Chiweruzo cha Yehova pa Aphunzitsi Onama
“Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona chinthu chowopsetsa; achita chigololo, ayenda monama, . . . onse akhala kwa ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ake ngati Gomora.”—YEREMIYA 23:14.
1. Kodi nchifukwa ninji munthu wokhala ndi phande m’chiphunzitso chaumulungu amasenza thayo lolemera kwambiri?
ALIYENSE amene amakhala ndi phande m’chiphunzitso chaumulungu amasenza thayo lalikulu kwambiri. Pa Yakobo 3:1 pamachenjeza kuti: “Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziŵa kuti tidzalangika koposa.” Inde, aphunzitsi a Mawu a Mulungu ali ndi thayo lalikulu kwambiri la kuŵerengeredwa mlandu kuposa la Akristu ena onse. Kodi zimenezi zidzatanthauzanji kwa awo amene amatsimikizira kukhala aphunzitsi onama? Tiyeni tione mkhalidwe wa m’tsiku la Yeremiya. Tidzaona mmene mkhalidwewo unachitira chitsanzo zimene zikuchitika lerolino.
2, 3. Kodi ndichiweruzo chotani chimene Yehova anapereka kupyolera mwa Yeremiya ponena za aphunzitsi onama a Yerusalemu?
2 Mu 647 B.C.E., chaka cha 13 cha kulamulira kwa Mfumu Yosiya, Yeremiya anasankhidwa kukhala mneneri wa Yehova. Yehova anali ndi chidandaulo pa Yuda, chotero anatumiza Yeremiya kukachilengeza. Aneneri, kapena aphunzitsi, onama a Yerusalemu anali kuchita ‘zinthu zoipitsitsa’ m’maso mwa Mulungu. Kuipa kwawo kunali kwakukulu kwakuti Mulungu anayerekezera Yerusalemu ndi Yuda kukhala ofanana ndi Sodomu ndi Gomora. Pa Yeremiya chaputala 23 pamatiuza zimenezi. Vesi 14 limati:
3 “Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona chinthu chowopsetsa; achita chigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ochita zoipa; ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zake; onse akhala kwa ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ake ngati Gomora.”
4. Kodi ndimotani mmene chitsanzo choipa cha makhalidwe a aphunzitsi a Yerusalemu chimafananira ndi Dziko Lachikristu la lerolino?
4 Inde, aneneri ameneŵa, kapena aphunzitsi, anapereka zitsanzo zoipa kwambiri za makhalidwe ndipo, kwenikweni, analimbikitsa anthu kuchita zofananazo. Onani mikhalidwe imene ili m’Dziko Lachikristu lerolino! Kodi sili yofanana ndi ija ya m’tsiku la Yeremiya? Lerolino atsogoleri achipembedzo amalola achigololo ndi ogonana ofanana ziŵalo kukhalabe m’mathayo awo ndipo ngakhale kuwalola kuchititsa mapemphero m’tchalitchi. Kodi nkodabwitsa kuti ziŵalo zambiri za tchalitchi zolembedwa zilinso zamakhalidwe oipa?
5. Kodi nchifukwa ninji makhalidwe oipa a Dziko Lachikristu amapambana aja a Sodomu ndi Gomora?
5 Yehova anafanizira nzika za Yerusalemu ndi zija za Sodomu ndi Gomora. Koma mkhalidwe woipa wa Dziko Lachikristu ngwoipa kuposa uja wa Sodomu ndi Gomora. Inde, ilo lili ndi liŵongo lalikulu pamaso pa Yehova. Aphunzitsi ake amapeputsa malamulo Achikristu a makhalidwe abwino. Ndipo zimenezi zimapititsa patsogolo kululuzika kwamakhalidwe kumene kuli m’mitundu yosiyanasiyana yonyengerera kuchita zoipa. Mkhalidwe umenewu wafalikira kwambiri kwakuti lerolino machitidwe oipa amaonedwa kukhala oyenera.
