Kodi Nliti Pamene Mtendere Wokhalitsa Udzabweradi?
“NKHONDO ndiyo chimodzi cha zinthu zokhalapo nthaŵi zonse m’mbiri, ndipo siinamezedwe ndi kutsungula kapena demokrase,” analemba motero Will ndi Ariel Durant m’bukhu lawo lakuti The Lessons of History. “Mtendere ndiwo mphamvu yosakhazikika, imene ingasungidwe kokha ndi ulamuliro wozindikiridwa kukhala wapamwamba kapena mphamvu yofanana nawo.”
Ndithudi, mosasamala kanthu ndi zoyesayesa zazikulu, mtendere wokhalitsa wazemba anthu. Chifukwa ninji? Chifukwa nchakuti zochititsa nkhondo nzozama kwenikweni kuposa mikangano ya ndale zadziko, yolimbanira nthaka, kapena mikangano ya zamayanjano imene timaiwona pamwamba pokha. A Durant anati: “Zochititsa nkhondo nzofanana ndi zochititsa mpikisano pakati pa anthu: kusirira, nkhalwe, ndi kunyada; chikhumbo cha chakudya, nthaka, milimo, mafuta, maluso.”
Komabe, Baibulo mwachindunji limadziŵitsa muzu wa mkangano ndi nkhondo pakati pa anthu ndi ya pamlingo waukulu. Timaŵerenga kuti: ‘Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera ku zikhumbitso zanu zochita nkhondo m’ziŵalo zanu? Mulakalaka, ndipo zikusoŵani; mukupha, nimuchita kaduka, ndipo simukhoza kupeza; mulimbana, nimuchita nkhondo.’—Yakobo 4:1, 2.
Pamenepo, nkhaniyo imafika pamfundo iyi: Kuti mtendere weniweni udze, tiyenera kuchotsapo osati zizindikiro zokha—nkhondo, kuukira, kugwetsa boma, kupandukira boma—komanso zochititsa zenizenizo—kukaikirana, umbombo, chidani, nkhalwe—mwa anthu onse. Izi ziyenera kuloŵedwa m’malo ndi machitidwe ogwirizana ndi mikhalidwe yopanda dyera yonga chikondi, kukoma mtima, kukhulupirika, ndi kuoloŵa manja. Kodi pali wina aliyense yemwe angathe kuchita zimenezi? Ngati izo nzodalira pa anthu opanda ungwiro, omafa, pamenepo yankho nlakuti ayi. Koma pali winawake yemwe iyi ndinkhani yapafupi kwa iye. Uyu ndiye ali ndi yankho la funso lakuti: Kodi nliti pamene mtendere udzabweradi?
Uyo Amene Angadzetse Mtendere
Zaka mazana 28 zapitazo, mneneri Yesaya anauziridwa kulengeza kuti: ‘Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa Mtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.’—Yesaya 9:6, 7.
Munthu ameneyu yemwe adzabweretsa mtendere wosatha anavumbulidwa pambuyo pake kusakhala wina aliyense kusiyapo Yesu Kristu, ‘Mwana wa Wamkulukulu.’ (Luka 1:30-33; Mateyu 1:18-23) Koma kodi nchifukwa ninji iyeyu adzapambana pamene akalonga ena onse ndi olamulira alephera? Choyamba, tiyenera kudziŵa kuti, “mwana” wolonjezedwayo sanayenera kungokhala khanda lopanda thandizo kwamuyaya, monga momwe ena angamulingalirire. Mmalomwake, iye anayenera kuchita “ulamuliro” monga ‘Kalonga wa Mtendere,’ kaamba ka dalitso lamuyaya kwa anthu.
Ulamuliro wa Yesu umaphatikizamo zambiri. Monga ‘Phungu Wodabwitsa,’ womvetsetsa chibadwa cha anthu mwapadera ndi luso lopambana koposa, adzakhoza kufika patsinde la nkhani zovuta ndipo mwakutero nkuthetsa mavuto okhwima omwe akuyang’anizana ndi olamulira adziko ndi kuwadodometsa lerolino. (Mateyu 7:28, 29; Marko 12:13-17; Luka 11:14-20) Ndiyeno, monga ‘Mulungu Wamphamvu,’ Yesu Kristu, woukitsidwa waumulunguyo, tsopano woikidwa pampando wachifumu kumwamba monga Mfumu Yaumesiya, adzagwira ntchito kudzetsa mtendere mwakuchitanso pamlingo waukulu zimene anachita pamene anali padziko lapansi—kuchiritsa odwala matenda osachiritsika, kugaŵira makamu a anthu zakudya ndi zakumwa, angakhale kulamulira mphepo yakunja. (Mateyu 14:14-21; Marko 4:36-39; Luka 17:11-14; Yohane 2:1-11) Monga “Atate Wosatha,” Yesu alinayo mphamvu yakuwabwezeretsa ku moyo amene anafa ndikuwapatsa moyo wamuyaya. Ndipo iyemwini adzakhala kosatha, motero kutsimikizira kuti ulamuliro wake ndi mtendere sizidzatha konse.—Mateyu 20:28; Yohane 11:25, 26; Aroma 6:9.
Chotero pokhala wokonzekeretsedwa motero, mwachiwonekere Yesu Kristu ndiye angakhoze kuchotsa zochititsa nkhondo ndi mkangano zozama kwambiri zimenezo. Iye sadzangochita pangano la mtendere kapena kupanga makonzedwe okhala pamtendere ndi mitundu ina, ndiyeno mtenderewo nkuswedwa ndi nkhondo inanso. Mmalomwake, iye adzachotsa chisalungamo chirichonse cha ndale zadziko, cholimbanira nthaka, cha mayanjano, ndi cha zachuma mwakuika anthu onse pansi pa ulamuliro wake umodzi, wa Ufumu Waumesiya. Mwakutsogoza anthu onse m’kulambiridwa kwa Mulungu yekha wowona, Yehova, iye adzachotsa chimene kaŵirikaŵiri chimachititsa nkhondo—chipembedzo chonyenga. Palibe chikaikiro kuti Yesu Kristu, Kalonga wa Mtendere, adzachita zonsezi. Funso nlakuti, Liti?
Zochitika Zotsogoza ku Mtendere Wokhalitsa
Pambuyo pa kuuka kwake ndi kukwera kunka kumwamba mu 33 C.E., Yesu anafunikira kudikirira nthaŵi yoikidwiratu yakuti achitepo kanthu. Ichi chinali m’chigwirizano ndi lamulo la Yehova lakuti: ‘Khalani pa dzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu. Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera ku Ziyoni; Chitani ufumu pakati pa adani anu.’ (Salmo 110:1, 2; Luka 22:69; Aefeso 1:20; Ahebri 10:12, 13) Kodi zimenezi zikuchitika liti? Kwa zaka zoposa 70, Mboni za Yehova zakhala zikulengeza kuzungulira padziko lonse mbiri yabwino yakuti Yesu Kristu anayamba kulamulira mu Ufumu wa Mulungu kumwamba m’chaka cha 1914.a
Koma mwina munganene kuti, ‘Sipanakhale mtendere chiyambire 1914. Mosiyana, mikhalidwe yaipa chiipire kuyambira pamenepo.’ Ndinu wolondola kotheratu. Kwenikweni ichi chimatsimikizira kuti zinthu zikuchitika monga momwe zinanenedweratu. Baibulo limatiuza kuti panthaŵi yeniyeni imene ‘Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wake: . . . amitundu anakwiya.’ (Chibvumbulutso 11:15, 18) Mmalo mogonjera ku ulamuliro wa Yehova Mulungu ndi Kalonga wake wa Mtendere, mitundu inadziloŵetsa m’kulimbanirana ulamuliro wa dziko kophangirana ndikusonyeza mkwiyo makamaka kwa Akristu omwe ankachitira umboni Ufumu wa Mulungu wokhazikitsidwawo.
Bukhu la Chibvumbulutso limavumbulanso kuti mwamsanga pamene Yesu Kristu anakhala paulamuliro wa Ufumu, anayamba kumchotsa Satana ndi ziŵanda zake kumwamba: ‘Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu.’ Chotulukapo nchotani? Cholembedwacho chikupitirizabe kuti: ‘Chifukwa chake, kondwerani miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo [mkwiyo, NW] waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.’—Chibvumbulutso 12:10, 12.
Chizindikiro Chomaliza
Izi zimatizindikiritsa chifukwa chimene mitundu siinakhoze kudzetsa mtendere mosasamala kanthu za zoyesayesa zawo zonse. Mkwiyo waukulu wa Mdyerekezi, wowonekera m’mitundu yeniyeniyo, wachititsa dziko kugwedezeka ndikukhala m’chipoloŵe kuposa ndikale lonse m’mbiri ya anthu. Kodi zonsezi zidzatha liti? Baibulo limapereka mfungulo yofunika kwambiri kuti: “Pamene kuli kwakuti iwo akunena: ‘Mtendere ndi chisungiko!’ pamenepo chiwonongeko chamwadzidzidzi chidzawafikira.”—1 Atesalonika 5:3, NW.
Kodi mukulizindikira tanthauzo la chenjezo limeneli? Zochitika zadziko zonga zimene tazifotokoza m’nkhani yapita zimasonyeza kuti olamulira ndi anthu ambiri akulankhula ponena za mtendere ndi kuukalamira kuposa ndi kale lonse. Ena akulingalira kuti pamene Nkhondo Yapakamwa yatha, chiwopsezo cha chipululutso cha nyukliya chinatha. Inde, mitundu yakhala ikukamba zambiri ponena za mtendere ndi chisungiko. Koma kodi mkhalidwe wa dziko ukupitadi kumeneko? Kumbukirani, Yesu ponena za okhala m’masiku otsiriza, kuyambira 1914 anati: ‘Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.’ (Mateyu 24:34) Inde, mtendere udzabweradi mkati mwa mbadwo uno koma osati mwa zoyesayesa za mitundu. Mtendere wokhazikitsidwa molimba, wolunjika, ndi wolungama wolonjezedwa ndi Yehova Mulungu ungathe kudza kokha kupyolera mwa ulamuliro ukudzawo wa Kalonga wa Mtendere, Yesu Kristu.—Yesaya 9:7.
Ngati mukukhumba kuwona tsiku limene mtendere udzabweradi ndikusangalala nawo limodzi ndi okondedwa anu, pamenepo yang’anani kwa Kalonga wa Mtendere ndipo sungani m’maganizo mawu ake opatsa chidaliro akuti: ‘Dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.’—Luka 21:36.
[Mawu a M’munsi]
a Onani tsatanetsatane wa kuŵerengera zaka kwa m’Baibulo ndi maulosi a Baibulo okwaniritsidwa, m’mitu 12 mpaka 14 ya bukhu la “Let Your Kingdom Come,” lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Bokosi patsamba 6]
MTENDERE UKULONGOSOLEDWA
Lerolino anthu ambiri amalingalira kuti mtendere ndiwo kusakhalapo kwa nkhondo kapena mkangano. Komabe, aŵa ndi malongosoledwe opereŵera kwenikweni a liwulo. M’nthaŵi za kulembedwa kwa Baibulo, liwu lakuti “mtendere” (Chihebri, sha·lohmʹ) kapena mawu akuti “Mtendere ukhale ndi iwe.” linagwiritsiridwa ntchito monga moni wamasiku onse. (Oweruza 19:20; Danieli 10:19; Yohane 20:19, 21, 26) Mwachiwonekere, silikungotanthauza kusakhalapo kwa nkhondo. Onani zimene bukhu lakuti The Concept of Peace likunena pamfundoyi: “Pamene liwu lakuti shalom ligwiritsiridwa ntchito kutanthauza mtendere, chimene oligwiritsira ntchito oyambirira adali nacho m’malingaliro chinali mkhalidwe wa dziko kapena wa chitaganya cha anthu chokhala ndi kukhazikika, chigwirizano, kukwanira, kukhutiritsa. . . . Pamene pali mtendere, ponse paŵiri olamulira ndi olamuliridwa amakhala atafikira mlingo wotheratu wa kakhalidwe koyembekezeredwa.” Pamene Mulungu abweretsa mtendere, anthu sadzangoleka “kuphunziranso nkhondo,” koma ‘adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake.’—Mika 4:3, 4.
[Chithunzi patsamba 7]
Anthu akumvadi kusakhalapo kwa mtendere chiyambire Nkhondo Yadziko ya I