Pobisalira Pawo—Bodza!
‘Tayesa mabodza pothaŵirapo pathu, ndi kubisala m’zonyenga.’—YESAYA 28:15.
1, 2. (a) Kodi ndi gulu liti lerolino limene liyenera kuzindikira chimene chinachitika kwa ufumu wakale wa Yuda? (b) Kodi nchidaliro cholakwika chotani chomwe Yuda anali nacho?
KODI mawu amenewo amagwira ntchito pa Chikristu Chadziko lerolino monga momwe anachitira kwa ufumu wa Yuda wakale wa mafuko aŵiri? Ndithudi, amatero! Ndipo kufanana kumeneko kumalengeza tsoka pa Chikristu Chadziko chalerolino. Kumatanthauza kuti posachedwapa chiwonongeko chidzagwera gulu lachipembedzo lampatukolo.
2 Kumpoto kwa Yuda kunali ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi. Pamene Israyeli anatsimikizira kukhala wosakhulupirika, Yehova anamlola kugonjetsedwa ndi Asuri mu 740 B.C.E. Ufumu unzake, Yuda, unachitira umboni chochitika chatsoka chimenechi koma mwachiwonekere unalingalira kuti chinthu choterocho sichikachitika konse kwa uwo. ‘Kuchitikiranji,’ atsogoleri ake anadzitukumula motero, ‘kodi kachisi wa Yehova sadakagwirabe ntchito m’Yerusalemu? Kodi ife sitiri anthu oyanjidwa ndi Mulungu? Kodi ansembe athu ndi aneneri sakunenera m’dzina la Yehova?’ (Yerekezerani ndi Yeremiya 7:4, 8-11.) Atsogoleri achipembedzo amenewo anali ndi chidaliro chakuti anali achisungiko. Komatu anali olakwa! Iwo adali opanda chikhulupiriro mofanana ndi achibale awo akumpoto. Motero, chomwe chinachitikira Samariya chikachitikiranso Yerusalemu.
3. Kodi nchifukwa ninji Chikristu Chadziko chimalingalira kukhala chachidaliro ponena zamtsogolo, koma kodi pali chifukwa chabwino cha chidaliro chake?
3 M’njira yofananayo, Chikristu Chadziko chimati chiri ndi unansi wapadera ndi Mulungu. ‘Eya,’ icho chimadzitama motero, ‘tiri ndi zikwi makumi ambiri za matchalitchi ndi akatswiri a atsogoleri achipembedzo, limodzinso ndi mamiliyoni mazanamazana a nzika. Tiri nalonso Baibulo, ndipo timagwiritsira ntchito dzina la Yesu m’kulambira kwathu. Motsimikizirika, tiri oyanjidwa ndi Mulungu!’ Koma chomwe chinachitikira Yerusalemu wakale chikukhala chenjezo lamphamvu. Mosasamala kanthu za zochitika zachilendo zandale zadziko zaposachedwapa, tikudziŵa kuti Yehova posachedwapa adzachitapo kanthu motsimikiza motsutsana ndi Chikristu Chadziko ndi zipembedzo zonyenga zonse.
“Pangano ndi Imfa”
4. Kodi ndipangano lotani limene Yuda anaganiza kuti analipanga?
4 M’nthaŵi zamakedzana, Yerusalemu wosakhulupirikayo analandira machenjezo ambiri kupyolera mwa aneneri owona a Mulungu, koma iye sanawakhulupirire. Mmalomwake, iye anadzikuza kuti imfa siikamgwetsera mu Shelo, manda, monga momwe inaphera ufumu wakumpoto wa Israyeli. Mneneri Yesaya anauziridwa kunena kwa Yuda kuti: ‘Chifukwa chake imvani mawu a Yehova, inu amuna amnyozo, olamulira anthu aŵa a m’Yerusalemu. Chifukwa inu munati, Ife tapangana pangano ndi imfa, tavomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothaŵirapo pathu, ndi kubisala m’zonyenga.’—Yesaya 28:14, 15.
5. (a) Kodi pangano la Yuda ndi imfa lolingaliridwa linali chiyani? (b) Kodi ndichenjezo lotani loperekedwa kwa Mfumu Asa limene Yuda anaiŵala?
