Mutu 12
“Kodi Sanachite Zimenezi Chifukwa Chakuti Anali Kundidziwa?”
1, 2. N’chifukwa chiyani sichinali chinthu chanzeru kuti Yehoyakimu ayambe ntchito yomanga nyumba yake?
MFUMU YEHOYAKIMU ankamanga nyumba yaikulu kwambiri. Iye anakonza zoti nyumbayo ikhale yosanja komanso ya zipinda zikuluzikulu. Anakonzanso zoti nyumbayo ikhale ndi mawindo akuluakulu n’cholinga choti nthawi zonse muzilowa kamphepo kayeziyezi komanso kuwala kwa dzuwa, zomwe zikanachititsa mfumuyo ndi banja lake kuti azisangalala. Anaganizanso zoti makoma a nyumbayo awakute ndi matabwa onunkhira a mkungudza wa ku Lebanoni. Kenako m’kati mwa nyumbayo anakonza zoti apakemo utoto wofiira wokongola kwambiri, wochokera kunja kwa dzikolo. Ndipo anthu olemera ndi otchuka a m’mayiko ena okha, ndi amene ankakwanitsa kupaka utoto umenewu m’nyumba zawo.—Yer. 22:13, 14.
2 Panafunika ndalama zambiri pa ntchito yomanga nyumbayi. Koma pa nthawiyo, chuma cha dzikolo sichinkayenda bwino chifukwa ndalama zambiri zinkathera pa ntchito yachitetezo komanso kupereka msonkho kudziko la Iguputo. (2 Maf. 23:33-35) Komabe Yehoyakimu anapeza njira yomuthandiza kuti asawononge ndalama zambiri pomanga nyumba yake yatsopanoyo. Iye sankalipira anthu omwe ankagwira ntchito yomangayo, koma ankawagwiritsa ntchito mwankhanza ngati akapolo, pongofuna kuti zake zimuyendere basi.
3. Kodi Yehoyakimu anali wosiyana bwanji ndi bambo ake, ndipo n’chifukwa chiyani zinali choncho?
3 Kudzera mwa Yeremiya, Mulungu anadzudzula Yehoyakimu chifukwa cha mtima wake wodzikonda.a Iye anamukumbutsa kuti Mfumu Yosiya, yemwe anali bambo ake, anali woolowa manja kwambiri kwa anthu olemera ndi osauka omwe, komanso ankawachitira zinthu mwachifundo kwambiri. Yosiya anafika mpaka poonetsetsa kuti milandu ya anthu osaukawa ikuweruzidwa mwachilungamo m’makhoti. Yehova atauza Yehoyakimu kuti akumbukire mmene Yosiya ankachitira zinthu moganizira anthu onyozeka, anamufunsa kuti: “Kodi sanachite zimenezi chifukwa chakuti anali kundidziwa?”—Werengani Yeremiya 22:15, 16.
4. N’chifukwa chiyani muyenera kuona kuti kudziwa Yehova n’kofunika kwambiri?
4 Pamene zinthu zikupitiriza kuipiraipira m’dziko la Satanali, tikufunikira kudalira Yehova kuti azititeteza ndi kutithandiza. Ndipotu iye amachita zimenezi kwa anthu amene amamudziwa bwino. Motero, tiyenera kuyesetsa kumuyandikira kwambiri. Tiyeneranso kutsanzira makhalidwe ake abwino kuti zinthu zizitiyendera bwino tikamagwira ntchito yolalikira uthenga wabwino. Komabe, mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi zingatheke bwanji kuti Mkhristu adziwe Yehova ngati mmene Mfumu Yosiya inachitira?’
KODI KUDZIWA MULUNGU KUMATANTHAUZA CHIYANI?
5, 6. (a) Kodi khalidwe la bambo wabwino limakhudza bwanji ana ake? (b) Mosiyana ndi Yehoyakimu, kodi ifeyo tiyenera kuchita chiyani pamene tadziwa njira za Yehova?
