Kupambana Nkhondo Yolimbana ndi Kuchita Tondovi
“CHINTHU chothetsa mphamvu chimene ndinayenera kuchita nacho chinali kudzimva waliŵongo la kupanda chiyembekezo popeza kuti, monga mmodzi wa atumiki a Yehova, ndinaganiza kuti sindinafunikire kudzimva motero,” anaulula tero Lola. Kusamvetsetsa kofala kumeneku kaŵirikaŵiri kumakhala mdani woyamba wofunikira kugonjetsedwa ndi Mkristu wochita tondovi. Lola anawonjezera kuti: “Nditangoleka kudzimenya ndekha mwamaganizo chifukwa cha kudzimva monga mmene ndinachitira ndi kusumika pa kuwongokera, ndinakhoza kuchita ndi kuchita tondoviko.” Inde, kuchita tondovi mwa iko kokha sikuli chifukwa cha kulingalira kuti mwamlakwira Mulungu.
Monga momwe zatchulidwa kale mu nkhani yapita, zochititsa kuchita tondovi zingakhale zakuthupi. Mu 1915, kale kwambiri kufufuza kwamakono kogwirizanitsa kuchita tondovi ndi matenda akuthupi kusanayambe, The Watch Tower inalongosola kuti: “Kulemedwa ndi malingaliro kumeneku, kapena kudzimva wosungulumwa ndi wochita tondovi, nkwachibadwa pa nthaŵi zina kwa mtundu wa anthu . . . [Iko] kumakulitsidwa ku mlingo winawake ndi mkhalidwe wakuthupi wa umoyo.” Chotero, ngati mkhalidwe wa kuchita tondovi ulipo, kufufuza kochitidwa ndi dokotala kungakhale kothandiza. Ngati mkhalidwewo ngoipa kwambiri, mungafunikire thandizo la katswiri wa kuchita tondovi.a
Komabe ngakhale ngati chochititsa sichiri chakuthupi, nkopanda nzeru kulingalira kuti mtumiki wa Mulungu sadzavutika konse ndi chisoni kapena kukhumudwitsidwa. Tangolingalirani mmene Hana wokhulupirika anakhalira ndi ‘mtima wowawa naliratu misozi.’ (1 Samueli 1:7, 10) Nehemiya nayenso ‘analira misozi ndi kuchita maliro masiku ena’ ndipo anali ndi “chisoni cha mtima.” (Nehemiya 1:4; 2:2) Yobu ananyoza moyo wake naganiza kuti Mulungu anamutaya. (Yobu 10:1; 29:2, 4, 5) Mfumu Davide ananena kuti mzimu wake unakomoka ndipo mtima wake unatenga nkhaŵa. (Salmo 143:4) Ndipo mtumwi Paulo analankhula za kukhala ndi “m’katimo mantha” ndi kukhala “odzichepetsa” kapena “ogwetsedwa” mwamaganizo.—2 Akorinto 4:9; 7:5, 6.
Ngakhale kuti onsewa anali atumiki okhulupirika a Mulungu, zipsyinjo, nkhaŵa zosiyanasiyana, zitsutso, kapena zokhumudwitsa zowawa zinawapangitsa kumva chisoni kwa nthaŵi inayake. Komabe, Mulungu sanawataye kapena kuwachotsera mzimu wake woyera. Mkhalidwe wawo wochita tondovi sunali chifukwa cha kulephera kwauzimu. Pa nthaŵi imene Davide anakanthidwa, anachonderera m’pemphero kuti: “Kondweretsani moyo wa mtumiki wanu.” Mulungu anatonthoza Davide mkati mwa ‘tsiku la msauko’ ndipo m’kupita kwa nthaŵi anamthandiza kukondwera. (Salmo 86:1, 4, 7) Mofananamo Yehova adzathandiza atumiki ake tsopano.
Popeza kuti kuchita tondovi mwa iko kokha sikuli umboni wa kulephera kwauzimu kapena kufooka kwamaganizo, Mkristu wokanthidwa nako sayenera kukhala chete chifukwa cha manyazi. M’malomwake, ayenera kutenga limodzi la masitepe ofunika koposa m’kulimbana ndi vuto limeneli. Kodi ilo nchiyani?
