Akulu—Samalirani Gulu la Mulungu Mokoma Mtima!
“Tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga mmene mlezi afukatira ana ake a iye yekha.”—1 ATESALONIKA 2:7.
1. Kodi nchifukwa ninji Mboni ya Yehova yokhulupirika iriyonse ingadziwonere kukhala yosungika?
YEHOVA ali Mbusa Wamkulu. Amapereka chakudya chochuluka kwa atumiki ake onga nkhosa ndipo amawatsogolera “m’njira zachilungamo” kaamba ka dzina lake loyera. Chifukwa chake, ochita chifuniro chake safunikira kuwopa choipa chirichonse ndipo angayang’ane kwa Mulungu wawo wachifundo kaamba ka chitonthozo. Ndithudi, Mboni ya Yehova iriyonse yokhulupirika iri ndi chifukwa chabwino cha kukhalira yosungika m’chisamaliro chachikondi cha Mulungu.—Salmo 23:1-4.
2. Monga chisonyezero cha ulemerero wa Mulungu, kodi ndimikhalidwe yotani imene Yesu amasonyeza?
2 Yesu Kristu “ali chinyezimiro [cha Mulungu] cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake.” (Ahebri 1:1-4) Chotero Yesu, Mbusa Wabwino, amasonyezanso chikondi ndi chifundo. (Yohane 10:14, 15) Mwachitsanzo, pa nthaŵi ina “[a]nawona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.”—Marko 6:34.
3. (a) Mofanana ndi Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu, kodi abusa aang’ono Achikristu ayenera kusonyeza mikhalidwe yotani? (b) Ndi uphungu wotani ndi chenjezo zimene mtumwi Paulo anapereka kwa oyang’anira?
3 Akristu onse ayenera ‘kutsanzira Mulungu ndi kupitirizabe kuyenda m’chikondi monga mmene Kristu anawakondera.’ (Aefeso 5:1, 2) Chotero iwo ayenera kukhala achikondi ndi achifundo. Ndipo zimenezi ziyenera kukhala zowona makamaka kwa abusa aang’ono a gulu la Mulungu. Mtumwi Paulo ananena kuti: “Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera [u]nakuikani oyang’anira, kuti muŵete [mpingo, NW] wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa [Mwana wake, NW]. Ndidziŵa ine kuti, nditachoka ine, adzaloŵa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo; ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.”—Machitidwe 20:28-30.
4. (a) M’kupita kwa nthaŵi, kodi nchiyani chimene chinachitika mogwirizana ndi chenjezo la Paulo pa Machitidwe 20:29, 30? (b) Kodi ndimafunso otani amene tsopano afunikira kulingaliridwa?
4 M’kupita kwa nthaŵi, “mimbulu yosautsa” yopatuka inawonekera ndipo ‘sinachitire gululo mokoma mtima.’ Koma ndife osangalala chotani nanga kuti akulu pakati pa Mboni za Yehova samachita nkhalwe yoteroyo! Komabe, kodi okhulupirira anzathu angayembekezere kuchitiridwa motani ndi oyang’anira oikidwa ndi mzimu amenewa? Ndipo kodi ndimotani mmene oikidwa oterowo angasonyezere kukoma mtima ku nkhosa za Yehova?
Osachita Ufumu pa Gululo
5. (a) Kodi ndimotani mmene atsogoleri audziko kaŵirikaŵiri amachitira ndi nzika zawo? (b) Kodi Yesu anasonyeza motani kuti nkhalwe iribe malo pakati pa atsatiri ake?
