Mutu 6
“Chonde, Mverani Mawu A Yehova”
1, 2. Kodi anthu amene akungotsatira ‘njira imene anthu ambiri akuitsatira,’ kawirikawiri amakhala ndi mtima wotani, nanga n’chifukwa chiyani inuyo muyenera kupewa kukhala ndi mtima umenewo?
ANTHU ambiri masiku ano sakonda kumvera malamulo. Ndipo anthu ochuluka akamasankha zinthu zoyenera kuchita satsatira mfundo iliyonse yabwino, ngakhale mfundo yakuti, ‘Muzichita zabwino.’ M’malomwake, iwo amayendera mfundo yakuti, ‘Muzichita zimene mukufuna’ kapena yakuti, ‘Mukhoza kuchita chilichonse, bola asakugwireni.’ Mungathe kuona umboni wa zimenezi mukaona anthu oyendetsa galimoto akuphwanya malamulo apamsewu, anthu a mabizinezi akuphwanya malamulo azachuma, ndiponso akuluakulu a boma akuphwanya malamulo amene mwina iwowo anakhazikitsa nawo. Zimene anthu akuchita pothamangira “kunjira imene anthu ambiri akuitsatira,” ngakhale kuti n’zolakwika komanso zopweteketsa, zinkachitikanso kwambiri m’masiku a Yeremiya.—Yer. 8:6.
2 Koma inu mukudziwa bwino kuti anthu amene akufuna kuti Mulungu Wamphamvuyonse aziwakonda sayenera kungotsatira ‘njira imene anthu ambiri akuitsatira.’ Yeremiya anasonyeza bwino kusiyana kwa anthu amene “sanamvere mawu a Yehova” ndi anthu amene ankafunitsitsa kumumvera. (Yer. 3:25; 7:28; 26:13; 38:20; 43:4, 7) Choncho, aliyense wa ife ayenera kuganizira mozama zochita zake kuti aone mbali imene ali pa nkhaniyi. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi? Chifukwa chakuti masiku ano Satana wayamba kulimbana mwankhanza kwambiri ndi olambira oona amene akutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika. Iye ali ngati njoka imene yabisalira nyama n’cholinga choti nyamayo ikamadutsa, iilume modzidzimutsa n’kuivulaza kapena kuipheratu. Koma tikatsimikiza ndi mtima wonse kumvera Yehova, zimatithandiza kupewa kulumidwa ndi njoka imeneyo. Komabe, kodi n’chiyani chingatithandize kukhala ndi mtima wofunitsitsa kwambiri kumvera Yehova? Zimene Yeremiya analemba zingatithandize kwambiri.
KODI TIYENERA KUMVERA NDANI?
3. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova ndi woyenera kuti tizimumvera?
3 N’chifukwa chiyani Yehova ndi woyenera kuti tizimumvera pa chilichonse? Yeremiya anatiuza chifukwa chimodzi pamene anati Yehova “ndi amene anapanga dziko lapansi ndi mphamvu zake, amene mwanzeru zake anakhazikitsa dziko limene anthu amakhalamo.” (Yer. 10:12) Yehova ndiye Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse, choncho tiyenera kumuopa kuposa olamulira ena onse. Iye ali ndi ufulu wonse wotiuza kuti tizitsatira malamulo ake anzeru, ndipotu malamulowo ndi abwino kwa ife moti tikawatsatira, zinthu zimatiyendera bwino nthawi zonse.—Yer. 10:6, 7.
4, 5. (a) Kodi Ayuda anazindikira mfundo yoona iti pa nthawi za chilala? (b) Kodi Ayuda anataya bwanji “madzi amoyo” ochokera kwa Yehova? (c) Kodi inuyo mungatani kuti mumwe “madzi amoyo” ochokera kwa Mulungu?
