Mlandu wa Yehova ndi Mitundu ya Anthu
“Phokoso lidzadza ku malekezero a dziko lapansi; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi mitundu ya anthu.”—YEREMIYA 25:31.
1, 2. (a) Kodi nchiyani chimene chinachitika m’Yuda pambuyo pa imfa ya Mfumu Yosiya? (b) Kodi ndani amene anali mfumu yotsiriza ya Yuda, ndipo kodi ndimotani mmene anasautsidwira chifukwa cha kusakhulupirika kwake?
DZIKO la Yuda linayang’anizana ndi nthaŵi zoŵaŵitsa zovuta kuchita nazo. Mfumu ina imodzi yabwino, Yosiya, inaimitsa kwakanthaŵi mkwiyo waukulu wa Yehova. Koma kodi nchiyani chimene chinatsatira pamene Yosiya anaphedwa mu 629 B.C.E.? Mafumu amene anamloŵa mmalo ananyoza Yehova.
2 Mfumu yotsiriza ya Yuda, Zedekiya, mwana wachinayi wa Yosiya, inapitirizabe, monga momwe pa 2 Mafumu 24:19 pamanenera, ‘kuchita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adachita Yoyakimu [mkulu wake].’ Kodi nchiyani chinali chotulukapo chake? Nebukadinezara anaukira Yerusalemu, anagwira Zedekiya, anapha ana ake aamuna pamaso pake, anamuboola maso, ndi kumtengera ku Babulo. Ndiponso, Ababulo anafunkha ziwiya zogwiritsiridwa ntchito m’kulambira kwa Yehova, akumatentha ndi moto kachisi ndi mzindawo. Opulumuka ake anakhala andende ku Babulo.
3. Kodi ndinyengo yotani imene inayamba pachiwonongeko cha Yerusalemu mu 607 B.C.E., ndipo kodi nchiyani chimene chinalinkudzachitika pamapeto a nyengoyo?
3 Chaka chimenecho, 607 B.C.E., sichinangozindikiritsa kokha chipasuko chotsiriza cha Yerusalemu komanso chiyambi cha “nthaŵi zoikidwiratu za amitundu,” zotchulidwa pa Luka 21:24, NW. Nyengo ya zaka 2,520 imeneyi inathera m’zaka za zana lathu lino, m’chaka cha 1914. Panthaŵiyo nthaŵi inafika yakuti Yehova, kupyolera mwa Mwana wake wokhazikitsidwa pampando wachifumu, Yesu Kristu, amene ali wamkulu kuposa Nebukadinezara, alengeze ndi kupereka chiweruzo padziko loipa. Chiweruzo chimenechi chikuyamba pa mnzake wa Yuda wamakono, amene amanena mofanana naye kuti amaimira Mulungu ndi Kristu padziko lapansi.
4. Kodi ndimafunso otani amene tsopano akudzutsidwa mogwirizana ndi ulosi wa Yeremiya?
4 Kodi tikuona kufananako pakati pa chipwirikiti chimene chinalipo m’zaka zomalizira za Yuda pansi pa mafumu ake—chokhala ndi zochitika zosakaza zoyambukiranso mitundu yoyandikana naye—ndi chipwirikiti cha m’Dziko Lachikristu lerolino? Ndithudi tikutero! Nangano, kodi nchiyani chimene ulosi wa Yeremiya umasonyeza ponena za mmene Yehova adzachitira ndi nkhaniyo lerolino? Tiyeni tione.
5, 6. (a) Chiyambire 1914, kodi ndimotani mmene mkhalidwe m’Dziko Lachikristu wakhalira wofanana ndi uja wa m’Yuda atangotsala pang’ono kuwonongedwa? (b) Kodi ndiuthenga wotani umene Yeremiya wamakono watengera Dziko Lachikristu?
5 Katswiri wa zamasamu ndi nthanthi wa ku Britain Bertrand Russell anathirira ndemanga zaka 40 zapitazo kuti: “Chiyambire 1914, aliyense amene amadziŵa za zikhoterero za m’dzikoli wakhala wovutika maganizo kwambiri ndi chimene chikuonekera ngati kuguba kwatsoka ndi koikidwiratu komka kuchiwonongeko chachikulu kwambiri.” Ndipo katswiri wandale wa ku Germany Konrad Adenauer anati: “Chisungiko ndi bata zazimiririka m’miyoyo ya anthu chiyambire 1914.”
