Zipatso—Zabwino ndi Zoipa
“Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, mitanga iŵiri ya nkhuyu . . . Mtanga umodzi unali ndi nkhuyu zabwinobwino, ngati nkhuyu zoyamba kucha; ndipo mtanga umodzi unali ndi nkhuyu zoipaipa, zosadyeka, zinali zoipa.”—YEREMIYA 24:1, 2.
1. Kodi ndimotani mmene Yehova anasonyezera chifundo kwa anthu ake, Israyeli, koma kodi iwo analabadira motani?
CHAKACHO chinali 617 B.C.E. Kunali kutangotsala zaka khumi zokha kuti chiweruzo choyenera cha Yehova chiperekedwe pa Yerusalemu ndi anthu ake. Yeremiya anali atalalikira kale mwamphamvu kwazaka 30. Onani mafotokozedwe omvekera bwino a Ezara ponena za mkhalidwewo, monga momwe aliri pa 2 Mbiri 36:15: “Yehova Mulungu wa makolo awo anatumiza kwa iwo ndi dzanja la mithenga yake, nalaŵirira mamaŵa kuituma, chifukwa anamvera chifundo anthu ake, ndi pokhala pake.” Ndipo kodi kuyesayesa konseku kunapindulanji? Mwachisoni, Ezara akupitiriza kusimba mu vesi 16 kuti: “Koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mawu ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Mulungu unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.”
2, 3. Fotokozani masomphenya ochititsa chidwi amene Yehova anasonyeza Yeremiya.
2 Kodi zimenezi zinatanthauza kuti mtundu wa Yuda ukafafanizidwiratu? Kuti tipeze yankho, tiyeni tilingalire za masomphenya ofunika amene tsopano anaperekedwa kwa Yeremiya ndi kulembedwa m’chaputala 24 cha buku la dzina lake. Mulungu anagwiritsira ntchito mitanga iŵiri ya nkhuyu m’masomphenya ameneŵa kuphiphiritsira zochitika za anthu ake a pangano. Zimenezi zikachitiridwa chithunzi ndi mitundu iŵiri yosiyana ya zipatso, zabwino ndi zoipa.
3 Pa Yeremiya chaputala 24, pamavesi 1 ndi 2, pamafotokoza zimene mneneri wa Mulungu anaona kuti: “Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, mitanga iŵiri ya nkhuyu yoikidwa pakhomo pa kachisi wa Yehova; Nebukadirezara, mfumu ya ku Babulo atachotsa amnsinga Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akulu a Yuda, ndi amisiri ndi achipala, kuwachotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babulo. Mtanga umodzi unali ndi nkhuyu zabwinobwino, ngati nkhuyu zoyamba kucha; ndipo mtanga umodzi unali ndi nkhuyu zoipaipa zosadyeka, zinali zoipa.”
Nkhuyu Zabwino za m’Masomphenya
4. Kodi ndiuthenga wotonthoza wotani umene masomphenya a nkhuyu anali nawo kwa Aisrayeli okhulupirika?
4 Atafunsa Yeremiya zimene anaona, Yehova anapitiriza kunena m’mavesi 5 mpaka 7 kuti: “Monga nkhuyu zabwino izi, momwemo ndidzasamalira amnsinga a Yuda, [amene ndidzawatumiza kuchokera m’malo ano kumka kudziko la Akasidi, m’njira yabwino. Ndipo ndidzaika diso langa pa iwo m’njira yabwino, NW] ndipo ndidzawabwezanso kudziko ili: ndipo ndidzamangitsa mudzi wawo, osawapasula; ndi kuwabzala, osawazula iwo. Ndipo ndidzapatsa iwo mtima wakundidziŵa, kuti ndine Yehova; nadzakhala anthu anga, ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo; pakuti adzabwera kwa ine ndi mtima wawo.”
5, 6. (a) Kodi ndimotani mmene Aisrayeli ena ‘anatumizidwira m’njira yabwino’ kudziko la Akasidi? (b) Kodi ndimotani mmene Yehova ‘anaikira diso lake pa iwo m’njira yabwino’ pa Aisrayeli okhulupirika ogwidwa undende?
5 Chotero mwa zimene Yehova ananena panopa kukuonekera monga ngati kuti kutsogolo kunali nthaŵi yabwino, kuti mtundu wa Yuda sukafafanizidwa kotheratu. Koma kodi nchiyani chimene chili tanthauzo la mtanga wa nkhuyu zabwinobwino umenewu?