5 Inde, atsogoleri a Yerusalemu analingalira kuti anali ndi pangano, titero kunena kwake, ndi imfa ndi Shelo kotero kuti mzinda wawo ukasungidwa. Koma kodi pangano lolingaliridwalo la Yerusalemu ndi imfa linatanthauza kuti iye analapa machimo ake ndikuti tsopano anadalira Yehova kaamba ka chipulumutso? (Yeremiya 8:6, 7) Kutalitali! Mmalomwake, iye anatembenukira kwa olamulira andale zadziko aumunthu kaamba ka thandizo. Koma chidaliro chake pa mabwenzi akudziko chinali chinyengo, bodza. Mabwenzi akudziko omwe anawadalira sakanampulumutsa. Ndipo popeza kuti anasiya Yehova, Yehova anamsiyanso Yerusalemu. Zinachitika monga momwe mneneri Azariya anachenjezera Mfumu Asa kuti: “Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.”—2 Mbiri 15:2.
6, 7. Kodi Yuda anachitanji kuti apeze chisungiko, koma kodi panakhala chotulukapo chomalizira chotani?
6 Pokhala ndi chidaliro m’zigwirizano zawo za ndale zadziko, atsogoleri a Yerusalemu anali otsimikizira kuti panalibe “mliri wosefukira” wa magulu ankhondo oukira womwe ukayandikira kwa iwo kudodometsa mtendere ndi chisungiko chawo. Pamene anawopsezedwa ndi chigwirizano cha Israyeli ndi Suriya, Yuda anatembenukira kwa Asuri kaamba ka thandizo. (2 Mafumu 16:5-9) Pambuyo pake, pamene makamu ankhondo a Babulo anadza motsutsana naye, iye anapempha thandizo kwa Igupto ndipo Farao anavomera, natumiza gulu lankhondo kukathandiza.—Yeremiya 37:5-8; Ezekieli 17:11-15.
7 Koma magulu ankhondo a Babulo anali amphamvu kwambiri, kwakuti asirikali a Igupto anabwerera. Kuika chidaliro kwa Yerusalemu mwa Igupto kunatsimikizirika kukhala kolakwika, ndipo mu 607 B.C.E., Yehova anamsiya kuchiwonongeko chimene adaneneratu. Chotero olamulira ndi ansembe a Yerusalemu anali olakwa! Chidaliro chawo m’zigwirizano zadziko kaamba ka mtendere ndi chisungiko zinali “bodza” limene linasesedwa ndi mliri wosefukira wa magulu ankhondo a Babulo.
Kukana “Mwala Woyesedwa”
8. Kodi ndimotani mmene Chikristu Chadziko chatengera kaimidwe kofanana ndendende ndi kaja ka Yuda wakale?
8 Kodi pali mkhalidwe wofanana lerolino? Inde, ulipodi. Atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko amalingaliranso kuti palibe tsoka limene lidzawagwera. Kwenikweni, monga momwe Yesaya ananeneratu iwo amati: ‘Ife tapangana pangano ndi imfa, tavomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothaŵirapo pathu, ndi kubisala m’zonyenga.’ (Yesaya 28:15) Mofanana ndi Yerusalemu wakale, Chikristu Chadziko chayang’ana ku zigwirizano zadziko kaamba ka chisungiko, ndipo atsogoleri achipembedzo ake amakana kuthaŵira kwa Yehova. Eya, iwo samagwiritsira ntchito ngakhale dzina lake, ndipo amaseka ndi kuzunza amene amalemekeza dzina limenelo. Atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko achita mofanana ndendende ndi mmene ansembe aakulu Achiyuda m’zaka za zana loyamba anachitira pamene anakana Kristu. Iwo kwenikweni, anena kuti, “Tiribe Mfumu koma Kaisara.”—Yohane 19:15.
9. (a) Kodi ndani lerolino amene akuchenjeza Chikristu Chadziko m’njira imene Yesaya anachenjezera Yuda? (b) Kodi Chikristu Chadziko chiyenera kutembenukira kwa yani?