6 Lerolino, monga momwe kunaliri m’tsiku la Yeremiya, kuyandikira kwa mapeto a dongosolo la zinthu kukusonyezedwa ndi kukhetsedwa kwa mwazi wochuluka wa anthu opanda liŵongo, makamaka m’nkhondo zadziko ziŵiri za m’zaka za zana lino. Kwakukulukulu, nkhondo zimenezi zinamenyedwa ndi mitundu ya Dziko Lachikristu, imene imanena kuti imalambira Mulungu wa Baibulo. Nchinyengo chotani nanga! Chifukwa chake Yehova watumiza Mboni zake kwa iwo, zikumati, m’mawu a pa Yeremiya 25:5, 6: “Mubwerere tsopano nonsenu, yense kuleka njira yake yoipa, . . . musatsate milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, musautse mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu; ndingachitire inu choipa.”
7. Kodi ndiumboni wotani umene ulipo wakuti Dziko Lachikristu lanyalanyaza machenjezo a Yehova?
7 Komabe, mitundu ya Dziko Lachikristu yalephera kubwerera. Zimenezi zasonyezedwa mwa kupereka kwawo nsembe zowonjezereka kwa mulungu wankhondo ku Korea ndi Vietnam. Ndipo ikupitirizabe kulipirira amalonda a imfa, opanga zida zankhondo. Maiko a Dziko Lachikristu anapereka mbali yaikulu ya madola pafupifupi tiriliyoni imodzi olipirira zida zankhondo chaka chilichonse mkati mwa ma 1980. Kuyambira 1951 kufikira 1991, ndalama zotheredwa pa zankhondo za United States yekha zinaposa mapindu a makampani onse a ku America kuwaphatikiza pamodzi. Chiyambire kutha kwa Nkhondo Yamawu kolengezedwa kwambiri, pakhala kuchepetsedwa kwa zida zankhondo zakale za nyukliya, koma mafakitale aakulu a zida zankhondo zina zakupha adakalipo ndipo akupitirizabe kukulitsidwa. Tsiku lina zimenezi zingadzagŵiritsidwe ntchito.
Chiweruzo pa Dziko Lachikristu Lolekerera Zoipa
8. Kodi ndimotani mmene mawu a pa Yeremiya 25:8, 9 adzakwaniritsidwira pa Dziko Lachikristu?
8 Mawu owonjezereka a Yehova, opezeka pa Yeremiya 25:8, 9, tsopano akukwaniritsidwa mwachindunji pa Dziko Lachikristu, limene lalephera kutsatira miyezo Yachikristu ya chilungamo: “Chifukwa chake Yehova wa makamu atero: Popeza simunamvera mawu anga, taonani, ine ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo pa dziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.” Chotero, chisautso chachikulu chidzayambira pa anthu odzinenera kukhala a Mulungu, Dziko Lachikristu, potsirizira pake chidzafalikira padziko lonse, ‘pamitundu yonse yozungulira.’
9. Kodi ndim’njira zotani mmene mkhalidwe wauzimu wa Dziko Lachikristu wakhalira woipa m’nthaŵi yathu?
9 Inalipo nthaŵi pamene Baibulo linalemekezedwa m’Dziko Lachikristu, pamene moyo wa ukwati ndi banja zinaonedwa kukhala magwero achimwemwe ndi munthu aliyense, pamene anthu anauka mmaŵa ndi kupeza chikhutiro m’ntchito yawo yatsiku ndi tsiku. Ambiri anatsitsimula mitima yawo mwa kuŵerenga kapena kuphunzira Mawu a Mulungu usiku mounikiridwa ndi nyale. Koma lerolino, uchiwerewere, chisudzulo, kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala oledzeretsa ndi kuledzera, kupulupudza kwa ana, dyera, ulesi pantchito, kumwerekera ndi TV, ndi mikhalidwe ina yoipa yawononga moyo kufikira pamlingo wowopsa. Zimenezi zili zoyambirira kuchitika chipasuko chisanadze chimene Yehova Mulungu ati apereke pa Dziko Lachikristu lolekerera zoipa.