6 Yekoniya, kapena Yehoyakini, anali atakhala mfumu ya Yuda kwa miyezi itatu yokha ndi masiku khumi asanapereke Yerusalemu modzifunira kwa Mfumu Nebukadinezara. Pakati pa otengedwa undende limodzi naye panali Danieli ndi mabwenzi ake Achihebri atatu Hananiya, Misaeli ndi Azariya, ndiponso Ezekieli. Miyoyo yawo inasungidwa ndi mfumu ya ku Babulo, chotero kunganenedwe kuti Yehova anaona miyoyo ya andende onseŵa kukhala yotumizidwa mwanjira yabwino kudziko la Akasidi. Kodi mwaona kuti Yehova analonjezanso ‘kuika diso lake pa iwo m’njira yabwino’? Kodi zimenezi zinakwaniritsidwa motani? Mu 537 B.C.E., zaka 80 pambuyo pake, Yehova anachititsa Mfumu Koresi kupereka lamulo la kulola otsalira a mbadwa zawo kubwerera kudziko la Yuda. Ayuda okhulupirika ameneŵa anamanganso mzinda wa Yerusalemu; anaimika kachisi watsopano wolambiriramo Mulungu wawo, Yehova; ndipo anabwerera kwa iye ndi mtima wawo wonse. Chotero mu zonsezi, kwa Yehova andende ameneŵa ndi mbadwa zawo anali ngati nkhuyu zabwino kwambiri zoyamba kucha.
7. Kodi ndiliti ndipo ndimotani mmene diso la Yehova pakagulu kamakono ka Yeremiya linaliri “m’njira yabwino”?
7 Mungakumbukire kuti munkhani yapitayo yonena za mawu a ulosi wa Yeremiya, tinaona kuti mawuwo ali ndi tanthauzo la m’zaka za zana lathu la 20 lino. Ndipo chaputala 24 nachonso chimatero. Mkati mwa zaka zowopsa za Nkhondo Yadziko I, atumiki odzipatulira a Yehova ambiri anayambukiridwa ndi Babulo Wamkulu m’njira zosiyanasiyana. Koma diso la Yehova loyang’anira ‘linali pa iwo m’njira yabwino.’ Ndipo zinali motero kuti kupyolera mwa Koresi Wamkulu, Yesu Kristu, Yehova anachotsa mphamvu ya Babulo Wamkulu pa iwo ndipo mwapang’onopang’ono anawalowetsa m’paradaiso wauzimu. Aisrayeli auzimu ameneŵa analabadira ndi kubwerera kwa Yehova ndi mtima wawo wonse. Ndiyeno, mu 1931, iwo anali osangalala kulandira dzina lakuti Mboni za Yehova. Zowonadi, tsopano kunanenedwa kuti iwo anali atakhala ngati mtanga wa nkhuyu zabwino kwambiri m’maso mwa Yehova.
8. Kodi ndim’njira yotani imene Mboni za Yehova zalengezera konse kukoma kwa uthenga wa Ufumu konga kwa nkhuyu?
8 Ndipo Mboni za Yehova sizinaphonye chifuno cha kukoma mtima kwapadera kwa Mulungu powamasula ku Babulo Wamkulu. Izo sizinadzisungire kutsekemera konga kwa nkhuyu kwa uthenga wa Ufumu wa mbiri yabwino, koma zakulengeza kulikonse mogwirizana ndi mawu a Yesu pa Mateyu 24:14, NW: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kumitundu yonse.” Ndipo chotulukapo chake? Anthu onga nkhosa oposa 4,700,000 amene sali Aisrayeli auzimu atuluka m’Babulo Wamkulu!
Masomphenya a Nkhuyu Zoipa
9. Kodi ndani amene nkhuyu zoipa za m’masomphenya a Yeremiya zinaimira, ndipo nchiyani chimene chinali kudzawachitikira?
9 Koma bwanji za mtanga wa nkhuyu zoipa m’masomphenya a Yeremiya? Tsopano Yeremiya akutembenukira pa mawu a Yehova opezeka pa Yeremiya chaputala 24, mavesi 8 mpaka 10 akuti: “Monga nkhuyu zoipa, zosadyeka, poti nzoipa; ntheradi atero Yehova, Chomwecho ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi akulu ake, ndi otsala a m’Yerusalemu, amene atsala m’dziko ili, ndi amene akhala m’dziko la Aigupto. Ndipo ndidzawapatsa akhale chowopsetsa choipa ku maufumu a dziko lapansi; akhale chitonzo ndi nkhani ndi choseketsa, ndi chitemberero, monse mmene ndidzawapitikitsiramo. Ndipo ndidzatuma lupanga, ndi njala, ndi chaola mwa iwo, mpaka athedwa m’dziko limene ndinapatsa iwo ndi makolo awo.”
