupiriri anzathu akuchitira ndi nkhanizi pamene eninyumba adandaula?
13 Abale ena mwachifundo anauza odandaula tsiku lenileni la kuchezera kwapapitapo ndipo anagawira magazini a posachedwa, kuchipanga icho kukhala chomvekera kuti nkhanizo zimasiyana kuchokera ku zija zimene ziri m’magazini amene tinali nawo pa nthaŵi yapita imene tinaitanira. Kulingalira ndi eninyumba oterowo, ife tinganene kuti mwinamwake iwo analandira manyuzipepala ambiri ndi magazini kuyambira pa ulendo wathu womalizira, koma izi nthaŵi zonse sizinatenge mbiri yabwino. Tingalongosole kuti tikubweretsa mbiri yabwino ndipo kuti maulendo athu sali aatali. Koma ngati mwininyumba ali wotanganitsidwa kwambiri, tinganene kuti: “Ngati ino si nthaŵi yabwino koposa kulankhula ndi inu, ndingakuwoneni pa kuitanira kwanga kotsatira m’kupita kwa mlungu kapena tero.”
14 Nchiyani chinanso chimene chinganenedwe? Ichi chimadalira pa mkhalidwe wa mwininyumba ndipo ndi kulandiridwa kwachizoloŵezi kumene tingayembekezere kumene timakhala. Mlongo mmodzi mu Japan akulongosola maulendo athu obwerezabwereza m’njira iyi: ‘Nkhani za pa wailesi ya kanema zidzasimba za njira ya mphepo ya mkuntho mobwerezabwereza, kubwereza chidziŵitsocho kaŵirikaŵiri kaamba ka phindu la awo omwe angakhale anaphonya kuwulutsidwa kwa papitapo. Ichi chimachitidwa chifukwa miyoyo ikuyambukiridwa. Kubwerezabwereza kwa maripotiwo kumawonjezereka pamene mkunthowo ukuyandikira. Chotero, pamene mkuntho wa Armagedo ukuyandikira, uthenga wochenjeza uyenera kulalikidwa mobwerezabwereza monga mmene kungathekere kuti tipulumutse miyoyo.’ Ndithudi, tikapanga ndemanga yoteroyo mwachifundo ndipo mowona mtima, tikumayembekezera kufikira mtima wa womvetsera.
Kukumanizana ndi Chitokoso cha Kupanda Chikondwerero
15. (a) Nchiyani chimene chingakhale chitokoso chomakulakula pamene tikugwira ntchito m’magawo athu mobwerezabwereza? (b) Nchifukwa ninji anthu ena ali osakondweretsedwa?
15 Pamene kubwerezabwereza kwa maulendo athu kukuwonjezereka, chitokoso chomakula chiri kupanda chikondwerero kumene kaŵirikaŵiri timakumana nako. Koma kusanthula kwa zina za zochititsa kupanda chikondwerero kungatilimbikitse ife kudziŵa kuti chingakhale chothekerabe kufikira mitima ya ena a anthu awa. Kupanda chikondwerero kwawo kungasonyeze kuipidwa kwawo ndi kusowa chiyembekezo. Iwo angadzimve kuti kulibe njira yotulukira ku mkhalidwe wa dziko ulipowu, akumalingalira kuti adzangokhala ndi miyoyo mwa njira yabwino koposa imene angathere. Ena ali okwiyitsidwa chifukwa atsogoleri ena a chipembedzo amadzilowetsa m’ndale zadziko, ali a liwongo la makhalidwe oipa a chisembwere, kapena amalephera kutenga kaimidwe kolimba motsutsana ndi mkhalidwe woipa wa chisembwere. Chotero eninyumba amenewa ali okhumudwitsidwa ndipo amangokhala ndi moyo kokha kaamba ka lero.
