Kodi Muli Ndi “Mtima Wodziwa” Yehova?
“Ndidzawapatsa mtima wodziwa kuti ine ndine Yehova. Iwo adzakhala anthu anga.”—YER. 24:7.
1, 2. N’chifukwa chiyani anthu ena amakonda nkhuyu?
KODI inuyo munalawapo nkhuyu? Anthu ambiri amakonda nkhuyu moti m’madera ena zimalimidwa kwambiri. Ayuda akale ankaona kuti nkhuyu n’zofunika kwambiri. (Nah. 3:12; Luka 13:6-9) Masiku anonso, anthu ena amanena kuti nkhuyu zili ndi zinthu zambiri zothandiza kuti mtima wathu ukhale wathanzi.
2 Yehova anayerekezera nkhuyu ndi mtima. Koma sikuti Mulungu ankangonena mmene nkhuyu zimatithandizira kuti tikhale ndi thanzi labwino. Zimene iye ananena zinali zophiphiritsa. Mawu ake, kudzera mwa mneneri Yeremiya, akukhudza mtima wanu komanso wa anzanu. Tikamakambirana zimene Yehova ananena, ganizirani zimene Akhristufe tingaphunzirepo.
3. Kodi nkhuyu zotchulidwa mu chaputala 24 cha buku la Yeremiya zinkaimira ndani?
3 Choyamba tiyeni tikambirane zimene Mulungu ananena m’nthawi ya Yeremiya zokhudza nkhuyu. Mu 617 B.C.E., Ayuda sankatumikira Mulungu mokhulupirika. Mulungu anaonetsa Yeremiya masomphenya onena zimene zidzachitike m’tsogolo. Iye anayerekezera anthu a m’nthawiyo ndi mitundu iwiri ya nkhuyu, zina “zabwino kwambiri” ndipo zina “zoipa kwambiri.” (Werengani Yeremiya 24:1-3.) Nkhuyu zoipazo zinkaimira Mfumu Zedekiya komanso anthu ena ngati iyeyo amene anadzazunzidwa ndi Mfumu Nebukadinezara ndi gulu lake la asilikali. Koma nkhuyu zabwino zinkaimira Ezekieli, Danieli ndi anzake atatu omwe anali kale ku Babulo ndiponso Ayuda ena omwe ankayembekezera kutengedwanso kupita ku Babulo. Ena a anthu amenewa anali oti adzabwerera ku Yerusalemu n’kukamanganso kachisi.—Yer. 24:8-10; 25:11, 12; 29:10.
4. Kodi ndi mawu olimbikitsa ati amene Mulungu ananena okhudza nkhuyu zabwino?
4 Ponena za anthu amene anali ngati nkhuyu zabwino, Yehova anati: “Ndidzawapatsa mtima wodziwa kuti ine ndine Yehova. Iwo adzakhala anthu anga.” (Yer. 24:7) Lemba limeneli ndi lolimbikitsa kwambiri ndipo m’pamene pachokera mutu wa nkhaniyi. Mulungu amafuna kupatsa anthu ‘mtima womudziwa,’ kapena kuti kutithandiza kukhala anthu amene akufunitsitsa kumudziwa ndiponso kukhala m’gulu lake. Muyenera kuti inunso mukufuna mutakhala ndi mtima woterewu. Kuti zimenezi zitheke, muyenera kuphunzira Mawu a Mulungu ndiponso kutsatira zomwe mukuphunzirazo. Muyeneranso kulapa ndi kutembenuka, kudzipereka kwa Mulungu komanso kubatizidwa m’dzina la Atate, Mwana ndi mzimu woyera. (Mat. 28:19, 20; Mac. 3:19) N’kutheka kuti munachita kale zimenezi, kapena mumasonkhana nthawi zonse ndi Mboni za Yehova ndipo mukuganiza zodzabatizidwa.
