“Sankhani Moyo Kuti Mukhale Ndi Moyo”
“Ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo.”—DEUTERONOMO 30:19.
1, 2. Kodi munthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu m’njira zotani?
“TIPANGE munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu.” Awa ndi mawu a Mulungu omwe analembedwa m’chaputala choyamba cha Baibulo. Mogwirizana ndi mawuwo, lemba la Genesis 1:26, 27 limati: “Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adam’lenga iye.” Motero, munthu woyamba anali wosiyana kwambiri ndi zolengedwa zonse za padziko lapansi. Iye anali wofanana ndi Mlengi, chifukwa naye ankatha kuganiza, kusonyeza chikondi, chilungamo, nzeru, ndiponso mphamvu. Anali ndi chikumbumtima kuti azisankha kuchita zinthu zom’pindulitsa ndiponso zosangalatsa Kholo lake la kumwamba. (Aroma 2:15) Mwachidule, tingati Adamu anali ndi ufulu wosankha. Poona mmene anapangira mwana wake wapadziko lapansiyu, Yehova ananena kuti: “Taonani, [zili] zabwino ndithu.”—Genesis 1:31; Salmo 95:6.
2 Popeza ndife mbadwa za Adamu, ifenso tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu ndiponso monga mwa chikhalidwe chake. Koma kodi tilidi ndi mwayi wosankha tokha zoyenerera kuchita? Inde, chifukwa ngakhale kuti Yehova amatha kudziwiratu zochitika zam’tsogolo, iye salemberatu zinthu zimene ifeyo tidzachite ndiponso zotulukapo zake. Iye salola kutero kwa ana ake a padziko pano. Kuti timvetse kufunika kogwiritsa ntchito mwanzeru ufulu wathu wosankha, tiyeni tione kaye zimene tingaphunzirepo pa zomwe zinachitikira mtundu wa Israyeli.—Aroma 15:4.
Aisrayeli Anali ndi Ufulu Wosankha
3. Kodi lamulo loyamba pa Malamulo Khumi linali loti chiyani, ndipo Aisrayeli okhulupirika anasankha bwanji kumvera lamuloli?
3 Yehova anauza Aisrayeli kuti: “Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa m’dziko la Aigupto, m’nyumba ya akapolo.” (Deuteronomo 5:6) M’chaka cha 1513 B.C.E., mtundu wa Israyeli unalanditsidwa mozizwitsa kuchoka mu ukapolo ku Aigupto, motero unalibe chifukwa chilichonse chokayikirira mawu amenewa. Mu lamulo loyamba la Malamulo Khumi, Yehova anauza Aisrayeli kudzera mwa mneneri wake Mose, kuti: “Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha.” (Eksodo 20:1, 3) Panthawi imeneyi, mtundu wa Israyeli unasankha kumvera Mulungu. Mwakufuna kwawo, iwo anasankha kulambira Yehova yekha.—Eksodo 20:5; Numeri 25:11.
4. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene Mose anauza Aisrayeli kusankhapo? (b) Kodi masiku ano tiyenera kusankha pakati pa zinthu ziti?
4 Patatha zaka 40, Mose analankhula mwamphamvu pokumbutsa mbadwo wina wa Aisrayeli zakuti mbadwowo uli ndi ufulu wosankha pakati pa zinthu ziwiri. Iye anati: “Ndichititsa mboni lero kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbewu zanu.” (Deuteronomo 30:19) Masiku anonso tingathe kusankha. Inde, tingasankhe kutumikira Yehova mokhulupirika n’kudzakhala ndi moyo wosatha, kapena tingasankhe kusamvera Yehova n’kudzalandira mphoto ya kusamverako. Taganizirani zitsanzo ziwiri za anthu amene anasankha zinthu zosiyana.
5, 6. Kodi Yoswa anasankha kuchita zinthu zotani ndipo anapindula nazo motani?