5 Moyenerera tingayembekezere akulu Achikristu kutisamalira mwachifundo. Iwo sali ofanana ndi olamulira akudziko, amene kaŵirikaŵiri amachita ufumu pa nzika zawo. Mwachitsanzo, kwasimbidwa kuti mfumu Yachifrank Charlemagne (amene analamulira mu 768-814 C.E.) “anakakamiza Asaxon, kulandira ubatizo, pansi pa chilango chowawa cha imfa, ndi kuweruzidwira ku chilango chokakala akuswa Lent, ndipo kulikonse anali kukakamiza mmalo mwa kukopa.” (The History of the Christian Church, lolembedwa ndi William Jones) Nkhalwe iribe malo pakati pa atsatiri a Yesu, popeza kuti iye anati: “Inu mumadziŵa kuti olamulira akunja amachita ufumu pa iwo, ndipo amuna awo olamulira amawachitira nkhalwe. Sikufunikira kutero pakati panu, koma aliyense amene afuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala mtumiki wanu, ndipo aliyense wofuna kukhala ndi malo oyamba pakati panu ayenera kukhala kapolo wanu, monga momwe Mwana wa Munthu anadzera osati kudzatumikiridwa, koma kutumikira anthu ena, ndi kupereka moyo wake kuwombola ena ambiri.”—Mateyu 20:25-28, An American Translation.
6. (a) Ponena za akulu, kodi ndi mbali zazikulu zotani zimene zimawonekera mwapadera? (b) Kodi mpingo uli ndi chifukwa chabwino kuyembekezerera chiyani kuchokera kwa akulu, ndipo kodi amuna amenewa ayenera kudziwona motani?
6 Mwamuna Wachikristu amene ‘akukalamira malo antchito ya woyang’anira akukhumba ntchito yabwino.’ (1 Timoteo 3:1) Pamene tilingalira zimenezi ndi uphungu wa Yesu wongotchulidwa kumene, mbali zazikulu izi zimawonekera mwapadera: (1) Akulu Achikristu sayenera kuchitirana nkhalwe; (2) osenza thayo pakati pa atsatiri a Yesu ayenera kukhala akapolo awo, osati ambuye awo; ndipo (3) amuna okalamira malo antchito a woyang’anira ayenera kuwawona monga “ntchito yabwino,” osati monga malo apamwamba. (Miyambo 25:27; 1 Akorinto 1:31) Liwu lakuti “mkulu” silimakweza mwamuna aliyense pamwamba pa alambiri ena a Yehova. M’malomwake, mpingo uli ndi chifukwa chabwino cha kuyembekezerera akulu onse kukhala amuna achikulire mwauzimu, ozoloŵera, ndi odzichepetsa amene amatsogolera mu utumiki wopatulika. Ndithudi, akulu ayenera kudziwona monga akapolo osanunkha kanthu a Yehova Mulungu, Yesu Kristu, ndi Akristu anzawo.—Aroma 12:11; Agalatiya 5:13; Akolose 3:24.
7. (a) Kodi ndimotani mmene akulu ayenera kugwiritsirira ntchito 2 Akorinto 1:24 pochita ndi ena? (b) Kodi nchiyani chimene akulu ayenera kuchita ndi malangizo olandiridwa kuchokera ku Bungwe Lolamulira?
7 Mwachibadwa kutumikira ena modzichepetsa kumatetezera mkulu kusayesa “kuchita ufumu” pa iwo. Ndipo nkwabwino chotani nanga mmene kuliri kuti oyang’anira athu amasonyeza mkhalidwe wofanana ndi wa Paulo! Iye anawuza Akristu ku Korinto kuti: ‘Sindife ambuye pa chikhulupiriro chanu, koma ndife antchito anzanu kaamba ka chimwemwe chanu.’ (2 Akorinto 1:24) Motero, awo amene amasonyeza uyang’aniro wachikondi samalemetsa okhulupirira anzawo ndi malamulo osayenerera aumunthu. M’malomwake, oyang’anira pakati pa Mboni za Yehova amatsogozedwa ndi malamulo amakhalidwe abwino Amalemba ndi kupereka utumiki wachifundo, ndi wothandiza. Iwo amasonyezanso nkhaŵa yaikulu kaamba ka gulu la Mulungu mwa kugwiritsira ntchito mofulumira malangizo olandiridwa kuchokera ku Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova.—Machitidwe, mutu 15.
8. Kodi ndi mkhalidwe wotani umene Paulo anali nawo kulinga kwa okhulupirira anzake, ndipo kodi ndimotani mmene ichi chiyenera kuyambukirira akulu a m’zaka za zana la 20?
