Yehova Amapereka Mphamvu kwa Wotopa
“Iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga.”—YESAYA 40:31.
1, 2. Kodi nchiyani chimene Yehova amapatsa awo amene amamkhulupirira, ndipo tidzalingalira za chiyani?
ZIOMBANKHANGA zili pakati pa mbalame zamphamvu koposa zouluka m’mwamba. Zikhoza kuyenda mitunda yaitali popanda kukupiza mapiko ake. Pokhala ndi mapiko amene akhoza kutambasuka mamita oposa aŵiri, “Mfumu ya Mbalame” imeneyo, chiombankhanga chofiirira, chili “chimodzi cha ziombankhanga zochititsa chidwi koposa; chomauluka pamwamba pa mapiri ndi zigwa, [icho] chimauluka kwa maola ambiri pamwamba pa mitandadza ya mapiri, ndiyeno chimakwera m’mwamba mopeyuka kufikira pamene chikhala kadontho mu mlengalenga.”—The Audubon Society Encyclopedia of North American Birds.
2 Polingalira za kukhoza kuuluka kwa chiombankhanga, Yesaya analemba kuti: “[Yehova] alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu. Ngakhale anyamata adzalefuka ndi kulema ndi amisinkhu adzagwa ndithu: koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.” (Yesaya 40:29-31) Nkotonthoza mtima chotani nanga kudziŵa kuti Yehova amapatsa mphamvu ya kupitirizabe kwa awo amene amamkhulupirira, monga ngati kuti akuwapatsa mapiko osatopawo a chiombankhanga chouluka pamwamba! Tsopano, lingalirani za makonzedwe ena amene wapanga a kupatsa mphamvu kwa otopa.
Mphamvu ya Pemphero
3, 4. (a) Kodi Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuchitanji? (b) Kodi tingayembekezere Yehova kuchitanji poyankha mapemphero athu?
3 Yesu analimbikitsa ophunzira ake “kupemphera nthaŵi zonse, [ndipo osaleka, NW].” (Luka 18:1) Kodi kutsanulira Yehova mtima wathu kungatithandizedi kupezanso mphamvu ndi kupeŵa kugonja pamene zitsenderezo za moyo zikhala zochuluka? Inde, koma pali zinthu zina zimene tiyenera kukumbukira.
4 Tiyenera kukhala oona mtima pa zimene timayembekezera Yehova kuchita poyankha mapemphero athu. Mkristu wina amene anagwera mu mkhalidwe waukulu wa tondovi pambuyo pake anati: “Monga momwe zilili ndi matenda ena, panthaŵi ino Yehova samachita zozizwitsa. Koma iyeyo amatithandiza kulimbana nawo ndi kuchira malinga ndi mlingo wa dongosolo lino.” Polongosola chifukwa chake mapemphero ake anathandiza, iye anawonjezera kuti: “Ndinali wokhoza kugwiritsira ntchito mzimu woyera wa Yehova kwa maola 24 patsiku.” Motero, Yehova samatitetezera pa zitsenderezo za moyo zimene zimatilemetsa, koma amapereka “mzimu woyera kwa iwo akumpempha iye.” (Luka 11:13; Salmo 88:1-3) Mzimu umenewo ungatikhozetse kulimbana ndi mayeso kapena chitsenderezo chilichonse chimene tingayang’anizane nacho. (1 Akorinto 10:13) Ngati kuli kofunika, ungathe kutipatsa “ukulu woposa wamphamvu” kuti tipirire kufikira Ufumu wa Mulungu utachotsa mavuto onse otsendereza m’dziko latsopano limene layandikira kwambiri.—2 Akorinto 4:7.
5. (a) Kuti mapemphero athu agwire ntchito, kodi ndi zinthu ziŵiri ziti zimene zili zofunika? (b) Kodi tingapemphere motani ngati tikulimbana ndi chifooko china chakuthupi? (c) Kodi mapemphero athu akhama ndi olunjika adzasonyezanji kwa Yehova?