5 M’chaka cha 1473 B.C.E., Yoswa anatsogolera Aisrayeli kulowa mu Dziko Lolonjezedwa. Asanamwalire, Yoswa anauza mtundu wonsewo mawu amphamvu kwambiri akuti: ‘Ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzam’tumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m’dziko lawo.’ Kenaka, ponena za banja lake, iye anapitiriza kuti: “Koma ine, ndi a m’nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.”—Yoswa 24:15.
6 Izi zisanachitike, Yehova anauza Yoswa kuti alimbe mtima ndi kuchita chamuna, ndipo anamulangiza kuti asasiye kumvera Chilamulo cha Mulungu koma aziwerenga buku la Chilamulo usiku ndi usana, kuti zinthu zimuyendere bwino pa moyo wake. (Yoswa 1:7, 8) Izi n’zimenedi zinachitika. Yoswa anadalitsidwa chifukwa chosankha zinthu mwanzeru. Iye anati: “Sikadasowa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israyeli; zidachitika zonse.”—Yoswa 21:45.
7. Kodi ndi zinthu zotani zimene Aisrayeli ena anasankha kuchita m’nthawi ya Yesaya, nanga zinawathera bwanji?
7 Komano taganizirani mmene zinthu zinalili ku Israyeli patadutsa zaka 700. Panthawiyi, Aisrayeli ambiri ankatsatira miyambo yachikunja. Mwachitsanzo, pa tsiku lotsirizira la chaka, anthu ankasonkhana pochita phwando lokhala ndi zakudya zokoma zosiyanasiyana ndi vinyo wotsekemera. Ili silinali phwando wamba ayi. Linali phwando lachipembedzo lotamanda milungu iwiri yachikunja. Mneneri Yesaya analemba mmene Mulungu ankaonera kusakhulupirika kotereku. Iye anati: ‘Koma inu mwasiya Yehova, mwaiwala phiri langa lopatulika, ndi kukonzera mlungu wamwayi gome, ndi kudzazira mlungu waimfa zikho za vinyo wosanganiza.’ Iwowa ankakhulupirira kuti angapeze zokolola zambiri ngati atasangalatsa ‘mulungu wa mwayi’ ndi ‘mulungu waimfa,’ osati ngati atadalitsidwa ndi Yehova. Koma kwenikweni, iwo anadzigwetsa m’vuto chifukwa cha moyo wawo wopandukawo ndiponso mtima wawo wosankha dala zoipawo. Yehova anati: “Ndidzasankhiratu inu kulupanga, ndipo inu nonse mudzagwada ndi kuphedwa; pakuti pamene ndinaitana, inu simunayankhe; pamene ndinanena, simunamve; koma munachita choipa m’maso mwanga, ndi kusankha chimene Ine sindinakondwera nacho.” (Yesaya 65:11, 12) Kusankha zinthu mopanda nzeru kunawaphetsa, ndipo milungu yawo yaimfa ndi yamwayi siinawateteze.
Kusankha Zinthu Moyenera
8. Malingana ndi lemba la Deuteronomo 30:20, kodi ndi zinthu zotani zimene tiyenera kutsatira kuti tisankhe zinthu moyenera?
8 Polimbikitsa Aisrayeli kuti asankhe moyo, Mose anatchulapo zinthu zitatu zimene iwo anayenera kuchita. Iye anati zinthu zake ndizo “kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kum’mamatira iye.” (Deuteronomo 30:20) Tiyeni tione zinthu zitatuzi pazokhapazokha kuti tizisankha zinthu moyenerera.
9. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timam’konda Yehova ?