5. Kodi zimene Yeremiya analemba zinkakhudza ndani kwenikweni?
5 Kaya tinabatizidwa kale kapena tikuchita zinthu zosonyeza kuti tikufuna kubatizidwa, tonsefe tiyenera kuganizira za khalidwe lathu komanso mmene timaonera zinthu. Tikutero chifukwa cha zimene Yeremiya analemba zokhudza mtima. Machaputala ena a m’buku la Yeremiya amanena za anthu a mitundu imene inazungulira Ayuda. Koma kwenikweni uthenga umene uli m’bukuli unali wopita kwa Ayuda pa nthawi ya maulamuliro a mafumu 5. (Yer. 1:15, 16) Choncho Yeremiya ankanena za amuna, akazi ndiponso ana amene anali mu mtundu womwe unadzipereka kwa Yehova. Makolo awo anasankha okha kukhala mtundu wodzipereka kwa Mulungu. (Eks. 19:3-8) M’nthawi ya Yeremiya, anthuwa anatsimikiziranso kuti ndi mtundu wodzipereka kwa Mulungu. Iwo anati: “Tabwera kwa inu, pakuti inu Yehova ndinu Mulungu wathu.” (Yer. 3:22) Koma kodi mukuganiza kuti anthuwa anali ndi mtima wotani?
PANAFUNIKA OPALESHONI YA MTIMA WOPHIPHIRITSIRA
6. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita chidwi ndi zimene Mulungu ananena zokhudza mtima?
6 Masiku ano, madokotala amagwiritsa ntchito zipangizo zatsopano pofuna kudziwa mmene mtima ulili komanso mmene ukugwirira ntchito. Koma Yehova amadziwa kwambiri mtima wa munthu ngati mmene ankachitira m’nthawi ya Yeremiya. Izi zikuonekera m’mawu ake akuti: “Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa. Ndani angaudziwe? Ine Yehova ndimafufuza mtima, . . . Munthu aliyense ndimamuchitira zinthu monga mwa zochita zake, mogwirizana ndi zipatso za ntchito zake.” (Yer. 17:9, 10) Yehova ‘akamafufuza mtima,’ sayeza mtima wathu weniweni umene pa zaka 70 kapena 80 ukhoza kugunda nthawi 3 biliyoni. Koma iye amafufuza mtima wathu wophiphiritsa. Mtima umenewu ukutanthauza munthu yense wamkati. Ukuimira zokhumba za munthu, maganizo ake, khalidwe lake, mmene amaonera zinthu komanso zolinga zake. Inunso muli ndi mtima umenewu. Mulungu amaufufuza ndipo inunso mukhoza kutero, ngakhale kuti sizingafanane ndi mmene Mulungu amachitira.
7. Kodi Yeremiya ananena kuti Ayuda ambiri a m’nthawi yake anali ndi mtima wotani?
7 Kuti tithe kufufuza mtima wathu, tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi mtima wophiphiritsa wa Ayuda ambiri a m’nthawi ya Yeremiya unali wotani?’ Kuti tiyankhe funso limeneli, taganizirani zimene Yeremiya analemba. Iye anati: “Anthu onse a m’nyumba ya Isiraeli sanachite mdulidwe wa mitima yawo.” Pamenepa Yeremiya sankatanthauza mdulidwe weniweni umene amuna achiyuda ankachita. Tikutero chifukwa iye anati: “Yehova wanena kuti, ‘Taona masiku akubwera ndipo ndidzaimba mlandu aliyense wodulidwa koma amene sanachite mdulidwe wa mtima wake.’” Choncho ngakhale Ayuda omwe anali odulidwa, ‘sanachite mdulidwe wa mtima wawo.’ (Yer. 9:25, 26) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?
8, 9. Kodi Ayuda ambiri ankafunika kuchita chiyani ndi mtima wawo?
