CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 17-21
Muzilola Kuti Yehova Aziumba Maganizo ndi Makhalidwe Anu
Muzivomereza ndi mtima wonse kuti Yehova akuumbeni
Yehova amatiumba pogwiritsa ntchito malangizo kapena uphungu
Tiyenera kukhala oumbika komanso omvera
Yehova satikakamiza kuchita zinthu zimene sitikufuna
Woumba amatha kuchita zimene akufuna ndi chinthu chimene akuumbacho
Popeza Yehova anatipatsa ufulu wosankha zochita, tingasankhe kuvomereza kuti azitiumba kapena kukana
Yehova amachita zinthu ndi anthu mogwirizana ndi mmene anthuwo akutsatirira malangizo ake