‘Kuyenda Monama’
6. Kodi nchiyani chimene Yeremiya ananena ponena za kuipa kwa aneneri a Yerusalemu?
6 Tsopano onani zimene vesi 14 limanena ponena za aneneri a Yerusalemu. Iwo anali ‘kuyenda monama.’ Ndipo mbali yotsirizira ya vesi 15 imati: “Kwa aneneri a ku Yerusalemu kuipitsa kwatulukira kumka ku dziko lonse.” Ndiyeno vesi 16 limawonjezera kuti: “Yehova wa makamu atero, Musamvere mawu a aneneri amene anenera kwa inu; akuphunzitsani zachabe; anena masomphenya a mtima wawo, si a m’kamwa mwa Yehova.”
7, 8. Kodi nchifukwa ninji atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu ali ofanana ndi aneneri onama a Yerusalemu, ndipo kodi ndimotani mmene zimenezi zayambukirira opita kumatchalitchi?
7 Mofanana ndi aneneri onama a Yerusalemu, atsogoleri a Dziko Lachikristu nawonso akuyenda monama, akumawanditsa ziphunzitso zampatuko, ziphunzitso zosapezeka m’Mawu a Mulungu. Kodi nziti zimene zili zina za ziphunzitso zonama zimenezi? Kusakhoza kufa kwa moyo, Utatu, purigatoriyo, ndi moto wa helo wozunzira anthu kwamuyaya. Amayabwitsanso makutu a omvetsera awo mwa kulalikira zimene anthu amakonda kumva. Amabwerezabwereza kunena kuti palibe tsoka limene likuyang’anizana ndi Dziko Lachikristu chifukwa chakuti lili ndi mtendere wa Mulungu. Koma atsogoleri achipembedzo akulankhula “masomphenya a mtima wawo.” Izo nzonama. Awo amene amakhulupirira mabodza otero akupatsidwa poizoni yauzimu. Iwo akusocheretsedwa kuloŵa m’chiwonongeko chawo!
8 Lingalirani zimene Yehova akunena kwa aphunzitsi onama ameneŵa mu vesi 21: “Sindinatuma aneneri awa, koma anathamanga; sindinanena ndi iwo, koma ananenera.” Chotero lerolino, atsogoleri achipembedzo sanatumidwe ndi Mulungu, ndipo samaphunzitsa chowonadi chake. Chotulukapo chake? Umbuli waukulu wa kusadziŵa Baibulo uli pakati pa opita kutchalitchi chifukwa chakuti atumiki awo amawaphunzitsa nthanthi zadziko.
9, 10. (a) Kodi ndimaloto amtundu wotani amene aphunzitsi onama a Yerusalemu anali nawo? (b) Kodi ndimotani mmene atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu mofananamo aphunzitsira “maloto onama”?
9 Ndiponso, atsogoleri achipembedzo lerolino amalengeza ziyembekezo zonama. Onani vesi 25: “Ndamva chonena aneneri, amene anenera zonama m’dzina langa, kuti, Ndalota, ndalota.” Kodi iwo ndimaloto amtundu wanji? vesi 32 limatiuza kuti: “Taonani, ine ndidana ndi amene anenera maloto onama, ndi kuwafotokoza ndi kusokeretsa anthu anga ndi zonama zawo, ndi matukutuku awo achabe; koma ine sindinatuma iwo, sindinauza iwo; sadzapindulira konse anthu awa, ati Yehova.”
10 Kodi ndimaloto onama otani kapena ziyembekezo, zimene atsogoleri achipembedzo aphunzitsa? Eya, akuti chiyembekezo chokha cha munthu kaamba ka mtendere ndi chisungiko lerolino ndicho gulu la Mitundu Yogwirizana. M’zaka zaposachedwapa iwo atcha UN kukhala “chiyembekezo chotsiriza cha chigwirizano ndi mtendere,” “bwalo lapamwamba la mtendere ndi chiweruzo cholungama,” “chiyembekezo chachikulu koposa cha mtendere wa dziko.” Nchinyengo chotani nanga! Chiyembekezo chokha cha mtundu wa anthu ndicho Ufumu wa Mulungu. Koma atsogoleri achipembedzo samalalikira ndi kuphunzitsa chowonadi chonena za boma lakumwamba limenelo, limene linali mutu waukulu wa ulaliki wa Yesu.
