Kubadwa kwa Mwana Kwakukulu Koposa kwa Padziko Lapansi Kutsogolera ku Chisungiko cha Dziko Lonse
“Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa Mtendere.’’—YESAYA 9:6.
1. Ndi pansi pandani mmene chisungiko chadziko lonse chiri chotsimikizirika, ndipo ndimotani mmene timadziwira ichi?
CHISUNGIKO CHA DZIKO LONSE! Pansi pa “Kalonga wa dziko iri,” Satana Mdyerekezi, liri loto losathekera. (Yohane 12:31, The New English Bible) Koma chisungiko cha dziko lonse pansi pa “Kalonga wa Mtendere,” Yesu Kristu, chiri chotsimikizirika kwenikweni. Yehova amatitsimikizira ife za ichi mu ulosi wake ponena za kubadwa ndi ntchito ya “Kalonga wa Mtendere.” Pa Yesaya 9:6, 7 timawerenga: “Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa Mtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruzo ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.”
2. (a) Kodi ndi iti imene inali mikhalidwe pansi pa imene ulosi wa Yesaya 9:6, 7 unaperekedwa? (b) Kodi timadziwa motani kuti Yehova mosalephera adzamamatira ku pangano limene anapangana ndi Davide kaamba ka ufumu wosatha mumzera wa mbadwo wake?
2 Uli ulosi wozizwitsa chotani nanga! Chidzakhala chosangalatsa kwambiri kusanthu aponena za ulosi umenewu wonena za kubadwa kwa mwana kwakukulu koposa kwa padziko lapansi. Koma tisanayamikire mokulira, tikafunikira kuyang’ana pa mikhalidwe pansi pa imene ulosiwo unaperekedwa. Inali nthawi ya chiwembu cha dziko lonse mkati mwa masiku a mfumu ya Yuda pansi pa Mfumu Ahazi. Ngakhale inali yosakhulupirika kwa Yehova, mfumuyo inaloledwa kukhala pa mpando wachifumu wa Yehova. Chochitika chimenechi chinawonetsedwa kwa iye chifukwa chapangano limene Yehova anali atapanga ndi Davide kaamba ka ufumu wosatha m’mzera wa mbadwo wake. Ngakhale kuti Davide anakanizidwa mwawi wakumangira Yehova kachisi, Mulungu anamupatsa iye dalitso lina. Iri linaperekedwa m’mawu a mneneri Natani: “ Yehova wakuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja. Ndipo nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.” (2 Samueli 7:11, 16) Lonjezo laumulungu limenelo linatsimikizira kukhala lokhutiritsa kwa Mfumu Davide kotero kuti iye anayang’ana kutsogolo kukukwaniritsidwa kwake kwaulemerero.
3. (a) Kodi ndi mwandani mmene pangano limenelo ndi Davide limakwaniritsidwira, ndipo ndimotani mmene pangano limenelo linaliri lapadera? (b) Kodi nchiyani chimene Mdyerekezi anapanga monga chonulirapo chake mchigwirizano nai pangano la Ufumu?
3 Pangano limenelo ndi Davide limapeza kukwaniritsidwa kwake mu Mwana wamkulu wa Davide, Yesu Kristu, “Kalonga wa Mtendere.” Palibe nyumba ina ya ufumu pa nkhope ya dziko lapansili yomwe inasangalalapo ndi pangano loterolo kaamba ka ufumu, wopanda malire ku kuchuluka kwa ulamuliro wa ukalonga, wopanda malire ku mtendere. Koma pangano la Ufumu limenelo linabweretsa chitokoso ku maufumu onse apadziko amene Satana ali kalonga, kapena wolamulira. Chotero Mdyerekezi ndi ziwanda zake zinachipanga icho kukhala chonulirapo chawo kuyesa kuwononga nyumba ya Davide ndipo mwa kutero kufafaniza zoyembekezera za kukhala kwake m’malo okhazikika. Satana anapeza zida zokonzekeratu mwa Mfumu Rezini ya Aramu, mwa Mfumu Peka ya ufumu wa mafuko khumi a Israyeli, ndi mwa Mfumu ya Asuri.
Chiwembu Motsutsana ndi Pangano la Ufumu
4. Kodi ndimotani mmene Mdyerekezi anapitirizra mzoyesayesa zake za kuimitsa kugwira ntchito kwapangano la Ufumu la Yehova lomwe linapangidwa ndi Davide?