8 Zimene Mulungu anauza Ayuda kuchita zikutithandiza kudziwa tanthauzo la ‘kusachita mdulidwe wa mtima.’ Iye anati: “Chitani mdulidwe wa mitima yanu . . . inu anthu a ku Yuda ndi okhala mu Yerusalemu. Chitani zimenezi kuti mkwiyo wanga usayake . . . chifukwa cha zochita zanu zoipa.” Kodi zochita zawo zoipazo zinkachokera kuti? Zinkachokera mumtima mwawo. (Werengani Maliko 7:20-23.) Kudzera mwa Yeremiya, Mulungu ananena kumene kunkachokera zochita zoipa za Ayuda. Mitima yawo inali itapanduka kwambiri. Yehova sankasangalalanso ndi zochita ndiponso zolinga zawo. (Werengani Yeremiya 5:23, 24; 7:24-26.) Choncho Mulungu anauza Ayudawo kuti: “Chitani mdulidwe wa mitima yanu pamaso pa Yehova.”—Yer. 4:4; 18:11, 12.
9 Mofanana ndi Ayuda a m’nthawi ya Mose, Ayuda a m’nthawi ya Yeremiya ankafunika “mdulidwe wa mitima” kapena kuti kuchitidwa opaleshoni ya mtima yophiphiritsira. (Deut. 10:16; 30:6) Izi zinkatanthauza kuti iwo anafunika kusintha maganizo, zokonda komanso zolinga zawo zimene zinali zosemphana ndi zofuna za Mulungu. Zinthuzi n’zimene zinkawachititsa kukhala ndi mtima wosamvera.—Mac. 7:51.
KODI INUYO MULI NDI “MTIMA WODZIWA” YEHOVA?
10. Potengera chitsanzo cha Davide, kodi tiyenera kuchita chiyani?
10 Tikuyamikira kwambiri kuti Mulungu watithandiza kudziwa mtima wophiphiritsa. Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi zimenezi n’zofunikanso kwa Mboni za Yehova masiku ano?’ Sikuti Akhristu ambiri akuchita zoipa moti tingati iwo ndi “nkhuyu zoipa” ngati mmene analili Ayuda akale. Atumiki a Mulungu masiku ano ndi anthu odzipereka komanso oyera. Komabe ganizirani zimene Davide anapempha Yehova. Iye anati: “Ndifufuzeni, inu Mulungu, ndi kudziwa mtima wanga. Ndisanthuleni ndi kudziwa malingaliro anga amene akundisowetsa mtendere, ndipo muone ngati mwa ine muli chilichonse chimene chikundichititsa kuyenda m’njira yoipa.”—Sal. 17:3; 139:23, 24.
11, 12. (a) N’chifukwa chiyani aliyense afunika kufufuza mtima wake? (b) Kodi sitiyenera kuyembekezera Mulungu kuchita chiyani?
11 Yehova amafuna kuti tonsefe tikhale anthu ovomerezeka pa maso pake. Ponena za munthu wolungama, Yeremiya analemba kuti: “Inu Yehova wa makamu, mumasanthula munthu wolungama. Mumaona impso ndi mtima wake.” (Yer. 20:12) Ngati Mulungu Wamphamvuyonse amasanthula mitima, ngakhale ya olungama, kodi nafenso sitiyenera kuyesetsa kufufuza mtima wathu? (Werengani Salimo 11:5.) Tikamachita zimenezi, tikhoza kuzindikira kuti tili ndi khalidwe, zolinga kapena maganizo enaake amene ndi osayenera. Tingazindikire kuti pali chinachake chomwe chikutichititsa kukhala ndi mtima wosamvera, chimene tingafunike kuchichotsa. Kuchita zimenezi kuli ngati kuchitidwa opaleshoni ya mtima yophiphiritsa. Mukaona kuti m’pofunika kufufuza mtima wanu wophiphiritsa, kodi muyenera kuyang’ana zinthu ziti? Nanga mungatani kuti musinthe?—Yer. 4:4.
