Kulungamitsa Zinthu Pakati pa Mulungu ndi Inu
“Ngakhale zoipa zanu ziri zofira, zidzayera ngati matalala.”—YESAYA 1:18.
1, 2. (a) Nchiyani chimene mungalingalire ngati wina wake ananena kuti “Idzani tsopano, ndipo lolani tilingalire pamodzi?” (b) Nchifukwa ninji sitifunikira kuyembekezera kukhala ndi kupereka ndi kutenga ndi Mulungu?
NGATI, CHIFUKWA cha cholakwa china chakale kapena kupanda kukoma mtima, unansi womangika unakhalapo pakati pa inu ndi wina, ndimotani mmene mungayankhire ku mawu awa: “Bwerani tsopano, ndipo tiyeni tilingalire pamodzi”? Chimenechi chingakhale chiitano cha kukhala pansi kaamba ka kupereka ndi kutenga, ndi chigwirizano chenicheni ndi kugonjerana. Aliyense angapereke kawonedwe kake, ndipo aliyense angavomereze ukulu wina wa kulakwa kapena kusamvetsetsa.
2 Koma kodi inu mungalingalire kuti Mlengi m’nkhani imeneyi angachonderere, “Bwerani tsopano, ndipo tiyeni tilingalire pamodzi,” monga mmene Yesaya 1:18 amaŵerengera m’maBaibulo ambiri? Kutalitali. Palibe aliyense wa ife amene angayembekezere “kukangana” (The New English Bible) kapena kukhala ndi kupereka ndi kutenga ndi Yehova, ngati kuti iye angafune kuvomereza cholakwa ndi kugonjera. Ngati, ngakhale kuli tero, tikufuna mtendere ndi Mulungu, nchiyani chimene Yesaya 1:18 akufuna?
3. Ndi liti limene liri lingaliro loyenerera la liwu la Chihebri limene nthaŵi zina limatembenuzidwa “kulingalira pamodzi” pa Yesaya 1:18?
3 Liwu la Chihebri logwiritsiridwa ntchito kuti “kulingalira limodzi” m’chenicheni limatanthauza “kusankha, kugamulapo, kutsimikizira.” Liri ndi zokometsera za lamulo, kusonyeza kokha anthu oposa aŵiri akulingalira pamodzi. Chosankha chinaphatikizidwapo.a (Genesis 31:37, 42; Yobu 9:33; Masalmo 50:21; Yesaya 2:4) Wilson’s Old Testament Word Studies amapereka tanthauzo iri “Kukhala wolondola, kulingalira, kusonyeza chimene chiri cholondola ndi chowona.” Mulungu anali kulamula: “Bwerani tsopano, tiyeni tilungamitse nkhani (The New American Bible) kapena, “Tiyeni tilungamitse zinthu.”
4-6. Ndi ndani amene anali Yesaya, ndipo ndi liti pamene anayamba kutumikira monga mneneri?
4 Yehova Mulungu anagwiritsira ntchito mneneri Yesaya kupereka uthenga wamphamvu umenewu. Kodi Yesaya anali ndani, ndipo nchifukwa ninji uthenga wake unali woyenerera m’nthaŵi yake? M’kuwonjezerapo, ndimotani mmene tingapindulire kuchokera ku iwo?
5 Pa kutchulidwa kwa “mneneri,” ambiri lerolino angapange malingaliro a mwamuna wachichepere wodzikana kotheratu yemwe anali kulalikira kawonedwe kake kosokonezeka ka zenizeni. Ena angalingalire za munthu wakale wampatuko yemwe anadzipangitsa iyemwini monga woweruza wa mikhalidwe ya panthaŵiyo. Ndimosiyana naye chotani nanga mmene analiri munthu wolinganizika ndi wodziŵa kulinganiza Yesaya, amene Yehova Mulungu anam’gwiritsira ntchito kulemba bukhu la Baibulo lokhala ndi dzina lake!