11. (a) Kodi ndichiyambukiro choipa chiti chimene aphunzitsi onama a Yerusalemu anali nacho padzina la Mulungu mwini? (b) Mosiyana ndi kagulu ka Yeremiya, kodi aphunzitsi onama achipembedzo lerolino achitanji ponena za dzina lamulungu?
11 Vesi 27 limatiuza zowonjezereka. “Aganizira kuti adzaiwalitsa anthu anga dzina langa, ndi maloto awo amene anena munthu yense kwa mnansi wake, monga makolo awo anaiwala dzina [langa kupyolera mwa, NW] Baala.” Aneneri onama a Yerusalemu anachititsa anthu kuiwala dzina la Mulungu. Kodi aphunzitsi onama achipembedzo alerolino sanachite mofananamo? Iwo achita moipitsitsa, akumabisa dzina la Mulungu, Yehova. Amaphunzitsa kuti sikuli kofunikira kuligwiritsira ntchito, ndipo amalichotsa m’matembenuzidwe awo a Baibulo. Amatsutsa mwamphamvu aliyense amene amaphunzitsa anthu kuti dzina la Mulungu ndilo Yehova. Koma kagulu ka Yeremiya, otsalira a Akristu odzozedwa ndi mzimu, limodzi ndi atsamwali awo, achita monga momwe Yesu anachitira. Iwo aphunzitsa mamiliyoni ambiri dzina la Mulungu.—Yohane 17:6.
Kuvumbula Liŵongo Lawo
12. (a) Kodi nchifukwa ninji pali liŵongo lalikulu la mwazi pa aphunzitsi onama achipembedzo? (b) Kodi atsogoleri achipembedzo akhala akuchitanji m’nkhondo zadziko ziŵiri?
12 Kagulu ka Yeremiya kavumbula mobwerezabwereza atsogoleri achipembedzo kukhala aphunzitsi onama amene akutsogolera magulu awo ankhosa kunjira yotakata yachiwonongeko. Inde, otsalira amveketsa bwino lomwe chifukwa chake amalotowo akuyenerera chiweruzo chowopsa cha Yehova. Mwachitsanzo, atumiki a Yehova kaŵirikaŵiri asonyeza lemba la Chivumbulutso 18:24, limene limanena kuti mwa Babulo Wamkulu munapezeka mwazi wa “onse amene anaphedwa padziko.” Taganizirani za nkhondo zonse zimene zamenyedwa chifukwa cha mikangano ya zipembedzo. Nlalikulu chotani nanga liŵongo la mwazi limene lili pa aphunzitsi onama achipembedzo! Ziphunzitso zawo zachititsa magawano ndipo zachirikiza udani wa pakati pa anthu osiyana zipembedzo ndi mafuko. Ponena za Nkhondo Yadziko I, buku lakuti Preachers Present Arms limati: “Atsogoleri achipembedzo anapereka kunkhondoyo tanthauzo lake lofunika losonkhezera lauzimu ndi changu. . . . Mwa kutero tchalitchi chinafikira kukhala mbali yeniyeni ya dongosolo la nkhondo.” Zinalinso motero mu Nkhondo Yadziko II. Atsogoleri achipembedzo anachirikiza kotheratu mitundu yothirana nkhondo ndi kudalitsa magulu awo ankhondo. Nkhondo zadziko ziŵirizo zinayambira m’Dziko Lachikristu mmene achipembedzo chimodzimodzicho anaphana wina ndi mnzake. Magulu akudziko ndi achipembedzo mkati mwa Dziko Lachikristu akupitirizabe kukhetsa mwazi kufikira lerolino. Nzotulukapo zowopsa chotani nanga za ziphunzitso zawo zonama!
13. Kodi ndimotani mmene lemba la Yeremiya 23:22 limatsimikizira kuti atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu alibe unansi ndi Yehova?
