Zolengedwa Zatsopano Zipangidwa!
KALELO Mfumu yanzeru Solomo inati: “Palibe kanthu katsopano pansi pano.” (Mlaliki 1:9) Zimenezo nzowona ponena za dziko lakuthupi limene tikukhalamo, koma bwanji ponena za malo aakulukulu achilengedwe chauzimu a Yehova? M’malo amenewo, ndithudi wamkulu kwambiri kuposa Solomo, amene anali munthu wamkulu koposa onse anakhalapo, anafikira kukhala cholengedwa chatsopano chapadera. Kodi izi zinachitika motani?
M’chaka cha 29 cha Nyengo yathu Ino, munthu wangwiro, Yesu, anadzipereka kukabatizidwa ndi Yohane mu Mtsinje wa Yordano. ‘Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m’madzi: ndipo wonani, miyamba inamtsegukira iye, ndipo anapenya mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa iye; ndipo wonani, mawu akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.’ (Mateyu 3:16, 17) Chotero, munthuyo Kristu Yesu anali woyamba wa chilengedwe chatsopano, wodzozedwera kuchita chifuniro cha Mulungu. Pambuyo pake, pamaziko a imfa yake yopereka nsembe, Yesu anakhala Nkhoswe ya pangano latsopano pakati pa Mulungu ndi kagulu ka anthu osankhidwa. Aliyense wa amenewa wafikira kukhala “chilengedwe chatsopano,” wobadwa ndi mzimu wa Mulungu kuchiyembekezo chakumwamba, akuyembekezera kudzalamulira limodzi ndi Yesu mu Ufumu wake wakumwamba.—2 Akorinto 5:17; 1 Timoteo 2:5, 6; Ahebri 9:15.
M’kupita kwa zaka mazana ambiri, odzozedwa amenewa, Akristu obadwa ndi mzimu asonkhanitsidwira m’chigwirizano ndi Kristu monga mpingo wowona Wachikristu, umene mwa uwo wokha uli chilengedwe chatsopano. Mulungu anautulutsa m’dziko lino kaamba ka chifuno, monga momwe mtumwi Petro akufotokozera kuti: ‘Inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, muloŵe kuunika kwake kodabwitsa.’ (1 Petro 2:9) Mofanana ndi Kristu Yesu, chilengedwe chatsopano choyamba cha Mulungu, chilengedwe chatsopano chotsatira chimenechi chiri ndi thayo lalikulu lakulalikira mbiri yabwino. (Luka 4:18, 19) Aliyense payekha, ziŵalo zake, zonse pamodzi zokwanira 144,000, ziyenera ‘kuvala umunthu watsopano, umene unalengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero.’ (Aefeso 4:24; Chivumbulutso 14:1, 3) Izi zifunikiritsa kuti iwo akulitse ‘zipatso za mzimu,’ zofotokozedwa pa Agalatiya 5:22, 23, ndi kusamalira udindo wawo mokhulupirika.—1 Akorinto 4:2; 9:16.
Bwanji ponena za chilengedwe chatsopano chimenechi m’nthaŵi zamakono? M’chaka cha 1914, monga momwe programu yanthaŵi ya Baibulo imasonyezera, mawu a pa Chivumbulutso 11:15 anakwaniritsidwa akutiwo: ‘Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu [Yehova], ndi wa Kristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthaŵi za nthaŵi.’ Chochita choyamba cha Kristu monga Mfumu yoikidwa chatsopano paufumu chinali chakuponya Satana ndi angelo ake auchiŵanda kuchokera kumwamba kudza pafupi ndi dziko lapansi. Izi zinadzetsa “tsoka mtunda ndi nyanja,” mumpangidwe wa nkhondo yoyamba yadziko ndi nsautso zake zotulukapo.—Chivumbulutso 12:9, 12, 17.
Zimenezi zinatumikiranso kusonyeza kwa otsalira achilengedwe chatsopano padziko lapansi kuti ayenera kukhala ndi phande m’kukwaniritsa ulosi wa Yesu wakuti: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu [wokhazikitsidwa] idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” Kodi “mapeto” amenewo nchiyani? Yesu akupitirizabe kufotokoza kuti: “Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitike chiyambire chiyambi cha dziko kufikira tsopano, inde, ndipo sichidzachitikanso. Kunena zowona, ngati akadapanda kufupikitsidwa masiku amenewo, palibe munthu aliyense amene akadapulumutsidwa; koma chifukwa cha osankhidwa masiku amenewo adzafupikitsidwa.”—Mateyu 24:3-14, 21, 22, NW.