5 Taganizirani mmene khalidwe la bambo wabwino limakhudzira moyo wa ana ake. Mwachitsanzo, ana akaona kuti bambo awo amathandiza ndi mtima wonse anthu osauka, nawonso nthawi zambiri amaphunzira kukhala owolowa manja. Akamaona bambo awo akuchita zinthu mwachikondi ndiponso mwaulemu ndi mayi awo, nawonso amaphunzira kuchita zinthu mwaulemu ndi anthu omwe si amuna kapena akazi anzawo. Akamamva kuti bambo awo amachita zinthu mwachilungamo komanso moona mtima pa nkhani za ndalama, nawonso amayamba kuchita zinthu mwachilungamo ndiponso moona mtima. Zoonadi, ana akamaona makhalidwe a bambo awo, nthawi zambiri akamakula amafunitsitsa kuwatsanzira akamachita zinthu ndi ena.
6 Mofanana ndi zimenezi, Mkhristu amene akudziwa Yehova ngati mmene Yosiya ankamudziwira, amachita zambiri osati kungodziwa kuti Yehova ndiye Wolamulira wa Chilengedwe Chonse basi. Mkhristu akamawerenga Baibulo, amazindikira mmene Mulungu amachitira zinthu ndi ena, ndipo kenako amayesetsa kutsanzira Atate wake wakumwamba. Iye amayamba kukonda kwambiri Yehova, ndipo tsiku ndi tsiku amayesetsa kutsanzira Mulungu pa zinthu zimene amakonda ndi zimene amadana nazo. Mosiyana ndi zimenezi, munthu amene amanyalanyaza malamulo ndi malangizo a Mulungu, amakhala akukana kuti Mulungu azimutsogolera pa moyo wake, ndipo zimenezi zimamuchititsa kuti asadziwe Mulungu woona. Munthu wotero amafanana ndi Yehoyakimu, amene anatentha ndi moto mawu amene Yehova anawapereka kudzera mwa Yeremiya.—Werengani Yeremiya 36:21-24.
7. N’chifukwa chiyani muyenera kukhala ndi mtima wofuna kudziwa Yehova ngati mmene Mfumu Yosiya inachitira?
7 Tiyenera kumudziwa bwino Yehova kuti zinthu zizitiyendera bwino pochita utumiki wathu wopatulika komanso kuti tikhale ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo m’dziko latsopano. (Yer. 9:24) Tsopano tiyeni tione ena mwa makhalidwe a Mulungu amene atchulidwa m’mabuku amene Yeremiya analemba. Tikamakambirana makhalidwe amenewa, yesetsani kuona zimene inuyo mungachite kuti mumudziwe bwino Mulungu komanso kuti muzimutsanzira, ngati mmene Mfumu Yosiya inachitira.
N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mfumu Yosiya inkamudziwa bwino Yehova? Kodi inuyo muyenera kuchita chiyani kuti mum’dziwe Yehova ngati mmene Yosiya anam’dziwira?
“KUKOMA MTIMA KWAKE KOSATHA KUDZAKHALAPOBE MPAKA KALEKALE!”
8. Kodi kukoma mtima kosatha kumatanthauza chiyani?
8 M’zinenero zambiri, n’zovuta kupeza mawu amene angapereke tanthauzo lokwanira lonena za khalidwe la Mulungu la kukoma mtima kosatha, kapena kuti chikondi chokhulupirika. Malinga ndi buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo, mawu achiheberi amene anawamasulira kuti kukoma mtima kosatha amasonyeza mphamvu, kusasunthika, ndiponso chikondi. Bukulo linapitiriza kufotokoza kuti: “Munthu akawerenga mawu amenewa m’chinenero chake, koma osaganizira za mphamvu, kusasunthika, ndiponso chikondi, ndiye kuti mawuwo akuperewera penapake.” Choncho, munthu amene amasonyeza ena kukoma mtima kosatha sikuti amangokhala munthu wabwino basi. Iye amakhudzidwa kwambiri ndi zimene zikuchitikira ena ndipo amayesetsa kuwathandiza mmene angathere, makamaka mwauzimu. Cholinga chake chachikulu pochita zinthu mwanjira imeneyo ndiponso mosadzikonda, chimakhala kukondweretsa Mulungu Wamphamvuyonse.