5 Komabe, kuti mapemphero athu agwire ntchito, tiyenera kuchita khama, ndipo tiyenera kukhala olunjika. (Aroma 12:12) Mwachitsanzo, ngati nthaŵi zina mutopa chifukwa chakuti mukulimbana ndi chifooko china chakuthupi, pachiyambi cha tsiku lililonse, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kusagonja pa chifooko chimenecho tsikulo. Pempherani mofananamo tsiku lonse ndiponso musanakagone usiku uliwonse. Ngati mubwereza kuchichita, pemphani Yehova kukukhululukirani, komanso muuzeni chimene chinakupangitsani kubwereza kuchita chinthucho ndi zimene mudzachita kuti mupeŵe mikhalidwe imeneyo mtsogolo. Mapemphero akhama ndi olunjika otero adzasonyeza kwa “Wakumva pemphero” ameneyo za kufunitsitsa kwanu kupambana mu nkhondoyo.—Salmo 65:2; Luka 11:5-13.
6. Kodi nchifukwa ninji moyenerera tingayembekezere Yehova kumva mapemphero athu ngakhale pamene tilingalira kukhala osayenera kupemphera?
6 Komabe, nthaŵi zina, awo amene amatopa angaganize kuti ali osayenerera kupemphera. Mkazi wina Wachikristu amene analingalira motero anati pambuyo pake: “Kumeneko ndiko kuganiza kwangozi kwambiri chifukwa chakuti zimatanthauza kuti tadziika kukhala oweruza, komatu kuweruza sikwathu.” Zoonadi, “Mulungu mwini wake ndiye [W]oweruza.” (Salmo 50:6) Baibulo limatitsimikizira kuti ngakhale kuti “mmene monse mtima wathu utitsutsa; . . . Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.” (1 Yohane 3:20) Nkotonthoza chotani nanga kudziŵa kuti pamene tidziweruza kukhala osayenerera kupemphera, Yehova sangatilingalire motero! Iye ‘azindikira zonse’ za ife, kuphatikizapo mikhalidwe m’moyo wathu imene ingakhale itatichititsa kudziona kukhala osayenerera. (Salmo 103:10-14) Chifundo chake ndi kumvetsa kwake kwakukulu zimamchititsa kumvetsera mapemphero a “mtima wosweka ndi wolapa.” (Salmo 51:17) Kodi angakane bwanji kumvetsera kufuula kwathu kopempha thandizo pamene iye mwiniyo amatsutsa “wotseka makutu ake polira waumphaŵi”?—Miyambo 21:13.
Chikondi cha Ubale
7. (a) Kodi ndi makonzedwe ena otani amene Yehova wapanga otithandiza kupezanso mphamvu? (b) Kodi ndi kudziŵa za chiyani ponena za ubale wathu kumene kungatilimbitse?
7 Makonzedwe ena amene Yehova wapanga otithandiza kupezanso mphamvu ndiwo ubale wathu Wachikristu. Ndi mwaŵi wamtengo wapatali chotani nanga kukhala mbali ya banja la padziko lonse la abale ndi alongo! (1 Petro 2:17) Pamene tilemetsedwa ndi zitsenderezo za moyo, chikondi cha abale athu chingatithandize kupezanso mphamvu. Motani? Kungodziŵa kuti sitili tokha polimbana ndi zovuta zotsenderezazo mwa iko kokha kungakhale kolimbitsa. Pakati pa abale ndi alongo athu, mosakayikira pali ena amene anakumana ndi zitsenderezo kapena mayeso amodzimodziwo ndi amene akhala ndi malingaliro ofanana kwambiri ndi athu. (1 Petro 5:9) Nkotonthoza kudziŵa kuti zimene tikukumana nazo si zachilendo ndi kuti malingaliro athu saali achilendo.
8. (a) Kodi ndi zitsanzo zotani zimene zimasonyeza mmene tingapezere thandizo ndi chitonthozo mu ubale wathu? (b) Kodi inuyo mwathandizidwa motani kapena kutonthozedwa ndi ‘bwenzi lenileni’?