9 Lerolino, Mboni za Yehova zimachenjeza kuti kusefukira kwa makamu ankhondo akupha posachedwapa kudzasesa Chikristu Chadziko. Ndiponso, izo zimasonya ku malo owona obisalirako kusefukira kumeneko. Izo zimagwira mawu a pa Yesaya 28:16, omwe amati: ‘Chifukwa chake Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika m’Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangondya, wa mtengo wake wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.’ Kodi ndani yemwe ali ‘mwala wa pangondya wa mtengo wake’ ameneyu? Mtumwi Petro anagwira mawu ameneŵa ndikuwagwiritsira ntchito kwa Yesu Kristu. (1 Petro 2:6) Chikristu Chadziko chikadafuna mtendere ndi Mfumu ya Yehova, Yesu Kristu, pamenepo icho chikadapeŵa mliri wosefukira ukudzawo.—Yerekezerani ndi Luka 19:42-44.
10. Kodi Chikristu Chadziko chakulitsa mayanjano otani?
10 Komabe, icho sichinachite tero. Mmalomwake, m’kufunafuna kwake mtendere ndi chisungiko, icho chadziloŵetsa m’chiyanjo cha atsogoleri a ndale zadziko a mitundu—icho chachita zimenezi mosasamala kanthu za chenjezo la Baibulo lakuti ubwenzi ndi dziko ndiwo udani ndi Mulungu. (Yakobo 4:4) Ndiponso, mu 1919 icho chinachirikiza mwamphamvu Chigwirizano cha Amitundu kukhala chiyembekezo chabwino koposa cha anthu kaamba ka mtendere. Chiyambire 1945 icho chaika chiyembekezo chake mu Mitundu Yogwirizana. (Yerekezereni ndi Chibvumbulutso 17:3, 11.) Kodi kudziloŵetsa kwake m’gulu limeneli nkwakukulu motani?
11. Kodi chipembedzo chiri ndi kuimiridwa kotani ku UN?
11 Bukhu laposachedwapa limapereka lingaliro pamene limati: “Mabungwe Achikatolika oposa makumi aŵiri mphambu anayi amaimiridwa ku UN. Atsogoleri achipembedzo adziko ochuluka achezera gulu la mitundu yonse limeneli. Kokumbukika koposa ndiko kuchezetsa kwa Papa Paul VI Woyera pa Msonkhano Waukulu mu 1965 ndi Papa John Paul II mu 1979. Zipembedzo zambiri ziri ndi mapembedzo apadera, mapemphero, nyimbo ndi mautumiki zokonzedwera Mitundu Yogwirizana. Zitsanzo zofunika koposa ndi zija za zipembedzo za Akatolika, a Unitarian- Universalist, a Baptist ndi a Bahai.”
Ziyembekezo za Mtendere Zopanda Pake
12, 13. Mosasamala kanthu za ziyembekezo zofalikira zakuti mtendere wayandikira, kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova ziri zachidaliro kuti machenjezo awo ngowona?
12 Mmodzi wa atsogoleri a ndale zadziko wotchuka koposa anatchula ziyembekezo za anthu ambiri pamene anati: “Mbadwo uwu wa anthu okhala padziko lapansi ungawone kubwera kwa nyengo ya mtendere yosabwezeretseka m’mbiri ya kutsungula.” Kodi iye anali wolondola? Kodi zochitika zaposachedwapa zimatanthauza kuti machenjezo amene Mboni za Yehova zapereka ponena za kupereka chiweruzo kwa Yehova pa mitundu sadzakwaniritsidwa? Kodi Mboni za Yehova nzolakwa?
13 Ayi, izo sizolakwa. Izo zimadziŵa kuti zimene zikunena nzowona chifukwa chakuti zimaika chidaliro chawo mwa Yehova ndi Baibulo, limene ndilo Mawu enieni a Mulungu a chowonadi. Tito 1:2 akuti: ‘Mulungu . . . sanganame.’ Chotero izo ziri ndi chidaliro chotheratu chakuti pamene ulosi wa Baibulo umati chakuchakuti chidzachitika, icho chidzachitikadi osalephera. Yehova iyemwini anena kuti: ‘Momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka mkamwa mwanga, sadzabwerera kwa ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna.’—Yesaya 55:11.
14, 15. (a) Kodi atsogoleri a Yuda anali kulengeza chiyani pamene chiwonongeko cha Yerusalemu chinayandikira mu 607 B.C.E.? (b) Kodi nchiyani chimene Paulo analosera kuti chikalengezedwa chiwonongeko chamwadzidzidzi chisanakanthe dziko lino? (c) Kodi tingayembekezere chiyani pachimake pa chilengezo choloseredwa pa 1 Atesalonika 5:3?