10. Fotokozani mkhalidwe wa Dziko Lachikristu chiweruzo cha Yehova chitaperekedwa.
10 Yehova akulengeza, monga momwe timaŵerengera pa Yeremiya chaputala 25, mavesi 10 ndi 11 kuti: “Ndidzawachotsera mawu akusekera ndi mawu akukondwera, ndi mawu a mkwati, ndi mawu a mkwatibwi, mawu a mphero, ndi kuŵala kwa nyali. Ndipo dziko lonseli lidzakhala labwinja, ndi chizizwitso.” Kudzakhaladi kozizwitsa pamene akachisi aakulu ndi nyumba zachifumu za Dziko Lachikristu zidzagwa kukhala bwinja. Kodi chiwonongekochi chidzakhala chachikulu motani? M’nthaŵi ya Yeremiya, chipasuko cha Yuda ndi mitundu yoyandikana nayo chinakhalako kwazaka 70, zimene Salmo 90:10 limazifotokoza kukhala zikuimira utali weniweni wa moyo wa munthu. Chiweruzo choperekedwa ndi Yehova lerolino chidzakhala chotheratu, chamuyaya.
Chiweruzo pa Babulo Wamkulu
11. Kodi ndani amene adzakhala chida chowonongera Dziko Lachikristu? Chifukwa ninji?
11 Monga momwe kunanenedweratu pa Chivumbulutso 17:12-17, nthaŵi idzafika pamene Yehova adzayamba ntchito yake yachilendo mwa kuika m’mitima ya “nyanga khumi”—ziŵalo zokonzekera nkhondo za Mitundu Yogwirizana—“kuchita za m’mtima mwake” za kusakaza ulamuliro wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Kodi zimenezi zidzachitika motani? Pali njira zambiri zimene “nyanga khumi” za Chivumbulutso chaputala 17, m’mawu a muvesi 16, zingafikire pa ‘kudana ndi mkazi wachigololoyo, . . . nizidzampsereza ndi moto.’ Zowonadi, zida zankhondo za nyukliya zafalikira ndipo zikufalikirabe m’malo ena ambiri owopsa padziko lapansi. Koma tiyenera kuyembekezera ndi kuona mmene Yehova adzaikira m’mitima ya olamulira lingaliro la kubwezera chilango chake.
12. (a) Kodi nchiyani chimene chinachitikira Babulo atawononga Yerusalemu? (b) Kodi nchiyani chimene chidzachitikira mitundu pambuyo pa chiwonongeko cha Dziko Lachikristu?
12 M’nthaŵi zakale nthaŵi inafika yakuti nayenso Babulo ayang’anizane ndi mkwiyo waukulu wa Yehova. Motero, kuyambira Yeremiya chaputala 25, vesi 12, ulosiwo umafotokoza nkhaniyo m’lingaliro losinthidwa, la pambuyo pake. Posakhalanso Wakupha wa Yehova, Nebukadinezara ndi Babulo tsopano akuphatikizidwa pakati pa mitundu ya dziko. Zimenezi zili zofanana ndi mkhalidwewo lerolino. “Nyanga khumi” za m’Chivumbulutso chaputala 17 zidzawononga chipembedzo chonyenga, komano pambuyo pake izo zenizenizo zidzawonongedwa pamodzi ndi ena onse a “mafumu a dziko,” monga momwe kwafotokozedwera m’Chivumbulutso chaputala 19. Pa Yeremiya 25:13, 14 pamafotokoza mmene Babulo, limodzi ndi “mitundu yonse” imene yalima pamsana anthu a Yehova, ikuweruzidwira. Yehova anagwiritsira ntchito Nebukadinezara monga wakupha polanga Yuda. Komabe iyeyo ndi mafumu a Babulo apambuyo pake modzitukumula anadzikweza motsutsana ndi Yehova mwiniyo, monga momwe mwachitsanzo, kwasonyezedwera ndi kunyozetsa ziwiya za kachisi wa Yehova. (Danieli 5:22, 23) Ndipo pamene Ababulo anawononga Yerusalemu, mitundu yoyandikana ndi Yuda—Moabu, Amoni, Turo, Edomu, ndi ina—inakondwera ndi kuseka anthu a Mulungu. Nayonso inayenera kulandira chilango choyenera kuchokera kwa Yehova.
Chiweruzo pa “Mitundu Yonse”
13. Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa ndi “chikho cha vinyo wa ukaliwu,” ndipo kodi nchiyani chikuchitikira awo amene akumwa chikhocho?