8 Chifukwa chakuti Paulo anali wokoma mtima kulinga ku gulu la Mulungu, iye anakhoza kuwuza Akristu ku Tesalonika kuti: “Tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga mmene mlezi afukata ana ake a iye yekha; kotero ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.” (1 Atesalonika 2:7, 8) Paulo anachita monga momwe amachitira mlezi, amene amakonda ana ake mozama kwambiri kotero kuti amaika ubwino wawo pamwamba pa wake ndipo ali ndi nkhaŵa yachifundo kwa iwo. Ndimotani nanga mmene ichi chiyenera kufulumizira akulu a m’zaka za zana la 20 kuchitira gulu la Mulungu mokoma mtima!
Magwero a Mpumulo ndi Chitsitsimulo
9. Kodi ndi mikhalidwe yotani ya anthu amakono a Yehova yonenedweratu pa Yesaya 32:1, 2?
9 Akuloza ku nthaŵi ino ya ulamuliro wa Ufumu wochitidwa ndi Yesu Kristu, mneneri Yesaya ananeneratu kuti mfumu ikakhoza ‘kulamulira m’chilunjiko’ ndipo “akalonga” akalamulira ‘m’chilungamo.’ Chotero, akulu m’gulu lateokratiki lamakono akusamalira zabwino za Ufumu wa kumwamba wokhazikitsidwa—ndithudi utumiki waukalonga! Kwa amuna okhala ndi thayo amenewa kumagwira ntchito mawu owonjezereka a ulosi wa Yesaya akutiwo: “Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndipo pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.”—Yesaya 32:1, 2.
10. Kodi mkulu aliyense pakati pa Mboni za Yehova ayenera kukhala magwero a chiyani?
10 Mosiyana ndi atsogoleri achipembedzo otsendereza a Dziko Lachikristu, akulu pakati pa Mboni za Yehova ali magwero a mpumulo ndi chitsitsimulo. Monga mabungwe a amuna achikulire, amapititsa patsogolo mtendere, bata, ndi chisungiko pakati pa anthu a Yehova. Monga munthu, mkulu aliyense angathandizire ku mkhalidwe wabwino kwambiri umenewu mwa kuchitira gulu la Mulungu mokoma mtima.
Ndi Chiweruzo ndi Chilungamo
11. (a) Kodi ndi mkhalidwe wozoloŵereka wotani pakati pa Akristu a m’zaka za zana loyamba umene uli wofunga m’mipingo yambiri ya Mboni za Yehova lerolino? (b) Kodi oyang’anira ali ndi thayo lotani kulinga ku mpingo, ndipo chifukwa ninji?
11 Ngakhale kuti mavuto anabuka m’mipingo ina Yachikristu ya m’zaka za zana loyamba, mkhalidwe wawo wozoloŵereka unali wamtendere, umodzi, ndi chisangalalo. (1 Akorinto 1:10-12; 3:5-9; Aefeso 1:2; Yakobo 2:1-9; 3:2-12; 4:11, 12; 1 Yohane 1:3, 4) Mkhalidwe wabwino kwambiri wauzimu ulimonso m’mipingo yambiri ya Mboni za Yehova lerolino chifukwa cha dalitso la Mulungu, utsogoleri wa Kristu, ndi ntchito yokhulupirika ya oyang’anira oikidwa. Kutsimikizira mtendere, umodzi, ndi chisangalalo za mpingo, amuna amenewa amapempha thandizo la Mulungu ndipo amayesayesa mwaphamphu kusunga gulu la Mulungu liri loyera, mwa makhalidwe ndi mwauzimu. (Yesaya 52:11) Gulu lodetsedwa silikakhoza konse kukhala lamtendere ndi lachimwemwe, ndipo ilo ndithudi silikakhala ndi chivomerezo cha Mulungu ndi dalitso. Iye ali “wamaso osalakwa, osapenya choipa,” sakhoza kulekerera choipa. (Habakuku 1:13) Pamenepo, pakati pa zinthu zina, akulu akuyembekezeredwa kusamalira nkhani zachiweruzo mu mkhalidwe waubwino, Wamalemba. Koma kodi ndi ziti za nsonga zofunikira kukumbukira pamene akusamalira nkhani zoterozo?