4 Monga mmene taonera, Yehova ndi Wolamulira wa chilengedwe chonse. Kuwonjezera pa zimenezi, iye ndi amene anatipatsa moyo komanso ndi amene amatisamalira kuti tikhalebe ndi moyo. Zimene zinachitika m’nthawi ya Yeremiya zinathandiza Ayuda kumvetsa bwino kwambiri mfundo imeneyi. Dziko la Iguputo linkadalira kwambiri madzi a mumtsinje wa Nailo, koma si mmene zinalili m’Dziko Lolonjezedwa. Anthu a Mulungu ankadalira kwambiri mvula yomwe inkagwa pa nyengo yake, ndipo nthawi zambiri ankasunga madzi amvulawo m’zitsime. (Deut. 11:13-17) Ndi Yehova yekha amene akanatha kuwabweretsera mvula kuti inyowetse nthaka n’cholinga choti mbewu zimere. Komanso iye akanatha kuletsa mvulayo kuti isabwere. M’nthawi ya Yeremiya, Ayuda ambiri anali osamvera Mulungu. Choncho m’dziko lawo munkagwa chilala mobwerezabwereza ndipo zimenezi zinachititsa kuti minda yawo ya mpesa komanso ya mbewu zina ikhale youma, ndipo zitsime zawo zinaumanso.—Yer. 3:3; 5:24; 12:4; 14:1-4, 22; 23:10.
5 Ngakhale kuti Ayudawo ankaona kuti madzi enieni ndi ofunika kwambiri, iwo anakana “madzi amoyo” amene Yehova ankawapatsa mowolowa manja. Anachita zimenezi pokana mwadala kumvera Chilamulo cha Mulungu ndiponso podalira mapangano amene ankachita ndi mayiko oyandikana nawo. Mofanana ndi zimene zingachitikire munthu amene pa nthawi yosowa madzi, amathira madziwo m’chitsime chong’ambika chomwe sichingathe kusunga madzi, Ayudawo anakumana ndi mavuto chifukwa cha kusamvera kwawoko. (Werengani Yeremiya 2:13; 17:13.) Choncho, ifeyo tili ndi zifukwa zomveka zopewera kuchita zinthu ngati Ayudawo n’kudzibweretsera mavuto oopsa. Yehova akupitiriza kutipatsa malangizo ambiri ochokera m’Mawu ake ouziridwa. Koma ngati tikufuna kuti “madzi amoyo” amenewa atipindulitse, tiyenera kuwaphunzira nthawi zonse komanso kuyesetsa kutsatira zimene tikuphunzirazo.
6. (a) Fotokozani mtima umene Mfumu Zedekiya anali nawo pa nkhani yomvera Yehova. (b) N’chifukwa chiyani mukuona kuti mfumuyo inachita zinthu mopanda nzeru?
6 Tsiku loti Mulungu aweruze Ayuda litatsala pang’ono kufika, zinali zofunika kwambiri kuti iwo ayambe kumvera Mulungu. Myuda aliyense amene ankafuna kuti Yehova azimukonda komanso kuti adzamuteteze, anafunika kulapa n’kuyamba kumvera Yehovayo. Nayenso Mfumu Zedekiya anafunika kusankha chochita pa nkhani imeneyi, koma iye analibe mtima wofunitsitsa kuchita zinthu zoyenera. Mwachitsanzo, pa nthawi ina anthu ake atamuuza kuti akufuna kupha Yeremiya, iye analephera kuwaletsa. Monga mmene taonera m’mutu wapitawu, mneneriyu anapulumuka chiwembucho mothandizidwa ndi Ebedi-meleki, ndipo kenako analimbikitsa Zedekiya kuti: “Chonde, mverani mawu a Yehova.” (Werengani Yeremiya 38:4-6, 20.) Choncho, zikuonekeratu kuti mfumuyo inafunikira kusankha kuyamba kumvera Mulungu ndi mtima wonse kuti zinthu ziiyendere bwino.
N’chifukwa chiyani m’pake kuti Yeremiya anauza Ayuda mobwerezabwereza kuti azimvera Mulungu?
TIKUFUNIKA KUMVERA YEHOVA MWAMSANGA
7. Kodi ndi mayesero ati amene mungakumane nawo pa nkhani yomvera?
7 Masiku anonso, kumvera ndi nkhani yofunika kwambiri ngati mmene zinalili m’nthawi ya Yeremiya. Kodi inuyo ndinu ofunitsitsa kumvera Yehova ndi mtima wonse? Mwachitsanzo, kodi zitachitika kuti mwangozi mwaona zithunzi zolaula pa Intaneti, kodi mungapitirizebe kuziyang’anitsitsa, kapena mungapewe mayeserowo potseka malo a pa Intanetiwo nthawi yomweyo? Nanga mungatani ngati munthu wa kusukulu kwanu kapena kuntchito kwanu yemwe si wa Mboni, atakufunsirani? Kodi mungalimbe mtima n’kumukana? Komanso kodi mungachite chidwi kapena munganyansidwe ndi mabuku a anthu ampatuko kapena malo awo a pa Intaneti? Mukakumana ndi mayesero amenewa kapena mayesero ena, muzikumbukira mawu a palemba la Yeremiya 38:20.