16. Ndimotani mmene mtima wa munthu wopanda chikondwerero ungafikiridwire?
16 Tikudziŵa kuti atumiki Achikristu akale mwachipambano anachita ndi mkhalidwe umodzimodziwo, popeza anthu ena pa nthaŵiyo ananena kuti: “Tidye timwe pakuti mawa timwalira.” (1 Akorinto 15:32) Chotero, tikudziŵa kuti tiri ndi kokha chimene anthu amenewo amafuna kumva. Komabe, ndimotani mmene tingafikire mtima wawo? Njira imodzi iri kuika pambali mabukhu athu a Baibulo kwa kamphindi, kuwalola iwo kuwona ife tikuchita tero. Kenaka tingawafunse iwo mafunso okonzekeretsedwa bwino monga ngati awa: “Kodi mukuganiza kuti pali yankho ku mavuto athu a nthaŵi ino? Kodi chiri chakuti anthu ambiri sanapeze kokha mayankho? Kodi mukuganiza kuti tiyenera kukhala otsimikiza ndi kupitiriza kufunafuna?” Kwa ena, tinganene kuti: “Ndithudi mumavomereza kuti chiri chabwino kukhala amoyo ndi chiyembekezo koposa kukhala opanda chiyembekezo kaamba ka zinthu zabwino. Nchiyani chimene mumayembekeza kuwona?” Tingafunse kuti: “Nchiyani chimene inu eni mukudzimva kukhala chokhumudwitsa chachikulu kwambiri ku umodzi ndi mtendere wa dziko?” Enabe angafunsidwe kuti: “Kodi mukuganiza kuti zipembedzo zonse ziri zofanana ndi chimene mwachilongosola?” Nthaŵi zambiri mafunso oterowo adzapangitsa eninyumba kulongosola kawonedwe kawo. Kenaka, pamene iwo ayankha, khalani otsimikizira kumvetsera. Inde, aloleni iwo kutsanulira mtima wawo kwa inu. Ambiri a iwo ‘akuusa moyo ndi kulira pa zonyansa zonse zomwe zikuchitidwa.’—Ezekieli 9:4.
17. Ndimotani mmene zofalitsidwa zathu zingagwiritsidwire ntchito kufikira ena ngakhale pamene iwo poyamba amawumirira kuti sali okondweretsedwa?
17 Kafikiridwe kena ku kupanda chikondwerero kali kuzindikira nsonga ya chitsutso chopangidwa ndi eninyumba ndi kubwerera ndi magazini kapena chofalitsidwa china cha Watch Tower chochita ndi nkhaniyo. Poyamba, ingakhale nkhani yomwe siiri ya chipembedzo nkomwe, monga ngati nkhani pa kufa kwa mwana kwadzidzidzi kapena kufa kwa nkhalango. Longosolani kuti munali kulingalira za chimene chinakondweretsa mwininyumbayo ndipo munakumbukira nkhaniyi. Kenaka lozerani ku nsonga zazikulu ku nkhaniyo. Mkazi mmodzi yemwe anali atangokana kumene mabukhu athu analandira magazini kokha timphindi tochepa pambuyo pake. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti Mboniyo inafunsa ngati mkaziyo anadziŵa kuti panali kuchotsa mimba 55 miliyoni chaka chirichonse. Atazizwitsidwa pa kudziŵa chimenechi, iye anafunsa kaamba ka magazini yokhala ndi chidziŵitso chimenecho.
Kuiwona Iyo Kufikira Mapeto
18, 19. (a) Ndi ku nsonga zowonjezereka zotani zimene tiyenera ‘kupereka chisamaliro’ pamene tikuchita utumiki wathu? (b) Ndi malingaliro onyada otani amene anthu ena ali nawo ponena za ife ndi zikhulupiriro zathu, ndipo ndimotani mmene tingawayankhire iwo?