13 Chonde onani zimene Yeremiya chaputala 23, vesi 22 akunena: “Koma akadaima mu upo wanga, akadamvetsa anthu anga mawu anga, akadatembenuza iwo ku njira yawo yoipa, ndi ku choipa cha ntchito zawo.” Ngati aneneri achipembedzo a Dziko Lachikristu akadaima mu upo wa Yehova, muunansi wapafupi naye monga ngati kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, pamenepo nawonso akanakhala akukhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo ya Mulungu. Nawonso akanakhala akupangitsa anthu a Dziko Lachikristu kumva mawu a Mulungu mwiniyo. Mmalomwake, aphunzitsi onama amakono achititsa otsatira awo kukhala atumiki akhungu a Mdani wa Mulungu, Satana Mdyerekezi.
14. Kodi ndikuvumbulidwa kwamphamvu kotani kwa atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu kumene kunalengezedwa mu 1958?
14 Kuvumbulidwa poyera kwa atsogoleri achipembedzo kochitidwa ndi kagulu ka Yeremiya kwakhala kwamphamvu. Mwachitsanzo, pa Msonkhano wa Mitundu Yonse wa Chifuniro cha Mulungu wa Mboni za Yehova ku New York City mu 1958, wachiŵiri kwa prezidenti wa Watch Tower Society anapereka ndemanga imene mwapang’ono inati: “Popanda kusinjirira kulikonse kapena kukayikira tikulengeza kuti nakatande wa upandu wonse, kupulupudza kwa ana, udani, mikangano, tsankho, . . . ndi chisokonezo chachikulu ndicho chipembedzo cholakwika, chipembedzo chonyenga; chimene chimachirikizidwa ndi mdani wa anthu wosaonekayo, Satana Mdyerekezi. Anthu amene ali ndi thayo lalikulu koposa la mkhalidwe wa dziko ndiwo alangizi ndi atsogoleri achipembedzo; ndipo aliŵongo lalikulukulu pa onsewa ndiwo atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu. . . . Pambuyo pa zaka zonsezi chiyambire Nkhondo Yadziko I, Dziko Lachikristu kwa Mulungu lili m’kaimidwe konga ka Israyeli m’nthaŵi ya Yeremiya. Inde, Dziko Lachikristu likuyang’anizana ndi chiwonongeko chowopsa kwambiri ndi chowononga kuposa chimene Yeremiya anaona chikuchitikira Yerusalemu.”
Chiweruzo pa Aphunzitsi Onama
15. Kodi ndimawu olosera otani onena za mtendere amene anenedwa ndi kagulu ka atsogoleri achipembedzo? Kodi adzakwaniritsidwa?
15 Mosasamala kanthu za chenjezo limeneli, kodi atsogoleri achipembedzo achita motani chiyambire panthaŵiyo? Monga momwe vesi 17 likusimbira kuti: “Anena chinenere kwa iwo akundinyoza ine, ati Yehova, Mudzakhala ndi mtendere; ndipo kwa yense amene ayenda m’kuumirira kwa mtima wake amati, Palibe choipa chidzagwera inu.” Kodi zimenezi nzowona? Ayi! Yehova adzavumbula chiyengo cha maulosi ameneŵa a atsogoleri achipembedzo. Iye sadzakwaniritsa zimene iwo akunena m’dzina lake. Komabe, chitsimikiziro chonama cha atsogoleri achipembedzo chakuti ali pamtendere ndi Mulungu nchonyenga kwambiri!
16. (a) Kodi mkhalidwe wamakhalidwe wa dzikoli ngwotani, ndipo kodi ndani amene ali ndi mbali ya liŵongo lake? (b) Kodi kagulu ka Yeremiya kakuchitanji ponena za malingaliro a makhalidwe oluluzika a dzikoli?