8, 9. (a) N’chifukwa chiyani ndi bwino kumvera akulu akamakuthandizani? (b) Kodi muyenera kuuona motani uphungu wobwerezabwereza wochokera kwa akulu?
8 Nthawi zambiri Yehova ankatumiza Yeremiya kuti akauze anthu ake uthenga wochonderera, monga wakuti: “Chonde, aliyense wa inu atembenuke kusiya njira yake yoipa ndipo muyambe kuyenda m’njira zabwino ndi kuchita zinthu zabwino.” (Yer. 7:3; 18:11; 25:5; werengani Yeremiya 35:15.) Mofanana ndi Yeremiya, akulu achikhristu masiku ano amayesetsa kuthandiza Akhristu anzawo amene moyo wawo wauzimu uli pangozi. Ngati nthawi ina akulu atakupatsani uphungu kuti mupewe kuchita zinthu zopanda nzeru kapena zolakwika, muyenera kumvera. Akamachita zimenezo, akuluwo amakhala ndi cholinga chofanana ndi cha Yeremiya.
9 Akulu angakukumbutseni mfundo za m’Malemba zimene anakuuzani kale m’mbuyomu. Muzikumbukira kuti kupereka uphungu mobwerezabwereza si kophweka, komanso kumakhala kovuta kwambiri ngati munthu amene akuthandizidwayo, akusonyeza mtima wangati wa Ayuda ambiri amene ankamva uthenga wa Yeremiya. Akulu akamayesa kukuthandizani mobwerezabwereza, muziona kuti imeneyo ndi njira imene Yehova akukusonyezerani chikondi. Kumbukiraninso kuti Yeremiya sakanafunikira kupereka machenjezowo mobwerezabwereza zikanakhala kuti anthuwo anamvera. Choncho, tikapatsidwa uphungu, ndi bwino kumvera nthawi yomweyo kuti tipewe kupatsidwa uphunguwo mobwerezabwereza.
YEHOVA SACHEDWA KUKHULULUKA KOMA SIKUTI AMANGOKHULULUKA MWACHISAWAWA
10. N’chifukwa chiyani Yehova sakhululuka machimo mwachisawawa?
10 M’dziko loipali, sitingakwanitse kumvera Yehova ndendende osalakwitsako chilichonse, ngakhale titayesetsa chotani. Choncho, tikuthokoza Mulungu chifukwa iye sachedwa kutikhululukira tikalakwa. Komabe, sikuti iye amangokhululuka machimo mwachisawawa. N’chifukwa chiyani zili choncho? Chifukwa chakuti Yehova amanyansidwa kwambiri ndi uchimo. (Yes. 59:2) Motero, iye asanakhululukire munthu, amayamba waona kaye ngati munthuyo ali woyenereradi kumukhululukira.
11. N’chifukwa chiyani n’zosatheka kubisira Mulungu machimo?
11 Monga mmene taonera, kawirikawiri Ayuda ambiri a m’nthawi ya Yeremiya sankamvera Mulungu ndipo zimenezi zinkasonyeza kuti sakuyamikira kuleza mtima ndi chifundo cha Mulungu. Kodi masiku ano zingachitikenso kuti mmodzi mwa atumiki a Mulungu akhale ndi mtima ngati wa Ayudawo? Inde, zingachitike ngati iye atanyalanyaza malangizo a Yehova n’kuyamba kuchita tchimo. Nthawi zina, ena achitapo zimenezi mochita kuonetsera, monga kulowa m’banja pamene iwowo kapena mnzawoyo sali womasuka mwamalemba kuchita zimenezi. Komabe, ngakhale tchimo litakhala lobisika kwa anthu, moyo wauzimu wa munthu amene sakumvera Yehovayo umakhala pangozi. Munthu amene ali ndi moyo wachiphamaso angaganize kuti, ‘Palibe munthu amene angadziwe zimenezi.’ Koma zoona zake n’zakuti Mulungu amaona mumtima ndi m’maganizo mwathu ndipo angaone zimene munthu akuchita mobisa. (Werengani Yeremiya 32:19.) Ndiye kodi munthu amene waphwanyadi lamulo la Mulungu ayenera kutani?