4 Kodi nchiyani chimene chinali makonzedwe a Mdyerekezi? Cholinga chake chinali kukakamiza Mfumu Ahazi ya Yuda, ndi mantha, kulowa m’chigwirizano chosayenera ndi Mfumu ya Asuri. Ndimotani mmene Mdyerekezi akanachitira chimenechi? Chabwino, iye anapangitsa Mfumu Peka ya Israyeli ndi Mfumu Rezini ya Aramu kulowa mu chiwembu motsutsana ndi nyumba ya Davide. Iwo anachita chiwembu kumuchotsa Ahazi pa mpando wachifumu wa Yuda ndi cholinga chofuna kukhazikitsa munthu wawo, mwana wa Tabeeli, monga mfumu yomva ziri zonse. Kodi ndani amene anali mwana wa Tabeeli ameneyu? Chiri chodziwikiratu kuti iye sanali mbadwa ya nyumba ya Davide. Chotero, iye sanali munthu amene kudzera mwa iye chipangano cha Mulungu kaamba ka Ufumu chikanapita kufikira chitapeza Mlowa Mmalo wake wokhazikika mwa “Kalonga wa Mtendere.” Iye akanakhala munthu wawo, osati munthu wa Mulungu, pampando wachifumu wa Yuda. Chotero Baibulo linavumbulutsa zoyesayesa za Satana za kuimitsa kugwira ntchito kwa pangano la Ufumu la Yehova lomwe anapangana ndiDavide.
5, 6. Kodi ndimotani mmene Ahazi anachitira ku chiwembu chotsutsana ndi nvumba ya Davide, ndipo kodi ndi uthenga wolimbikitsa wotani umene Yehova anamupatsa iye?
5 Kodi ndimotani mmene Mfumu Ahazi anachitira kuchiwopsezo ichi? lye ndi anthu ake ananjenjemera ndi mantha. Chotero, Yehova anampatsa iye chidziwitso cha chilimbikitso kusapanga chigwirizano cha chitetezero ndi mfumu yomakwera yamphamvu ya dziko lonse, Asuri. Yehova anatumiza mneneri wake Yesaya kukumana ndi Ahazi ndi kupereka uthenga uwu wopezeka pa Yesaya 7:4-9:
6 “Usawope . . . chifukwa Aramu ndi Efraimu [chiwalo chotsogolera cha ufumu wa Israyeli] ndi mwana wa Remaliya [Peka] apangana kukuchitira zoipa, nati: Tiyeni, tikwere timenyane ndi Yuda, timvute; tiyeni tidzifumulire mpata, pamenepo tikhazike mfumu pakati pake, ngakhale mwana wamwamuna wa Tabeeli.’ Atero Ambuye Yehova: ‘Upo wawo sudzaima, sudzachitidwa . . . mukapanda kukhulupirira ndithu simudzakhazikika.’”
Chizindikiro cha Kulephera kwa Chiwembucho
7. (a) Kodi nchiyani chimene chinatsogolera ku ulosi wodziwika kwambiri wa Yesaya 7:14? (b) Kodi kubadwa kwa Imanueli kunali chizindikiro chotsimikizirika cha chiyani, ndipo kodi ana a Yesaya anayenera kutumikira monga chiyani?
7 Chotero, Yehova ananeneratu za kugwetsedwa kwa achiwembuwo. Panthawi imeneyo inabwera nthawi kaamba ka ulosi waumulungu wofunika kwambiri padziko lonse, popeza unaloza ku Mlowa Mmalo wa pangano la Ufumu ndi Davide. Koma kodi nchiyani chimene chinatsogolera ku ulosi wodziwika umenewo? Chabwino, Yehova anali kulankhula ndi Mfumu Ahazi. Iye anamuuza Ahazi kupempha kaamba ka chizindikiro chozizwitsa chomwe iye akanachilingalira, ndipo kenaka Yehova adzachipanga icho monga chitsimikiziro chakuti Mulungu adzaphwanya chiwembu chotsutsana ndi nyumba ya Davide. Koma Ahazi anakana kupempha kaamba ka chizindikiro chimenecho. Kodi nchiyani chotsatira chinachitika? Yesaya 7:14 amatiuza ife: “Chifukwa chake Yehova iye mwini adzakupatsani inu chizindikiro; tawonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamutcha dzina lake Imanueli.” Dzina limenelo limatanthauza “Mulungu Ali Nafe.” Popeza Imanueli ndi ana amuna ena awiri a Yesaya anayenera kutumikira monga zizindikiro, mneneriyo ananena pa Yesaya 8:18: “Tawonani! Ine ndi ana amene Yehova wandipatsa ine, tiri zizindikiro ndi zodabwitsa mwa Israyeli, kuchokera kwa Yehova wa makamu.” Chotero kubadwa kwa Imanueli chinali chizindikiro chotsimikizirika chakuti achiwembu onse ndi ziwembu zawo motsutsana ndi pangano la Ufumu la Mulungu ndi Mlowa Mmalo wake sizidzachitika!