16 Kodi mukuganiza kuti, ‘Chiyani, ineyo kupusisitsidwa ndi ziphunzitso zonama za atsogoleri achipembedzo? Kutalitali!’ Ayi, musakhale wotsimikizira motero! Kumbukirani kuti ziphunzitso zonama za atsogoleri achipembedzo zachirikiza makhalidwe oluluzika onyengerera onyansa. Ziphunzitso zawo zolekerera zimalungamitsa pafupifupi chilichonse, mosasamala kanthu kuti nchoipa motani. Ndipo mkhalidwe woluluzika umenewu umapezeka m’mitundu yonse ya zosangulutsa, akanema, TV, magazini, ndi nyimbo. Pamenepo, ife tiyenera kusamala kwambiri, apo phuluzi tidzagwera m’chisonkhezero cha mkhalidwe woluluzika ndi wokopa umenewu. Achichepere angagwidwe mumsampha wa mavidiyo oluluza ndi nyimbo. Kumbukirani kuti mzimu wakuti chilichonse nchololedwa umenewu wa anthu lerolino uli chotulukapo chachindunji cha ziphunzitso zonama za atsogoleri achipembedzo ndi kulephera kwawo kuchirikiza miyezo yolungama ya Mulungu. Kagulu ka Yeremiya kakulimbana ndi malingaliro oipa ameneŵa ndipo kakuthandiza atumiki a Yehova kuti akane kuipa kumene kukukantha Dziko Lachikristu.
17. (a) Malinga ndi kunena kwa Yeremiya, kodi ndichiweruzo chotani chimene chinalinkudza pa Yerusalemu woipa? (b) Kodi nchiyani chimene chidzachitikira Dziko Lachikristu posachedwapa?
17 Kodi nchiweruzo chotani chimene aphunzitsi onama a Dziko Lachikristu adzalandira kwa Yehova, Woweruza wamkulu? Mavesi 19, 20, 39, ndi 40 akuyankha kuti: “Taonani, chimphepo cha Yehova, kupsa mtima kwake, kwatuluka, inde chimphepo chozungulira; chidzagwa pamutu pa woipa. Mkwiyo wa Yehova sudzabwerera, mpaka atachita, mpaka atatha maganizo a mtima wake; . . . chifukwa chake, taonani, ndidzakuiŵalani inu konse, ndipo ndidzakuchotsani, ndi mudzi umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, ndidzauchotsa pamaso panga; ndipo ndidzakutengerani inu chitonzo chamuyaya, ndi manyazi amuyaya, amene sadzaiŵalika.” Zonsezo zinachitikira Yerusalemu woipa ndi kachisi wake, ndipo tsopano tsoka lofananalo lidzachitikira Dziko Lachikristu loipalo!
Kulengeza “Katundu wa Yehova”
18, 19. Kodi Yeremiya analengeza za “katundu wa Yehova” wotani kwa Yuda, ndipo ali ndi manthauzo otani?
18 Chotero, kodi ndithayo lotani limene lili la kagulu ka Yeremiya ndi atsamwali awo? Vesi 33 limatiuza kuti: “Pamene anthu awa, kapena mneneri, kapena wansembe, adzakufunsa iwe, kuti, Katundu wa Yehova ndichiyani? pamenepo uziti kwa iwo, Katunthu wanji? [Anthu inu—ndinu katunduyo!, NW] Ndidzakuchotsani inu, ati Yehova.”
19 Liwu Lachihebri lotembenuzidwa kuti “katundu” lili ndi matanthauzo aŵiri. Lingatanthauze chilengezo champhamvu chaumulungu kapena kanthu kena kolemetsa munthu ndi komtopetsa. Panopo mawu akuti “katundu wa Yehova” amatanthauza ulosi wamphamvu—chilengezo chakuti Yerusalemu anali kudzawonongedwa. Kodi anthu anakonda kumva mawu aulosi olemera otero amene Yeremiya analengeza mobwerezabwereza ochokera kwa Yehova? Ayi, anthuwo ananyodola Yeremiya akumati: ‘Kodi uli ndi ulosi (katundu) wotani tsopano? Tikudziŵa kuti ulosi wako udzakhalanso katundu wina wotopetsa!’ Koma kodi Yehova anawauzanji? Izi: “Anthu inu—ndinu katunduyo! Ndidzakuchotsani inu, ati Yehova.” Inde, anthu ameneŵa anali katundu kwa Yehova, ndipo analinganiza zowachotsa kuti asamtopetsenso.