9. Kodi mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Aisiraeli zikusonyeza chiyani?
9 Njira yabwino kwambiri imene ingatithandize kumvetsa tanthauzo la mawu a m’Baibulo akuti “kukoma mtima kosatha,” n’kuphunzira mmene Mulungu wakhala akuchitira zinthu ndi olambira ake oona kwa zaka zambiri. Yehova anateteza ndi kudyetsa Aisiraeli kwa zaka 40 pamene iwo anali m’chipululu. Atafika m’Dziko Lolonjezedwa, Mulungu anawapatsa oweruza kuti aziwapulumutsa kwa adani awo ndiponso kuti awathandize kuyambiranso kulambira koona. Popeza Yehova sanawasiye kwa nthawi yonseyo, pa nyengo zabwino ndi zovuta zomwe, n’chifukwa chake anawauza kuti: “Ine ndakukonda ndipo ndidzakukonda mpaka kalekale. N’chifukwa chake ndakukoka mwa kukoma mtima kwanga kosatha.”—Yer. 31:3.b
10. Tikaganizira za Ayuda amene anali ku Babulo, kodi tikuona kuti Yehova amasonyeza bwanji kukoma mtima kosatha pa nkhani yomvetsera mapemphero?
10 Masiku ano, Mulungu akupitiriza kusonyeza kukoma mtima kosatha m’njira zimene zimathandiza mwachindunji olambira ake. Mwachitsanzo, taganizirani nkhani ya pemphero. Yehova amamva mapemphero onse ochokera pansi pa mtima, koma amamvetsera mwapadera kwambiri mapemphero a atumiki ake odzipereka. Ngakhale zitachitika kuti takhala tikupempherera vuto lomwelomwelo kwa zaka zambiri, iye amamvetserabe ndipo satopa nafe. Pa nthawi ina, Yehova anauza Yeremiya kuti atumize uthenga kwa Ayuda amene anali kale pa ukapolo ku Babulo. Iwo anali kutali kwambiri ndi kachisi, abale awo komanso anzawo ku Yuda, pa mtunda woposa makilomita 800. Komabe, Yehova sanasiye kumvetsera mapemphero awo opempha kuti awakomere mtima komanso omutamanda, ngakhale kuti iwo anali kutali ndi kachisi. Masiku ano mukamapemphera mochokera pansi pa mtima, mungalimbikitsidwe ngati mmene Ayudawo analimbikitsidwira atamva mawu a Mulungu opezeka palemba la Yeremiya 29:10-12.—Werengani.
11, 12. (a) Kodi Yehova anawalonjeza chiyani anthu a ku Yerusalemu? (b) Kodi munthu amene anapatsidwa chilango choyenerera angathandizidwe bwanji?
11 Umboni wina wosonyeza kuti Yehova amasonyeza kukoma mtima kosatha, ndi wakuti iye nthawi zonse amafunira zabwino anthu ake. Mwachitsanzo, Yerusalemu atatsala pang’ono kuwonongedwa, anthu a mumzindawo anapitiriza kukana kugonjera Ababulo, ndipo zimenezi zinasonyeza kuti iwo sankamvera Mulungu. Kodi anthuwo anali ndi tsogolo lotani? Mwina akanatha kufa ndi njala kapena kuphedwa ndi Ababulo. Anthu omwe akanapulumuka ku zinthu zimenezi mwina akanatengedwa n’kukakhala nthawi yaitali ku ukapolo m’dziko lachilendo, mwinanso n’kufera komweko. Komabe, Yehova anapereka “lonjezo” labwino kwa anthu amene analapa ndi kusintha moyo wawo, ndipo anawalonjeza kuti ‘adzawacheukira.’ Iye anawauza kuti adzawabwezeretsanso ‘pamalo awo,’ kapena kuti kudziko lawo, kuchokera kudziko lakutali la Babulo. (Yer. 27:22) Zotsatira zake n’zakuti iwo adzafuula kuti: “Tamandani Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndi wabwino. Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale!”—Yer. 33:10, 11.
12 Chifukwa choti Yehova amasonyeza kukoma mtima kosatha, iye amalimbikitsa kwambiri anthu amene ali m’mavuto aakulu zedi. Masiku ano, pali anthu ena omwe anali mumpingo wachikhristu koma anapatsidwa chilango choyenerera ndiponso chachilungamo. Anthu amenewa angamadzione kuti ndi olakwa kwambiri ndipo angamazengereze kubwerera m’gulu la anthu a Mulungu. Iwo angamakayikire ngati Yehova angawakhululukiredi n’kuwalandiranso m’gulu lake. Koma Mulungu Wamphamvuyonse akupereka “lonjezo” labwino kwa anthu onse otero. Iwo angathandizidwe mwachikondi kuti asinthe maganizo awo ndiponso zochita zawo. Zimene tawerenga m’ndime yapitayi zingagwirenso ntchito kwa anthu otere, ndipo Yehova adzawabwezeretsa ‘pamalo awo,’ m’gulu la anthu ake achimwemwe.—Yer. 31:18-20.
