Mtendere wa Umulungu Kaamba ka Awo Ophunzitsidwa ndi Yehova
“Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova, ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu—YESAYA 54:13.
1, 2. Kodi chikondwerero cha mtendere chimadalira pa chiyani?
MTENDERE! Kodi uli wokhumbika motani! Koma mbiri ya mtundu wa anthu siinakhale china chake koma ya mtendere. Kodi nchifukwa ninji icho chiri tero?
2 Kusangalala ndi mtendere kuli mokulira kogwirizana ndi ulemu kaamba ka ulamuliro. Ndipo kodi ndi ndani amene ali wolamulira wamkulu dziko lonse? Mlengi, Yehova Mulungu. Chiyanjo chovomerezedwa ndi iye chotero chiri choyenerera kaamba ka mtendere. (MaSalmo 29:11;119:165) Ngati chiyanjo chofunika Kwambiri chimenecho chaphwanyidwa, chiri chosathekera kukhala Ndi mtendere weniweni ndi Mulungu, ndi Anthu anzathu, kapena mwa ife eni.—Yesaya 57:21.
Chifukwa Chake Dziko Liribe Mtendere
3. Kodi ndimotani mmene unansi wa mtundu wa anthu ndi Mulungu unawonongedwera?
3 Monga mmene timadziwira bwino, panali mwamsanga pambuyo pa kubadwa kwa mbiri ya munthu pamene mwana wauzimu wa Mulungu anawukira motsutsana ndi Yehova. Kuwukira kuli mkhalidwe wa nkhondo. Wothetsa mtendere ameneyu, amene anadzadziwika ndi dzina lakuti Satana Mdyerekezi, anakakamiza Hava kusalola lamulo la Mulungu kuima munjira imene iye akachitira zinthu ngati iye anadzimva kuti chikakhala ku ubwino wake. Mdyerekezi anakhotetsa zenizeni kumupanga iye kuganiza kuti anali kumanidwa china chake chabwino mwa kumvera Mulungu. Chikakamizocho chinali kudzikonda, mzimu wa ine choyamba. Mwamsanga mwamuna wake anagwirizana naye mu mkhalidwe wake wakusamvera, ndipo monga chotulukapo chake, mbadwa zawo zonse zayambukiridwa ndi mzimu umenewo.—Genesis 3:1-6, 23, 24; Aroma 5:12.
4, 5. (a) Ndi ku mlingo wotani kumene Satana wapeza chipambano mkusonkhezera malingaliro a anthu? (b) Kodi ndi zotulukapo zotani zimene ichi chakhala nacho pa zoyesayesa za anthu kufikira mtendere?
4 Siiri mbali yochepa yokha ya mtundu wa anthu yomwe imaika pambali lamulo la umulungu. Malemba amatiuza ife kuti Satana “akunyenga dziko lonse.” (Chivumbulutso 12:9) Anthu ena ali moipitsitsa osayeruzika, kusonyeza kusalingalira kwenikweni kaamba ka Mulungu ndi anthu anzawo; ena ali mochepera otero. Koma Satana wakhala wachipambano mu kusonkhezera kulingalira kwa mtundu wa anthu kotero kuti mtumwi Yohane akananena kuti; “Dziko lonse ligona mwawoipayo.” (1 Yohane, 5:19) Kaya anthu amadzinenera kukhala akukhulupirira kuti Mdyerekezi alipo kapena ayi, iwo amachita zimene iye amafuna. Iwo amamumvera iye, chotero iye ali wolamulira wawo. Monga chotulukapo chake, mtundu wa anthu uli wopatulidwa kuchokera kwa Mulungu, uli pa udani ndi iye. Mu mkhalidwe woterowo, kodi chingakhale chodabwitsa kuti zoyesayesa za munthu za kuufikira mtendere zasokonezedwa?—Akolose 1:21.