6 “Yesaya mwana wa Amozi” anakhala mu Yuda ndipo mokangalika anatumikira Yehova “m’masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a Yuda,”—zaka zoposa 40. Modzichepetsa, Yesaya sanapereke chidziŵitso chambiri ponena za iyemwini. Mwambo umanena kuti iye anali wogwirizana ndi banja la chifumu la Yuda. Timadziŵa motsimikizirika kuti iye anali munthu wa banja amene mkazi wake anamubalira iye ana amuna aŵiri. Iye angakhale anakwatiranso pamene mkazi wake anafa, kukhala tate wa mwana wa mwamuna wina, mwaulosi wotchedwa Imanueli.—Yesaya 1:1; 7:3, 14; 8:3, 18.
7. Nchifukwa ninji tiyenera kukhala osangalatsidwa mu ulosi wa Yesaya?
7 Pali kufanananso pakati pa nthaŵi ya Yesaya ndi yathu. Mwawona kale kuti tikukhala m’nthaŵi ya kupsyinjika kwa mitundu yonse, kwa nkhondo kapena chiwopsyezo. Pamene atsogoleri a chipembedzo ndi andale zadziko akudzinenera kukhala akulambira Mulungu amadziwonetsera iwo eni kukhala monga zitsanzo zoti zitsatiridwe, ife mokhazikika timawona maripoti a manyuzipepala a kusakaza kwawo ndalama ndi makhalidwe abwino. Ndimotani mmene Mulungu amawonera atsogoleri oterowo, makamaka awo ogwirizana ndi Dziko la Chipembedzo? Nchiyani chimene chiri kutsogolo kaamba ka iwo ndi awo amene amawatsatira? M’bukhu la Yesaya, timapeza ndemanga zaumulungu zomwe ziri zogwira ntchito koposa ku mikhalidwe yatsopano yotereyi. Tikupezanso maphunziro kaamba ka aliyense wa ife pamene mwaumwini tikukalamira kutumikira Mulungu.
Mneneri ku Mtundu Wolakwa
8. Nchiyani chimene bukhu la Yesaya liri nacho, ndipo ndi mu mtundu wotani mmene linalembedwera?
8 Kuŵerenga bukhu la Yesaya, mudzapeza uthenga wonena za kulakwa kwa Yuda ndi Yerusalemu, tsatanetsatane wa mbiri ya kulowa kwa adani, zilengezo za kukhalitsidwa bwinja kwa mitundu yowazinga, ndi zoneneratu zolimbikitsa za kubwezeretsedwanso ndi chipulumuko kwa Israyeli. Izi zalembedwa mu mkhalidwe wowoneka bwino, ndi wogwira mtima. Dr. I. Slotki ananena kuti: “Ophunzira amapereka ulemu wa mtima wonse ku kuwala kodabwitsa kwa malingaliro a Yesaya ndi kulongosola kwake kowoneka bwino ndi komveka, lamulo lake la mawu ophiphiritsira amphamvu, kugwiritsira ntchito mawu okhala ndi makonsonati kapena mavawelo ofanana, kugwiritsira ntchito mawu akamvekedwe kofanana, ndi kulinganizika kwabwino ndi kumvekera bwino kwa mawu ofanana katchulidwe m’masentensi ake.” Tiyeni tisanthule m’chenicheni mawu otsegulira a Yesaya—aja opezeka m’mutu 1.
9. Nchiyani chimene tikudziŵa ponena za nthaŵi ndi mikhalidwe ya polembedwa pa Yesaya mutu 1?
9 Mneneriyo sakunena mwachindunji ndi liti pamene analemba mutuwu. Yesaya 6:1-13 amasonyeza masiku kuyambira m’chaka chimene Mfumu Uziya anafa. Chotero ngati kunali kumayambiriro kumene Yesaya analemba mitu yake, iyo ingawunikire mikhalidwe yobisika mkati mwa ulamuliro wa Uziya. M’chenicheni, Uziya (829-777 B.C.E.) “anapitiriza kuchita zowongoka pamaso pa Yehova,” chotero Mulungu anadalitsa ulamuliro wake ndi ulemerero. Komabe, tikudziŵa kuti zonse sizinayende bwino, popeza “anthu anali kuperekabe nsembe ndi kupanga utsi wa nsembe pa malo okwezeka” Mulungu asanakanthe Uziya (kapena, Azariya) ndi khate kaamba ka kupereka kwake kodzitukumula nsembe ya chonunkhira m’kachisi. (2 Mbiri 26:1-5, 16-23; 2 Mafumu 15:1-5) Kuipa komwe kunali m’nthaŵi ya Uziya kungakhale kunatsogolera ku chotulukapo cha kuipa kumene timaŵerenga kokhudza m’dzukulu wake Mfumu Ahazi (762-745 B.C.E.), kumene kungakhalenso kumene Yesaya anali kulongosola. Koma chofunika koposa tsiku lenileni la mutu 1 chiri chimene chinafulumiza Mulungu kunena kuti: “Tiyeni tsono tiweruzane.”