10. Kodi nchifukwa ninji Yehova anaona Zedekiya kukhala ‘nkhuyu yoipa’?
10 Chotero Zedekiya anakhaladi ‘nkhuyu yoipa’ m’maso mwa Yehova. Iye sanangopandukira kokha Mfumu Nebukadinezara mwa kuswa lumbiro la kukhulupirika limene anapanga kwa mfumu imeneyo m’dzina la Yehova komanso anakana kotheratu chifundo choperekedwa ndi Yehova kwa iye kupyolera mwa Yeremiya. Kunena zowona, anafikiradi ngakhale pakuika Yeremiya muukaidi! Nchifukwa chake Ezara amafotokoza mwachidule mkhalidwe wa maganizo a mfumuyo pa 2 Mbiri 36:12 kuti: “Nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wake; sanadzichepetsa.” M’maso mwa Yehova, Zedekiya ndi awo amene anatsala mu Yerusalemu anali ngati mtanga wa zipatso zoipa, zowola!
Nkhuyu Zowola Zophiphiritsa m’Tsiku Lathu
11, 12. Kodi ndani amene akudziŵikitsidwa kukhala nkhuyu zoipa lerolino, ndipo kodi nchiyani chimene chidzawachitikira?
11 Tsopano unguzani padziko lapansi lerolino. Kodi muganiza kuti tingapeze mtanga wophiphiritsira wa nkhuyu zoipa? Tiyeni tipende zenizeni mwa kuyerekezera tsiku lathu ndi la Yeremiya. M’zaka za zana la 20 lino, Yehova wagwiritsira ntchito kagulu ka Yeremiya, otsalira odzozedwa, kuchenjeza mitundu mopitirizabe za mkwiyo wake ulinkudzawo pachisautso chachikulu. Iye wafulumiza mitundu ya anthu kuti imlemekeze chifukwa cha dzina lake, kumlambira mumzimu ndi m’chowonadi, ndi kuvomereza Mwana wake wolamulira, Kristu Yesu, kukhala Wolamulira dziko lapansi woyenera. Kodi pakhala kulabadira kotani? Ndendende ndi m’tsiku la Yeremiya. Mitundu ikupitirizabe kuchita zoipa pamaso pa Yehova.
12 Kodi ndani amene akusonkhezera mzimu wachipanduko umenewu? Kodi ndani amene akupitirizabe kunyodola amithenga onga Yeremiya a Mulungu ameneŵa mwa kutsutsa kuyenera kwawo kwa kukhala atumiki a Mulungu? Kodi ndani amene akupitirizabe kunyoza Mawu a Mulungu? Kodi ndani lerolino amene akhala osonkhezera zochuluka za zizunzo za Mboni za Yehova? Yankho lake kwa onse lili poyera—ndilo Dziko Lachikristu, makamaka atsogoleri achipembedzo! Ndipo tangoonani zipatso zonse zowola, zoipa za Dziko Lachikristu zimene zinafotokozedwa m’nkhani yapitayo. O, inde, ulipodi mtanga wophiphiritsira wa nkhuyu zoipa m’dziko lapansi lerolino. Kwenikweni, Yehova akunena kuti ‘sizingadyedwe chifukwa cha kuipa kwake.’ Mawu a Yehova kupyolera mwa Yeremiya akumvekabe kufikira m’tsiku lathu lino akuti: ‘Adzafikira chimaliziro chawo!’ Mkwiyo wa Yehova pa Dziko Lachikristu sudzakhala ndi cholanditsa.
Phunziro Lotichenjeza
13. Polingalira za mawu a Paulo opezeka pa 1 Akorinto 10:11, kodi tiyenera kuzindikira motani masomphenya a mitanga iŵiri ya nkhuyu?
13 Pamene tikupenda matanthauzo a uthenga wachenjezo wouziridwa wa Yeremiya, mawu a mtumwi Paulo pa 1 Akorinto 10:11 akumveka m’makutu mwathu: “Koma izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthaŵi ya pansi pano adafika pa ife.” Kodi ifeyo talabadira chenjezo loperekedwa kwa ife ndi masomphenya a mitanga iŵiri ya nkhuyu amenewa? Zimene takhala tikukambitsirana ndizo mbali yofunika ya zinthu zimene zinagwera Israyeli monga chitsanzo chotichenjeza.