13. N’chifukwa chiyani muyenera kulimbikitsidwa ndi nkhani yokhudza mmene Yehova anasamalirira Yeremiya?
13 Popeza Yehova ndi Mulungu amene amasonyeza kukoma mtima kosatha, iye nthawi zonse amathandiza atumiki ake okhulupirika. M’masiku otsiriza a dziko la Satanali, tili ndi chifukwa chabwino chokhulupirira kuti Yehova adzathandiza ndi kuteteza anthu onse amene amafunafuna Ufumu wake choyamba. Musaiwale kuti Yerusalemu atatsala pang’ono kuwonongedwa, Yeremiya ankadalira Yehova kuti azimupatsa chakudya ndiponso kumuteteza, ndipo Mulungu sanagwiritse mwala mneneri wakeyu. (Yer. 15:15; werengani Maliro 3:55-57.) Ngati mutapezeka kuti mwapanikizika ndi mavuto enaake, khulupirirani kuti Yehova akukumbukira zinthu zonse zimene mwakhala mukuchita mokhulupirika. Chifukwa choti iye amasonyeza kukoma mtima kosatha, amafunitsitsa kuti akuthandizeni n’cholinga choti ‘musafafanizidwe.’—Maliro 3:22.
Kodi ndi mbali iti ya kukoma mtima kosatha kwa Yehova imene imakuchititsani kuti muzimukonda kwambiri, ndipo n’chifukwa chiyani zili choncho?
“PALI YEHOVA MULUNGU WAMOYO, . . . NDI CHILUNGAMO”
14. Kodi chaposachedwapa inuyo mwaona zinthu zotani zopanda chilungamo?
14 Anthu ena amakhala zaka zambiri m’ndende pa milandu yongowanamizira. Nthawi zina makhoti aweruzapo kuti munthu aphedwe, koma kenako umboni wosonyeza kuti munthuyo anali wosalakwa n’kupezeka, iye ataphedwa kale. M’mayiko ena makolo amasowa mtengo wogwira chifukwa cha njala, moti amagulitsa ana awo kuti akhale akapolo n’cholinga choti banja lawo lipeze chakudya. Kodi inuyo mumamva bwanji mumtima mukamva zinthu zopanda chilungamo ngati zimenezi masiku ano? Nanga mukuganiza kuti Yehova amamva bwanji? Baibulo limafotokoza mosapita m’mbali kuti iye akufuna kuchotsa zinthu zonse zimene zimachititsa kuti anthu azivutika. Ndipotu ndi iye yekha amene angakwanitse kuchita zimenezi. Choncho, zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri kwa anthu osauka komanso osalakwa amene akuvutika masiku ano. Yehova, yemwe ndi Mulungu wachilungamo, wayambapo kale kuchita zinthu zimene zidzathetse mavuto amene anthuwo akukumana nawo panopa.—Yer. 23:5, 6.
15, 16. (a) Kodi Yeremiya anatsindika mfundo yotani yokhudza Yehova? (b) N’chifukwa chiyani muyenera kukhulupirira malamulo ndi malonjezo a Mulungu?
15 M’nthawi ya Yeremiya, anthu ena ankadziwa bwino kuti chilungamo cha Mulungu n’chapamwamba kwambiri. Mwachitsanzo, mneneriyu anasonyeza kuti n’zotheka kuti Aisiraeli alape machimo awo n’kusintha njira zawo. Ndipo mwa zochita zawo, iwo akanakhala ngati akunena kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, Mulungu wachoonadi ndi chilungamo.” (Yer. 4:1, 2) Izi zili choncho chifukwa Yehova sachita chinthu chilichonse chopanda chilungamo pokwaniritsa zolinga zake. Koma pali maumboni enanso osonyeza kuti Yehova amakonda chilungamo.
16 Mulungu amakwaniritsa malonjezo ake onse ndiponso sachita zinthu mwachiphamaso. Yehova amakwaniritsa chilichonse chimene walonjeza, mosiyana ndi anthu ambiri amene sakwaniritsa malonjezo awo. Ngakhale malamulo a m’chilengedwe amene Mulungu anakhazikitsa, omwe amatipindulitsa kwambiri, sasintha ndipo sadzatha. (Yer. 31:35, 36) Tiyeneranso kudalira malonjezo ake ndi zigamulo zake, chifukwa nthawi zonse zimakhala zabwino.—Werengani Maliro 3:37, 38.