8 M’chikondi cha ubale wathu timapezamo ‘mabwenzi enieni’ amene, pamene tili m’mavuto, amapereka thandizo lalikulu limene timafuna kwambiri ndi chitonthozo. (Miyambo 17:17) Kaŵirikaŵiri, chomwe chimafunika ndicho mawu okoma mtima kapena machitidwe olingalira ena. Mkristu amene analimbana ndi malingaliro a kukhala wopanda pake akukumbukira kuti: “Panali mabwenzi amene anandiuza zinthu zolimbikitsa ponena za ine mwini kuti andithandize kugonjetsa malingaliro osakondweretsa amene ndinali nawo.” (Miyambo 15:23) Imfa ya mwana wake wamkazi itachitika, mlongo wina anapeza kukhala kovuta poyamba kuimba nyimbo za Ufumu pamisonkhano yampingo, makamaka nyimbo zimene zinatchula chiukiriro. “Nthaŵi ina,” iye akukumbukira motero, “mlongo wina amene anali kumbali ina ya mipando anandiona ndikulira. Anafika pa ine, nandikupatira, ndi kuimba nane nyimbo yonseyo. Ndinadzazidwa ndi chikondi cha abale ndi alongo ndipo ndinali wachimwemwe chifukwa chakuti tinafika pamisonkhanopo, tikumazindikira kuti tidzapezapo thandizo, pa Nyumba ya Ufumupo.”
9, 10. (a) Kodi tingachirikize motani chikondi cha ubale wathu? (b) Kodi ndani makamaka amene amafunikira mayanjano abwino? (c) Kodi tingachitenji kuti tithandize awo amene afunikira chilimbikitso?
9 Ndithudi, aliyense wa ife ali ndi thayo la kuchirikiza chikondi cha ubale Wachikristu. Motero, mitima yathu iyenera ‘kufutukuka’ kuti tikonde abale ndi alongo athu onse. (2 Akorinto 6:13, NW) Zingakhale zachisoni chotani nanga kwa awo amene atopa kulingalira kuti chikondi cha abale kulinga kwa iwo chazirala! Komabe, Akristu ena amasimba kuti ali osungulumwa ndi onyanyalidwa. Mlongo wina amene mwamuna wake amatsutsa choonadi anadandaula kuti: “Kodi ndani amene sakhumba kapena kufuna ubwenzi womangirira, chilimbikitso, ndi mayanjano achikondi? Chonde kumbutsani abale ndi alongo athu kuti timawafuna!” Inde, makamaka aja amene ali olemetsedwa ndi mikhalidwe yawo ya moyo—aja okhala ndi anzawo a mu ukwati osakhulupirira, makolo olera okha ana, aja a matenda osatha, okalamba, ndi ena—amafuna mayanjano abwino. Kodi enafe tingatofunikira kukumbutsidwa zimenezo?
10 Kodi tingachitenji kuti tiwathandize? Tiyeni tifutukule chikondi chathu. Posonyeza mkhalidwe wa kuchereza, tisaiŵaletu awo amene afunikira chilimbikitso. (Luka 14:12-14; Ahebri 13:2) M’malo mwa kuwaganizira kuti mikhalidwe yawo imawaletsa kuvomera, bwanji osayesabe kuwaitanira kwanu? Ndiyeno aloleni kuti adzisankhire. Ngakhale ngati sangavomere, mosakayikira iwo adzalimbikitsidwa kudziŵa kuti ena amawalingalira. Mwina zimenezo ndizo zokha zimene akufuna kuti apezenso mphamvu.
