-
N’chiyani Chimachitikira Munthu Amene Wamwalira?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
2. Kodi kudziwa zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira n’kothandiza bwanji?
Anthu ambiri amachita mantha ndi imfa ngakhalenso ndi anthu amene anamwalira. Koma mukaphunzira zimene Baibulo limanena zokhudza imfa mulimbikitsidwa kwambiri. Yesu anati: “Choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti pali chinachake chimene chimapitiriza kukhala ndi moyo munthu akamwalira. Koma Baibulo siliphunzitsa zimenezi. Choncho munthu akamwalira savutika kapena kumva kupweteka. Komanso akufa sangativulaze chifukwa sadziwa chilichonse. Choncho, sitiyenera kuchita chilichonse chosonyeza kuti tikulambira kapena kulemekeza akufa poopa kuti angativulaze.
Anthu ena amanena kuti angathe kulankhula ndi amene anamwalira. Koma zimenezi sizingatheke. Monga mmene taphunzirira, anthu amene anamwalira, “sadziwa chilichonse.” Amene amaganiza kuti akulankhulana ndi achibale awo amene anamwalira, amakhala akulankhulana ndi ziwanda zimene zimayerekezera kukhala munthu womwalirayo. Choncho kudziwa zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira, kumatiteteza kuti tisamavutitsidwe ndi ziwanda. Yehova amatichenjeza kuti tisayese kulankhulana ndi anthu amene anamwalira chifukwa amadziwa kuti kulankhulana ndi ziwanda kungatibweretsere mavuto aakulu.—Werengani Deuteronomo 18:10-12.
-
-
N’chiyani Chimachitikira Munthu Amene Wamwalira?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
4. Kudziwa zenizeni zimene zimachitikira munthu amene wamwalira n’kothandiza
Tikadziwa zoona zenizeni zokhudza imfa, sitimaopa anthu amene anamwalira. Werengani Mlaliki 9:10, kenako mukambirane funso ili:
Kodi anthu amene anamwalira angatichitire zinthu zinazake zoopsa?
Kudziwa zenizeni zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya imfa kungatithandize kuti tisamakhulupirire bodza lakuti anthu amene anamwalira amafunika kuwalambira, kuwalemekeza kapenanso kuwachitira zinazake kuti asatipweteke. Werengani Yesaya 8:19 ndi Chivumbulutso 4:11, kenako mukambirane funso ili:
Kodi mukuganiza kuti Yehova amamva bwanji akaona munthu akulambira kapena kupempha chithandizo kwa munthu amene anamwalira?
-