17. (a) Kodi Yehova amachita chiyani akamaweruza? (b) N’chifukwa chiyani simuyenera kukayikira mmene akulu amaweruzira milandu mumpingo? (Onani bokosi lakuti “Amaweruza M’malo mwa Yehova,” patsamba 148.)
17 Sikuti Yehova amangoweruza asanaunike bwinobwino nkhani yonse. Iye amaunika nkhani yonse mozama kuti apeze mfundo zina zimene ena sangathe kuziona. Iye amaunikanso bwinobwino mumtima mwa munthu kuti adziwe chimene chinamuchititsa kuti achite zinazake. Mwachitsanzo, madokotala masiku ano amatha kugwiritsa ntchito makina ndiponso njira zina zamakono kuti aunike mtima wa munthu amene akudwala. Iwo amachita zimenezi mtimawo ukugwira ntchito, ndipo zimawathandiza kuti adziwe mmene mtimawo ulilidi. Iwo angathenso kuunika impso pamene zikugwira ntchito yake yosefa magazi. Komatu Yehova amaunika zambiri kuposa madokotala. Iye amaunika mtima wathu wophiphiritsa, womwe ndi maganizo athu, komanso impso zathu zophiphiritsa, zomwe ndi zolinga za mumtima mwathu. Motero, iye amatha kudziwa zimene zinachititsa munthu kuchita zinthu mwanjira inayake ndiponso mmene munthuyo akumvera mumtima akaganizira zimene anachitazo. Ndipo Mulungu Wamphamvuyonse akamaunika nkhani mwanjira imeneyi, sasokonezedwa maganizo ndi kuchuluka kwa mfundo zimene wapeza. Popeza iye amaposa woweruza aliyense wanzeru, amagwiritsa ntchito mosamala kwambiri mfundo zonse zimene wapeza. Iye amachita zimenezi m’njira yabwino kuti apereke chiweruzo choyenera.—Werengani Yeremiya 12:1a; 20:12.
18, 19. Kodi kudziwa khalidwe la Mulungu la chilungamo kuyenera kutikhudza bwanji?
18 Zimenezi zikukupatsani chifukwa chomveka chokuthandizani kuti muzikhulupirira kwambiri Yehova, ngakhale kuti nthawi zina chikumbumtima chanu chingamakuvutitseni chifukwa cha zolakwa zina zimene munachitapo m’mbuyomu. Muzikumbukira kuti Yehova si woweruza wankhanza amene amangofunira ena zifukwa kuti awalange, koma ndi Woweruza wachifundo amene amafunitsitsa kuthandiza anthu. Ngati mumavutikabe mumtima chifukwa cha zimene munkachita kale, kapena chifukwa cha nkhani imene ikukhudzanso munthu wina, pemphani Yehova kuti akuweruzireni “milandu” yanu, kutanthauza kuti akuchotsereni nkhawa zanu, n’cholinga choti muiwale nkhaniyo.c Mulungu angakuthandizeni kuzindikira kuti iye amasangalala kwambiri ndi utumiki wopatulika umene mumachita nthawi zonse.—Werengani Maliro 3:58, 59.
19 M’pomveka kuti Mulungu yemwe ndi wachilungamo amayembekezera kuti anthu onse amene akufuna kuti iye aziwakonda, nawonso azichita zinthu mwachilungamo. (Yer. 7:5-7; 22:3) Kulalikira uthenga wabwino mopanda tsankho, ndi njira yofunika kwambiri yosonyezera kuti tikutsanzira Mulungu pa nkhani ya chilungamo. Inuyo mukamayesetsa mwakhama kuchita maulendo obwereza ndiponso kuchititsa maphunziro a Baibulo, mumakhala mukusonyeza chilungamo m’njira yabwino kwambiri. Komanso mumakhala mukutsanzira chilungamo cha Yehova, chomwe n’chapamwamba kwambiri. N’chifukwa chiyani zili choncho? Chifukwa chakuti iye akufuna kuti anthu a mitundu yonse aphunzire za iye ndiponso adzapulumuke. (Maliro 3:25, 26) Mulitu ndi mwayi waukulu kwambiri wogwira ntchito limodzi ndi Mulungu ndi kusonyeza chilungamo chake pogwira ntchito yopulumutsa moyoyi.