11. Kodi awo amene ali olemetsedwa angafunikire thandizo m’njira ziti?
11 Awo amene amalemetsedwa angafunikire thandizo m’njira zina. Mwachitsanzo, nakubala wina wolera yekha ana, angafune mbale wina wokula msinkhu kuti azicheza ndi mwana wake wamwanuna wamasiye. (Yakobo 1:27) Mbale kapena mlongo wodwala kwambiri angafune munthu womthandiza kukagula zinthu kapena wochita ntchito za panyumba. Wokalamba angalakalake kukhala ndi bwenzi kapena angafune thandizo la kupita mu utumiki wakumunda. Pamene thandizo lotero lili lofunika mopitiriza, zimenezi zimadzetsa ‘mayeso a kuona kwa chikondi chathu.’ (2 Akorinto 8:8) M’malo mwa kunyalanyaza ofuna thandizo chifukwa cha kuwopa nthaŵi ndi zoyesayesa zimene zimafunika, tipambanetu pa mayeso a chikondi cha Chikristu mwa kukhala achifundo ndi othandiza pa zosoŵa za ena.
Mphamvu ya Mawu a Mulungu
12. Kodi Mawu a Mulungu amatithandiza motani kupezanso mphamvu?
12 Munthu amene amaleka kudya, nyonga yake kapena mphamvu sikhalira kumthera. Motero, njira ina imene Yehova amatipatsiramo mphamvu ya kupitirizabe ndiyo ya kuonetsetsa kuti tikudyetsedwa bwino mwauzimu. (Yesaya 65:13, 14) Kodi nchakudya chauzimu chotani chimene wagaŵira? Choposa zonse, ndicho Mawu ake, Baibulo. (Mateyu 4:4; yerekezerani ndi Ahebri 4:12.) Kodi angatithandize motani kupezanso mphamvu? Pamene zitsenderezo ndi mavuto amene timayang’anizana nawo ziyamba kutha nyonga yathu, tingapeze nyonga mwa kuŵerenga za malingaliro ndi nkhondo zenizeni za m’moyo za amuna ndi akazi okhulupirika a m’nthaŵi za Baibulo. Ngakhale kuti anali zitsanzo zabwino kwambiri za osunga umphumphu, iwowo anali anthu “akumva zomwezi tizimva ife.” (Yakobo 5:17; Machitidwe 14:15) Anayang’anizana ndi mayeso ndi zitsenderezo zofanana ndi zathu. Nazi zitsanzo zina.
13. Kodi ndi zitsanzo za m’Malemba zotani zimene zimasonyeza kuti amuna ndi akazi okhulupirika m’nthaŵi za Baibulo anali ndi malingaliro ndi zokumana nazo zofanana kwambiri ndi zathu?
13 Khololo Abrahamu analira kwambiri pa imfa ya mkazi wake ngakhale kuti anakhulupirira chiukiriro. (Genesis 23:2; yerekezerani ndi Ahebri 11:8-10, 17-19.) Davide wolapayo analingalira kuti machimo ake anamchititsa kukhala wosayenera kutumikira Yehova. (Salmo 51:11) Mose analingalira kuti anali wosakhoza kuchita zinthu. (Eksodo 4:10) Epafrodito anapsinjika mtima pamene onse anadziŵa kuti nthenda ina yaikulu inamlepheretsa utumiki wake mu “ntchito ya Kristu.” (Afilipi 2:25-30) Paulo analimbana ndi thupi lochimwa. (Aroma 7:21-25) Euodiya ndi Suntuke, akazi aŵiri odzozedwa a mpingo wa ku Filipi, mwachionekere anali ndi vuto la kusamvana. (Afilipi 1:1; 4:2, 3) Nkolimbikitsa chotani nanga kudziŵa kuti anthu okhulupirika ameneŵa anali ndi malingaliro ndi zokumana nazo zonga zanu, komabe sanagonje! Ndiponso Yehova sanawasiye.
14. (a) Kodi ndi chiŵiya chiti chimene Yehova wagwiritsira ntchito kutithandiza kupezanso nyonga m’Mawu ake? (b) Kodi nchifukwa ninji magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! asimba nkhani zonena za chikhalidwe cha anthu, banja, ndi nkhani za malingaliro?