Mzimu wa Yehova unasonkhezera odzozedwawo a chilengedwe chake chatsopano kutanganitsidwa mu mkupiti wakulalikira waukulu koposa yonse imene inachitika pa dziko lino lapansi. Kuchokera pa zikwi zochepekera mu 1919, chiŵerengero cha olengeza Ufumu achangu amenewa chinawonjezereka kufikira pafupifupi 50,000 podzafika pakati pa ma 1930. Monga momwe kunaloseredwera, ‘liwu lawo linatulukira kudziko lonse lapansi, ndi maneno awo kumalekezero a dziko lokhalamo anthu.’—Aroma 10:18.
Kodi otsalira achilengedwe chatsopano akakhala osonkhanitsidwa okha kuti apulumuke? Ayi, pakuti ulosi unafotokoza kuti angelo a Mulungu akagwira mphepo za chisautso chachikulu kufikira kusonkhanitsidwa kunamalizidwa osati kwa Aisrayeli auzimu achiyembekezo chakumwamba okha amenewa komanso kwa ena, a ‘khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.’ Kodi chiyembekezo chawo chikakhala chotani? Eya, iwo akatuluka osavulazidwa mu “chisautso chachikulu” kusangalala ndi moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso!—Chivumbulutso 7:1-4, 9, 14.
Mokondweretsa, khamu lalikulu limeneli, losonkhanitsidwa kuchokera m’maiko pafupifupi 229, lawonjezereka mofulumira kufikira Mboni zokangalika pafupifupi 4,500,000. Ena owonjezereka akudza, monga momwe kwasonyezedwera ndi okwanira 11,431,171 ofika pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu pa April 17 chaka chatha. Mwa mamiliyoni onsewa, okwanira 8,683 okha, amene amadzinenera kukhala otsalira padziko lapansi a chilengedwe chatsopano, anadya zizindikiro za Chikumbutso. Akagulu kochepa kameneka sakanatha konse, mwa iwo okha, kukwaniritsa ntchito yolalikira yonse ya lerolino. Mamiliyoni amene tsopano amapanga khamu lalikulu amagwira ntchito phewa ndi phewa limodzi nawo kuti ntchitoyo itsirizidwe. (Zefaniya 3:9) Ndiponso, ziŵalo zophunzitsidwa bwino za khamu lalikulu tsopano zikuchita ntchito zakuyang’anira ndi ntchito zina limodzi ndi Bungwe Lolamulira la odzozedwa Aisrayeli wauzimu, monga momwe Anetini osakhala Aisrayeli anagwirira ntchito limodzi ndi ansembe pokonzanso malinga ogumuka a Yerusalemu.—Nehemiya 3:22-26.
Chilengedwe cha “Miyamba Yatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano”
Nchikondwerero chotani nanga chimene chikutsagana ndi kusonkhanitsa kumeneku! Kuli monga momwedi Yehova ananenera kuti zikatero: “Pakuti tawonani, ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala, ku nthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga; pakuti tawonani, ndilenga Yerusalemu wosangalala ndi anthu ake okondwa. Ndipo ndidzasangalala m’Yerusalemu, ndi kukondwera mwa anthu anga; ndipo mawu akulira sadzamvekanso mwa iye, pena mawu akufuula.” (Yesaya 65:17-19) Miyamba yatsopano yolengedwa ndi Yehova potsirizira pake idzaphatikizapo Kristu Yesu ndi ziŵalo zoukitsidwa za a 144,000 achilengedwe chatsopano amene agulidwa kuchokera mwa anthu mkati mwa zaka mazana 19 zapitazo. Ilidi yaulemerero kwambiri kuposa boma lina lirilonse la padziko lapansi limene linalamulirapo Yerusalemu weniweni, ngakhale la m’tsiku la Solomo. Limaphatikizapo Yerusalemu Watsopano, mzinda wakumwamba, wofotokozedwa kukhala wokongola monyezimira m’Chivumbulutso chaputala 21.
Yerusalemu watsopano ndiye mkwatibwi wauzimu wa Kristu, otsatira ake odzozedwa a 144,000, amene amagwirizana ndi Mkwati wawo kumwamba pambuyo pa imfa yawo ndi chiukiriro chauzimu. Iwo akuchitiridwa chithunzi pa Chivumbulutso 21:1-4 kukhala “ulikutsika kumwamba kwa Mulungu,” ndiko kuti, ukugwiritsidwa ntchito ndi iye m’kupereka madalitso kwa anthu pano pa dziko lapansi. Mwanjirayi ulosi ukukwaniritsidwa wakuti: ‘Tawonani, chihema cha Mulungu chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵawitsa; zoyambazo zapita.’
Tingakhale oyamikira chilengedwe cha Mulungu cha miyamba yatsopano imeneyo chotani nanga! Mosiyana ndi maulamuliro osinthasintha, opanda chilungamo amene kwanthaŵi yaitali avutitsa mtundu wa anthu, kakonzedwe ka boma la Mulungu kameneka kadzakhala kachikhalire. Chilengedwe chatsopano ndi ana ake auzimu, khamu lalikulu, akusangalala ndi zimene Mulungu akulonjeza mowonjezera kuti: “Pakuti monga m’mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano limene ndidzalenga, lidzakhalabe pamaso pa ine, ati Yehova, momwemo adzakhalabe ana anu ndi dzina lanu.”—Yesaya 66:22.
“Dziko lapansi latsopano” likuyamba ndi mbadwa zimenezi za odzozedwa a chilengedwe chatsopano. Chiri chitaganya chatsopano, chowopa Mulungu cha anthu padziko lapansi. Udani, upandu, chiŵawa, chisalungamo, ndi chisembwere m’chitaganya cha anthu lerolino zasonyezadi kufunika kwa kusinthira kotheratu ku chimangidwe cha dziko latsopano, chogwira ntchito motsogozedwa ndi miyamba yatsopano yaulemerero. Ndizo zimene Yehova walinganiza. Monga momwe walengera miyamba yatsopano, chotero iye akulenga dziko lapansi latsopano mwakusonkhanitsa khamu lalikulu kukhala maziko a chitaganya cha dziko latsopano cha mtendere. Chitaganya chokhachi, chidzapulumutsidwa chiri chamoyo “kutuluka m’chisautso chachikulu.”—Chivumbulutso 7:14.
Kodi tingayembekezere chiyani pambuyo pa chisautso chachikulu? Polankhula kwa atumwi ake, oyambirira a awo opanga miyamba yatsopano imene idzalamulira dziko lapansi latsopano, Yesu analonjeza kuti: ‘Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata ine, m’kubadwanso, pamene Mwana wa munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iŵiri.’ (Mateyu 19:28) A 144,000 onsewo a Yerusalemu Watsopano ameneyu adzakhala ndi phande limodzi ndi Yesu kuweruza mtundu wa anthu. Pamenepo chikondi chidzaloŵa mmalo dyera ndi udani monga maziko pamene chitaganya chaumunthu chidzamangidwapo. Mavuto aufuko, amawonekedwe akhungu, ndi autundu adzachotsedwa. Mwapang’onopang’ono chiukiriro chidzabwezeretsera okondedwawo ku moyo. Mabiliyoni a anthu okhulupirika adzafikira kukhala banja limodzi lalikulu logwirizana, otukulidwira ku moyo wosatha padziko lapansi losandulizidwa kukhala paradaiso.
Zimenezi sizidzakhala kokha kuyerekezera kapena zamkhutu. Zidzakhala chilengedwe chachikhalire—“miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo lake, ndipo m’zimenezi chilungamo chidzakhalamo”! (2 Petro 3:13, NW) Ndithudi, chimenechi chiri chiyembekezo chabwino koposa, lonjezo laulemerero loperekedwa ndi uyo amene anati: “Tawonani, ndikupanga zinthu zonse zatsopano,” ndi amene anawonjezera mawu olimbikitsa chikhulupiriro akutiwo: “Mawu awa ali okhulupirika ndi owona.”—Chivumbulutso 21:5, NW.