14. Kodi ndimotani mmene Israyeli analabadirira chisamaliro chachikondi cha Yehova?
14 Potsirizira pake, tiyeni tikumbukire mawu a Yehova kwa Mfumu Davide ponena za Israyeli, monga momwe timawapezera pa 2 Samueli 7:10 kuti: “Ndipo ndidzaikira anthu anga Israyeli malo, ndi kuwaoka.” Yehova anasamalira mwachikondi anthu ake, Israyeli, m’njira iliyonse. Panali chifukwa chabwino chakuti Aisrayeli atulutse zipatso zabwino m’miyoyo yawo. Iwo anangofunikira kokha kumvetsera chiphunzitso chaumulungu cha Yehova ndi kusunga malamulo ake. Komabe, oŵerengeka okha anachita zimenezo. Ambiri a iwo anali ouma khosi ndi amayendedwe osalongosoka kwakuti anabala zipatso zoipa, zowola.
15. Kodi ndimotani mmene Israyeli wauzimu lerolino ndi atsamwali awo onga nkhosa alabadirira chifundo cha Yehova?
15 Chabwino, bwanji za tsiku lathu? Yehova wasonyeza chifundo chachikulu kwa otsalira ake a Israyeli wauzimu ndi atsamwali awo onga nkhosa. Diso lake lakhala lili pa iwo nthaŵi zonse chiyambire kulanditsidwa kwawo kwauzimu mu 1919. Monga momwe ananeneratu kupyolera mwa Yesaya, iwo amalandira malangizo aumulungu tsiku ndi tsiku kuchokera kwa Mphunzitsi wamkulu koposa m’chilengedwe chonse, Yehova Mulungu. (Yesaya 54:13) Chiphunzitso chaumulungu chimenechi, choperekedwa kupyolera mwa Mwana wake wokondedwa, Yesu Kristu, chachititsa mtendere wochuluka pakati pawo ndipo chawadzetsa mosalekeza muunansi wapafupi ndi Yehova. Ndimkhalidwe wauzimu wokondweretsa chotani nanga umene zimenezi zimapereka kwa tonsefe kuti tidziŵe Yehova, kumumvetsera, ndi kupitirizabe kubala zipatso zabwino m’miyoyo yathu—zipatso zimene zimadzetsa chitamando kwa Yehova! Zimasungitsa moyo wathu weniweniwo!
16. Kodi ndikugwiritsira ntchito kwaumwini kotani kwa masomphenya a mitanga iŵiri ya nkhuyu kumene aliyense wa ife angapange?
16 Koma mosasamala kanthu za chifundo chachikulu cha Mulungu, padakali ena amene amakhala opanduka ndi amitima youma, monga momwe ambiri anachitira m’Yuda wakale, ndi amene amabala zipatso zoipa, zowola m’miyoyo yawo. Nzatsoka chotani nanga zimenezi! Aliyense wa ife asaphonyetu phunziro lachenjezo lofotokozedwa bwino lomwe kwa ife ndi mitanga iŵiri imeneyi ya nkhuyu ndi zipatso zake—zabwino ndi zoipa. Pamene chiweruzo choyenera cha Yehova pa Dziko Lachikristu lopatuka chikudza mofulumira, tilabadiretu chilangizo cha mtumwi Paulo chakuti: “Mukayende koyenera [Yehova, NW] kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino.”—Akolose 1:10.
Kupenda “Zipatso—Zabwino ndi Zoipa” ndi ndime 1-4 za “Mlandu wa Yehova ndi Mitundu ya Anthu”
◻ Kodi mtanga wa nkhuyu zabwino umaimiranji?
◻ Kodi ndimotani mmene mtanga wa m’masomphenya wa nkhuyu zoipa waonekerera?
◻ Kodi ndiphunziro lochenjeza lotani limene uthenga wa Yeremiya umapereka kwa ife?
◻ Kodi nchiyani chimene chinali chapadera ndi chaka cha 607 B.C.E.? ndi 1914 C.E.?
[Chithunzi patsamba 15]
Mofanana ndi nkhuyu zabwino, anthu a Mulungu abala zipatso zokoma za Ufumu
[Chithunzi patsamba 15]
Dziko Lachikristu latsimikizira kukhala ngati mtanga wa nkhuyu zoipa