14 Kuti atithandize kupeza nyonga m’Mawu ake, Yehova amagwiritsira ntchito kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kutipatsa “zakudya panthaŵi yake” mosalekeza. (Mateyu 24:45) Kapolo wokhulupirikayo wagwiritsira ntchito magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwanthaŵi yaitali kuchirikiza choonadi cha Baibulo ndi kulengeza Ufumu wa Mulungu kukhala chiyembekezo chokha cha anthu. Makamaka m’zaka makumi angapo zapitazo, magazini ameneŵa afotokoza nkhani za panthaŵi yake za m’Malemba zonena za chikhalidwe cha anthu, banja, ndi zovuta za malingaliro zimene ngakhale ena a anthu a Mulungu amakumana nazo. Kodi chidziŵitso chimenecho chafalitsidwa kaamba ka chifuno chiti? Kuthandizadi awo amene akukumana ndi zovuta zimenezi kuti apeze nyonga ndi chilimbikitso m’Mawu a Mulungu. Koma nkhani zimenezo zimathandizanso tonsefe kuti tikhale ndi chithunzithunzi chabwino cha zimene ena a abale ndi alongo athu angakhale akukumana nazo. Motero timakhala okonzekera bwino kulabadira mawu a Paulo akuti: “Limbikitsani amantha mtima. Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.”—1 Atesalonika 5:14.
Akulu Amene Ali “Pobisalira Mphepo”
15. Kodi Yesaya analoseranji ponena za awo amene akutumikira monga akulu, ndipo ndi thayo lotani limene zimenezi zimaika pa iwo?
15 Yehova wapereka chinthu chinanso chotithandiza pamene titopa—akulu a mumpingo. Ponena za ameneŵa mneneri Yesaya analemba kuti: “Munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje ya madzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.” (Yesaya 32:1, 2) Pamenepo, akulu ali ndi thayo lofunikira kulikwaniritsa mogwirizana ndi zimene Yehova ananeneratu za iwo. ‘Ayenera kukhala’ otonthoza ndi otsitsimula kwa ena ndi ofunitsitsa “kupitiriza kunyamula zothodwetsa [kapena, “zinthu zovutitsa”; ndiko kuti, “zinthu zolemera”] za wina ndi mnzake.” (Agalatiya 6:2, mawu amtsinde, NW) Kodi iwo angachite motani zimenezi?
16. Kodi nchiyani chimene akulu angachite kuti athandize munthu amene akudziona kukhla wosayenerera kupemphera?
16 Monga momwe tatchulira poyamba, nthaŵi zina munthu amene watopa angaganize kuti ali wosayenerera kupemphera. Kodi akulu angachitenji? Angapemphere naye pamodzi ndi kumpempherera. (Yakobo 5:14) Kupempha Yehova, munthu wotopayo akumvetsera, kuti amthandize kudziŵa mmene iyeyo amakondedwera ndi Yehova ndiponso ndi ena kungakhaledi kotonthoza. Kumva pemphero laphamphu, la pansi pa mtima la mkulu kungathandize kulimbitsa chidaliro cha munthu wovutikayo. Iye angathandizidwe kulingalira kuti ngati akuluwo akukhulupirira kuti Yehova adzayankha mapemphero operekedwa m’malo mwakewo, pamenepo nayenso angakhalenso ndi chikhulupiriro chimenecho.
17. Kodi nchifukwa ninji akulu ayenera kukhala omvetsera achifundo?
17 “Munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula,” Yakobo 1:19 akutero. Kuti athandize otopa kupezanso mphamvu, akulu ayeneranso kukhala omvetsera achifundo. M’zochitika zina ziŵalo za mpingo zingakhale zikulimbana ndi mavuto kapena zitsenderezo zimene sizingathetsedwe m’dongosolo lino la zinthu. Pamenepo, chimene angafunikire sindicho ‘chothetsera’ vuto lawo koma kulankhula ndi womvetsera wabwino—munthu amene sadzawauza mmene ayenera kulingalirira koma ndiye amene adzamvetsera popanda kuweruza.—Luka 6:37; Aroma 14:13.
18, 19. (a) Kodi kukhala wofulumira kumva kwa mkulu kungathandize motani kupeŵa kupangitsa mtolo wa wotopayo kukhala wolemera kwambiri? (b) Kodi nchiyani chimene chimachitika pamene akulu asonyeza “chifundo”?