12. Ngakhale kuti akulu safunikira kuyang’ana m’zochitika zaumwini za munthu zimene sizimaswa malamulo a Baibulo kapena malamulo a makhalidwe abwino, kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa mogwirizana ndi Agalatiya 6:1?
12 Choyamba, m’nkhani zophatikizapo kusemphana kwaumwini, kungakhale kothekera kwa anthuwo kuthetsa nkhanizo pakati pawo. (Mateyu 18:15-17) Popeza kuti akulu sali ‘ambuye a chikhulupiriro chathu,’ iwo sakuyembekezeredwa kufufuza nkhani zaumwini kotheratu zosaphatikizapo kuswedwa koipitsitsa kwa malamulo a Baibulo kapena malamulo a makhalidwe abwino. Mwachibadwa, ngati pali umboni wakuti munthu wina watenga “njira yoipa iye asanaizindikire,” okhala ndi ziyeneretso zauzimu ayenera kuyesa “kubweza munthu woteroyo mu mzimu wodekha.”—Agalatiya 6:1, NW.
13. Kodi Malemba amasonyeza motani kuti akulu ayenera kuchitapo kanthu kokha ngati pali umboni wa cholakwa, osati mphekesera?
13 Akulu afunikira kutumikira “m’chiweruzo,” nthaŵi zonse akumakhala opanda tsankho. Chotero ayenera kuchita mogwirizana ndi umboni wa cholakwacho, osati kokha mphekesera. Paulo analangiza kuti: “Pa mkulu usalandire chomnenera, koma pakhale mboni ziŵiri kapena zitatu.” (1 Timoteo 5:19) Mogwirizana ndi miyezo ya Yehova, mu Israyeli wakale munthu wozengedwa mlandu wakupha munthu anafunikira kuphedwa ‘pakamwa pa mboni ziŵiri kapena zitatu, osati imodzi.’ Ndiponso, mwachiwonekere wonenezedwa mlandu anali ndi mwaŵi wa kuyang’anizana ndi omneneza mlanduwo, ndipo ngati umboni unali wokwanira, ‘dzanja la mbonizo linafunikira kuyamba kumupha.’—Deuteronomo 17:6, 7.
14. (a) Kodi nchiyani chimene Deotrefe molakwika anayesera kuchita? (b) Kodi Mulungu amayembekezera chiyani kwa akulu pamene akusamalira nkhani zachiweruzo?
14 Pafunikira kukhala maziko abwino Amalemba operekera chiweruzo. Ndife achimwemwe chotani nanga kuti oyang’anira a mpingo sali ofanana ndi Deotrefe wonyada wa m’zaka za zana loyamba C.E.! Iye anayesayesa molakwa “kuchotsa mu mpingo” anthu okhumba kulandira abale oyendayenda mowoloŵa manja. Mtumwi Yohane sanawone mopepuka kachitidwe kolakwika kameneka ndi nkhalwe zina koma anachenjeza kuti: “Nditabwera ndidzakumbukira ntchito zake.” (3 Yohane 9, 10) Chotero, komiti yachiweruzo yamakono iyenera kutsimikizira kuti pali maziko Abaibulo kaamba ka mchitidwe wa kuchotsa uliwonse umene achita.a Ndithudi, Mulungu amayembekezera akulu Achikristu kukhala olungama pochita ndi ena. Ndithudi, awo osamalira zochitika za gulu la padziko lapansi la Yehova ayenera kukhala “amuna okhoza, owopa Mulungu, okhulupirika.”—Eksodo 18:21, NW.
15. Kodi ndi mbali yotani imene pemphero liyenera kuchita pa nkhani zachiweruzo?
15 Komiti yachiweruzo Yachikritsu iriyonse iyenera kufunafuna chithandizo cha Yehova mwapemphero lochokera mu mtima. Msonkhano wokumana ndi mbale kapena mlongo wonenezedwa mlandu wa cholakwa chachikulu uyenera kutsegulidwa ndi pemphero. M’chenicheni, kukakhala koyenera kupemphera pa nthaŵi iriyonse mkati mwa kukambitsirana pamene kufunikira chithandizo cha Mulungu kungabuke.—Yakobo 5:13-18.