5 Angakhale kuli tero, chiwerengero chomakulakula kuchokera ku mitundu yonse chikuyang’anizana ndi mtendere waumulungu, mtendere umene umachokera kwa Mulungu. Kodi ndimotani mmene ichi chachitikira?
Mtendere Wokhutiritsa Umene Mulungu Amapereka
6. (a) Kodi ndi chigogomezero chotani chimene Baibulo limaika pa mtendere? (b) Ndi kudzera mwandani mmene chiriri chothekera kaamba ka ife kusangalala ndi mtendere umene Mulungu amapereka?
6 Pa Aroma 15:33 Yehova moyenerera walongosoledwa kukhala “Mulungu amene amapereka mtendere.” Kuyambira pa chiyambi penipeni, chinali chifuniro cha Mulungu kaamba ka zolengedwa zake zonse kusangalala ndi mtendere. Koposa nthawi 300 Mawu ake ouziridwa, Baibulo, amalozaku mtendere. Limamveketsa kuti Yesu Kristu ali “Kalonga wa Mtendere.” (Yesaya 9:6, 7) Iye ali amene watumizidwa ndi Mulungu kudzaphwanya ntchito za wowononga mtendere woyambirira, Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 3: 8) Ndipo kudzera mwa “Kalonga wa Mtendere” chiri chothekera , kwa aliyense wa ife kusangalala ndi mtendere wokhutiritsa umene Mulungu amapereka.
7. (a) Kodi nchiyani chimene mtendere wopatsidwa ndi Mulungu umaphatikiza? (b) Kodi ndi chifukwa ninji suli china chake chimene tiyenera kudikira kufikira dongosolo iri la zinthu lipita ndi kukhala titapeza ungwiro?
7 Uli mtendere wosangalatsa chotani nanga umenewo! Iwo uli woposa kusoweka kwa nkhondo. Liwu la Chihebri sha. lohm’, lomwe kawirikawiri limatanthauzidwa “mtendere,” limasonyeza umoyo, kupita patsogolo, ndi moyo wabwino. Mtendere wa Mulungu umene uli chotengera cha Akristu owona uli wapadera mwanjira yakuti sumadalira pa mikhalidwe yotizinga. Ichi sichikutanthauza kuti mikhalidwe yowazinga yoipa simawakhudza iwo. Koma iwo amakhala ndi kulimbitsa mtima kwa mkatikati komwe kumatheketsa iwo kupewa kuwonjezera ku phokoso mwa kubwezera pamene liwakhudza iwo. (Aroma 12:17, 18) Ngakhale kuti munthu angakhale wodwala mwakuthupi kapena wokhala ndi zochepa mwakuthupi, iye angakhalebe wa umoyo wabwino ndi wopita patsogolo pa kaimidwe kauzimu ndipo motero kusangalala ndi mtendere umene Mulungu amapereka. Mwachiwonekere, mtendere umene woteroyo amakhala nawo ungapititsidwe patsogolo pamene dziko iri ladyera lipita, ndipo udzazama pamene mtundu wonse wa anthu udzafika ku ungwiro. Koma mtendere wa umulungu womwe uli wothekera tsopano uli mkhalidwe wodekha wa maganizo ndi mtima, mkhalidwe wofatsa wa mkatikati mosasamala kanthu za zimene zingakhale ziri kumachitika kunja. (Masalmo 4:8) Iwo umabuka kuchokera pa mayanjano ovomerezedwa ndi Mulungu. Chiri chotengera cha mtengo wapatali chotani nanga!