Kodi mfundo yakuti Yehova ndi wachilungamo imakulimbikitsani bwanji? Nanga inuyo mungalimbikitse bwanji ena potsanzira Mulungu yemwe ndi wachilungamo?
“SINDIDZAKHALA WOKWIYA MPAKA KALEKALE”
20. (a) Kodi Yeremiya anatsindika mfundo iti yokhudza mmene Mulungu amachitira zinthu ndi anthu ake? (b) Kodi mfundo yakuti Yehova ‘amasintha maganizo’ ikugwirizana bwanji ndi yoti iye amakhululuka? (Onani bokosi lakuti “Kodi Yehova ‘Amasintha Bwanji Maganizo Ake’?”)
20 Anthu ambiri amaona kuti m’mabuku a Yeremiya ndi Maliro mwangodzaza mauthenga a ziweruzo zoipa okhaokha. Anthu amene ali ndi maganizo amenewa amanyalanyaza mfundo zolimbikitsa zomwe zili m’mabukuwa, zimene Yehova ankauza anthu ake powapempha kuti alape. Mwachitsanzo, iye analimbikitsa Ayuda kuti: “Chonde, aliyense wa inu atembenuke kusiya njira yake yoipa ndipo muyambe kuyenda m’njira zabwino ndi kuchita zinthu zabwino.” Pa nthawi inanso, Yeremiya anawalimbikitsa kuti: “Konzani njira zanu ndi zochita zanu kuti zikhale zabwino ndipo muzimvera mawu a Yehova Mulungu wanu. Mukatero, Yehova adzasintha maganizo ake pa tsoka limene wanena kuti akugwetserani.” (Yer. 18:11; 26:13) M’nthawi yathu ino, Yehova akupitirizabe kukhululukira anthu onse amene amalapadi mochokera pansi pa mtima ndi kusiya zoipa zimene ankachita.
21. Kodi Yehova amakhala ndi cholinga chotani akamakhululukira munthu?
21 Sikuti Yehova amangolankhula ndi pakamwa chabe kuti angakhululukire anthu ochimwa, koma amawakhululukiradi. Pa nthawi ina, Yehova anagwiritsa ntchito Yeremiya kuti alimbikitse anthu ake kuti: “Bwerera Isiraeli wopanduka iwe. Sindidzakuyang’anani mokwiya anthu inu pakuti . . . sindidzakhala wokwiya mpaka kalekale.” (Yer. 3:12) Mulungu akakhululukira munthu, samusungira chakukhosi kapena kupitiriza kumukwiyira. M’malomwake, iye amafunitsitsa kuti ubwenzi wake ndi munthuyo ukonzedwenso ngakhale kuti munthuyo anachitadi tchimo. Munthu wochimwa akalapa moona mtima ndiponso akapempha Mulungu kuti amukhululukire, Yehova amayambiranso kukonda munthuyo komanso kumudalitsa. Iye amachita zimenezi ngakhale kuti munthuyo anachita machimo ambiri. (Yer. 15:19) Mfundo imeneyi ingalimbikitse aliyense amene panopa salinso pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu woona, kuti abwerere kwa iye. Kodi simukuvomereza kuti mfundo yakuti Yehova amakhululuka imatichititsa kufunitsitsa kumuyandikira?—Werengani Maliro 5:21.
22, 23. Kodi muyenera kukhala ndi cholinga chotani mukamatsanzira Yehova pa nkhani ya kukhululuka?
22 Ngati munthu wina wakukhumudwitsani chifukwa sanakulankhuleni bwino kapena wakuchitirani zinthu mosaganiza bwino, kodi mudzatsanzira Yehova? Ponena za Ayuda akale, Mulungu ananena kuti ‘adzayeretsa’ anthu amene wawakhululukira. (Werengani Yeremiya 33:8.) Iye amatha kuyeretsa anthu amene alapa, potaya machimo awo ndipo sawakumbukiranso. Kenako, Mulungu amapereka mwayi kwa anthuwo kuti ayambirenso kumutumikira. Koma Mulungu akakhululukira munthu, sizitanthauza kuti munthuyo wayeretsedwa ku uchimo wobadwa nawo ndipo tsopano wakhala wangwiro, kapena kuti wopanda tchimo lililonse. Komabe, tingaphunzirepo kanthu pa zimene Mulungu ananena, zokhudza kuyeretsa anthu. Tingayesetse kutaya kapena kuiwala zimene munthu wina anatilakwira, ndipo mophiphiritsa, kuchita zimenezi kuli ngati kuyeretsa munthuyo chifukwa timasintha mmene timamuonera mumtima mwathu. Kodi tingachite zimenezi motani?