8. (a) Kodi nchiyani chimene ulosi wa pa Yesaya 7:15, 16 unanena ponena za mnyamata Imanueli, ndipo kodi nchiyani chimene chinali chotulukapo chake? (b) Kodi nchiyani chimene chingakhale chifukwa chake chakuti chizindikiritso cha Imanueli m’masiku a Yesaya chidakali chosatsimikizirika?
8 Mbiri ya Baibulo simanena ndi ndani amene anabala mwana wamwamuna wotchedwa Imanueli. Mwinamwake angakhale mdzakazi Wachiyuda yemwe anakhala mkazi wachiwiri wa mneneri Yesaya. Mu chochitika chiri chonse, ulosiwo unapitiriza kunena kuti mwanayo asanakule kufikira pa kuzindikira chabwino ndi choipa, mafumu awiri ochita chiwembu motsutsana ndi nyumba ya Davide adzafika kumapeto osakaza. (Yesaya 7:15, 16) Ichi chinatsimikizira kukhala chowona. Chenicheni chakuti chizindikiritso cha Imanueli m’masiku a Yesaya chakhalabe chosatsimikizirika kwa ife chingakhale chifukwa chakusafuna kuchotsa chidwi cha mibadwo ikudzayo kuchokera ku Imanueli Wokulira pamene iye anawoneka monga chizindikiro chozizwitsa kuchokera kumwamba.
9. (a) Kodi nchiyani chimene kukwaniritsa kwa chizindikiro ndi kugwetsedwa kwa chiwembu chotsutsana ndi pangano la Ufumu kunatsimikizira? (b) Kodi nchiyani chimene chiri chiwembu chachikulu kwambiri cha padziko lapansi chanthawi zonse?
9 Ngakhale kuli tero, m’masiku a Ahazi, kunali kukwaniritsidwa kochepera kokha kwa chizindikiro ndi kugwetsedwa kwa chiwembu cha dziko motsutsana ndi pangano la Ufumu la Mulungu. Komabe kukwaniritsidwa koyambirira kumeneko kunatsimikizira kuti chizindikiro ndi kugwetsedwa kwa chiwembu chadziko kudzakwaniritsidwa mokulira m’nthawi yathu yovuta. Lerolino tikuyang’anizana mwachindunji ndi chiwembu chachikulu kwambiri chadziko chanthawi yonse. M’lingaliro lotani? M’chenicheni chakuti mitundu kotheratu yanyalanyaza makonzedwe a Yehova akubweretsera mtendere wosatha, ndipo iwo amatsutsa ngakhale oimira a “Kalonga wa Mtendere.” Chiwembucho chiridi motsutsana ndi Mlowa Mmalo wapangano la Ufumu, “Kalonga wa Mtendere.” Bwanji, tsopano, ponena za kukwaniritsidwa kotheratu kwa ulosiwo? Ngati tizindikira chizindikiro, ndiye kuti tidzayamikira kuti tsoka la chiwembu chadziko chimenechi ali mapeto opitiratu.
Kubadwa kwa “Kalonga wa Mtendere”
10. (a) Mkukwaniritsidwa kotheratu kwa Yesaya 7:14, kodi ndi ndani amene anabala mwana monga chizindikiro ndi Mlowa Mmalo wapangano la Ufumu? (b) Kodi ndimotani mmene wolemba mbiri Mateyu akugwirizanitsira chizindikiro cha Imanueli ndi nyumba ya Davide?
10 M’kukwaniritsidwa kotheratu kwa ulosiwo, mdzakazi amene anabala mwana monga chizindikiro ndi Mlowa Mmalo wapangano la Ufumu anali Mariya, namwali Wachiyuda wochokera kwa Mfumu Davide. Mngelo Gabrieli anamuuza iye kuti iye adzabala mwana wamwamuna yemwe adzatchedwa Yesu, ndi kuti Yehova Mulungu adzamupatsa iye “mpando wachifumu wa Davide atate wake,” ndi kuti “ufumu wake sudzatha.” (Luka 1:26-33) Wolemba mbiri wouziridwa Mateyu akugwirizanitsa chizindikiro cha Imanueli ndi nyumba ya Davide. Timawerenga pa Mateyu 1:20-23: “Mngelo wa Yehova anawonekera kwa iye [Yosefe] m’kulota, nanena: ‘Yosefe, mwana wa Davide, usawope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chiri cha mzimu woyera. Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti iyeyu adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo’. Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa aneneri, ndi kuti, ‘onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake Imanueli,’ ndilo losandulika, ’Mulungu ali nafe.’”
11. Ndi liti ndipo ndi kuti kumene kunenedweratu kwa kubadwa kwa Imanueli kunachitikira?
11 Ndi liti ndipo ndi kuti kumene kunenedweratu kwa kubadwa kwa Imanueli kumeneku kunachitikira? Maso onse a Chiyuda anatembenukira ku njira yolondola ndi mawu opezeka pa Mika 5:2, ogwidwa mawu pa Mateyu 2:6: “Ndipo iwe Betelehemu, dziko la Yudeya, sukhala konse wamng’onong’ono mwa akulu a Yudeya. Pakuti wotsogolera adzachokera mwa iwe, amene adzaweta anthu anga Aisrayeli.” Munali mu chaka ca 2 B. C.E. mumzinda wa Betelehemu kuti “Kalonga wa Mtendere” anabadwa, ndipo ulosi wosangalatsa wa Yesaya 9: 6, 7 unayamba kukwaniritsidwa
12, 13. Ndi kwandani kumene kubadwa kwa “Kalonga wa Mtendere” kunabweretsa ulemu wokulira, ndipo kodi ndi ulemerero ndi zochitika zaulemerero zotani zimene zinapezekapo pa kubadwa kumeneku?
12 Ndani wa ife amene sangachilingalire icho ulemu ndi chimwemwe kukhala kholo la m’modzi amene adzakhala ndi dzina lakuti “Kalonga wa Mtendere”? Icho chotero chinabweretsa ulemerero waukulu kwa Tate wa chifumu wa Kalonga ameneyu. M’chenicheni, sichinachitike konse, ayi sichinachitike nkomwe kalelo, kuti kubadwa kwa munthu kunakhala kogwirizana ndi ulemerero woterowo ndi zochitika zosangalatsa
13 Mngelo wowala wa Yehova anawonekera kwa abusa okhala kubusa oyang’anira zoweta zawo usiku kunja kwa Betelehemu, ndipo “kuwala kwa Yehova kunaunikira kuzungulira.” Mngeloyo kenaka analengeza kubadwaku m’kukwaniritsidwa kwa ulosi waumulungu, nati: “Wakubadwirani inu lero, m’mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye.” Monga ngati kuti chimenecho sichinali chaulemerero wokwanira, munawoneka m’thambo khamu la angelo akulemekeza Atate a mwana wobadwa chatsopanoyo ndi kunena ndi liwu limodzi lokweza: “Ulemerero ukhale kwa Mulungu kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo.” Chinali choyenerera chotani kwa angelowo kulengeza kubadwa kwa “Kalonga wa Mtendere” wokhazikitsidwiratu kuti kudzakhala mtendere waumulungu kaamba ka anthu onse omwe ali ndi chikondwerero cha Mulungu!—Luka 2:8-14
14, 15. (a) Ndi pazochitika zotani pamene ana akumwamba a Mulungu analemekezera Yehova? (b) Kodi nchifukwa ninji palibe mwana wina aliyense m’mbiri ya munthu adzayerekezedwa ndi mwana ameneyo?
14 Kale kwambiri asanabadwe “Kalonga wa Mtendere,” angelo anali atalemekeza Mulungu pachochitika chapadera. Pamenepo panali pamene, pachilengedwe, anakhazikitsa dziko lapansi. (Yobu 38:4) Kodi munawonapo zithunzithunzi za dziko lathu lapansi zitatengedwa ndi opita ku mwezi kuchokera kunja kwa dziko? Ndiye kuti munawona kokha chimene angelowo anawona kufikira nthawi zaposachedwa. Ndipo kodi ndimotani mmene angelowo anavomerezera? Yobu 38:7 amatiuza ife: “Muja nyenyezi za m’mawa zinayimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anapfuula ndi chimwemwe.”
15 Kubadwa kwakukulu koposa koyambirira komwe kudzalemekeza dziko lapansi kwanthawi yoyamba sikudzakhala chochitika chochepera cha chimene ana a Mulungu anadzigwirizanitsa m’mawu awo oyimba mu nyimbo ya ulemerero. Monga mmene atate wapadziko lapansi amayamikiridwira pa kubadwa kwa mwana wake woyamba wamwamuna, choteronso Atate wakumwamba amene ali ndi thayo kaamba ka kubadwa kwakukulu koposa kochitika pa dziko lapansi kumeneku anayenera kulemekezedwa ndi nyimbo ndi ziwalo za banja lake lakumwamba. Ndi mokongola chotani nanga mmene konsatiyo inasangalalidwira ndi cholengedwa cha Umulungu pakukhala kwake kwanthawi yoyamba tate mu mkhalidwe wa zinthu wosiyana kotheratu! Sichinachitikepo ndi kale lonse mu mbiri yonse ya dziko lonse kuti kunakhala kubadwa kwa mwana koyerekezedwa ndi kuja kwa “Kalonga wa Mtendere” woikidwiratu
“Kuunika Kwakukulu” Kuwala
16. Ndi liti ndipo ndimotani mmene kunaliri kukwaniritsidwa kopitirira kwa Yesaya mutu 9?
16 Pamene Yesu anayamba uminisitala wake wapoyera, panali kukwaniritsidwa kowonjezereka kwa Yesaya mutu 9. Ichi chinagwirizana ndi maversi ake awiri oyambilira, omwe ananeneratu kuti “kuwala kwakukulu” kudzawala pa anthu “oyenda mumdima.” Kukwaniritsidwa kwa maversi amenewo kwalongosoledwa kaamba ka ife ndi wolemba mbiri wouziridwa Mateyu pa mutu 4, maversi 13 mpaka 17: “Ndipo atachoka ku Nazarete [Yesu] anadza nakhalitsa iye m’Kapernao wa pambali pa nyanja, m’malire a Zebuloni ndi Nafitali, kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti: Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali, njira ya kunyanja, kutsidya lija la Yordano, Galileya la anthu akunja! anthu akukhala mumdima adawona kuwala kwakukulu, ndi kwa iwo okhala m’malo a mthunzi wa imfa; kuwala kunaturukira iwo.’ Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena: ‘Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa ku mwamba wayandikira.’ ”
17. Ndimotani mmene Yesu akanapangira kuunika kuwala pa anthu a mu Zebuloni ndi Nafitali, ndipo kodi nchiyani chimene kuwala kumeneko kudzatanthauza kwa awo okhala mumdima?
17 Zebuloni ndi Nafitali anali kumpoto kwenikweni kwa Israyeli ndipo anaphatikiza dziko la Galileya. Nafitali anachita malire ndi gombe la kum’mwera kwa Nyanja ya Galileya. Chotero panali pa kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu mu madera amenewo kuti Yesu, limodzi ndi ophunzira ake, anapangitsa kuunika kuwala kwa anthu kumeneko omwe kwanthawi yaitali anakhala ali mumdima. Yesu anena pa Yohane 8:12: “Ine ndiine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.” Chotero, mwa Yesu “awo okhala mu dera la imfa ya mdima” anatheketsedwa kukhala ndi “kuunika kwamoyo” chifukwa iye anapereka moyo wake “monga dipo la anthu ambiri.” Iye ali amene Yehova anamgwiritsira ntchito kubweretsa kuwala panjira imene anthu angapezere moyo.—Mateyu 4: 23; 20:28.
18. (a) Kodi ndi chifukwa ninji “kuunika kwakukulu kumeneku sikunayenera kutsekerezedwera kwa anthu a ku Galileya okha? (b) Kodi nchiyani chimene tidzalingalira m’nkhani yotsatira?
18 “Kuunika kwakukulu” kumeneku kolonjeza chipulumutso kuchokera ku imfa ndi zitsenderezo sikunatsekerezedwere kwa anthu a ku Galileya. Kodi Yesaya sananeneretu kuti kuchuluka kwa bomalo kudzakhala kosatha? Ndipo kodi Yesaya sananeneretu kuti ntchito ya “Kalonga wa Mtendere” idzakhala yosangalatsa? Inde, popeza Yesaya 9: 6, 7 amati: “Ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa Mtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.” Mu nkhani yotsatirayi, tidzalingalira ntchito ya Yesu Kristu monga “Wauphungu, Mulungu Wamphamvu, Tate Wosatha,” ndiponso monga “Kalonga wa Mtendere.”
Kodi Mumakumbukira—
◻ Ndi ohiwembu chotani chimene chinachitika m’masiku a Mfumu Ahazi?
◻ Nchiyani chimene chinali kukwaniritsidwa kochepera kwa chizindikiro cha mu Yesaya 7:14?
◻ Nchiyani chimene chinali kukwaniritsidwa kotheratu kwa chizindikiro chimenecho?
◻ Nchifukwa ninji kubadwa kwa “Kalonga wa Mtendere” kunali kubadwa kwamwana kwakukulu koposa padziko lapansi?