14 M’zakazo Yerusalemu asanawonongedwe mu 607 B.C.E., Yeremiya anasimba kuti atsogoleriwo ankafuula kuti, “Mtendere, mtendere.” (Yeremiya 8:11) Komabe, limenelo linali bodza. Yerusalemu anawonongedwa kukwaniritsa machenjezo ouziridwa a aneneri owona a Yehova. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti chinthu chofananacho chikachitika m’tsiku lathu. Iye anati anthu akakhala akufuula kuti “Mtendere ndi [chisungiko, NW].” Ndiyeno, iye anati, ‘pomwepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera.’—1 Atesalonika 5:3.
15 Pamene tinaloŵa m’ma 1990, manyuzipepala ndi magazini kulikonse ankanena kuti Nkhondo Yoputana ndi Mawu yatha ndikuti mtendere wadziko lonse pomalizira pake wayandikira. Koma kenaka panabuka nkhondo yowomberana mfuti ku Middle East. Komabe, posachedwapa mkhalidwe wa dziko udzasintha kufika pamene mfuu ya “Mtendere ndi chisungiko” zoloseredwa pa 1 Atesalonika 5:2, 3 idzakula kufika pachimake. Pokhala ndi ziyembekezo zathu zozikidwa molimba m’Mawu a Mulungu, timadziŵa kuti, pamene chimakecho chifikiridwa, ziweruzo za Mulungu zidzaperekedwa mofulumira ndipo mosalakwa. Palibe zilengezo za mtendere ndi chisungiko zosatsimikizirika zimene ziyenera kutiganiziritsa kuti chiwonongeko chonenedweratu ndi Mulungu sichidzabwera. Ziweruzo za Yehova nzolembedwa mosasinthika m’Mawu ake Baibulo. Chikristu Chadziko, limodzinso ndi zipembedzo zina zonyenga, zidzawonongedwa. Ndipo pamenepo ziweruzo za Yehova zowononga zidzaperekedwa motsutsana ndi dziko lonse la Satana. (2 Atesalonika 1:6-8; 2:8; Chibvumbulutso 18:21; 19:19-21) Popeza kuti Mboni za Yehova nzachidaliro kuti Yehova adzakwaniritsa mawu ake, izo zimapitirizabe kukhala zamaso pansi pa chitsogozo cha gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ndipo mosamalitsa zimaona mmene zochitika za dziko zikuvumbulukira. (Mateyu 24:45-47) Motsimikizirikadi, palibe zoyesayesa zokhazikitsa mtendere za anthu zimene ziyenera kutipangitsa kuganiza kuti Yehova wasiya chifuniro chake chakubweretsa kusefukira kwa chiwonongeko pa Chikristu Chadziko chodzaza ndi machimo.
‘Mulungu Ndiye Pothawirapo Pathu’
16, 17. Kodi Mboni za Yehova zimachita motani ngati ena akwiitsidwa ndi uthenga wawo wopanda mantha?
16 Ena angakwiitsidwe pamene Mboni za Yehova zilengeza chimenechi mopanda mantha. Komabe, pamene izo zinena kuti atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko abisala m’makonzedwe onyenga, izo zingokamba zimene Baibulo limanena. Pamene izo zinena kuti Chikristu Chadziko chifunikira chilango chifukwa chakuti chakhala mbali ya dziko, zikungosimba zimene Mulungu mwiniwake amanena m’Baibulo. (Afilipi 3:18, 19) Ndiponso, chifukwa chakuti Chikristu Chadziko chaika chidaliro chake m’makonzedwe olinganizidwa ndi dziko lino, icho kwenikweni chimachirikiza mulungu wa dziko lino, Satana Mdyerekezi, yemwe Yesu anati ali tate wa bodza.—Yohane 8:44; 2 Akorinto 4:4.
17 Chifukwa chake, Mboni za Yehova zimalengeza kuti: Kwa ife, sitimalimbikitsa ziyembekezo zonyenga za mtendere wa dziko chifukwa cha kusintha kwa ndale zadziko. Mmalomwake, timalengeza mawu a wamasalmo akuti: ‘Mulungu ndiye pothawirapo ife. . . . Anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu akulu ndi bodza: pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.’ (Salmo 62:8, 9) Makonzedwe a anthu opititsa patsogolo ndi kuchirikiza Chikristu Chadziko ndi dongosolo lonse lazinthu liripoli zonse nchinyengo, bodza! Zonse kuziika pamodzi ziribe mphamvu yokhoza kulepheretsa zifuno za Yehova monga momwe kamwa yodzala ndi mpweya wotentha imachitira!