12. Kodi akulu ayenera kuchita chiyani nthawi zina kuti ateteze mpingo?
12 Ayuda ambiri ankanyoza thandizo limene Yehova ankawapatsa mobwerezabwereza kudzera mwa Yeremiya. Mofanana ndi zimenezi, masiku anonso munthu amene wachita tchimo lalikulu nthawi zina amakhala wosalapa ndipo amakana thandizo limene akulu amupatsa. Zimenezi zikachitika, akulu ayenera kutsatira malangizo a m’Malemba oti ateteze mpingo pochotsa mumpingo munthu wolakwayo. (1 Akor. 5:11-13; onani bokosi lakuti “Moyo Wosatsatira Chilamulo,” patsamba 73.) Koma kodi zimenezo zikutanthauza kuti munthu wotero sangasinthenso mpaka kalekale ndipo Yehova sangathenso kumukonda? Ayi, sichoncho. Mwachitsanzo, kwa nthawi yaitali, Aisiraeli sankamvera Mulungu, komabe iye anawauza kuti: “Bwererani, inu ana opanduka. Ndidzachiritsa kusakhulupirika kwanu.” (Yer. 3:22)a Yehova amaitana anthu ochita zoipa kuti abwerere kwa iye, ndipo amachita kuwalimbikitsa kuti achite zimenezi.
N’chifukwa chiyani n’chinthu chanzeru kupempha Mulungu kuti atikhululukire tikalakwa?
MVERANI YEHOVA POBWERERA KWA IYE
13. Ngati munthu akufuna kubwerera kwa Yehova, kodi ayenera kuzindikira chiyani?
13 Mogwirizana ndi zimene Yeremiya ananena, kuti munthu abwerere kwa Mulungu, ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene ndachitazi n’zabwino?’ Kenako mogwirizana ndi mfundo za m’Malemba, munthuyo ayenera kuvomereza moona mtima yankho limene wapeza. Koma Ayuda osalapa a m’nthawi ya Yeremiya sanadzifunse funso limeneli. Iwo sanafune kuvomereza machimo awo, motero Yehova sanawakhululukire. (Werengani Yeremiya 8:6.) Mosiyana ndi zimenezi, munthu wochimwa amene walapa amazindikira kuti wanyozetsa dzina la Mulungu pamodzi ndi mpingo wachikhristu chifukwa chosamvera Yehova. Munthu amene walapadi amamva chisoni kwambiri akaganizira mmene zochita zakezo zakhudzira anthu osalakwa. Iye amafunikanso kuzindikira kuti ngati akufuna kuti Yehova aganizire pempho lake loti amukhululukire, iyeyo ayenera kumvetsa bwino kukula kwa tchimo limene anachitalo komanso mmene linakhudzira ena. Komabe pali zinanso zimene munthuyo ayenera kuchita kuti abwerere kwa Mulungu.
14. Kodi munthu angatani kuti ‘abwerere kwa Yehova’? (Onaninso bokosi lakuti “Kodi Kulapa N’kutani?”)
14 Munthu amene walapadi ayenera kudzifufuza kuti adziwe zolinga zake, zimene amalakalaka ndiponso makhalidwe ake. (Werengani Maliro 3:40, 41.) Munthuyo amaunika moyo wake bwinobwino kuti adziwe mbali zimene ali wofooka. Iye angafunike kudziunika pa nkhani monga kucheza ndi anthu omwe si amuna kapena akazi anzake, kumwa mowa kapena kusuta fodya, kugwiritsa ntchito Intaneti, komanso bizinezi kapena ntchito imene amagwira. Mofanana ndi mayi amene akusesa m’nyumba mwake, yemwe akuyesetsa mwakhama kusesa paliponse ndi malo obisika omwe n’cholinga choti nyumbayo ikhale yaukhondo, munthu amene walapadi ayenera kuchita khama kuti ayeretse maganizo ake komanso zimene amachita akakhala kwayekha. Iye ayenera ‘kubwerera kwa Yehova’ pochita zinthu zimene Mulungu akufuna ndiponso poyesetsa kuti moyo wake uzigwirizana ndi mfundo za Mulunguyo. Ayuda ena a m’nthawi ya Yeremiya anabwerera kwa Yehova “mwachiphamaso” chabe. Iwo ankanamizira kuti akumva chisoni kwambiri ndi machimo amene anachita koma sanasinthe mitima yawo kapena moyo wawo. (Yer. 3:10) Mosiyana ndi Ayudawo, munthu amene akupempha Yehova moona mtima kuti amukhululukire sayesa kupusitsa Yehovayo ndi mpingo wake. M’malo mongofuna kuoneka ngati munthu wabwino pamaso pa anthu ena, kapena kungofuna kuyambanso kucheza ndi achibale ake kapena anthu ena mumpingo, iye amasiyiratu machimo amene ankachita. Akachita zimenezi, Mulungu amam’khululukira ndipo amayambanso kumukonda.