13 Chifukwa chake, Yeremiya akulengeza, monga momwe kwalembedwera pa chaputala 25, mavesi 15 ndi 16 kuti: “Yehova, Mulungu wa Israyeli, atero kwa ine, Tenga chikho cha vinyo wa ukaliwu pa dzanja langa, ndi kumwetsa mitundu yonse, imene ndikutumizirako. Ndipo adzamwa, nadzayenda dzandidzandi, nadzachita misala, chifukwa cha lupanga limene ine ndidzatumiza mwa iwo.” Kodi nchifukwa ninji chikutchedwa ‘chikho cha vinyo wa ukali wa Yehova’? Pa Mateyu 26:39, 42 ndi Yohane 18:11, Yesu analankhula za “chikho” kukhala chizindikiro cha chifuniro cha Mulungu kwa iye. Mofananamo, chikho chimagwiritsiridwa ntchito kuimira chifuniro cha Yehova kaamba ka mitundu kuti ilandire chilango chake chobwezera chaumulungu. Pa Yeremiya 25:17-26 pandandalikidwa magulu a mitundu ameneŵa amene amaimira mitundu lerolino.
14. Malinga ndi ulosi wa Yeremiya, kodi ndani amene akumwa chikho cha vinyo wa mkwiyo wa Yehova, ndipo kodi zimenezi zimaimiranji m’tsiku lathu?
14 Dziko Lachikristu, mofanana ndi Yuda, litakhalitsidwa ‘chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya,’ pali chiwonongeko chimene chikuyembekezera mbali yonse yotsala ya ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Kenako, dziko lonse, monga momwe laphiphiritsidwa ndi Igupto, liyenera kumwa chikho cha vinyo wa mkwiyo wa Yehova! Inde, “mafumu onse a kumpoto, a kutali ndi a kufupi, wina ndi mnzake; ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala pansi pano” ayenera kumwa. Potsirizira pake, “mfumu ya Sesaki adzamwa.” Ndipo kodi ndani amene ali “mfumu ya Sesaki” imeneyi? Sesaki ndilo dzina lophiphiritsa, loyerekezera, kapena chizindikiro cha Babulo. Monga momwe Satana analiri mfumu yosaoneka pa Babulo, choteronso iye ndiye “wolamulira wa dziko” kufikira lerolino, monga momwe Yesu anasonyezera. (Yohane 14:30, NW) Motero, lemba la Yeremiya 25:17-26 limagwirizana ndi Chivumbulutso chaputala 18 kufikira 20 pomveketsa bwino zochitika zotsatizana pamene chikho cha mkwiyo wa Yehova chiperekedwa. Choyamba, ulamuliro wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga uyenera kugwa, kenako olamulira andale zadziko, ndiyeno Satana mwiniyo adzaponyedwa m’phompho.—Chivumbulutso 18:8; 19:19-21; 20:1-3.
15. Kodi nchiyani chimene chidzachitika pamene mfuu ya “mtendere ndi chisungiko” imvedwa?
15 Pakhala manenanena ochuluka a mtendere ndi chisungiko chiyambire pamene Nkhondo Yamawu inanenedwa kuti inatha, pakumatsala ulamuliro wamphamvu kopambana umodzi wokha. Monga momwe kwanenedwera pa Chivumbulutso 17:10, ulamuliro wamphamvu kopambana umenewo, mutu wachisanu ndi chiŵiri wa chilombo, uyenera “kukhala kanthaŵi.” Koma “kanthaŵi” kameneko kakuyandikira mapeto ake. Posachedwapa, mfuu zonse za “mtendere ndi chisungiko” zandale zidzathera mu “chiwonongeko chamwadzidzidzi [chimene] chidzawagwera pomwepo.” Mtumwi Paulo akutero.—1 Atesalonika 5:2, 3, NW.
16, 17. (a) Ngati aliyense ayesa kupeŵa chiweruzo cha Yehova, kodi chidzachitika nchiyani? (b) Kodi ndim’njira yowononga yotani imene chifuniro cha Yehova chidzachitikira padziko lapansi posachedwapa?
16 Dongosolo la dziko lonse la Satana, kuyambira pa Dziko Lachikristu, liyenera kumwa chikho cha chilango chobwezera cha Yehova. Lamulo lake lowonjezereka kwa Yeremiya lolembedwa pa chaputala 25, mavesi 27 mpaka 29, limatsimikizira zimenezo mwa kunena kuti: “Ndipo uziti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Imwani inu, ndi kuledzera, ndi kusanza, nd kugwa, osanyamukanso konse, chifukwa cha lupanga limene ndidzatumiza mwa inu. Ndipo padzakhala, ngati akana kutenga chikho padzanja lako kuti amwe, uziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Kumwa muzimwa. Pakuti, taonani, ndiyamba kuchita choipa pamudzi umene utchedwa ndi dzina langa, kodi inu mudzakhala osalangidwa konse? Simudzakhala osalangidwa; pakuti ndidzaitana lupanga ligwe pa onse okhala m’dziko lapansi, ati Yehova wa makamu.”