9 Kukonda Yehova Mulungu wanu: Timasankha kutumikira Yehova chifukwa choti timamukonda. Pomvera machenjezo a zochitika za m’nthawi ya Aisrayeli, timapewa ziyeso zonse zokhudza chiwerewere ndipo timapewa kutengeka ndi zinthu zimene zingatipatse mtima wa dzikoli wokonda chuma. (1 Akorinto 10:11; 1 Timoteo 6:6-10) Timakhala nganganga pambuyo pa Yehova ndipo timasunga malamulo ake. (Yoswa 23:8; Salmo 119:5, 8) Aisrayeli asanalowe m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anawalimbikitsa kuti: “Taonani, ndinakuphunzitsani malemba ndi maweruzo, monga Yehova Mulungu wanga anandiuza ine, kuti muzichita chotero pakati pa dziko limene mumkako kulilandira likhale lanulanu. Chifukwa chake asungeni, achiteni; pakuti ichi ndi nzeru zanu ndi chidziwitso chanu pamaso pa mitundu ya anthu akumva malemba.” (Deuteronomo 4:5, 6) Ino ndiyo nthawi yosonyeza kuti timakonda Yehova poika chifuniro chake patsogolo m’moyo wathu. Ndithu, iye atidalitsa tikasankha kuchita zimenezi.—Mateyu 6:33.
10-12. Kodi zomwe zinachitika m’nthawi ya Nowa zikutipatsa maphunziro otani?
10 Kumvera mawu ake: Nowa anali “mlaliki wa chilungamo.” (2 Petro 2:5) Chigumula chisanachitike, pafupifupi anthu onse anali otanganidwa ndi zinthu zina, moti “sanadziwa kanthu” kalikonse kokhudza uthenga wa Nowa wowachenjeza. Kodi zinawathera bwanji? “Chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse.” Yesu anachenjeza kuti masiku athu ano, panthawi ya “kufika [kukhalapo, NW] kwake kwa Mwana wa munthu,” zinthu zidzakhala chimodzimodzi. Zimene zinachitika m’nthawi ya Nowa ndi chenjezo lamphamvu kwa anthu a masiku ano amene safuna kumvera uthenga wa Mulungu.—Mateyu 24:39.
11 Anthu amene amanyoza machenjezo a Mulungu amene atumiki ake akunena masiku ano ayenera kuzindikira mphoto ya kusamvera machenjezowa. Za anthu onyozawa, mtumwi Petro anati: “Pakuti ichi aiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mawu a Mulungu; mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidawonongeka; koma miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mawu omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.”—2 Petro 3:3-7.
12 Tayerekezerani zimenezi ndi zimene anasankha Nowa pamodzi ndi banja lake. “Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa.” Iye anapulumutsa banja lake chifukwa chomvera chenjezo. (Ahebri 11:7) Nafenso tichite changu potsatira uthenga wa Mulungu umene tamva.—Yakobo 1:19, 22-25.
13, 14. (a) N’chifukwa chiyani ‘kumamatira kwa Yehova’ kuli kofunika? (b) Tizitani kuti Yehova, yemwe ali Muumbi wathu, azitiumba?
13 Kumamatira kwa Yehova: Kuti ‘tisankhe moyo ndi kukhala ndi moyo,’ tiyenera kukonda Yehova ndi kumumvera komanso tiyenera ‘kumamatira Yehova,’ kapena kuti kulimbikirabe kuchita chifuniro chake. Yesu anati: “Mudzakhala nawo moyo wanu m’chipiriro.” (Luka 21:19) Kwenikweni, zimene timasankha pa nkhani imeneyi zimasonyeza zimene zili m’mtima mwathu. Lemba la Miyambo 28:14 limati: “Wodala munthu wakuopa kosalekeza; koma woumitsa mtima wake adzagwa m’zoipa.” Chitsanzo cha munthu wotere ndi Mfumu Farao ya ku Aigupto. M’malo moopa Mulungu, Farao anaumitsa mtima wake panthawi ya mliri uliwonse pa Miliri Khumi imene inakantha dzikolo. Yehova sindiye anachititsa Farao kusamvera, Iye anangofuna kuti wolamulira wodzikuzayu asankhe yekha zoyenera kuchita. Komabe chifuniro cha Mulungu chinakwaniritsidwa, monga mmene Paulo analongosolera pofotokoza mmene Yehova anali kuonera Farao. Malinga n’kunena kwa Paulo, Yehova anati: “Chifukwa cha ichi, ndinakuutsa iwe, kuti ndikaonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe pa dziko lonse lapansi.”—Aroma 9:17.