12 Dziwani kuti Yehova sangatikakamize kuti tisinthe. Iye ananena kuti Ayuda, omwe anali ngati “nkhuyu zabwino,” ‘adzawapatsa mtima womudziwa.’ Sananene kuti adzawakakamiza kuti asinthe mtima wawo. Iwo ankafunika kulakalaka kukhala ndi mtima womvera, wosonyeza kuti amamudziwa Mulungu. Kodi ifenso sitikufunika kulakalaka kukhala ndi mtima ngati umenewu?
13, 14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mtima wa Mkhristu ukhoza kumuchititsa zoipa?
13 Yesu ananena kuti: “Maganizo oipa, za kupha anthu, za chigololo, za dama, za kuba, maumboni onama, ndi zonyoza Mulungu, zimachokera mumtima.” (Mat. 15:19) M’bale akachita chigololo chifukwa cha mtima wosamvera koma sakulapa, sangakhalenso pa ubwenzi ndi Mulungu. Komabe munthu amene sanachite tchimo lalikulu ngati limeneli akhoza kulola maganizo oipa kukula mumtima mwake. (Werengani Mateyu 5:27, 28.) Ndiye chifukwa chake kudzifufuza n’kothandiza kwambiri. Kodi inuyo mukafufuza mtima wanu, mumaona kuti muli ndi maganizo olakwika ofunika kuwachotsa, okhudza munthu wina yemwe si mkazi kapena mwamuna mnzanu?
14 Zingathekenso m’bale kukhala ndi maganizo olakwika mumtima mwake mpaka kuyamba kudana kwambiri ndi Mkristu mnzake, ngakhale kuti sanafike ‘pomupha.’ (Lev. 19:17) Kodi sizingakhale bwino kuyesetsa kuchotsa maganizo amenewa omwe angachititse munthu kukhala ndi mtima wosamvera?—Mat. 5:21, 22.
15, 16. (a) Kodi zingatheke bwanji Mkhristu kukhala wosadulidwa mumtima? (b) N’chifukwa chiyani Yehova sasangalala ndi anthu amene “sanachite mdulidwe wa mitima yawo”?
15 N’zosangalatsa kuti Akhristu ambiri alibe ‘vuto la mtima’ ngati limeneli. Komabe, Yesu ananenanso za kukhala ndi “maganizo oipa.” Amenewa ndi maganizo olakwika amene angawononge khalidwe lathu. Mwachitsanzo, munthu angakhale ndi maganizo olakwika pa nkhani ya kukhala wokhulupirika kwa achibale. N’zoona kuti Akhristu ayenera ‘kukonda achibale awo’ kuti asakhale ngati anthu amene alibe chikondi choterechi “masiku otsiriza” ano. (2 Tim. 3:1, 3) Koma n’zothekanso kusonyeza chikondi chimenechi monyanyira. Ambiri amati “chibale n’chipsera.” Choncho m’bale wawo akalakwiridwa, amaona kuti nawonso alakwiridwa ndipo sangangozisiya. Mwachitsanzo, taganizirani zimene achimwene ake a Dina anachita chifukwa chokhala ndi maganizo ngati amenewa. (Gen. 34:13, 25-30) Komanso taganizani zomwe zinali mumtima wa Abisalomu zimene zinamuchititsa kupha mchimwene wake Aminoni. (2 Sam. 13:1-30) Kodi sitinganene kuti anthu amenewa anachita zimenezi chifukwa chokhala ndi “maganizo oipa”?