15. Kodi munthu wolapadi amapereka mapemphero otani kwa Mulungu?
15 Pemphero ndi mbali yofunika kwambiri pa nkhani ya kulapa. Kale, kawirikawiri anthu ankakweza manja awo m’mwamba popemphera. Masiku ano, mogwirizana ndi zimene Yeremiya anafotokoza, munthu amene walapadi akamapemphera, ‘amachonderera Mulungu kumwamba ndi mtima wonse, ndipo [amakhala ngati] wakweza manja ake m’mwamba.’ (Maliro 3:41, 42) Munthu wochimwa amene walapadi amamva chisoni kwambiri mumtima mwake ndi zimene anachitazo, ndipo mtima umenewo umamuchititsa kuti ayambe kuchita zinthu zogwirizana ndi pempho lake lakuti Mulungu amukhululukire. Choncho mapemphero ake amakhala oona mtima ndiponso ochokera pansi pa mtima.
16. N’chifukwa chiyani n’chinthu chanzeru kubwerera kwa Mulungu?
16 Mosakayikira mungavomereze kuti munthu wochimwa amayenera kusiya kunyada n’kudzichepetsa kwambiri kuti afike povomerezadi machimo ake. Komabe, mfundo yaikulu ndi yakuti: Yehova akufuna kuti anthu ochimwa abwerere kwa iye. Mulungu akayang’ana mumtima mwa munthu wochimwa n’kuona kuti walapadi, nayenso amasangalala mumtima mwake. Popeza iye ndi wachifundo komanso wachikondi, amakhala ngati m’mimba mwake “mukubwadamuka” chifukwa chofunitsitsa kukhululukira anthu machimo awo, mofanana ndi mmene anachitira ndi Aisiraeli amene anabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo. (Yer. 31:20) N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Mulungu amapereka mtendere wa mumtima ndi chiyembekezo kwa anthu amene amamumvera. (Yer. 29:11-14) Iwo angakhalenso ndi malo m’gulu la atumiki odzipereka a Mulungu.
KUMVERA KUNGAKUTETEZENI
17, 18. (a) Kodi Arekabu anali ndani? (b) Monga mmene chithunzi cha patsamba 77 chikusonyezera, kodi iwo amadziwika bwino pa nkhani yotani?
17 Kumvera Yehova ndi mtima wonse n’kothandiza kwambiri. Tingaone zimenezi m’chitsanzo cha Arekabu a m’nthawi ya Yeremiya. Zaka zoposa 200 Yeremiya asanabadwe, iwo anapatsidwa malamulo angapo owaletsa zinthu zosiyanasiyana. Yemwe anawapatsa malamulowo anali kholo lawo Yehonadabu wamtundu wachikeni, amene pa nthawi ina anathandiza Yehu mokhulupirika kwambiri. Lamulo limodzi mwa malamulo amene iye anawapatsa linali lakuti asamamwe vinyo. M’nthawi ya Yeremiya, Yehonadabu anali atamwalira kalekale, komabe Arekabu anapitiriza kumumvera. Pofuna kuwayesa, Yeremiya anawatenga n’kupita nawo m’chipinda chodyera cha pakachisi ndipo anawaikira vinyo pamaso pawo n’kuwalimbikitsa kuti amwe. Koma iwo anamuyankha kuti: “Sitingamwe vinyo.”—Yer. 35:1-10.
18 Arekabu ankaona kuti kumvera kholo lawo lomwe linali litamwalira kalekale inali nkhani yofunika kwambiri. Mofanana ndi zimenezi, nawonso olambira oona ayenera kumvera malamulo a Mulungu wawo wamoyo mokhulupirika kwambiri. Yehova anasangalala kwambiri ndi mtima womvera umene Arekabu anali nawo, ndipotu mtima umenewu unawachititsa kukhala osiyana kwambiri ndi Ayuda, omwe anali osamvera. N’chifukwa chake Mulungu analonjeza Arekabu kuti adzawateteza pa nthawi ya tsoka limene linali litatsala pang’ono kubwera m’dzikolo. Monga mmene zinalili ndi Arekabu, masiku anonso Yehova akulonjeza anthu amene amamumvera ndi mtima wonse kuti adzawateteza pa chisautso chachikulu.—Werengani Yeremiya 35:19.