18 Akulunu, kukhala wofulumira kumva kungakuthandizeni kupeŵa kupangitsa katundu wa wotopayo kukhala wolemera kwambiri mosadziŵa. Mwachitsanzo, ngati mbale kapena mlongo waphonya misonkhano ina kapena wayamba kuzirala mu utumiki wakumunda, kodi iye afunikiradi uphungu wonena za kuchita zambiri mu utumiki kapena wonena zakuti azifika pamisonkhano nthaŵi zonse? Mwinamwake. Koma kodi muli ndi chithunzi chonse cha mkhalidwe wake? Kodi pali kudwaladwala kowonjezereka? Kodi mathayo a banja asintha posachedwapa? Kodi pali mikhalidwe ina kapena zitsenderezo zimene akulemedwa nazo? Kumbukirani kuti, mwina munthuyo angakhale akumva kale liwongo ponena za kusakhoza kuchita zambiri.
19 Nangano, kodi ndimotani mmene mungathandizire mbale kapena mlongoyo? Musanagamule ndi kupereka chilangizo, mvetserani! (Miyambo 18:13) ‘Chititsani’ munthuyo ‘kulankhula’ za mumtima ndi mafunso aluntha. (Miyambo 20:5) Musanyalanyaze malingaliro ameneŵa—alemekezeni. Munthu wotopayo angafunikire kutsimikiziridwa kuti Yehova amasamala za ife ndipo amamvetsa kuti nthaŵi zina mikhalidwe yathu ingatiletse kuchita zina. (1 Petro 5:7) Pamene akulu asonyeza “chifundo” chotero, otopawo ‘adzapeza mpumulo wa miyoyo yawo.’ (1 Petro 3:8; Mateyu 11:28-30) Pamene apeza mpumulo wotero, sadzafunikira kuuzidwa kuchita zowonjezereka; mitima yawo idzawasonkhezera kuchita moyenera zonse zimene akhoza mu utumiki wa Yehova.—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 8:12; 9:7.
20. Popeza kuti mapeto a mbadwo woipawu ayandikira kwambiri, kodi tiyenera kutsimikizira kuchitanji?
20 Tikukhaladi ndi moyo m’nthaŵi yovuta kwambiri m’mbiri yonse ya anthu. Zitsenderezo za kukhala m’dziko la Satana zikuwonjezereka pamene tikuloŵa kwambiri m’nthaŵi ya mapeto. Kumbukirani kuti, monga mkango wosaka nyama, Mdyerekezi amatiyembekezera kuti titope ndi kugonja kotero kuti atigwire mosavuta. Tikuthokoza chotani nanga kuti Yehova amapatsa mphamvu kwa wotopa! Tigwiritsiretu ntchito mokwanira mwaŵi wa makonzedwe amene wapanga akutipatsa mphamvu ya kupitiriza, monga ngati kuti watipatsa mapiko aakulu a chiombankhanga chouluka mu mlengalenga patali. Popeza kuti mapeto a dongosolo loipali ayandikira kwambiri, tsopano sili nthaŵi yoleka kuthamanga mu mpikisano wathu wamphothowo—moyo wosatha.—Ahebri 12:1.
Kodi Yankho Lanu Nlotani?
◻ Kodi tingayembekezere Yehova kuchitanji poyankha mapemphero athu?
◻ Kodi ndi m’njira zotani mmene tingapezere nyonga mu ubale wathu Wachikristu?
◻ Kodi Mawu a Mulungu amatithandiza motani kupezanso mphamvu?
◻ Kodi nchiyani chimene akulu angachite kuti athandize otopa kupezanso mphamvu?
[Chithunzi patsamba 17]
Posonyeza kuchereza, tisaiŵaletu awo amene amafuna chilimbikitso
[Chithunzi patsamba 18]
Akulu angapemphe Yehova kuthandiza otopa kudziŵa mmene amawakondera