17 Amenewo ndimawu amphamvu—indedi, mawu ochititsa mantha, pakuti akunenedwa ndi Ambuye Mfumu wa chilengedwe chonse, Yehova Mulungu. Mkati mwa nthaŵi ya zaka zikwizikwi, iye wapirira moleza mtima mitonzo, kunyonzedwa, ndi kudedwa kumene kwakundikidwa padzina lake loyera. Komabe, potsirizira pake nthaŵi yafika yakuti ayankhe pemphero limene Mwana wake wokondedwa, Yesu Kristu, anaphunzitsa ophunzira ake pamene anali padziko lapansi pano kuti: “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Chili chifuniro cha Yehova kuti Yesu achite monga lupanga Lake m’kupereka chilango chobwezera.
18, 19. (a) Kodi ndani amene akukwera kavalo kukalakika m’dzina la Yehova, ndipo kodi iye akuyembekezeranji asanamalize chilakiko chake? (b) Pamene angelo amasula chimphepo cha mkwiyo wa Yehova, kodi nzochitika zowopsa zotani zimene zidzachitika padziko lapansi?
18 M’Chivumbulutso chaputala 6, choyamba timaŵerenga za kukwera kwa Yesu pakavalo woyera ‘wotulukira wolakika kuti akalakike.’ (Vesi 2) Kumeneku kunayamba ndi kukhazikitsidwa kwake pampando wachifumu monga Mfumu yakumwamba mu 1914. Akavalo ena ndi owakwera akumtsatira, akumaimira nkhondo yotheratu, njala, miliri imene yakantha dziko lathu lapansi chiyambire pamenepo. Koma kodi chipwirikiti chonsechi chidzatha liti? M’Chivumbulutso chaputala 7 mumatiuza kuti angelo anayi akugwira zolimba “mphepo zinayi za dziko” kufikira Israyeli wauzimu ndi khamu lalikulu lotuluka m’mitundu yonse litasonkhanitsidwa kaamba ka chipulumutso. (Vesi 1) Ndiyeno chiyani?
19 Yeremiya chaputala 25, pamavesi 30 ndi 31, pamapitiriza kuti: “Yehova adzabangula kumwamba, nadzatchula mawu ake mokhalamo mwake moyera; adzabangulitsira khola lake; adzafuula, monga iwo akuponda mphesa, adzafuulira onse okhala m’dziko lapansi. Phokoso lidzadza ku malekezero a dziko lapansi; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi mitundu ya anthu, adzatsutsana ndi anthu onse; koma oipa, adzawapereka kulupanga, ati Yehova.” Palibe mtundu umene udzapulumuka pakumwa motero chikho cha mkwiyo wa Yehova. Chifukwa chake, nkofulumira kuti anthu onse amtima wowongoka adzilekanitse ndi kuipa kwa amitundu angelo anayiwo asanamasule chimphepo cha namondwe wa mkwiyo wa Yehova. Namondwedi, pakuti ulosi wa Yeremiya pamavesi a 32 ndi 33 umati:
20. Kodi nchochitika chotani chimene chikugogomezera kuwopsa kwa chiweruzo cha Yehova, koma kodi nchifukwa ninji mchitidwe umenewu uli wofunika?
20 “Yehova wa makamu atero, Taonani, zoipa zidzatuluka ku mtundu kumka m’mitundu, ndipo namondwe adzauka kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kuchokera ku malekezero ena a dziko lapansi kumka ku malekezero ena a dziko lapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka.” Chidzakhaladi chochitika chowopsa ndi chochititsa kakasi, koma mchitidwe umenewu uli wofunikira kuti dziko lapansi liyeretsedwe pa kuipa konse Paradaiso wa lonjezo la Mulungu asanadze.
Abusa Adzakuwa ndi Kulira
21, 22. (a) Pa Yeremiya 25:34-36, kodi ndani amene anali “abusa” a Israyeli, ndipo nchifukwa ninji anaumirizika kukuwa? (b) Kodi ndiabusa ati amakono amene akuyenerera mkwiyo wa Yehova, ndipo nchifukwa ninji akuuyenereradi motero?