Tsanulani Maganizo Anu
Ayenera kulankhula ndi winawake ponena za icho. Miyambo 12:25 ikulongosola kuti: “Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu; Koma mawu abwino aukondweretsa.” Palibe munthu wina aliyense amene angadziŵe ukulu wa nkhaŵa imene iri mu mtima mwanu kusiyapo kokha ngati mutamasuka ndi kulankhula za iyo. Mwakudalira mwa munthu wolingalira ena amene angathandize, mwachidziŵikire mungadziŵe kuti ena adali ndi malingaliro ndi mavuto ofananawo. Ndiponso, kusonyeza kudzimva kwanu m’mawu kulinso njira yochiritsa, popeza kumamasula chochitika chowawacho m’malo mochisunga. Chotero, miyoyo yochita tondovi iyenera kudalira mwa mnzawo wa mu ukwati, kholo, kapena bwenzi lofikapo mwauzimu ndi lachifundo.—Agalatiya 6:1.
Mbali ina ya vuto la Marie (wotchulidwa m’nkhani yapitayo) inali yakuti anasunga malingaliro ovutitsa amene anatsogoza ku kuchita kwake tondovi. “Kwa zaka zonsezi, ndachita chinyengo chimenechi,” iye anatero. “Ena sakanalota kuti ndinali ndi vuto lochita ndi kudzimva wopanda pake.” Koma Marie analankhula kwa mkulu wa mu mpingo. Kudzera mwa mafunso olingalira mkuluyo ‘anatunga’ mu mtima mwake nkhaŵa imene anali nayo ndi kumthandiza kudzimvetsetsa. (Miyambo 20:5) Mawu ake abwino ochokera m’Malemba anampatsa chitsimikizo. “Kwa nthaŵi yoyamba, ndinayamba kupeza thandizo la kuchita ndi malingaliro ena amene anadzetsa kuchita kwanga tondovi,” analongosola motero Marie.
Chotero kulankhula kwa mkulu womvetsetsa kungapereke “madzi” odzetsa mpumulo mwauzimu kwa wina amene “moyo [wake] ulira . . . monga dziko lolira mvula.” (Yesaya 32:1, 2; Salmo 143:6) Phungu wolingalira wauzimu angakuthandizeni kuwona mmene mungatengere masitepe othandiza kuchita ndi umene mungawuganizire kukhala mkhalidwe wopanda chiyembekezo. (Miyambo 24:6) Koma zambiri zimafunikira koposa kudalira mwa wina.
Zindikirani Phindu Lanu Lenileni
Malingaliro a kupanda pake ali nsonga yaikulu m’kuchita tondovi. Mwinamwake chifukwa cha ubwana wopanda chimwemwe, Akristu ena ali ndi ulemu waumwini wochepera. Komabe ngakhale kuti kuipsyidwa kwakuthupi, maganizo, kapena kwakugonana kwa nthaŵi yakale kwasiya zipsyera zamaganizo, zimenezi sizimasintha mtengo wa munthu. Chotero, muyenera kukalimira kukhala ndi kawonedwe kolinganizika ka phindu lanu lenileni monga munthu. “Ndingawuze munthu aliyense wa inu,” anafulumiza tero mtumwi Paulo, “kuti asadziyese koposa pa phindu lake lenileni, koma aganize modziletsa yekha.” (Aroma 12:3, Charles B. Williams) Pamene mukuchenjera ndi kudzikuza, muyenera kuyesera kusanka ku mapeto enawo. Awo amene ali ndi unansi ndi Mulungu ali ofunika, okhumbirika kwa iye, popeza kuti amasankha anthu kuti akhale “chuma [chake] chapadera.” Ndi mwaŵi wapamwamba wotani nanga!—Malaki 3:17; Hagai 2:7.
