Mtengo ‘Umene Tsamba Lake Silifota’
KODI munafikapo kudera kumene kuli mitengo yambiri yobiriwira? Muyenera kuti munasangalala kwambiri mutaiona. Kodi mutaona mitengo ikuluikulu ya masamba obiriwira Mungaganize zoti kudera limenelo kuli chilala? Ayi ndithu. Mutha kungodziwiratu kuti kuderalo kuli madzi ambiri amene akuchititsa kuti mitengoyo izisangalala.
N’chifukwa chake Baibulo limayerekezera anthu athanzi mwauzimu ndi mitengo ikuluikulu yokhala ndi masamba obiriwira. Mwachitsanzo, taonani mavesi atatu oyamba a Salmo loyambirira.
“Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m’njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza. Komatu m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.”
Pa Yeremiya 17:7, 8 palinso mawu ofanana ndi amenewa. Lembali limati: “Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene chikhulupiriro chake ndi Yehova. Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuli madzi, wotambalitsa mizu yake pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lake likhala laliwisi; ndipo suvutika chaka cha chilala, suleka kubala zipatso.”
M’nkhani zonsezi, mitengo ikuyerekezeredwa ndi munthu amene amachita zinthu zoyenera, kusangalala ndi malamulo a Mulungu komanso kumukhulupirira ndi mtima wonse. Ndiyeno mwina mungafunse kuti, ‘kodi zimatheka bwanji kuti mwauzimu munthu wotereyu akhale ngati mtengo wobiriwira.’ Tiyeni tikambirane bwinobwino mavesi amenewa.
‘Kuwokedwa pa Mitsinje ya Madzi’
Mitengo imene tikukambiranayi akuti inawokedwa “pa mitsinje ya madzi” kapena kuti kumene “kuli madzi” osati pa kamtsinje kamodzi kokha ayi. Mawu ngati amenewa amapezekanso pa Yesaya 44: 3, 4. Palembali Yehova Mulungu anafotokoza zimene adzachite posamalira Ayuda olapa amene adzachoka ku ukapolo wa ku Babulo. Kudzera mwa mneneri Yesaya Yehova anati: “Pakuti ndidzathira madzi pa dziko limene lilibe madzi, ndi mitsinje pa nthaka youma. . . . Ndipo iwo adzaphuka pakati pa maudzu, ngati msondodzi m’mphepete mwa madzi.” Lembali likuti anthu odalitsidwa ndi Yehova adzaphuka ngati msondodzi chifukwa choti ali pa “mitsinje” kapena kuti “mphepete mwa madzi.”
Masiku ano pali madera ena komwe alimi amathirira mbewu zawo ndi madzi ochokera m’mitsinje, m’zitsime, m’nyanja kapenanso m’madamu. Nthawi zina anthu amapanga ngalande zoti muzidutsa madzi okathirira minda yawo ya zipatso. M’minda ina madzi omwewa amathandizanso pothirira mitengo yobiriwira ya m’malire a mundawo.
Kodi mitengo imene yawokedwa pa malo otere imakula bwanji? Lemba la Masalmo 1:3 limanena za mtengo umene ‘umabala chipatso chake pa nyengo yake.’ M’nthawi ya Baibulo, kunali mitengo ya mkuyu, makangaza, maapulo, mgwalangwa ndi maolivi. Mosiyana ndi mitengo yambiri ya zipatso, mtengo wa mkuyu umatha kutalika mamita 9 komanso kukhala ndi nthambi zikuluzikulu. Ndipo imakhala yosangalala kwambiri n’kumabala zipatso panthawi yake.
Kale mitengo yambiri ya msondodzi inkamera m’mphepete mwa mitsinje ya ku Suriya ndi ku Palestina. Malemba ambiri amatchula za madzi kapena mitsinje pofotokoza za mitengo ya msondodzi. (Levitiko 23:40) Mtundu winanso wa msondodzi unkapezeka m’malo amene ali ndi madzi ambiri. (Ezekieli 17:5) Mitengo ikuluikulu imeneyi imasonyeza bwino zimene wamasalmo komanso Yeremiya analemba. Iwo anati anthu amene amatsatira malamulo a Mulungu n’kumamukhulupirira ndi mtima wonse amakhala athanzi mwauzimu ndipo ‘zonse zimene amachita amapindula nazo.’ Ndipotu aliyense amafuna kuti zinthu zizimuyendera bwino.
Kusangalala ndi Chilamulo cha Yehova
Masiku ano anthu amachita zinthu zosiyanasiyana kuti akhale osangalala. Amachita khama pa zinthu zimene amaona kuti zingawathandize kukhala otchuka komanso kupeza mwayi winawake. Koma vuto ndi lakuti nthawi zambiri zimenezi sizitheka. Komano kodi n’chiyani makamaka chimene chingam’thandize munthu kukhaladi wosangalala pa moyo wake? Mawu amene Yesu ananena pa ulaliki wa paphiri amayankha funso limeneli. Iye anati: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, popeza ufumu wa kumwamba ndi wawo.” (Mateyo 5:3) Inde, chimwemwe chenicheni sichibwera chifukwa chokhala ndi zinthu zambiri zakuthupi, koma chimabwera chifukwa chozindikira zosowa zathu zauzimu ndi kuyesetsa kuzipeza. Tikatero timakhala athanzi mwauzimu ngati mtengo wathanzi umene umabereka zipatso panthawi yake. Komano kodi tingatani kuti tikhale athanzi mwauzimu?
Wamasalmo anasonyeza kuti choyamba tiyenera kupewa zinthu zinazake. Zina mwa zinthu zimene anatchula ndi “uphungu wa oipa,” “njira ya ochimwa,” ndi “bwalo la onyoza.” Kuti tikhale osangalala tiyenera kukana kugwirizana ndi anthu amene amanyoza ngakhalenso amene amanyalanyaza malamulo a Mulungu.
Chachiwiri n’chakuti, tiyenera kuyamba kusangalala ndi chilamulo cha Yehova. Ngati chinthu chinachake chimatisangalatsa, kodi sitiyesetsa kupeza nthawi yoti tizichita chinthucho? Motero, ngati timasangalala ndi chilamulo cha Mulungu ndiye kuti timaona kuti Mawu a Mulungu n’chinthu chofunika kwambiri ndipo timafunitsitsa kuwadziwa bwino ndi kuwamvetsa.
Chotsiriza n’chakuti tiyenera kusinkhasinkha Mawu a Mulungu kapena kuti ‘kuwalingilira usana ndi usiku.’ Pamenepa ndiye kuti tiyenera kumawerenga Baibulo nthawi zonse, n’kumasinkhasinkha zimene tikuwerengazo. Tizikonda Mawu a Mulungu monga mmene ankawakondera wamasalmo amene ananena mawu akuti: “Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.”—Salmo 119:97.
Inde, tikadziwa Yehova Mulungu molondola n’kumumvetsa bwino komanso n’kuyamba kukhulupirira kwambiri malonjezo ake, n’zosakayikitsa ngakhale pang’ono kuti tidzakhala athanzi mwauzimu. Tikatero, tidzakhala ngati munthu wachimwemwe wotchulidwa ndi wamasalmo uja, amene “zonse azichita apindula nazo.”