Ana Ophunzitsidwa ndi Yehova
8. Kodi ndi ndani amene anali oyambirira kusangalala ndi mtendere umenewu ndi Mulungu kudzera mwa Yesu Kristu?
8 Kodi ndi ndani amene ali ndi mtendere wotero chifukwa cha kuphunzitsidwa ndi Yehova ndi kupereka chisamaliro ku malamulo ake? Mkuyankha, Baibulo choyamba limatsogoza chisamaliro chathu kwa awo amene amapanga Israyeli wauzimu. Iwo akulankhulidwa pa Agalatiya 6:16, pamene timawerenga: “Ndipo onse amene atsata chilangizo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israyeli wa Mulungu.” Awa ali 144, 000 omwe asankhidwa ndi Mulungu kugawana moyo wa kumwamba ndi Yesu Kristu.—Chivumbulutso 14:1.
9. Kodi nchiyani chimene chinali “lamulo lamkhalidwe” logwirizana ndi kusangalala ndi mtendere kwa Israyeli wauzimu?
9 Kubwerera mbuyo mu zana loyamba, awo aIsrayeli wauzimu anali kuphunzira chowonadi choyambirira, monga “lamulo lamkhalidwe,”lomwe linali mwachindunji logwirizana ndi kusangalala kwawo ndi mtendere. Chinali chofunika kwambiri kuti amvetsetse lamulo lamakhalidwe limeneli. Kwa zaka zoposa mazana 15, Yehova anagwiritsira ntchito Lamulo la Mose kusonyeza zithunzi za zinthu zabwino zirinkudza. Koma pambuyo pa imfa ya nsembe ya Yesu Kristu, ziyeneretso za Lamulo la Mose sizinali zomangirira. (Ahebri 10:1; Aroma 6: 14) Ichi chinawonetsedwa mwa chosankha cha bungwe lolamulira la Chikristu mu Yerusalemu pa nkhani ya mdulidwe. (Machitidwe 15:5, 28, 29) Icho chinagogomezeredwa kachiwiri mu kalata youziridwa kwa Agalatiya. Zinthu zabwino zimene Lamulo la Mose linaunikira zinali zitayamba kugwira ntchito. Mopirira Yehova anali kusindikiza m’maganizo ndi m’mitima ya otsatira odzozedwa a Kristu chiyenerero cha chifundo chake chosonyezedwa kudzera mwa Kristu. Mwa kusonyeza chikhulupiriro mu chopereka chimenechi, mwakudzisunga iwo mogwirizana ndi icho, iwo angasangalale ndi mtundu wa mtendere womwe unali usanakhale wothekera kaamba ka mtundu wa anthu ochimwa.—Agalatiya 3:24, 25; 6:16, 18.
10. (a) Israyeli wauzimu anali kuwona kukwaniritsidwa kwa lonjezo liti lolembedwa pa Yesaya 54: 13? (b) Kodi ndimotani mmene kuwalanga kwa Yehova kwakhala mbali mkupeza kwawo mtendere?
10 Awo a Israyeli wauzimu anali kuyang’anizana ndi kukwaniritsidwa kwa lonjezo lalikulu lolembedwa pa Yesaya 54:13. Pamenepo Yehova iye mwini ananena kwa gulu lake longa mkazi la zolengedwa zomvera zauzimu: “Ana ako onse adzakhala anthu ophunzitsidwa ndi Yehova, ndipo mtendere wa ana ako udzachuruka.” Komabe, Mwana wake woyamba ali Yesu Kristu iye mwini, wobweretsedwa monga Mesiya pamene iye anadzozedwa ndi mzimu woyera mu 29 C.E. Koma “mkazi” wa Yehova wakumwamba ali ndi ana owonjezereka—144, 000 ena omwe anakhala mbali yachiwiri ya mbali ya mbewu yonenedweratu pa Genesis 3: 15. Yehova analonjeza kuti iye adzakhala Mlangizi Wamkulu wa ana onse amenewa. Iye waphunzitsa iwo chowonadi ponena za iye mwini ndi zifuno zake. Iye wauza iwo mmene angamutumikirire iye. Pa nthawi zina, iye anayenera kuwapatsa iwo chilango. Ichi chakhala choyenerera pamene analephera kusamalira Mawu ake. Chilango chingakhale chovuta kuchitenga. Koma iwo modzichepetsa azindikira kufunika kwawo kwa icho ndi kupanga masinthidwe oyenerera, ndipo chilango chimenecho chikubala zotulukapo zabwino—“chipatso cha mtendere, ndicho, chilungamo.”—Ahebri 12:7, 11; Masalmo 85:8.