Ndiponso, uli ulemu wotani nanga kukhala “antchito anzake a Mulungu” mwa kudziloŵetsa mu ntchito Yachikristu ya kupanga ophunzira. (1 Akorinto 3:9; Mateyu 28:19, 20) Akristu ambiri ochita tondovi apeza kuti ntchito imeneyi imamangirira mtengo waumwini. “Ngakhale pambuyo pokhala Mkristu, ndinadzimva kukhala wosakwanira,” anavomereza motero Marie. Komabe, analimbikira mu ntchito yolalikira, ndipo tsiku lina anakumana ndi mkazi wovulala ubongo amene anafuna kuphunzitsidwa Baibulo. “Iye anafunikira winawake amene akakhala woleza mtima, popeza kuti anali wophunzira mochedwa,” anatero Marie. “Popeza kuti anatenga chisamaliro changa chachikulu, ndinaiwala za inemwini ndi kusakwanira kwanga. Iye anafunikira thandizo langa, ndipo ndinazindikira kuti ndingalipereke kwa iye ndi mphamvu ya Yehova. Kumuwona iye akubatizidwa kunandilimbikitsa kwabasi. Ulemu wanga waumwini unakula, ndipo kuchita tondovi kwakukuluko kunazimiririka.” Ha, nzowonadi kuti “wothirira madzi nayenso adzathiriridwa”!—Miyambo 11:25.
Komabe, anthu ambiri ochita tondovi amayankha monga mmene anachitira mkazi Wachikristu wochita tondovi moipitsitsa, amene anavomereza kuti: “Ngakhale kuti ndimagwira ntchito mwamphamvu kukonza m’nyumba ndi kuphika ndi kukhala wochereza, ndimatembenuka ndi kudzitsutsa pa kuphophonya kochepa kulikonse.” Kupeza zolakwa kosayenerera koteroko kumatsitsa ulemu waumwini. Kumbukirani kuti Mulungu wathu ndi womvetsetsa ndipo “satsutsana nawo nthaŵi zonse.” (Salmo 103:8-10, 14) Ngati Yehova, amene ali ndi kulingalira kwapamwamba kwa chabwino kuposa ife, samatitsutsa pa chophophonya chirichonse chaching’ono ndipo ali wofunitsitsa kusonyeza chifundo choterocho, kodi sitiyenera kukalimira kumtsanzira m’zochita zathu ndi ife eni?
Tonsefe tiri ndi zophophonya ndi zifooko. Komabe, tirinso ndi mphamvu. Mtumwi Paulo sanayembekezere kuchita bwino moposapo m’zoyesayesa zake zonse. “Ndipo ndingakhale ndiri wosaphunzira m’manenedwe, koma sinditero m’chidziwitso,” analongosola motero. Paulo sanadzimve wotsika kokha chifukwa chakuti mwina sakanapambana m’kulankhula poyera. (2 Akorinto 11:6) Mofananamo, ochita tondovi ayenera kulunjikitsa pa zinthu zimene amachita bwino.
“Nzeru iri ndi odzichepetsa,” kapena awo amene amazindikira ndi kuvomereza zopereŵera zawo. (Miyambo 11:2) Aliyense wa ife ali munthu wapadera wokhala ndi mikhalidwe yosiyana, mphamvu yakuthupi, ndi maluso. Pamene mukutumikira Yehova ndi mtima wonse, mukumachita zimene mungathe, iye amakondweretsedwa. (Marko 12:30-33) Mulungu sali amene samakhutiritsidwa ndi zoyesayesa za alambiri ake odzipereka. Leora, Mkristu amene analimbana mwachipambano ndi kuchita tondovi kwake, ananena kuti: “Sindimachita bwino kwambiri mofanana ndi wina aliyense m’zinthu zina, monga ngati ulaliki mu utumiki wakumunda. Koma ndikuyesera. Zimene ndimachita ndizo zabwino koposa zanga.”