18. Kodi nchenjezo la wamasalmo liti limene liri loyenerera lerolino?
18 Mboni za Yehova zimagwiranso mawu Salmo 33, vesi 17 mpaka 19, limene limalengeza kuti: ‘Kavalo [wa Igupto, wophiphiritsira nkhondo] safikana kupulumuka naye: chinkana mphamvu yake njaikulu sapulumutsa. Taonani, diso la Yehova liri pa iwo akumuopa iye, pa iwo akuyembekeza chifundo chake; kupulumutsa moyo wawo kwa imfa, ndi kuwasunga ndi moyo m’nyengo ya njala.’ Lerolino, Akristu owona amakhulupirira Yehova ndi Ufumu wake wakumwamba, makonzedwe okha omwe angabweretse mtendere wokhalitsa.
Chikristu Chadziko ‘Choponderezedwa Pansi’
19. Kodi nchifukwa ninji kudalira pa magulu a ndale zadziko kuti abweretse mtendere wadziko kuli chinyengo?
19 Kukhulupirira choloŵa m’malo Ufumu wa Mulungu chopangidwa ndi anthu chirichonse kumapangitsa choloŵa m’malocho kukhala fano, chinthu cholambiridwa. (Chibvumbulutso 13:14, 15) Motero, kulimbikitsa kudalira pa ziungwe za ndale zadziko, zonga ngati Mitundu Yogwirizana, kaamba ka mtendere ndi chisungiko kuli chinyengo, bodza. Ponena za zinthu za ziyembekezo zonyenga zoterozo, Yeremiya anati: ‘Pakuti fanizo lake lonyenga liri bodza, mulibe mpweya mwa iwo. Ndiwo chabe ndiwo chiphamaso; pa nthaŵi ya kulangidwa kwawo adzatha.’ (Yeremiya 10:14, 15) Chotero, akavalo ankhondo a Igupto wophiphiritsiridwa, ndiye, mphamvu za magulu ankhondo andale zadziko za mitundu ya lerolino, sadzatetezera ufumu wachipembedzo cha Chikristu Chadziko pa tsiku lake la tsoka. Kugwirizana kwa zipembedzo za Chikristu Chadziko ndi dziko lino motsimikizirika kudzalephera kuzitetezera.
20, 21. (a) Kodi nchiyani chimene chinachitika kwa Chigwirizano cha Amitundu, ndipo nchifukwa ninji Mitundu Yogwirizana siidzachita bwinopo? (b) Kodi ndimotani mmene Yesaya anasonyezera kuti zigwirizano za Chikristu Chadziko ndi dziko sizidzachipulumutsa?
20 Chikristu Chadziko chinaika ziyembekezo zake pa Chigwirizano cha Amitundu, koma icho chinagubuduzidwa ngakhale Armagedo isanadze. Tsopano chasamutsira chigwirizano chake ku Mitundu Yogwirizana. Koma posachedwapa chidzayang’anizana ndi ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse,’ ndipo sichidzapulumuka. (Chibvumbulutso 16:14) Ngakhale UN yodzutsidwanso imeneyo singabweretse konse mtendere ndi chisungiko. Mawu a Mulungu aulosi amasonyeza kuti gulu la Mitundu Yogwirizana ndi maiko okhala ziŵalo zake ‘adzachita nkhondo ndi Mwanawankhosa [Kristu m’kulamulira kwa Ufumu], ndipo Mwanawankhosa adzawalaka, chifukwa ali Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu.’—Chibvumbulutso 17:14.
21 Mboni za Yehova mwachidaliro zimanena kuti mulibe chipulumutso kaamba ka Chikristu Chadziko m’zigwirizano zake ndi dziko la Satana. Ndipo pamene zinena chimenechi, zingosonya kuchimene Baibulo lenilenilo limanena. Yesaya 28:17, 18 amagwira mawu Yehova kukhala akunena kuti: ‘Ndipo ndidzayesa chiweruziro chingwe chowongolera, ndi chilungamo chingwe cholungamitsira chiriri; ndipo matalala adzachotsa pothaŵirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo. Ndipo pangano lanu ndi imfa lidzathedwa, ndi kuvomerezana kwanu ndi kunsi kwa manda kudzalephereka; popita mliri wowopsa udzakuponderezani pansi.’