21 Mavesi 34 mpaka 36 amafotokoza zowonjezereka ponena za chiweruzo cha Yehova, kuti: “Kuwani, inu abusa, lirani, gubudukani, inu akulu a zoŵeta; pakuti masiku a kuphedwa kwanu akwanira ndithu, ndipo ndidzakuphwanyani inu, ndipo mudzagwa ngati chotengera chofunika. Ndipo abusa adzasoŵa pothawira, mkulu wa zoŵeta adzasoŵa populumukira. Mau akufuula abusa, ndi kukuwa mkulu wa zoŵeta! pakuti Yehova asakaza busa lawo.”
22 Kodi abusa ameneŵa ndani? Sali atsogoleri achipembedzo, amene amwa kale mkwiyo wa Yehova. Iwo ndiwo abusa a magulu a nkhondo, amene afotokozedwanso pa Yeremiya 6:3, amene akusonkhanitsa magulu awo ankhondo m’magulu aakulu monyalanyaza Yehova. Iwo ndiwo olamulira andale zadziko, amene akhala olemera chifukwa cholima pamsana awo olamuliridwa. Ambiri a ameneŵa ndiwo akatswiri m’malonda, odziŵa psete. Iwo akhala akuzengereza kuthetsa njala imene yapha anthu ochuluka m’maiko osauka. Iwo amalemeretsa “akulu a zoŵeta,” monga ngati eni mabizinesi a zida zankhondo ndi owononga malo okhala adyera, pamene akunyalanyaza kupereka thandizo la mankhwala ndi chakudya zimene angagule pamtengo waung’ono kuti apulumutse ana mamiliyoni makumi ambiri omafa.
23. Fotokozani mkhalidwe wa dongosolo la Satana pambuyo pa zochita za Yehova za kuwononga.
23 Nkosadabwitsa kuti lemba la Yeremiya chaputala 25, pamavesi 37 ndi 38, likumaliza mwa kunena za ameneŵa amene anafunafuna mtendere wa iwo eni mwadyera kuti: “Makola amtendere adzawonongeka chifukwa cha mkwiyo wowopsa wa Yehova. Wasiya ngaka yake, monga mkango; pakuti dziko lawo lasanduka chizizwitso chifukwa cha ukali wa lupanga losautsa, ndi chifukwa cha mkwiyo wake waukali.” Chizizwitsodi! Komabe, mkwiyo waukulu wa Yehova udzaperekedwadi kupyolera mwa Uyo amene wafotokozedwa pa Chivumbulutso 19:15, 16 kukhala “Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye,” amene aŵeta mitundu ndi ndodo yachitsulo. Ndipo kodi nchiyani chimene chikutsatira?
24. Kodi ndimadalitso otani amene adzadzetsedwa kwa anthu olungama ndi chiwonongeko cha chipembedzo chonyenga ndi cha dziko lonse la Satana?
24 Kodi munayamba mwapulumukapo chimphepo cha namondwe? Chikhoza kukhala chokumana nacho chowopsa. Koma mmaŵa mwake, ngakhale kuti mungaone zowonongedwa ponseponse, kaŵirikaŵiri pamakhala mphepo yabwino ndi bata lotsitsimula kwambiri kwakuti mukhoza kuthokoza Yehova kaamba ka tsiku labwino kwambirilo. Mofananamo, pamene mkuntho wa chisautso chachikulu uzirala, inu mungayembekezere kukhala padziko lapansi limodzi ndi chiyamiko chakuti muli ndi moyo ndipo muli wokonzekera kukhala ndi phande m’ntchito yowonjezereka ya Yehova ya kusanduliza dziko loyeretsedwalo kukhala paradaiso waulemerero. Mlandu wa Yehova ndi mitundu ya anthu udzakhala utafikitsidwa pamapeto ake kotheratu, akumayeretsa dzina lake ndi kulambulira njira chifuniro chake kuti chichitike padziko lapansi pansi pa Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Ufumu Waumesiya. Ufumuwo udzetu msanga!
Kupenda ndime 5-24 za nkhaniyi
◻ Kodi ndinjira zachinyengo zotani za Dziko Lachikristu zimene tsopano zaloŵa m’chiweruzo?
◻ Kodi ndilingaliro liti lofutukulidwa la chiweruzo limene likuzindikiridwa pa Yeremiya 25:12-38?
◻ Kodi ndichikho chotani cha kubwezera chimene chikuperekedwa kumitundu yonse?
◻ Kodi ndani amene ali abusa amene akukuwa ndi kufuula, ndipo nchifukwa ninji akuvutika?
[Chithunzi patsamba 18]
Yehova wasankha chida chowonongera Dziko Lachikristu
[Chithunzi patsamba 23]
Mkuntho wa chisautso chachikulu utapita, padzakhala dziko lapansi loyeretsedwa