18 Pamwamba pa zonse, tifunikira kukhala oleza mtima ndi anthu. Lankhulani pang’onopang’ono ndipo ndi kutentha. Sonyezani chikondi ndi kukoma mtima. (Agalatiya 5:22, 23) Musanapite ku khomo lotsatira, lingalirani pa zimene zachitika pa khomo lapitalo kuwona pamene kuwongolera kuli kothekera. Khalani omvetsetsa, popeza anthu ambiri ali ndi malingaliro olakwa ponena za Mboni za Yehova. Iwo anganene kuti: ‘Mumapewa ndale zadziko ndi mathayo a boma,’ ‘Mumakana utumiki wa nkhondo,’ kapena, ‘Mumaswa mabanja.’ Koma kawonedwe kameneka kali kofanana ndi kaja ka dziko kulinga kwa akhulupiriri anzathu a m’zana loyamba. Sonyezani eninyumba ichi, mwinamwake kugwiritsira ntchito mawu pansi pa mutu wakuti “Uchete” (Neutrality) m’bukhu la Reasoning.
19 Ponena za Akristu oyambirira, katswiri wa mbiri yakale Will Durant analemba kuti: “Kwa Mkristu chipembedzo chake chinali chinachake chosiyana ndipo chokulira pa chitaganya cha ndale zadziko; chimvero chake chapamwamba koposa chinali osati kwa Kaisara koma kwa Kristu. . . . Kudzichotsa kwa Mkristu kuchokera ku zochitika zapadziko kunawoneka kwa akunja kuthaŵa thayo la boma, kufooketsa kwa chomangira cha mtundu ndi chifuno. Tertullian analangiza Akristu kukana utumiki wa nkhondo; . . . Akristu anachenjezedwa ndi atsogoleri awo kupewa osakhala Akristu, kupewa maseŵera awo a phwando monga ankhalwe, ndi mabwalo awo a zamaseŵera monga malo a zoipa. . . . Chikristu [pamene chinali kupanga atembenuzi] chinazengedwa mlandu wa kuswa nyumba.”—Caesar and Christ, tsamba 647.
20, 21. (a) Nchiyani chimene tikufuna kukhala otsimikizira pamene anthu savomereza? (b) Nchifukwa ninji sitiyenera “kuleka” koma kupitiriza ntchito yathu yabwino yolalikira Ufumu?
20 Anthu ena sadzamvetsera, mosasamala kanthu za zimene tinganene. Koma chimenecho chiyenera kukhala chifukwa cha kukana kwawo uthenga wa Ufumu, osati chifukwa cha kulephera kwathu kupanga maperekedwe a mtundu wabwino mu utumiki wathu. (Luka 10:8-11; Machitidwe 17:32; Ezekieli 3:17-19) Tiyenera kuchita ubwino wathu wothekera ndi thandizo la Mulungu, ndipo Yehova adzawona ntchitoyo kufikira mapeto.—Yerekezani ndi Afilipi 1:6.
21 Ndi chidaliro chowonjezereka, chotero, pitirizani kukhala ndi “zochuluka m’ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse podziŵa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe.” (1 Akorinto 15:58) “[Pereka chisamaliro chokhazikika kwa iwemwini ndi chiphunzitso chako, NW]. Uzikhala mu izi, pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi akumva iwe.” (1 Timoteo 4:16) Pamwamba pa zonse, “tisaleme pakuchita zabwino, pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanga kufooka.”—Agalatiya 6:9.
Kodi Mungakumbukire?
◻ Ndi ziti zomwe ziri njira zina zosungira mkhalidwe wabwino m’magawo ogwiridwa ntchito mobwerezabwereza?
◻ Ndimotani mmene tingafunire mosamalitsa oyenerera?
◻ Ndimotani mmene tingayesere kuchita ndi awo amene amadandaula kuti timaitanira mobwerezabwereza?
◻ Ndi mwanjira zotani mmene tingakumanizirane ndi chitokoso cha kupanda chikondwerero?
◻ Nchiyani chomwe chidzawongolera mtundu wa utumiki wathu?
[Bokosi patsamba 20]
PAMENE KUKWANIRITSIDWA KWA GAWO KUKUWONJEZEREKA,
“Perekani chisamaliro chokhazikika” ku:
◻ Mafikiridwe ndi maperekedwe abwino
◻ Mosamalitsa kufunafuna oyenerera
◻ Kuchita moleza mtima ndi odandaula
◻ Kuyang’anizana ndi zitokoso za kupanda chikondwerero ndi kusamvetsetsa