22. Pamene chiweruzo cholungama changwiro chigwiritsidwa ntchito pa Chikristu Chadziko, kodi padzakhala chotulukapo chotani?
22 Pamene chiweruzo cha Yehova chiperekedwa, chidzachitidwa molingana ndi chiweruzo cholungama changwiro. Ndipo maziko a Chikristu Chadziko a chidaliro, ‘pangano [lake] ndi imfa,’ adzasesedwa kotheratu mofanana ndi mliri wosefukira. Yesaya akupitirizabe kunena kuti: ‘M’mawa ndi m’mawa udzapita, usana ndi usiku; ndipo kudzakhala kuopsa kokha, kumva mbiri yake.’ (Yesaya 28:19) Kudzakhala kowopsa chotani nanga kwa openyerera kuchitira umboni mphamvu yotheratu ya chiweruzo cha Yehova! Kudzakhala tsoka lotani nanga kwa atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko ndi atsatiri awo kuzindikira mochedwa, kuti iwo aika chikhulupiriro chawo m’bodza!
Dzina la Yehova ndilo “Linga Lolimba”
23, 24. Mmalo mofuna chisungiko m’dziko lino, kodi nchiyani chimene Mboni za Yehova zidzachita?
23 Koma bwanji ponena za Mboni za Yehova? Ngakhale poyang’anizana ndi chidani cha mitundu yonse ndi chizunzo, izo zimanonomerabe kukhala zopatukana ndi dziko. Sizimaiŵala konse kuti Yesu ponena za otsatira ake anati: “Siali a dziko lapansi monga Ine sindiri wa dziko lapansi.” (Yohane 17:16) M’masiku otsiriza onseŵa, izo zaika chikhulupiriro chawo mu Ufumu wa Yehova, osati m’makonzedwe a anthu. Motero, tsoka la Chikristu Chadziko silidzaopsa Mboni za Yehova. Monga momwe Yesaya analosera kuti: “Wokhulupirira sadzafulumira.”—Yesaya 28:16.
24 Miyambo 18:10 imati: “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; Wolungama athamangiramo napulumuka.” Chotero tikuitana anthu onga nkhosa onse kupeza pobisalira pawo mwa Yehova ndi Ufumu wake mwa Kristu. Monga malo opulumukirako, Yehova sichinyengo! Ufumu wake mwa Kristu sibodza! Pobisalira pa Chikristu Chadziko ndi bodza, koma pobisalira pa Akristu owona ndi chowonadi.
Kodi Mungalongosole?
◻ Kodi ndimotani mmene Yuda wakale anafunira pothaŵirapo m’bodza?
◻ Kodi ndimotani mmene Chikristu Chadziko chayesera kubisala m’chinyengo?
◻ Kodi ndimotani mmene Yesaya anachenjezera Yuda, ndipo kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zimalengezera chenjezo lofananalo lerolino?
◻ Kodi ndimotani mmene Chikristu Chadziko chidzapezera kuti chidaliro chake chinaikidwa polakwika?
◻ Mosiyana ndi Chikristu Chadziko, kodi Mboni za Yehova zimasunga kaimidwe kotani?
[Bokosi patsamba 17]
ZIYEMBEKEZO ZAMPHAMVU ZOLENGEZEDWERA MITUNDU YOGWIRIZANA
“Kwanthaŵi yoyamba chiyambire pa Nkhondo Yadziko ya II, chitaganya cha mitundu yonse chagwirizana. Utsogoleri wa gulu la Mitundu Yogwirizana, chinthu chabwino choyembekezeredwa, tsopano ukutsimikizira masomphenya a oliyambitsa. . . . Chotero dziko lingatenge mwaŵiwu kukwaniritsa lonjezo loyembekezeredwa kwanthaŵi yaitali la dongosolo ladziko latsopano.”—Pulezidenti Bush wa United States mu uthenga wake wa “State of the Union” ku mtunduwo, January 29, 1991