Kusamalira Zophophonya ndi Kusamvana
Komabe, kodi bwanji ngati mupanga chophophonya chachikulu? Mwinamwake mumadzimva ngati Mfumu Davide, amene ‘anayenda woliralira tsiku lonse’ chifukwa cha zolakwa zake, kapena chimo. Koma kudzimva kotereku kungakhale umboni wakuti simunapite patali ndi kupanga chimo losakhululukidwa! (Salmo 38:3-6, 8) Malingaliro a liŵongo angasonyeze kuti wina amene wachimwa ali ndi mtima wowona ndi chikumbumtima chabwino. Chotero kodi liŵongolo lingasamaliridwe motani? Chabwino, kodi munayamba mwapempherera chikhululukiro cha Mulungu ndi kutenga masitepe a kuwongolera cholakwacho? (2 Akorinto 7:9-11) Ngati nditero, khalani ndi chikhulupiriro m’chifundo cha Iye amene amakhululukira kwakukulu, pamene muli ogamulapo kusabwerezanso cholakwacho. (Yesaya 55:7) Ngati munapatsidwa chilango, ‘musakomoke podzudzulidwa, pakuti iye amene Yehova amkonda amlanga.’ (Ahebri 12:5, 6) Kuwongolera koteroko kuli ndi cholinga chothandiza kukhazikitsanso nkhosa yosokera. Sikumamchotsera phindu lake monga munthu.
Ngakhale ngati mtima wathu weniweni utitsutsa, sitifunikira kumaliza kuti Yehova watisiya ife. “Tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pake, mmene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.” (1 Yohane 3:19, 20) Yehova amawona zoposa machimo athu ndi zophophonya. Iye amadziŵa za mikhalidwe yovuta, njira yathu yonse ya moyo, zolinga zathu ndi zifuno. Ukulu wa chidziŵitso chake umamtheketsa kumva mwachifundo mapemphero athu owona mtima kaamba ka chikhululukiro, monga mmene anamverera la Davide.
Kusamvana ndi ena ndi kukhala wodera nkhaŵa mopambanitsa ponena za kukhala ndi chivomerezo chawo kumathandiziranso ku kusoŵeka kwa kuyenera kwaumwini, mwinamwake kudzimva wokanidwa. Chifukwa cha kupanda ungwiro, Mkristu mnzathu angalankhule kwa inu m’njira imene ingawoneke kukhala yosalingalira kapena yopanda chifundo. Chikhalirechobe, kusamvana kwambiri kungathetsedwe mwakumuuza munthu mmene munayambukiridwira ndi ndemangayo. (Yerekezerani ndi Mateyu 5:23, 24.) Ndiponso, Solomo analangiza kuti: “Mawu onsetu onenedwa usawalabadire.” Chifukwa ninji? “Pakuti kaŵirikaŵiritu mtima wako udziŵa kuti nawenso unatemberera ena.” (Mlaliki 7:21, 22) Musadzinyenge mwakuyembekezera ungwiro kuchokera kwa inueni kapena ubwenzi wanu ndi anthu ena opanda ungwiro. Khalani wachangu kukhululukira ndi kulolerana.—Akolose 3:13.
Kuwonjezerapo, phindu lanu lenileni silimayesedwa kwakukulukulu ndikuti kaya mumakondedwa ndi ena kapena ayi. Kristu ‘sanalemekezedwe,’ ndipo ‘anayesedwa ndi muyeso wa ena’ waung’ono kwambiri. (Yesaya 53:3; Zekariya 11:13) Kodi zimenezi zinasintha mtengo wake weniweni kapena njira imene Mulungu anamuwonera? Ayi, popeza kuti ngakhale ngati tinali angwiro, mofanana ndi Yesu, sitikanakondweretsa aliyense.
Mphamvu ya Kupirira
Nthaŵi zina, kuchita tondovi kwakukulu kungakhalire mosasamala kanthu za zoyesayesa zathu za kukulaka. Kupweteka kwamaganizoko kungapangitse Akristu ena kudzimva monga mmene Yona anachitira: “Kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ayi.” (Yona 4:1-3) Komabe, kuipidwa kwake sikunali kosatha. Anakulaka. Chotero ngati kuchita tondovi kukuchititsa moyo wanu kukhala wosapiririka, kumbukirani kuti kuli kofanana ndi chisautso chimene Paulo ananena kuti chinali “cha kanthaŵi.” (2 Akorinto 4:8, 9, 16-18, NW) Chidzatha! Palibe mkhalidwe womwe uli wopanda chiyembekezo. Yehova akulonjeza “kudzutsanso mtima wa awo amene akumva kuwawa.”—Yesaya 57:15, Lamsa.