14 Patatha zaka zambiri Aisrayeli atalanditsidwa m’manja mwa Farao, mneneri Yesaya anati: “Yehova, Inu ndinu Atate wathu; ife tili dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu; ndipo ife tonse tili ntchito ya dzanja lanu.” (Yesaya 64:8) Tikamalola Yehova kutiumba mwa kuchita phunziro laumwini ndiponso kutsatira Mawu ake, pang’onopang’ono timayamba kuvala umunthu watsopano. Timakhala ofatsa ndiponso otha kusinthika, motero zimakhala zosavuta kuti timamatire mokhulupirika kwa Yehova chifukwa timafuna kum’sangalatsa ndi mtima wathu wonse.—Aefeso 4:23, 24; Akolose 3:8-10.
‘Muzidziwitsa’ Ena
15. Malingana ndi lemba la Deuteronomo 4:9, kodi Mose anakumbutsa Aisrayeli za udindo wa mbali ziwiri uti?
15 Kwa Aisrayeli amene anasonkhana pokonzekera kulowa mu Dziko Lolonjezedwa, Mose anati: “Chokhachi, dzichenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwachangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisachoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu; koma muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu.” (Deuteronomo 4:9) Kuti akadalitsidwe ndi Yehova ndiponso kuti akakhale ndi moyo wabwino m’dziko limene anatsala pang’ono kulowalo, Mulungu wawo Yehova anawapatsa anthuwo udindo wa mbali ziwiri. Mbali yoyamba ya udindowu inali yoti asaiwale zinthu zabwino zimene Yehova anawachitira, zomwe anaziona ndi maso awo, ndipo yachiwiri inali yoti zinthuzo akaphunzitsenso mibadwo yawo ya m’tsogolo. Anthu a Mulungu masiku ano tiyeneranso kuchita chimodzimodzi kuti ‘tisankhe moyo ndi kukhala ndi moyo.’ Koma kodi n’chiyani chimene Yehova watichitira chimene taona ndi maso athu?
16, 17. (a) Kodi ndi zinthu zotani zimene amishonale ophunzitsidwa ku sukulu ya Gileadi achita mu ntchito yolalikira Ufumu? (b) Kodi mukudziwapo zitsanzo ziti za anthu amene apitirizabe kulalikira mwakhama?
16 Timanyadira kwambiri kuona mmene Yehova wadalitsira ntchito yathu yolalikira ndi kupanga ophunzira. Chitsegulireni Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo mu 1943, amishonale athandiza kwambiri pa ntchito yopanga ophunzira m’mayiko ambiri. Tikunena pano, amishonale ena amene anachita nawo sukuluyi kalelo, akuchitabe khama pa ntchito yolalikira Ufumu, ngakhale kuti panopo n’ngokalamba ndipo ena sangathe kuchita zinthu zina. Chitsanzo chabwino cha anthu otere ndi Mary Olson, amene anamaliza maphunziro a sukulu ya Gileadi mu 1944. Iye anachita utumiki waumishonale ku Colombia, kenaka ku Uruguay, ndipo tsopano ali ku Puerto Rico. Ngakhale kuti mavuto a ukalamba amam’lepheretsa kuchita zinthu zina, Mlongo Olson amalalikirabe mwakhama. Poti amadziwa Chisipanishi, mlungu uliwonse amakonza nthawi yolowa mu utumiki wa kumunda ndi ofalitsa a kumeneko.