“Khamu Lalikulu” Lophunzitsidwa Mnjira za Mulungu
11. (a) Kodi ndaninso amene akuphunzitsidwa ndi Yehova mu tsiku lathu? (b) Kodi ndimotani mmene amasonyezera kuti iwo amayenerera kufotokozedwa kopezeka pa Yesaya 2:2, 3, ndipo ndi chotulukapo chotani kwa ena?
11 Mu tsiku lathu, Israyeli wauzimu sali gulu lokha limene Yehova akuliphunzitsa. Mkati mwa theka la zana lapita, chisamaliro chinatsogozedwa kwa ena. Yesaya anauziridwa kulemba ponena za iwo mu mutu 2, versi 2 ndi 3: “Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.” Inde, awo amene amafungatira kulambiridwa kwa Mulungu yekha wowona amakupatsa iko malo okwezeka kwambiri mu miyoyo yawo. Chotero kumaima pokwezeka pamwamba pa mtundu uliwonse wa kulambira mu umene iwo poyambirira anadzilowetsamo ndipo mu umene dziko lowazinga iwo limapitiriza kudzilowetsamo. Anthu a mitundu achiwona ichi. Iwo awona kuti, mosasamala kanthu za zikakamizo zopangidwa ndi olamulira a dziko kapena kukhalapo kwa machitidwe opanda chikristu mu dziko, awo amene amalambira Yehova; aika unansi wawo ndi iye pamwamba pa china chiri chonse. Oyang’anitsitsa awonanso chipatso chimene ichi chimatulutsa m’miyoyo ya olambira oterowo, ndi ambiri amene amafuna kugawana mkulambira kowona. Chotero anthu oposa mamiliyoni atatu akunena kwa ena tsopano: “Idzani, anthu inu, ndipo tiyeni tikwere ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda mu njira zake.”—Onaninso Zekariya 8:23.
12. Ndimotani mmene awo otchulidwa pa Yesaya 2:2, 3 apindulira mwa kukhala ndi Mulungu mong Mphunzitsi wawo, ndipo kodi ndi mbali iti yowonekera kwambiri ya malangizo omwe amawapatsa iwo?
12 Tangolingalirani nchiyani chimene icho chimatanthauza—kukhala ndi Mulungu monga Mphunzitsi wawo! Awo amene amalandira malangizo oterowo ndipo mowonadi kuyamikira magwero ake siali okanthidwa ndi kuwombana maganizo kokhazikika. Iwo samadzipeza iwo eni ogawanika pakati pa zosankha ziwiri kapena pa nyanga za ngozi ponena za nchiti chimene chiri cholondola. Chowonadi chochokeramu Mawu a Mulungu chiri chachimvekere. Ndipo nchiyani chimene Yesaya 2:4 amasonyeza kuti idzakhala mbali yowonekera ya maphunziro omwe amalandira? Iyo imaphatikizapo kusangalala ndi mtendere mu dziko logawanika. Mwakutero, mosasamala kanthu za zimene ena amasankha kuchita, awo amene amaphunzitsidwa ndi Yehova amatenga kuyesetsa kwa kusula malupanga awo kukhala zolimira ndi nthungo zawo kukhala anangwape. Iwo saphunziranso nkhondo.
13. Kodi ndi kuchokera ku mayambidwe otani kumene “khamu lalikulu” lachokera, koma nchiyani chimene chawapanga iwo kukhala mtundu wa anthu amene ali?
13 Liri gulu limodzimodziri lomwe limasonyezedwa pa Chivumbulutso 7:9, 10, 14, monga opulumuka kulowa mu dziko latsopano la mtendere la Mulungu lomwe limatsatira kubWera kwa “chisautso chachikulu.” “Khamu lalikulu” lopulumuka kuchokera ku magulu a mitundu yonse, mapfuko, anthu, ndi manenedwe. Ambiri a iwo amachokera ku magulu amene poyamba anali kumenyana nkhondo wina ndi mnzake. Ena anali kungolondola njira ya moyo yomwe mwachiwonekere inali yodzikonda; komabe, ichonso chinasokonezana ndi chikondwerero cha mtendere. Koma tsopano awo amene abwera kuchokera ku mitundu yonse ali okonda mtendere, anthu opititsa patsogolo mtendere. Ndipo kodi ndi chiyani chomwe chawapanga iwo kukhala otero? Iwo aphunzitsidwa ndi Yehova.—Yesaya 11:9.
Mtundu Wapadera wa Mtendere
14. Kodi mtendere wa anthu a Mulungu wazikidwa pa chiyani, ndipo ndimotani mmene ichi chiriri tero?
14 Mtendere umene Yehova amayanjira nawo anthu ake uli mowonadi wapadera. Sichiri chinthu chimene chimatulukapo pamene chigwirizano chogwedezeka chipangidwa pakati pa magulu awiri omwe sakhulupirirana wina ndi mnzake. Siumaphatikiza kugonjera. Uli wozikidwa pa chilungamo. (Yesaya 32:17) Koma kodi chimenechi chingakhale chowona motani ponena za mtendere umene umaphatikizamo anthu opanda ungwiro? Monga ochimwa, ndi chilungamo cha mtundu wanji chimene aliyense wa ife ali nacho? Chabwino,’ndi chikhulupiriro tingasangalale ndi chilungamo chomwe chimakhala chothekera kudzera m’mtengo wa nsembe yochotsa uchimo ya Yesu.
15. Mkati mwa uminisitala wa Yesu wa pa dziko lapansi, nchiyani chimene Yehova anali kuphunzitsa ana ake oyembekezera chomwe chinali chofunika kwambiri kaamba ka mtendere?
15 Ichi chimatithandiza ife kuyamikira chimene Yesu ananena monga chalembedwa pa Yohane 6:45-47. Pamenepo iye anali kulankhula kwa Ayuda omwe sanakokeredwe kwa iye monga Mesiya ndipo chotero anali kung’ung’udza motsutsana ndi iye. Koma chinali ndi chilozero kwa ophunzira ake kotero kuti iye anati: “Chalembedwa mwa aneneri [makamaka, pa Yesaya 54:13], ‘Ndipo iwo onse adzakhala ophunzitsidwa ndi Yehova.’ Yense amene adamva kwa Atate naphunzira adza kwa ine. Sikuti munthu wina wawona Atate, koma iye amene ali wochokera kwa Mulungu ameneyo wawona Atate. Indetu indetu ndinena ndi inu, iye wokhulupirira ali nawo moyo wosatha.” Ophunzira amenewo analandira malangizo omwe Yehova anawapatsa iwo. Iwo anakokeredwa kwa Yesu. Pamene ena anakana zinthu zimene iye anaphunzitsa ndi kumukana Yesu, atumwi ake anatsala. Monga Petro anati: “Takhulupirira ndi kudziwa kuti inu muli Woyera wa Mulungu.” (Yohane 6:69) Chifukwa cha chikhulupiriro chawo mwa Yesu Kristu, chikanakhala chothekera kaamba ka iwo kulowa mu chiyanjo cha mtendere ndi Yehova Mulungu, chiyanjo chimene chimatenga limodzi ndi chitsimikiziro cha moyo wosatha.
16. (a) Kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E., ndimotani mmene otsatira a Yesu apindulira kuchokera ku choperekedwa chopangidwa kudzera mwa Yesu Kristu? (b) Pambuyo pake, nchiyani chomwe chinayembekezedwa kuchokera kwa iwo?
16 Kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E., mapindu a nsembe ya Kristu anayamba kugwiritsidwa ntchito kwa otsatira okhulupirika a Yesu amenewo. Zimene Paulo pambuyo pake analemba pa Aroma 5:1 zinakhala zowona kwa iwo: “Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu.” Mwakubadwa onse a awa anali mbadwa za Adamu. Monga ochimwa, iwo anatalikiridwa ndi Mulungu. Ntchito iriyonse yabwino yomwe akanachita mwa umwini siikanatha kufafaniza chimo lawo la cholowa. Koma mwa chikondi chake chosatha, Yehova analandira nsembe ya Yesu ya moyo wa munthu wangwiro m’malo mwa mbadwa za Adamu. Kwa awo amene anasonyeza chikhulupiriro choperekedwa ichi, chinakhala chothekera kaamba ka iwo kukhala ndi chilungamo chitaperekedwa kwa iwo ndi kaamba ka iwo kuti atengedwe monga ana a Mulungu ndi chiyembekezo cha moyo kumwamba. (Aefeso 1:5-7) Koma kodi zowonjezereka zinali kufunikira ku mbali yawo? Inde, iwo anayenera kuyenda mu njira za Yehova. Iwo sanayeneranso kupanga chimo. Koma amazindikira kuti chilungamo chirichonse chimene ali nacho chiri chotulukapo cha chikondi cha Mulungu chosonyezedwa kudzera mwa Kristu. Monga mmene malemba amanenera, iwo ‘amasangalala ndi mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Yesu Kristu.’
17, 18. (a) Kodi a “nkhosa zina” amasangalala ndi mtendere woterowo ndi Mulungu? (b) Kodi ndi mafunso ati owonjezereka amene amafunikira kulingaliridwa?
17 Bwanji ponena za awo amene Yesu anawatchula monga “nkhosa zina”? (Yohane 10:16) Kodi iwo amasangalala ndi mtendere woterowo ndi Mulungu? Osati monga ana a Mulungu, koma Akolose 1:19, 20 amaphatikiza iwo monga olandira mtendere wa umulungu. Amanena kuti Mulungu anawona chabwino kudzera mwa Kristu “kuyanjanitsa zinthu zonse kwa iye mwini mwa kuchita mtendere mwa mwazi [wa Yesu] wokhetsedwa pa mtengo wozunzirapo, [NW] kapena za pa dziko [kunena kuti, awo omwe ayanjidwa ndi moyo wosatha pa paradaiso pa dziko lapansi] kapena zinthu za kumwamba.” Awo okhala ndi ziyembekezo za pa dziko lapansi alalikidwa olungama ndi kusangalala ndi mtendere ndi Mulungu ngakhale tsopano, osati monga ana, koma monga ‘mabwenzi a Mulungu,’ monga mmene analiri Abrahamu. Ali malo achiyanjo chotani nanga!—Yakobo 2:23.
18 Kodi inu mwaumwini mumasangalala ndi mtendere umenewo? Kodi mukuumva iwo modzaza monga kuliri kuthekera kaamba ka anthu omwe akukhala mu nthawi yowonekera kwambiri mu mbiri? M’nkhani yotsatirayi, tidzalingalira zina za zinthu zomwe zingathandize kupanga icho kukhala chothekera
Mafunso a Kapendedwe
◻ Ndi chifukwa ninji dziko liribe mtendere?
◻ Kodi ndi mtendere wotani umene Mulungu akupereka tsopano?
◻ Ndi ndani amene angasangalale ndi mtendere woterowo?
◻ Kodi ndimotani mmene chilungamo chiriri mbali yofunika kwambiri mu mtendere umenewu?
[Chithunzi patsamba 18]
“Yense yemwe wamva kuchokera kwa Atate adza kwa ine”