N’chifukwa chiyani kulapa tikachita tchimo lalikulu kuli mbali yofunika kwambiri yosonyezera kumvera? Kodi kumvera kungathandize bwanji munthu kuti apewe kuchita zinthu zimene zingadzamuchititse kuti afunikire kulapa?
YEHOVA AMATHANDIZA ANTHU AMENE AMAMUMVERA
19. Kodi Mulungu angakutetezeni bwanji ngati mukumumvera?
19 Tisaganize kuti Mulungu ankangoteteza anthu ake a m’mbuyo okha basi. Ngakhale masiku ano, Yehova amateteza anthu omvera kuti asakumane ndi ngozi mwauzimu. Mofanana ndi mipanda italiitali imene inkateteza mizinda yakale kwa adani, malamulo a Mulungu amateteza anthu amene amawaphunzira ndi kuwagwiritsa ntchito nthawi zonse. Kodi inuyo mupitiriza kukhala m’kati mwa mpanda wotiteteza, womwe ndi malamulo a Mulungu okhudza makhalidwe abwino? Dziwani kuti zinthu zidzakuyenderani bwino ngati mungachite zimenezi. (Yer. 7:23) Pali nkhani zambiri zimene zakhala zikuchitikira anthu osiyanasiyana zomwe zikutsimikizira mfundo imeneyi.—Onani bokosi lakuti “Kumvera Yehova Kumateteza.”
20, 21. (a) Mukamatumikira Yehova, kodi simuyenera kukayikira za chiyani? (b) Kodi Mfumu Yehoyakimu anachita chiyani atamva uthenga wa Mulungu kudzera mwa Yeremiya?
20 Anthu otsutsa amachititsa kuti atumiki a Mulungu azivutika kumulambira. Anthu amenewa angakhale a m’banja mwathu, kuntchito kapena kusukulu, kapenanso iwo angakhale ena mwa akuluakulu a boma kapena anthu audindo m’dera limene tikukhala. Komabe, dziwani kuti ngati mupitirizabe kumvera Yehova ndi mtima wonse, iye sadzakusiyani ngakhale zinthu zitavuta chotani. Musaiwale kuti Mulungu analonjeza Yeremiya kuti adzamuthandiza ngakhale atamatsutsidwa ndi anthu oopsa kwambiri. Ndipotu Yehova anachitadi zimenezo. (Werengani Yeremiya 1:17-19.) Umboni umodzi wotsimikizira kuti Mulungu ankathandizadi Yeremiya, ndi zomwe zinachitika m’nthawi ya Mfumu Yehoyakimu.
21 Pa mafumu onse a Isiraeli, ndi mafumu ochepa zedi amene ankatsutsa atumiki a Mulungu moopsa kwambiri, ngati Yehoyakimu. Tingamvetse zimenezi tikaona zimene zinachitikira mneneri Uliya, amene anakhalapo m’masiku a Yeremiya. Yehoyakimu, yemwe anali mfumu yoipa kwambiri, anatumiza anthu kuti akagwire Uliya amene anali atathawira kudziko lina. Anthuwo atagwira mneneri wa Yehovayo n’kubwera naye, mfumuyo inamupha. (Yer. 26:20-23) Ndiyeno m’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Yehoyakimu, Yehova analamula Yeremiya kuti alembe mawu onse amene Yehovayo anali atalankhula mpaka kufika pa nthawi imeneyo, ndipo kenako anamuuza kuti akawawerenge mokweza m’kachisi. Yehoyakimu atamva zimenezi, anatumiza munthu kuti akatenge mpukutu wa Yeremiyawo ndipo analamula nduna yake kuti iwerenge mpukutuwo pamaso pake. Pamene mpukutuwo unkawerengedwa, Yehoyakimu ankang’amba gawo limene ndunayo yamaliza kuwerenga n’kuliponya pamoto. Iye ankachita zimenezi ngakhale kuti ena mwa akalonga ake anayesetsa kumuletsa. Kenako mfumuyo inatumiza anthu kuti akagwire ndi kumanga Yeremiya ndi Baruki. Koma kodi zimenezi zinatheka? Ayi, Yeremiya ndi Baruki sanamangidwe chifukwa “Yehova anawabisa.” (Yer. 36:1-6; werengani Yeremiya 36:21-26.) Yehova sanalole kuti Yehoyakimu avulaze atumiki ake awiri okhulupirikawo.