23 Tayerekezerani kuti m’bale wanu wina wakupatsani mphatso ya njinga. Ngati njingayo ingachite dzimbiri pang’ono, kodi mukhoza kungoitaya? Ayi, simungachite zimenezo. Muyenera kuti mungayesetse mwakhama kuchotsa dzimbiri lonse, mwinanso mungaipake penti. Mungachite zonsezi n’cholinga choti njingayo ilimbe ndiponso kuti izioneka bwino. Mofanana ndi zimenezi, muyenera kuchita khama kuti muchotse maganizo alionse mumtima mwanu odana kapena oipidwa ndi m’bale kapena mlongo amene wakulakwirani. Yesetsani kulimbana ndi mtima womangoganizira zinthu zoipa zimene iye anakuchitirani kapena mawu opweteka amene anakulankhulani. Mukamayesetsa kuiwala zimene anakulakwiranizo, mumtima mwanu mumakhala mukuyeretsa chithunzi cha munthu yemwe munamukhululukirayo. Mukamayesetsa kupewa maganizo olakwika okhudza munthu yemwe mukumuyeretsa mumtima mwanu, mumakhala okonzeka kukhala nayenso pa ubwenzi, womwe unkaoneka ngati unatheratu.
24, 25. Ngati mutadziwa bwino Yehova monga mmene Mfumu Yosiya inamudziwira, kodi mungapeze madalitso otani?
24 Takambirana ena mwa makhalidwe a Yehova ndiponso taona mmene iye amachitira zinthu, ndipo kuphunzira zimenezi kwatithandiza kuti timudziwe bwino. Taonanso kuti kumudziwa bwino Yehova kumatithandiza, ndipo zimenezi zimatilimbikitsa kwambiri kuti tizimulambira m’njira yoyenerera. Tikamudziwa bwino Yehova ngati mmene anachitira Mfumu Yosiya, tidzakhala ndi chimwemwe kwambiri pa moyo wathu, chomwenso ndi khalidwe lina la Mulungu.
25 Komanso kumudziwa bwino kwambiri Yehova kudzatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi anthu ena. Tikamayesetsa mwakhama kusonyeza ena kukoma mtima kosatha, chilungamo ndiponso kuwakhululukira ngati mmene Yehova amachitira, ubwenzi wathu ndi Akhristu anzathu mumpingo udzakhala wabwino zedi ndiponso wolimba kwambiri. Zimenezi zidzatithandizanso kuti tiziphunzitsa mogwira mtima tikamapanga maulendo obwereza m’gawo lathu ndiponso tikamachititsa maphunziro a Baibulo opita patsogolo. Komanso anthu amene amachita chidwi ndi uthenga umene timalalikira angayambe kusirira moyo wathu wachikhristu akaona mmene tikuchitira zinthu pa moyo wathu. Choncho, zingakhale zosavuta kuti tiwathandize kuti azilambira Yehova m’njira yoyenera, kapena kuti ayambe kutsatira “njira yabwino.”—Yer. 6:16.
Kodi lemba la Maliro 5:21 lili ndi uthenga wotani kwa inu?
a Kuti mudziwe zinthu zomvetsa chisoni zimene zinachitikira Yehoyakimu pamapeto pake, onani Mutu 4 wa buku lino, ndime 12.
b Baibulo lina linamasulira mawu a Yehovawa kuti: “Ine ndakhala ndikukukonda kwambiri kuyambira kalekale, ndipo mpaka pano ndikupitirizabe kukusamalira mwachikondi.”—The New English Bible.
c Ngati m’bale kapena mlongo wachita zinthu zimene zikuonekeratu kuti waphwanya malamulo a Mulungu, akulu mumpingo ayenera kudziwitsidwa n’cholinga choti athandize munthuyo mogwirizana ndi Malemba.—Yak. 5:13-15.