10. Mkati mwa ulamuliro wa Mfumu Ahazi, ndi mkhalidwe wotani umene unalipo mu Yuda, makamaka pakati pa atsogoleri?
10 Yesaya mowona mtima analengeza kuti: “Tsoka ku mtundu wochimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbewu yakuchita zoipa, ana amene achita mowononga! Iwo amsiya Yehova, iwo ananyoza Woyera wa Israeli, iwo adana naye nabwerera m’mbuyo. . . . Mutu wonse ulikudwala, ndi mtima wonse walefuka. Kuchokera pansi pa phazi kufikira kumutu m’menemo mulibe changwiro.” (Yesaya 1:4-6) Ulamuliro wa zaka 16 wa Mfumu Ahazi unazindikirika ndi thayo la kulambira mafano. Iye anapsereza “ana ake a amuna [monga nsembe] m’moto, monga mwazonyansa za amitundu . . . ndipo [mokhazikika, NW] . . . anafukiza kumisanje, ndi ku zitunda, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira.” (2 Mbiri 28:1-4; 2 Mafumu 16:3, 4) Kupanda chilungamo, kudyera chiphuphu, ndi mkhalidwe woipa wa kugonana zinali zopita patsogolo pakati pa akalonga, amene anali oyenerera kukhala olamulira mu Sodomu wakale. (Yesaya 1:10, 21-23; Genesis 18:20, 21) Ndithudi, Mulungu sakanavomereza iwo. Ndipo ndi atsogoleri oterowo, ndimotani mmene anthu akakhalira?
11. Ndimotani mmene tiyenera kumverera Yesaya 1:29, 30?
11 Mneneri Yesaya anachitira chitsanzo mkhalidwe woipa wa anthu mwakutchula mitengo yopatulika ndi minda kumene iwo anapereka nsembe zawo za mafano ndi kutentha zonunkhiza ku milungu ya chikunja. “Mitengo ya mphamvu” imeneyi ikakhala chochititsa manyazi. (Yesaya 1:29; 65:3) Akutembenuzira chithunzicho kwa olambira mafanowo, Yesaya analemba kuti: “Chifukwa mudzakhala ngati mtengo wathundu, umene tsamba lake linyala, ngatinso munda wopanda madzi.” (Yesaya 1:30) Inde, anthu osiya Yehova “angafike ku mapeto awo.” Iwo angakhale ngati chingwe chabwazi (luzi lokhoza kuyaka la bwazi), ndipo mafano awo adzakhala nthethe—zonse zoyenera kudyedwa ndi moto.—Yesaya 1:28, 31.
12, 13. Ndi kufanana nako kotani kumene kungatengedwe pakati pa nthaŵi yathu ndi ya Ye-saya?
12 Tsopano yerekezani chimenecho ndi mkhalidwe lerolino. Mkati mwa mwezi umodzi wokha, ofalitsa nkhani mu United States anasimba kuti: Munthu wotsogolera yemwe anali pa masankho a uprezidenti anasiya m’kangano wa maripoti a “kukonda kwake akazi”; mtsogoleri wotchuka wa chipembedzo analowedwa m’malo pambuyo pa kuvomereza kuchita chigololo ndi kuzengedwa mlandu wa kugonana kwa anthu a ziwalo zofanana, kusinthana akazi, ndi kugwiritsira ntchito molakwika ndalama kulipira chitseka pakamwa. (Iye “akusimbidwa kukhala anatenga ndalama zokwanira $4.6 miliyoni m’kubwezera chiyambire 1984.” Time, May 11, 1987) Mu Austria chaka chatha, Abbot wa ku Rein ‘anachotsedwa ndi kuzengedwa mlandu wa kuba $6 miliyoni pa malo ogona a ku nkhalango ndi mapwando kaamba ka ziwalo za banja lakale lolamulira ndi akazi achichepere osakhala ndi chiyambi cha chifumu.’ Inu mwinamwake mungapereke zitsanzo zina za atsogoleri oterowo. Nchiyani chimene mukuganiza kukhala kawonedwe ka Mulungu pa iwo?
13 Ponena za anthu wamba, pali kusiyana kowonjezereka kwa zipembedzo. Ena amachoka ku chipembedzo oipidwa kapena opanda chikondwerero. Mwachitsanzo, kokha 3 peresenti ya chiŵerengero cha anthu mu England amapezeka pa matchalitchi okhazikitsidwa. Kumbali inayo, timapeza kupanda chipembedzo kokulira. Ichi chiri chowonekera mu zipembedzo zopanda lamulo zomakulakula, zokhala ndi chisonkhezero chawo cha malingaliro cha “kupulumutsidwa,” kulankhula m’malilime, kapena kuwona odwala “akuchiritsidwa.” Makamu amathamangira ku malo opatulika kuyembekezera zozizwitsa. Ena amapanga nsembe monga chisonyezero cha “chikhulupiriro,” monga ngati kukwawa ndi mawondo okukha mwazi kukawona Namwali wa ku Guadalupe [Mexico City]. Nyuzipepala inanena kuti: “Pamene kwa akunja kukhalapo kwake ndi ulemerero umene amalambiridwa nawo ungawoneke kukhala kusakaniza kopanda pake kwa Chikristu ndi chikunja, Namwaliyo ali moyenerera munthu wapamwamba koposa m’Chikatolika cha ku Mexico.”
Mungapeze Motani Chiyanjo Chake?
14. Kupyolera mwa Yesaya, ndimotani mmene Yehova anachimveketsera kuti Iye salandira awo onse odzinenera kukhala akulambira Iye?
14 Yehova Mulungu samasiya kusokonezeka kulikonse ponena za kawonedwe ka awo amene amadzinenera kukhala kumbali yake koma “samalambira Atate mu mzimu ndi m’chowonadi.” (Yohane 4:23) Ngati mtundu, gulu la chipembedzo, kapena munthu sakuchita mogwirizana ndi kaimidwe kovumbulidwa ka Mulungu, zisonyezero ziri zonse za chipembedzo ziri zopanda phindu. Mwachitsanzo, mapwando a chipembedzo ndi nsembe zinafunikira monga mbali ya kulambira kowona m’Israyeli wakale. (Levitiko mitu 1-7, 23) Komabe, Yesaya anakhazikitsa kawonedwe ka Mulungu—komwe sikanakomere Ayuda osakhulupirika omwe anasunga malamulo amenewo. Mulungu anati: “Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu ine sindidzamva.” (Yesaya 1:11-15) Zimenezo ziri zowona chotero lerolino. M’malo mwa mapwando chabe a chipembedzo kapena nthanthi ndi mapemphero oloweza, Mulungu amafuna mapemphero ndi zochita zabwino zomwe zimachokera mu mtima.
15. Nchifukwa ninji Yesaya 1:18 amapereka chifukwa kaamba ka chiyembekezo, ndipo nchiyani chimene chiri tanthauzo la mawu akuti, ‘Idzani ndi kulungamitsa zinthu’?
15 Kudziŵa kwathu zimenezo kumapereka maziko kaamba ka chiyembekezo. Anthu angapeze chiyanjo cha Mulungu. Motani? Yesaya anafulumiza kuti: “Sambani, dziyeretseni, chotsani machitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kuchita zoipa. Phunzirani kuchita zabwino; funani chilungamo.” Pa nsonga imeneyi Yesaya anapereka lamulo la Mulungu: “Tiyeni, tsono, tiweruzane.” Chotero Yehova sanali kufunsa kaamba ka gawo pakati pa anthu ofanana omwe akakhala pansi limodzi kaamba ka kupereka ndi kutenga. Mulungu anadziŵa chimene chinali cholondola, kapena chowongoka. Chiweruzo chake chinali: Masinthidwe aliwonse amene anali ofunikira anayenera kukhala mbali ya anthu, omwe anafunikira kugwirizana ndi kaimidwe kake kolungama ndi kowongoka. Mmenemo ndi mmene zirinso lerolino. Kusintha kuli kothekera, ndi chiyanjo chotulukapo. Ngakhale winawake amene njira yake yakhala mosakaikira yoipa angasinthe. Yesaya analemba kuti: “Ngakhale zoipa zanu ziri zofiira, zidzayera ngati matalala.”—Yesaya 1:16-18.
16. Ndimotani mmene ena avomerezera ku chenjezo lozikidwa pa Baibulo ponena za kuchita zolakwa?
16 Pali chikhoterero, ngakhale kuli tero, cha kudziŵa uphungu woterowo koma kulingalira kuti umagwira ntchito kwa ena. Mwachiwonekere, ambiri m’nthaŵi ya Yesaya anachita zimenezo. M’chenicheni, munthu aliyense payekha ayenera kudzisanthula iyemwini. Ngati Mkristu ali ndi liwongo la chimo lalikulu, kaya ndi kunama, kunyenga, mkhalidwe woipa wa kugonana, kapena zolakwa zina ziri zonse zazikulu, kulapa ndi ntchito zoyenera kulapa ziri zofunika kwambiri. (Machitidwe 26:20) Moyamikirika, ena achitapo kanthu ‘kulungamitsa zinthu pakati pawo ndi Yehova.’ Mwachitsanzo, Nsanja ya Olonda ya October 1, 1985, inalongosola nkhani ya kuwongolera zolakwa zimene zingakhale za chinsinsi kwa a kunja koma zingawonedwe ndi Mulungu. (Mateyu 6:6; Afilipi 4:13) Mbali zitatu kaamba ka chisamaliro zinatchulidwa: kulandira kuthiridwa mwazi mwachinsinsi, phyotophyoto, ndi kugwiritsira ntchito molakwa zakumwa zoledzeretsa. Pambuyo pa kulingalira nkhani imeneyi, unyinji wa aŵerengi analemba makalata a chiyamikiro; iwo anavomereza kuti iwo anali ndi zolakwa zimenezo, koma afulumizidwa kulapa ndi kusintha.
17. Ngakhale ngati sitichita zolakwa zazikulu, ndimotani mmene Yesaya 1:18 angagwirire ntchito kwa ife ndi kutithandiza ife?
17 Ndithudi, Akristu ambiri omwe akulingalira nkhani imeneyi sali ndi liwongo la mkhalidwe woipa kwambiri. Mosasamala kanthu za chimenecho, uthenga wa Yesaya ufunikira kutifulumizabe ife ku kufufuza kosanthula mtima. Kodi tingafunikire kulungamitsa zinthu zina ndi Mulungu? Mbali yofunika kwambiri ya uthenga wa Yesaya inali chisonkhezero cha mtima chabwino. Ponena za pemphero, wina angafunse kuti: ‘Kodi mapemphero anga amachokera mu mtima, ndipo ku ubwino wa kuthekera kwanga, kodi zochita zanga ziri zogwirizana ndi mapemphero anga?’ Ena amene apanga kusanthula koteroko awona kuti pali malo ofunikira kuwongolera. Iwo akhala akupemphera kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka cha chifuno cha Mulungu, koma amathera nthaŵi yochepa m’kuphunzira Baibulo ndi zofalitsidwa za Chikristu. Ena akhala akupemphera kaamba ka kukhala ndi phande lalikulu mu utumiki, koma amalondola njira ya moyo yomwe sinasiye malo kaamba ka kuchepetsako ndalama zawo mwa kuchepetsako ntchito yawo ya ku dziko. Kapena kodi mwakhala mukupemphera kuti Mulungu adalitse kupanga kwanu ophunzira? Ndi kuutali wotani, chotero, kumene mwakhala mukugwirira ntchito ku kukhala mphunzitsi wophulapo kanthu? Kodi inu mokhazikika mwawonjezera kupanga kwanu maulendo obwereza ndi kukhala ofunitsitsa kupereka nthaŵi ku kutsogoza phunziro la Baibulo mokhazikika ndi winawake? Kudzikakamiza inu eni m’chigwirizano ndi mapemphero anu kudzasonyeza kuti mowonadi mukufuna Mulungu kuti amvetsere.