Musaleke konse kupemphera, ngakhale ngati mapemphero anu akuwoneka kukhala opanda phindu. Davide anachonderera kuti: “Imvani mpfuu wanga, Mulungu . . . pomizika mtima wanga: Nditsogolereni ku thanthwe londiposa ine m’kutalika kwake.” (Salmo 61:1, 2) Kodi ndimotani mmene Mulungu amatitsogolera ku chidaliro chamkati chimene chimawoneka kukhala chosafikirika ndi mphamvu yathu? Eileen, yemwe walimbana ndi kuchita tondovi kwa zaka zambiri, akuyankha kuti: “Yehova sanandilole kuleka. Zimenezi zimandipatsa chiyembekezo chakuti ngati ndipitirizabe kuyesayesa, iye adzapitirizabe kundithandiza. Kudziŵa chowonadi Chabaibulo kwandipangitsa kukhala wamoyo. Kupyolera m’njira zambiri—pemphero, uminisitala, misonkhano, mabuku, banja, ndi mabwenzi—Yehova wapereka nyonga yakuti ndipitirizebe kuyesera.”
Wonani vutolo kukhala chiyeso cha chikhulupiriro chanu. “Mungakhulupirire Mulungu,” mtumwi Paulo akutitsimikizira. “Sadzalola kuti muyesedwe koposa kumene mungathe kupirira. Koma pamene muyesedwa, Iye adzapanganso njira yotulukira kotero kuti mupirire.” (1 Akorinto 10:13, Beck) Inde, Mulungu adzakupatsani “ukulu woposa wamphamvu” kuti munyamule katundu aliyense wa maganizo.—2 Akorinto 4:7.
Dziko Latsopano Lopanda Tondovi!
Mulungu walonjeza kuchotsapo posachedwapa, kupyolera mwa Ufumu wake wakumwamba, mikhalidwe yonse yochititsa tondovi pa dziko lathu lapansi. Mawu ake akulengeza kuti: “Ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga.” (Yesaya 65:17, 18) Mawu ameneŵa anakwaniritsidwa choyamba mu 537 B.C.E., pa nthaŵi imene mtundu wakale wa Israyeli unabwezeretsedwa ku dziko lakwawo. Anthu ake panthaŵiyo anaimba kuti: “Tinakhala ngati anthu akulota. Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, Ndi lilime lathu linafuula mokondwera.” (Salmo 126:1, 2) Chidzakhala chachikulu koposa chotani nanga chikwaniritso chomwe chiri pafupi kukwaniritsidwa cha ulosi wotonthoza mtima wa dziko latsopano la Mulungu!—2 Petro 3:13; Chibvumbulutso 21:1-4.
Pansi pa Ufumu wa Mulungu (“miyamba yatsopano”), chitaganya cholungama cha anthu pa dziko lapansi (“dziko lapansi latsopano”) adzabwezeretsedwa ku umoyo wangwiro wamaganizo, wakuthupi, ndi wauzimu. Sikuti ameneŵa sadzakumbuka zakale, koma poganizira zinthu zabwino zonse zimene adzazilingalira ndi kusangalala nazo, sipadzakhala chifukwa kwa iwo cha kukumbukira kapena kusumika maganizo pa zokumana nazo zoipa zakale. Tangolingalirani, kudzuka m’mawa uliwonse ndi maganizo abwino owala, ofunitsitsa kuchita ntchito ya tsikulo—osatsekerezedwa konse ndi mkhalidwe wa kuchita tondovi!
Akumakhala wokhutiritsidwa kotheratu za kuwona kwa chiyembekezo chimenechi, Lola (wotchulidwa poyambirirayo), ananena kuti: “Kukumbukira kuti Ufumu wa Yehova udzawongola mavuto ameneŵa kunali thandizo langa lalikulu kwambiri. Ndinadziŵa kuti kuchita tondovi sikudzakhalako kosatha.” Inde, mungakhale otsimikizira kuti posachedwapa Mulungu adzagonjetsa kotheratu kuchita tondovi!
[Mawu a M’munsi]
a Wonani “Attacking Major Depression—Professional Treatments” m’kope la Awake! la October 22, 1981.