20. Kodi nchiyani chimene chili “katundu wa Yehova” lerolino?
20 Kodi nchiyani chimene chili “katundu wa Yehova” lerolino? Ndicho uthenga wa ulosi wamphamvu wochokera m’Mawu a Mulungu. Ngwolemera ndi uthenga wa chiwonongeko, ukumalengeza chiwonongeko choyandikiracho cha Dziko Lachikristu. Ponena za anthu a Yehova, tili ndi thayo lalikulu la kulengeza “katundu wa Yehova” ameneyu. Pamene mapeto akuyandikira, tiyenera kuuza onse kuti anthu osokera a m’Dziko Lachikristu ali “katundu,” inde, “katundu!” kwa Yehova Mulungu, ndi kuti iye posachedwa adzataya “katundu” ameneyu mwa kulekerera Dziko Lachikristu kuloŵa m’tsoka.
21. (a) Kodi nchifukwa ninji Yerusalemu anawonongedwa mu 607 B.C.E.? (b) Pambuyo pa chiwonongeko cha Yerusalemu, kodi nchiyani chimene chinachitikira aneneri onama ndi mneneri wowona wa Yehova, zikumatipatsa chitsimikizo chotani lerolino?
21 Chiweruzo cha Yehova chinaperekedwa m’tsiku la Yeremiya pamene Ababulo anawononga Yerusalemu mu 607 B.C.E. Monga momwe kunanenedweratu, chimenecho chinachititsa ‘mtonzo ndi manyazi’ kwa Aisrayeli ouma khosi, opanda chikhulupiriro amenewo. (Yeremiya 23:39, 40) Chinawasonyeza kuti Yehova, amene anamnyoza mobwerezabwereza, potsirizira pake anali atawasiya kuti akumane ndi zotsatirapo za kuipa kwawo. Pomalizira pake pakamwa pa aneneri awo onama odzitukumulawo panatontholetsedwa. Komabe, pakamwa pa Yeremiya panapitirizabe kulosera. Yehova sanamsiye. Mofanana ndi zimenezi, Yehova sadzaziya kagulu ka Yeremiya pamene chigamulo chake champhamvu chitsogolera kukuphwanyidwa kwa moyo wa atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu ndi awo amene amakhulupirira mabodza awo.
22. Kodi Dziko Lachikristu lidzafikitsidwa kumkhalidwe uti ndi ziweruzo za Yehova?
22 Inde, mkhalidwe wosakazidwa, wabwinja wa Yerusalemu pambuyo pa 607 B.C.E. udzakhala wofanana ndendende ndi mmene Dziko Lachikristu lachipembedzo lidzaonekera litachotseredwa chuma chake ndi kuvumbulidwa mochititsa manyazi. Ichi nchiweruzo choyenerera chimene Yehova walamula kuti chiperekedwe pa aphunzitsi onama. Chiweruzocho sichidzalephera. Monga momwe mauthenga onse ouziridwa achenjezo a Yeremiya anakwaniritsidwira kalelo, adzakwaniritsidwanso m’nthaŵi yamakono. Chotero tikhaletu monga Yeremiya. Tiyenitu tilengeze mopanda mantha za katundu waulosi wa Yehova kwa anthu, kotero kuti adzadziŵa chifukwa chake mlingo wonse wa chiweruzo chake ukudza pa aphunzitsi onama onse achipembedzo!
Mafunso a Kupenda
◻ Kodi Yerusalemu wakale anali woipa motani m’lingaliro la Yehova?
◻ Kodi ndim’njira zotani mmene Dziko Lachikristu ‘layendera monama’?
◻ Kodi ndimotani mmene liŵongo la atsogoleri achipembedzo amakono lavumbulidwira?
◻ Kodi ndi “katundu wa Yehova” wotani amene tsopano akulengezedwa?
[Chithunzi patsamba 8]
Aneneri a Yerusalemu anachita ‘zinthu zoipitsitsa’
[Chithunzi patsamba 9]
“Anena masomphenya a mtima wawo”
[Chithunzi patsamba 10]
Yerusalemu pambuyo pa kuwonongedwa kwake amachitira fanizo choikidwiratu chotsiriza cha Dziko Lachikristu