16. Kodi ndi mu mkhalidwe wotani umene akulu ayenera kusamalira milandu yachiweruzo, ndipo nchifukwa ninji?
16 Akulu amadziŵa kuti wokhulupirira mnzawo wonenezedwa mlandu wakuchita choipa ali “nkhosa” m’gulu la Mulungu ndipo ayenera kuchitiridwa mokoma mtima. (Yerekezani ndi Ezekieli 34:7-14.) Nkhosa zenizeni zimafunikira chisamaliro chokoma mtima, popeza kuti ziri zolengedwa zamantha zodalira pa mbusa wawo kaamba ka chitetezo. Chotero, kodi bwanji ponena za nkhosa zophiphiritsira mu mpingo wa m’malowo? Izo mosakaikira zimadziwona kukhala zosungika m’chisamaliro cha Mbusa Wamkulu, Yehova Mulungu, ndi Mbusa Wabwino, Yesu Kristu. Koma abusa aang’ono a gulu ayenera kuchita m’njira zothandizira mtendere wa mkati ndi lingaliro lachisungiko cha atumiki onga nkhosa a Yehova. Ngati inu muli mbusa wam’ng’ono Wachikristu, pamenepo, kodi abale anu ndi alongo amadziwona kukhala osungika ndi abata m’chisamaliro chanu? Zowonadi, akulu ayenera kuchirikiza zolimba malamulo a Baibulo ndi malamulo a makhalidwe abwino. Koma iwo amafunikiritsidwa ndi Malemba kuchitira nkhosa mwachikondi ndi kuweruza milandu mu mkhalidwe wabata, wadongosolo, wachifundo, ndi wokoma mtima.
17. Kodi ndi mfundo za m’Malemba zotani zimene akulu ayenera kukumbukira, makamaka mkati mwa milandu yachiweruzo?
17 Pokhala opanda ungwiro, “timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri” m’zimene timanena. (Yakobo 3:2) Aliyense waife amafunikira chifundo cha Mulungu ndi “nsembe ya chiwombolo” ya Kristu. (1 Yohane 1:8–2:2; Salmo 130:3) Chotero mbusa wamng’ono Wachikristu afunikira kudziwona kukhala wosanunkha kanthu. Ayenera kukumbukiranso mawu a Yesu akutiwo: “Monga mufuna inu kuti anthu adzakuchitirani inu, muwachitire iwo motero inu momwe.” (Luka 6:31) Uphungu uwu uyenera kugwiritsidwa ntchito makamaka mkati mwa milandu yachiweruzo. Amuna oyeneretsedwa mwauzimu ayenera kuyesa kuwongolera Mkristu wolakwayo ‘mu mzimu wachifatso, pamene akudziyang’anira, kuwopera kuti nawonso angayesedwe.’—Agalatiya 6:1; 1 Akorinto 10:12.
18. (a) Kodi nchiyani chimene chingatulukepo ngati akulu amachitira ena mwaukali mkati mwa milandu yachimweruzo? (b) Chifukwa cha zimene Marko 9:42 amanena, kodi ndi motsutsana ndi kuchita chiyani kumene akulu ndi Akristu ena afunikira kukhala osamala?