18. Nchifukwa ninji tiyenera kupereka chisamaliro ku kulungamitsa zinthu zina pakati pa ife ndi Mulungu?
18 Chiri choyenerera kwa aliyense wa ife kukalamira kukhala ndi mbali zonse za moyo wathu ‘zolungamitsidwa’ ndi Mulungu, Mlengi wathu. Dziŵani mmene Yesaya analingalira m’chigwirizano ndi ichi: “Ng’ombe idziŵa mwini wake, ndi buru adziŵa pomtsekereza; koma Israyeli sadziŵa, anthu anga sazindikira.” (Yesaya 1:3) Palibe aliyense wa ife amene angakonde kuyerekezedwa kukhala wosadziŵa kwenikweni kapena wosayamikira monga ng’ombe kapena buru. Kalongosoledwe kameneko kangagwire ntchito, ngakhale kuli tero, ngati ife timva kuti sitinafunikire kugwirira ntchito pa kuphunzira ponena za Mpatsi wathu wa Moyo ndi zifuno zake ndipo kenaka mofunitsitsa kuyesera kukhala ndi moyo mogwirizana ndi izo.
19. Ndi chiyembekezo chotani chimene Yesaya anandandalikitsa kaamba ka awo olungamitsa zinthu ndi Mulungu, ndipo nchiyani chimene ichi chimatanthauza kwa ife?
19 Yesaya anapereka kwa anthu ake chifukwa kaamba ka kayang’anidwe kabwino. Iye ananena kuti kaimidwe kawo pamaso pa Yehova kakakhoza kutembenuzidwa kukhala koyera. Kangakhale ngati nsalu ya kapezi yomwe ingakhale yoyera ngati ubweya wa nkhosa woti mbuu kapena ngati chipale chofewa chokuta pamwamba pa Phiri la Hermoni. (Yesaya 1:18; Masalmo 51:7; Danieli 7:9; Chivumbulutso 19:8) Ngakhale ngati ambiri sanavomereze, ndipo chotero mtunduwo unaperekedwa ku lupanga ndi mu ukapolo, otsalira okhulupirika anabwerera. Mofananamo, tingapeze chiyanjo cha Yehova, mwinamwake ndi thandizo lokhazikika la oyang’anira omwe amatumikira mu mpingo monga ‘oweruza ndi aphungu’ achikondi. (Yesaya 1:20, 24-27; 1 Petro 5:2-4; Agalatiya 6:1, 2) Chotero khalani otsimikiziridwa, mungalungamitse zinthu pakati pa Mulungu ndi inu. Kapena, ngati muli kale ndi chiyanjo cha Mulungu, mungalimbikitse unansi wanu ndi iye. Icho mowonadi chiri choyenera kuyesasayesa kwanu kulikonse.
[Mawu a M’munsi]
a Dr. E. H. Plumptre akulongosola kuti: “[Kugwiritsira ntchito mu King James Version] kumasonyeza lingaliro la kukambitsirana pakati pa anthu ofanana. Chihebri chimasonyeza kutuluka kwa mawu kwa amene akupanga ulamuliro wapamwamba, monga ngati kuchokera kwa woweruza akulankhula kwa wozengedwa mlandu.”
Nsonga za Kubwereramo
◻ Ndi chiyani chimene chinatanthauzidwa ndi lamulo lakuti ‘idzani ndi kulungamitsa zinthu’ ndi Mulungu?
◻ Ndimotani mmene nthaŵi ya Yesaya inaliri yofanana ndi yathu?
◻ Nchiyani chimene Yesaya anasonyeza kuti chinafunika kaamba ka anthu kuti apeze chiyanjo cha Mulungu?
◻ Pambali pa chimo lalikulu, ndi m’mbali zina ziti zimene tingafunikire kulungamitsa zinthu pakati pa ife ndi Mulungu?
[Chithunzi patsamba 10]
Malo otsetsereka a chipale chofewa a Phiri la Hermoni, kuyang’ana kum’mwera cha kumadzulo modutsa ku mtunda kwa chigwa cha Yordano ku mapiri a Galileya
[Mawu a Chithunzi]
Photos, pages 10, 31: Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Chithunzi patsamba 13]
Yesaya ananena kuti ‘buru adziŵa pomtsekereza.’ Ndi phunziro lotani limene liri mu ichi?