17 Mlongo Nancy Porter, amene ndi mayi wamasiye yemwenso anamaliza maphunziro a sukulu ya Gileadi mu 1947, akuchitabe utumiki ku Bahamas. Nayenso amachita khama kwambiri pantchito yolalikira. M’nkhani ya moyo wawo, Mlongo Porter anati: “Kuphunzitsa anthu ena choonadi cha m’Baibulo kumandisangalatsa. Kumandithandiza kuti ndikhale ndi ndondomeko yabwino ya zinthu zauzimu ndiponso kuti ndikhale ndi moyo wokhazikika.”a Mlongo Porter komanso atumiki ena okhulupirika akaganizira za m’mbuyo, saiwala zimene Yehova wachita. Nanga bwanji ifeyo? Kodi timayamikira tikaona mmene Yehova wadalitsira ntchito ya Ufumu kwathu kuno?—Salmo 68:11.
18. Kodi tingaphunzire chiyani powerenga nkhani za moyo wa anthu omwe ali amishonale?
18 Timasangalala ndi zimene achikulire amenewa achita ndiponso zimene akupitiriza kuchita. Kuwerenga nkhani za moyo wawo kumatilimbikitsa kwambiri chifukwa choti tikaona zimene Yehova wachitira anthu okhulupirikawa, timapeza mphamvu zom’tumikira mosabwerera m’mbuyo. Kodi mumakonda kuwerenga nkhani zolimbikitsazi zimene zimafalitsidwa mu Nsanja ya Olonda ndi kusinkhasinkha mfundo zake?
19. Kodi makolo achikristu angatani kuti agwiritse ntchito bwino nkhani za moyo wa anthu osiyanasiyana za mu Nsanja ya Olonda?
19 Mose anakumbutsa Aisrayeli kuti asaiwale zinthu zonse zimene Yehova anawachitira ndi kuti zinthuzi zisachoke m’mitima yawo pa masiku onse a moyo wawo. Kenaka anawonjezera mfundo ina: “Muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu.” (Deuteronomo 4:9) Nkhani zoti zinachitikadi zimakhudza mtima kwambiri. Ana amakula bwino akakhala ndi zitsanzo zabwino. Alongo osakwatiwa angaphunzire pa zitsanzo za alongo okhulupirika achikulire amene nkhani za moyo wawo zimafotokozedwa mu Nsanja ya Olonda. Abale ndi alongo amakhala ndi mwayi waukulu wolalikira uthenga wabwino akamatumikira m’gawo la chinenero china m’dziko lawo lomwelo. Inu makolo achikristu, bwanji osagwiritsa ntchito nkhani monga za amishonale okhulupirika amene anapita ku sukulu ya Gileadi polimbikitsa ana anu kusankha kuchita utumiki wa nthawi zonse pa moyo wawo?
20. Tiyenera kutani kuti ‘tisankhe moyo’?
20 Nanga kodi aliyense wa ife ‘angasankhe moyo’ m’njira yotani? Angatero pogwiritsa ntchito ufulu wosankha m’njira yoti Yehova aone kuti timam’konda ndiponso popitiriza kum’tumikira ndi mtima wathu wonse panthawi yonse imene watilola kukhala ndi mwayi wapaderawu. Monga Mose ananenera, “pakuti iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka.”—Deuteronomo 30:19, 20.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani ya mutu wakuti “Wosangalala ndi Wothokoza Ngakhale pa Vuto Losautsa Mtima,” yomwe inatuluka mu Nsanja ya Olonda ya June 1, 2001, pa masamba 23 mpaka 27.
Kodi Mungathe Kukumbukira?
• Kodi mwaphunzirapo chiyani pa zitsanzo zimene takambirana za anthu amene anasankha zinthu zosiyana?
• Kodi tiyenera kuchita zinthu zotani kuti ‘tisankhe moyo’?
• Kodi ndi udindo wa mbali ziwiri uti umene tikulimbikitsidwa kuti tiukwaniritse?
[Chithunzi patsamba 26]
“Ndaika pamaso panu moyo ndi imfa”
[Chithunzi patsamba 29]
Kumvera mawu a Mulungu kunapulumutsa Nowa ndi banja lake
[Chithunzi patsamba 30]
Mary Olson
[Chithunzi patsamba 30]
Nancy Porter