16 N’zoona kuti Akhristu oona sapha anthu. Koma mwina amakhala ndi maganizo oipa kwa m’bale kapena mlongo amene analakwira wachibale wawo, kapena amangoganiza kuti anamulakwira. Iwo angakane chilichonse chochokera kwa Mkhristu amene akuganiza kuti anachitira zoipa wachibale wawo kapenanso angakane kuthandiza Mkhristuyo. (Aheb. 13:1, 2) Akhristu amene amakhala ndi maganizo olakwika oterewa, amasonyeza kuti alibe chikondi ndipo sayenera kudzikhululukira. Yehova, yemwe amasanthula mitima, angaone kuti Akhristu oterewa “sanachite mdulidwe wa mitima yawo.” (Yer. 9:25, 26) Kumbukirani anthu amene Yehova anawauza kuti: “Chitani mdulidwe wa mitima yanu.”—Yer. 4:4.
KHALANIBE NDI “MTIMA WODZIWA” MULUNGU
17. Kodi kuopa Yehova kungatithandize bwanji kukhala ndi mtima womvera?
17 Kodi mungatani ngati mwafufuza mtima wanu wophiphiritsa n’kuona kuti nthawi zina sumvera malangizo a Yehova komanso ukuoneka kuti ndi wosadulidwa? Mwina mumafuna kutchuka, kupeza chuma kapena mumaopa anthu. N’kuthekanso kuti muli ndi kamtima kosafuna kuuzidwa zochita. Dziwani kuti inuyo si woyamba. (Yer. 7:24; 11:8) Yeremiya analemba kuti Ayuda osakhulupirika a m’nthawi yake anali ndi “mtima wouma ndi wopanduka.” Iye analembanso kuti: “Mumtima mwawo sananene kuti: ‘Tsopano tiyeni tiope Yehova Mulungu wathu, amene amatigwetsera mvula. Amatigwetsera mvula yoyamba ndi yomalizira pa nyengo yake.’” (Yer. 5:23, 24) Zimenezi zikusonyeza kuti kuopa ndiponso kuyamikira kwambiri Yehova zingatithandize ‘kuchita mdulidwe wa mitima.’ Kuopa Yehova kutereku kungatithandize kukhala ndi mtima womvera umene Mulungu amafuna.
18. Kodi Yehova anawalonjeza chiyani anthu omwe ali m’pangano latsopano?
18 Tiyenera kuchita mbali yathu kuti Yehova atipatse ‘mtima womudziwa.’ Iye analonjeza odzozedwa omwe ali m’pangano latsopano kuti adzawapatsa mtima umenewu. Anati: “Ndidzaika chilamulo changa mwa iwo ndipo ndidzachilemba mumtima mwawo. Ine ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga.” Iye anawonjezeranso kuti: “Munthu sadzaphunzitsanso mnzake kapena m’bale wake kuti, ‘Mum’dziwe Yehova!’ pakuti aliyense wa iwo adzandidziwa, kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu . . . Ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.”—Yer. 31:31-34.a
19. Kodi Akhristu oona ali ndi chiyembekezo chosangalatsa chiti?
19 Kaya mukuyembekezera kudzapindula ndi pangano latsopano limeneli kumwamba kapena padziko lapansi, muyenera kukhala ndi mtima wofuna kudziwa Yehova komanso kukhala m’gulu la anthu ake. Kuti mupeze madalitso amenewa m’pofunika kukhululukidwa machimo anu pogwiritsa ntchito dipo la Khristu. Kuzindikira kuti machimo anu angakhululukidwe kuyenera kukuchititsani kukhululukira ena, kuphatikizapo amene mumaona kuti anakulakwirani. Kuchotsa mumtima mwanu chilichonse choipa kungathandize kuti mukhale ndi mtima wabwino. Kuchita zimenezi kungasonyeze kuti mukufuna kutumikira Yehova komanso kuti mukumudziwa bwino. Mudzakhala ngati anthu amene Yehova, kudzera mwa Yeremiya, ananena kuti: “Inu mudzandifunafuna ndipo mudzandipeza chifukwa mudzandifunafuna ndi mtima wanu wonse. Ndidzakulolani kuti mundipeze.”—Yer. 29:13, 14.
a Pangano latsopano lafotokozedwa m’mutu 14 m’buku lakuti Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya.