Mtendere—Zenizenizo
NDI oŵerengeka amene angasulize zolinga za zoyesayesa za Mitundu Yogwirizana za kupeza mtendere. “‘Tisule Malupanga akhale Zolimira’ chikulongosola tero chonulirapo cha Mitundu Yogwirizana cha mtendere wa dziko,” ikutero “The World Book Encyclopedia,” ikumawonjezera kuti, “Mitundu Yogwirizana iri ndi zonulirapo ziŵiri zazikulu: mtendere ndi ulemu wa munthu.”
Mawu ozokotedwa pansi pa chifano chosonyezedwa pano amalemba mofupikitsa mawu aulosi wa Baibulo pa Yesaya chaputala 2, vesi 4. Iwo amaŵerenga motere mogwirizana ndi matembenuzidwe amakono:
“Ndipo adzayenera kusula malupanga awo kukhala zolimira ndi nthungo zawo kukhala anangwape.”
Mawu okwezeka ameneŵa ayeneradi kukhala anauzira maboma a ziŵalo za UN kufuna kupeza mtendere wosatha ndi kuchotsapo zida. Koma momvetsa chisoni, chiyambire kukhazikitsidwa kwake pamapeto pa nkhondo yachiŵiri yadziko mu 1945, mbiri ya UN yavumbula zosiyanako. Kodi nchifukwa ninji? Kwakukulukulu chifukwa chakuti mawu ali pamwambawo ogwidwa kuchokera kwa Yesaya sangapatulidwe, monga mmene zakhalira ndi maboma a anthu. Mawu ozungulira mawuwo ngwofunika koposa. Lingalirani chifukwa chake.
Uthenga wa Yesaya
Yesaya anali mneneri. Iye akulankhula za masomphenya aulemerero a kugwirizana ndi mtendere wa anthu a mafuko onse. Masomphenya ameneŵa kuti akhale enieni, anthu ayenera kuchitapo kanthu. Chiyani? Lingalirani kufunika kwa mavesi 2 ndi 3 m’kugwirizana kwawo ndi vesi 4.
“[2] Ndipo kudzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. [3] Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake; chifukwa m’Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mawu a Yehova kuchokera m’Yerusalemu. [4] Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”
Choyamba, tiyenera kuvomereza kuti Mlengi wathu, Yehova, ali ndi kuyenera kwa kutilangiza za “njira zake,” zimene, monga mmene Yesaya pambuyo pake analembera, ziri ‘zokwezeka kuposa njira zathu.’ (Yesaya 55:9) Anthu ambiri, makamaka atsogoleri adziko odziwona kukhala ofunika, amachipeza ichi kukhala chinthu chovuta kuchivomereza. Kokha njira zawo ndi zimene ziri zolungama m’maso mwawo. Chikhalirechobe, chenicheni chakuti njira zawo sizinatsogolere ku mtendere wa dziko ndi kuchotsapo zida kukusonyezadi kupusa kwa kupitirizabe kulondola njira zoterozo.
Chachiŵiri, onani kufunika kwa chikhumbo chofunikira cha munthu aliyense payekha cha kugonjera ku malamulo a Mulungu: “Tidzayenda m’mayendedwe ake.” Kokha pa maziko amenewo ndi pamene malupanga angasulidwe kukhala zolimira ndi nthungo kukhala anangwape pa dziko lonse. Kodi ndimotani mmene chonulirapo chokhumbidwa koposa chimenecho chingafikiridwire?
Malangizo a Mulungu
Anthu ambiri ali nalo Baibulo, bukhu limene liri ndi malangizo a Yehova Mulungu, koma zambiri zimafunikira kuposa kungokhala nalo kokha. Yesaya akunena kuti chilamulo cha Yehova ndi mawu zikuchokera ku “Yerusalemu.” Kodi chimenecho chikutanthauza chiyani? M’tsiku la Yesaya, mzinda weniweniwo unali magwero a ulamuliro waufumu kumene Aisrayeli onse okhulupirika anayang’ana. (Yesaya 60:14) Pambuyo pake, pa nthaŵi ya atumwi a Yesu Kristu, Yerusalemu anali adakali maziko a malangizo amene anachokera ku bungwe lolamulira Lachikristu mu mzinda umenewo.—Machitidwe 15:2; 16:4.
Kodi bwanji ponena za lerolino? Onani kuti Yesaya akuyamba uthenga wake ndi ndemanga yakuti: “Ndipo kudzakhala masiku otsiriza.” Matembenuzidwe ena amati: “M’masiku otsiriza.” (New International Version) Umboni umaperekedwa mokhazikika m’masamba a magazine ano kuchilikiza kuti takhala tikukhala m’masiku otsiriza a dziko liripoli chiyambire 1914. Chotero, kodi nchiyani chimene tiyenera kuyembekezera kuwona, mogwirizana ndi mavesi 3 ndi 4?
Khamu lalikulu la anthu amene sakuphunziranso nkhondo amene ‘asula kale malupanga awo kukhala zolimira.’ Ndipo tikuwawonadi! Amuna, akazi, ndi ana oposa 3.5 miliyoni a mafuko onse m’maiko oposa 200 ogwirizana m’cholinga chimodzi, akukhala pamtendere wina ndi mnzake ndi kulalikira uthenga wa Baibulo wa mtendere kwa anansi awo. Iwo amadziŵika pa dziko lonse monga Mboni za Yehova.
Iwo ali ndi Bungwe Lolamulira lamakono la amuna achikulire Achikristu ochokera ku mbali zosiyanasiyana za dziko lapansi amene amapereka chiyang’aniro chofunikira ku ntchito ya dziko lonse ya anthu a Mulungu. Amuna ameneŵa, mofanana ndi atumwi ndi akulu mu Yerusalemu m’zaka za zana loyamba, ali ziŵalo zodzozedwa za kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ogaŵiridwa ndi Yesu kusamalira kaamba ka zikondwerero zake za Ufumu pano pa dziko lapansi. Mbiri yatsimikizira kuti iwo angadaliridwe kutsatira chitsogozo cha mzimu woyera ndipo kuti samadalira pa nzeru za munthu m’kuphunzitsa gulu la Mulungu njira za mtendere weniweni.—Mateyu 24:45-47; 1 Petro 5:1-4.
Kulambira Kowona
Choposa chidziŵitso cha m’mutu kapena ngakhale chikhumbo cha kukhala mogwirizana ndi malangizo a Mulungu kukuloŵetsedwamo m’kukhala pa mtendere. Kudzipereka kwa mtima ndi kulambira kwa Mlengi, Yehova, ziri zofunika, monga mmene Yesaya akumveketsera.
Mneneriyo akulongosola kuti “phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri” ndipo “lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda.” M’nthaŵi zakale, mapiri ena ndi zitunda zinatumikira monga malo a kulambira mafano ndi malo opatulika a milungu yonyenga. Pamene Mfumu Davide anabweretsa Likasa lopatulika ku hema woikidwa pa Phiri la Ziyoni (Yerusalemu), mamita 760 pamwamba pa malekezero a nyanja, iye mwachiwonekere ankachita mogwirizana ndi chitsogozo cha Mulungu. Pambuyo pake, pamene kachisi wamkulu wa Yehova anamangidwa pa Phiri la Moriya, liwu lakuti “Ziyoni” linafikira pa kuphatikiza malo a kachisi, chotero kachisi analinso pa malo okwezeka kuposa malo ozungulira achikunja. Yerusalemu weniweniyo ankatchedwanso “phiri lopatulika”; mwakutero, kulambira kwa Yehova kunakhalabe pa malo okwezeka.—Yesaya 8:18; 66:20.
Chotero lerolino, kulambira kwa Yehova Mulungu kwakhala kokwezeka mofanana ndi phiri lophiphiritsira. Kutchuka kwake nkofunikira kuti onse akuwone, popeza kwachita chinachake chimene palibe chipembedzo china chirichonse chimene chakhala chokhoza kuchichita. Kodi icho nchiyani? Iko kwagwirizanitsa alambiri onse a Yehova, amene mwachimwemwe asula malupanga awo kukhala zolimira ndipo sakuphunziranso nkhondo. Zoletsa zautundu ndi ufuko siziwalekanitsanso. Iwo amakhala monga anthu ogwirizana,paubale, ngakhale kuti ali omwazikana m’mitundu yonse ya dziko.—Salmo 33:12.
Nthaŵi ya Chosankha
Kodi zonsezi zikukuyambukirani motani? Mawu a mneneri wina Wachihebri ali oyenerera koposa: “Aunyinji, aunyinji m’chigwa chotsirizira milandu! Pakuti layandikira tsiku la Yehova m’chigwa chotsirizira milandu.” (Yoweli 3:14) Iri nthaŵi yofulumira ya kupanga chigamulo kwa mtundu wonse wa anthu, kaya kuphunzira njira zamtendere za Mulungu kapena kupitiriza kuchilikiza moyo wolunjikitsidwa pa nkhondo womwe udzatha posachedwapa.
Yesu ananeneratu kuti ntchito yaikulu yolalikira ikakwaniritsidwa m’tsiku lathu. Kulalikira kumeneko kumakhudza “mbiri yabwino” yakuti Ufumu wa Mulungu udzabweretsa mtendere ku dziko lapansi logawikana ndi nkhondo. (Mateyu 24:14) Chaka chatha maphunziro okhazikika Abaibulo apanyumba oposa mamiliyoni atatu anatsogozedwa ndi Mboni za Yehova pa dziko lonse. Ena a maphunziro a mlungu ndi mlungu ameneŵa anachitidwa ndi munthu payekha, koma ambiri anali a magulu a banja. Mwakutero mamiliyoni a ana akupatsidwa chiyembekezo chotsimikizirika kaamba ka mtsogolo mwawo, ndipo makolo awo amapeza chitsimikizo chakuti nkhondo, zonga zomwe achitira umboni ndipo mwinamwake kukhalamo ndi phande, sizidzakhala mbali ya dziko latsopano lopangidwa ndi Yehova Mulungu.
Lidzakhala dziko la kudalirana ndi mtendere lotani nanga! Sipadzakhala kufunika kwa kudandaula ndi kuchotsapo zida, popeza kuti zida zankhondo zidzakhala zinthu zakale. Ndipo chiyamikiro chipite kwa Yehova, “Mulungu wa mtendere,” amene mwachikondi akutilangiza tsopano kotero kuti tikonzekere kaamba ka moyo wokwanira pansi pa Ufumu wake wachilungamo.—Aroma 15:33.