22, 23. Kodi zimene zinachitikira mlongo wina wa m’chigawo chapakati ku Asia zikukutsimikizirani bwanji kuti Mulungu amasamalira atumiki ake?
22 Masiku anonso, ngati Yehova angaone kuti n’zoyenera, angateteze atumiki ake powabisa kuti asavulazidwe. Koma nthawi zambiri iye amawapatsa nzeru ndiponso amawathandiza kuti akhale olimba mtima kuti apitirizebe kumumvera komanso kulalikira uthenga wabwino. Mlongo wina yemwe tingomutchula kuti Gulistan, ndi chitsanzo cha munthu amene Yehova anamuthandiza. Mlongoyu amakhala m’dera lina lalikulu m’chigawo chapakati ku Asia, ndipo akulera yekha ana anayi. Kwa nthawi yaitali, wa Mboni za Yehova analipo yekha m’derali, ndipo ntchito yolalikira za Ufumu kumeneko ndi yoletsedwa ndi boma. Popeza kuderali kulibe mpingo wa Mboni za Yehova, mlongoyu amayenda mtunda wa makilomita 400 kuchokera kumene akukhala kuti akafike kumene kuli mpingowu. Zimenezi zimachititsa kuti mlongo Gulistan azingokumana mwa apo ndi apo ndi Akhristu anzake okhwima mwauzimu. Ngakhale kuti iye amatsutsidwa komanso amakumana ndi mavuto ena, amalalikira kunyumba ndi nyumba ndipo amapeza anthu ambiri achidwi. Malinga ndi lipoti laposachedwapa, iye ankaphunzira Baibulo ndi anthu okwana 20, ndiponso ankasamalira mwauzimu kagulu ka nkhosa za Yehova komwe kakukula m’deralo.
23 Mulungu ndi wokonzeka kuthandiza inuyo komanso atumiki ake ena omvera ngati mmene anathandizira Yeremiya ndiponso anthu ena a Mboni monga Gulistan. Choncho khalani otsimikiza ndi mtima wonse kumvera Mulungu monga Wolamulira, osati anthu. Mukachita zimenezi, mavuto osiyanasiyana monga kutsutsidwa, sadzakulepheretsani kutamanda Mulungu yekhayo yemwe ndi woona, pakati pa anthu a m’gawo lanu.—Yer. 15:20, 21.
24. Kodi ndi madalitso ati amene mumapeza chifukwa chokhala anthu omvera?
24 N’zosatheka kukhala wosangalaladi ngati tikukhala ndi moyo wosadalira Mlengi wathu. (Yer. 10:23) Popeza mwaphunzira zimene Yeremiya analemba pa nkhani ya kumvera, kodi tsopano mukutha kuona njira zimene inuyo mungasonyezere kuti mukulola Yehova kuti azikutsogolerani pa mbali zonse za moyo wanu? Njira yokhayo imene ingatithandize kukhala ndi moyo wosangalaladi, ndiyo kutsatira malamulo ake. Ndipotu Yehova akutilimbikitsa kuti: “Muzimvera mawu anga . . . kuti zinthu zikuyendereni bwino.”—Yer. 7:23.
Pa ubwenzi wanu ndi Mulungu, kodi mungagwiritse ntchito bwanji mfundo zokhudza kumvera zimene mwaphunzira m’buku la Yeremiya?
a Apa Yehova ankalankhula ndi anthu a mu ufumu wakumpoto wa Isiraeli wa mafuko 10. Pamene Yeremiya ankapereka uthengawu n’kuti anthu amenewa atakhala mu ukapolo kudziko la eni kwa zaka pafupifupi 100. Ndipo Yeremiya anasonyeza kuti pofika m’nthawi yake, mtunduwo unali usanalapebe. (2 Maf. 17:16-18, 24, 34, 35) Komabe, munthu aliyense payekha akanatha kubwerera kwa Mulungu ngakhalenso kubwerera kudziko lakwawo kuchoka ku ukapolo.