18 Ngati akulu achitira ena mwaukali pozenga milandu yachiweruzo, izi zingatsimikizire kukhala zovulaza kwa anthu oterowo. Koma ngakhale ngati kuvulaza kwamaganizo kapena kwakuthupi sikunachitike, pangakhale kuvulazika kokulira kwauzimu, ndipo ziyeneretso za oyang’anira zingakhoze kukaikiridwa. (Yerekezani ndi Yakobo 2:13.) Chifukwa chake, pozenga milandu yachiweruzo ndi pa nthaŵi zina zonse, akulu ayenera kukhala achifundo ndipo ayenera kusamala kusakhumudwitsa ena. Ndithudi, Akristu onse afunikira kusonyeza chisamaliro m’nkhaniyi, popeza Yesu ananena kuti: “Ndipo yense amene [adzakhumudwitsa, NW] kamodzi ka tiana timeneto takukhulupirira ine, kuli kwabwino kwa iye makamaka kuti mwala waukulu wamphero ukolowekedwe m’khosi mwake, naponyedwe iye m’nyanja.” (Marko 9:42) Mwala wa mphero unkakhala waukulu kwenikweni kotero kuti kaŵirikaŵiri nyonga ya nyama mwachibadwa inkafunika kuutembenuza, ndipo palibe aliyense woponyedwa m’nyanja ndi kulemera koteroko komangiridwa m’nkhosi mwake amene akapulumuka. Pamenepa, ndithudi, mkulu ayenera kusamala kusapereka chokhumudwitsa chomwe chikatulukira m’chivulazo chosatha chauzimu kwa iyemwini ndi munthu aliyense wokhumudwitsidwa motero.—Afilipi 1:9-11.
Pitirizani Kusonyeza Nkhaŵa Yachifundo
19. Kodi ndi uphungu wotani umene Petro anapereka kwa akulu anzake, ndipo kodi ndi chiyambukiro chotani chimene kuulabadira moyanja kuli nacho pa ziyembekezo zawo?
19 Mtumwi Petro anasonyeza mmene oyang’anira anzake akaŵetera gulu pamene analemba kuti: “Ŵetani gulu la Mulungu liri mwa inu, ndi kuliyang’anira, osati mokangamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo. Ndipo pakuwonekera mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota.” (1 Petro 5:2-4) Kokha mwa kugwiritsira ntchito uphungu woterowo ndi mwa kusonyeza nkhaŵa yachifundo ku gulu la Mulungu kuti oyang’anira odzozedwa angapeze mphoto ya kumwamba monga zolengedwa zosakhoza kufa zauzimu ndipamenenso akulu okhala ndi ziyembekezo za pa dziko lapansi angalandire moyo wosatha m’Paradaiso alinkudzayo wa chiwunda chonse.
20. (a) Kodi ndimotani mmene abusa aang’ono Achikristu afunikira kuchitira ndi okhulupirira anzawo? (b) Kodi mumamva bwanji ponena za utumiki wopereka chitsanzo ndi chisamaliro chokoma mtima cha akulu achikondi?
20 Onse aŵiri Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu ali Abusa achikondi, ndi achifundo. Chotero pamene kuli kwakuti abusa aang’ono Achikristu amachirikiza zolimba miyezo yaumulungu, iwo ayenera kusonyeza chikondi ndi chifundo pochita ndi okhulupirira anzawo onga nkhosa. Ndithudi, Mboni za Yehova zonse zokhulupirika zimayamikira kwambiri utumiki wopereka chitsanzo wa akulu odzipereka oterowo amene amachinjiriza choikiziridwa chawo ndi kuchitira gulu la Mulungu mokoma mtima. Chiyamikiro chimenecho, limodzi ndi ulemu woyenerera, zingasonyezedwe mwa kukhala omvera kwa oyang’anira pakati pathu.
[Mawu a M’munsi]
a Munthu angachitire apilu chosankha cha kuchotsedwa kwake ngati akhulupirira kuti panali cholakwa chachikulu chopangidwa poweruza.
Kodi Nchiyani Chimene Chiri Lingaliro Lanu?
◻ Kodi ndimotani mmene Yesu Kristu anasonyezera kuti nkhalwe iribe malo pakati pa atsatiri ake?
◻ Kodi akulu ayenera kuchita chiyani pamene malangizo alandiridwa kuchokera ku Bungwe Lolamulira?
◻ Mogwirizana ndi Yesaya 32:1, 2, kodi akulu ayenera kukhala magwero a chiyani?
◻ Kodi Malemba amasonyeza motani kuti akulu sayenera kuweruza pa maziko a mphekesera chabe?
◻ Kodi ndimotani mmene abusa aang’ono Achikristu afunikira kusamalilira gululo?
[Chithunzi patsamba 18]
Pemphero lochokera ku mtima nlofunika pamene komiti yachiweruzo ikumana ndi wokhulupirira mnzawo